Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ganizirani za Ubwino wa Gulu la Yehova

Ganizirani za Ubwino wa Gulu la Yehova

Ganizirani za Ubwino wa Gulu la Yehova

“Tidzakhuta nazo zokoma za m’nyumba yanu.”​—SALMO 65:4.

1, 2. (a) Kodi ntchito yomwe inkachitidwa pakachisi inawakhudza motani anthu a Mulungu? (b) Kodi ndi thandizo lotani lomwe Davide anapereka pantchito yomanga kachisi?

DAVIDE wa ku Israyeli wakale ndi mmodzi mwa anthu odziwika kwambiri ofotokozedwa m’Malemba Achihebri. Munthuyu yemwe anali mbusa, woimba, mneneri ndi mfumu, ankakhulupirira kwambiri Yehova Mulungu. Ubwenzi wolimba umene Davide anali nawo ndi Yehova unam’limbikitsa kukhala ndi chikhumbo chofuna kumangira Mulungu nyumba. Nyumba kapena kachisi ameneyu anadzakhala likulu la kulambira koona m’Israyeli. Davide ankadziwa kuti kachisi ndiponso ntchito yomwe inkachitika pakachisipo idzabweretsa chimwemwe ndi madalitso kwa anthu a Mulungu. Motero, Davide anaimba kuti: “Wodala munthuyo [amene inu Yehova] mum’sankha, ndi kum’yandikizitsa, akhale m’mabwalo anu: Tidzakhuta nazo zokoma za m’nyumba yanu, za m’malo oyera a Kachisi wanu.”​—Salmo 65:4.

2 Davide sanaloledwe kuyang’anira ntchito yomanga nyumba ya Yehova. M’malo mwake, udindo wapadera umenewu unapatsidwa kwa mwana wake Solomo. Davide sanadandaule poona kuti udindo umene ankaufuna kwambiri unapatsidwa kwa munthu wina. Chomwe ankafuna kwambiri chinali choti kachisi amangidwe. Iye anachirikiza ntchitoyi ndi mtima wonse mwa kupatsa Solomo mapulani a kamangidwe omwe Yehova anam’patsa. Ndiponso, Davide anagawa Alevi masauzande ambiri m’magulu otumikira ntchito zosiyanasiyana ndipo anapereka golidi ndi siliva wambiri ku ntchito yomanga kachisi.​—1 Mbiri 17:1, 4, 11, 12; 23:3-6; 28:11, 12; 29:1-5.

3. Kodi atumiki a Mulungu amakhala ndi maganizo otani pa dongosolo lonse la kulambira koona?

3 Aisrayeli okhulupirika anachirikiza nawo ntchito zonse za kulambira koona zomwe zinkachitika pa nyumba ya Mulungu. Ifenso monga atumiki amakono a Yehova, timachirikiza nawo dongosolo lonse la kulambira lochitika m’mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova. Mwa kuchita zimenezi timasonyeza kuti tili ndi maganizo ofanana ndi a Davide. Tilibe mzimu wodandaula. M’malo mwake, timaganizira za ubwino wa gulu la Mulungu. Kodi mwaganizirapo za zinthu zambiri zomwe tifunikiradi kuyamikira? Tiyeni tikambirane zina mwa zinthu zimenezi.

Kukhala Oyamikira Chifukwa cha Omwe Akutitsogolera

4, 5. (a) Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amachita bwanji ntchito yake? (b) Kodi Mboni zina zanena chiyani pankhani ya chakudya chauzimu chimene zimalandira?

4 Tili ndi zifukwa zomveka zokhalira oyamikira chifukwa cha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene waikidwa ndi Yesu Kristu kuyang’anira zinthu zake za padziko lapansi. Gulu la kapolo la Akristu odzozedwa ndi mzimu limatsogolera ntchito yolalikira uthenga wabwino, limakonza misonkhano, ndipo limafalitsa mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero zoposa 400. Anthu mamiliyoni ambiri padziko lapansi amadya nawo moyamikira ‘chakudya cha panthawi yake’ chauzimu chimenechi. (Mateyu 24:45-47) Ndithudi, palibe chifukwa chodandaulira.

