Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulendo Umene Unasintha Maganizo Ake

Ulendo Umene Unasintha Maganizo Ake

Ulendo Umene Unasintha Maganizo Ake

“SINDINACHEDWE kuwauza abale anga za ‘angelo’ awiri omwe Mulungu ananditumizira.” Analemba motero bambo wina yemwe anachezeredwa ndi atsikana awiri a Mboni za Yehova. Panthawi imene atsikanawo amakacheza kwa bamboyo panali patangodutsa milungu yochepa mkazi wake yemwe anali naye pabanja zaka 45 atamwalira. Choncho bamboyo anali ndi chisoni chachikulu. Ana ake achikulire anam’tonthoza, komabe iwo ankakhala kutali kwambiri. Panalibe mabwenzi ndi anthu oyandikana nawo nyumba omwe ankabwera kudzam’chezera.

“Sindipempheranso kwa Mulungu,” anatero bamboyo powauza atsikana omwe anadzam’chezerawo. Ndiyeno, atsikanawo anakhudzidwa mtima kwambiri ndipo anam’siyira bamboyo kapepala kankhani za m’Baibulo kakuti Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Okondedwa Akufa? Madzulo atsiku lomwelo, bamboyo anapeza chitonthozo atawerenga kapepalako.

Patapita masiku ochepa, a Mboni za Yehova aja anabweranso. Iwo anakumbukira za chisoni chomwe bamboyo anali nacho pa kucheza kwawo koyamba, choncho anabweranso kudzaona kuti ali bwanji. Bamboyo analemba kuti: “Ndinadabwa kwambiri kuona anthu omwe sindinkadziwana nawo, akundidera nkhawa ndiponso akufuna kudziwa za ine kuti ndili bwanji.” Analimbikitsidwa ndi mfundo zomwe anawerenga naye m’Baibulo, ndipo atsikanawo anauza bamboyo kuti adzabweranso tsiku lina. Bamboyo anasangalala kwambiri ndipo analemba mfundo zimenezi m’kalata yomwe anaitumiza ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya m’deralo.

Asanasamukire kudera lina la pafupi ndi komwe kuli ana ake, bamboyu anakasonkhana ndi Mboni za Yehova ndipo misonkhano itatha, anaitanidwa kubanja la mmodzi mwa atsikana aja komwe anakacheza ndi kudyera limodzi. Iye analemba kuti: “Ndikusamuka m’dera lino, koma ndipitiriza kukumbukira m’mapemphero anga anthu omwe anadzandichezera aja ndiponso tchalitchi chawo. Inde, masiku ano ndikumapemphera kwambiri. Maganizo anga asinthiratu. Atsikana a Mboni za Yehova aja andithandiza kwambiri, ndipo sindidzasiya kuwathokoza.”