5 Kwa zaka zambiri, Mboni ya Yehova ina yachikulire dzina lake Elfi, yapeza chitonthozo ndi thandizo chifukwa chogwiritsa ntchito malangizo a m’Malemba opezeka m’zofalitsa za gulu la kapolo. Chifukwa cha kuyamikira kwambiri iye analemba kuti: “Kodi ndikadatani pakadapanda gulu la Yehova?” Peter ndi Irmgard iwonso akhala atumiki a Mulungu kwa zaka zambiri. Irmgard akuyamikira chifukwa cha zofalitsa zonse zopangidwa ndi “gulu la Yehova lachikondi ndiponso lomwe limasamala.” Zofalitsa zimenezi zikuphatikizapo zinthu zomwe amakonzera anthu ofunikira thandizo lapadera, monga akhungu ndi ogontha.

6, 7. (a) Kodi ntchito zonse za mipingo padziko lapansi zimayang’aniridwa motani? (b) Kodi anthu ena anena chiyani pankhani ya mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova?

6 Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limaimira “kapolo wokhulupirika.” Bungweli ndi gulu laling’ono la amuna odzozedwa ndi mzimu omwe akutumikira ku likulu lapadziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, mu mzinda wa New York. Bungwe Lolamulira limaika atumiki a Yehova okhwima mwauzimu kuti atumikire pa maofesi a nthambi omwe amayang’anira ntchito ya mipingo yoposa 98,000 padziko lonse. Amuna omwe amakwaniritsa ziyeneretso za m’Baibulo amaikidwa kukhala akulu ndi atumiki othandiza m’mipingo imeneyi. (1 Timoteo 3:1-9, 12, 13) Akulu amatsogolera ndipo amaweta mwachikondi gulu la nkhosa la Mulungu lomwe lili mwa iwo. Lili dalitso lalikulu kukhala mbali ya gulu la nkhosa limeneli ndiponso kuona chikondi ndi umodzi zomwe zili pa gulu lonse la abale.​—1 Petro 2:17; 5:2, 3.

7 M’malo modandaula, anthu nthawi zambiri amayamikira zimene akulu akuchita, powatsogolera mwauzimu ndiponso mwachikondi. Mwachitsanzo, taganizirani za Birgit, Mkristu wokwatiwa wa zaka za m’ma 30. Nthawi imene anali ndi zaka za pakati pa 13 ndi 19 anayamba kucheza ndi anthu a makhalidwe oipa ndipo anatsala pang’ono kuchita cholakwa. Koma malangizo omveka bwino a m’Baibulo omwe akulu anam’patsa ndiponso thandizo la Akristu anzake zinamupulumutsa ku zinthu zomwe zikanamuwononga. Kodi Birgit tsopano amamva bwanji? Iye anati: “Ndikuyamikira kwambiri kuti ndidakali m’gulu la Yehova labwino kwambiri.” Andreas wa zaka 17 anati: “Ilitu ndi gulu la Yehova, gulu labwino kuposa lina lililonse padziko lapansi.” Kodi sizoona kuti tiyenera kuyamikira chifukwa cha ubwino wa mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova?

Anthu Omwe Akutsogolera ndi Opanda Ungwiro

8, 9. Kodi anthu ena a m’nthawi ya Davide anachita zinthu motani, ndipo iye anatani ndi zimene anachitazo?

8 N’zoona kuti amene asankhidwa kuti atsogolere kulambira koona ndi opanda ungwiro. Onse amalakwa, ndipo ena ali ndi zofooka zomwe akuyesetsa kulimbana nazo. Kodi tifunika kuvutika maganizo chifukwa cha zimenezi? Ayi. Ngakhale anthu omwe anapatsidwa udindo waukulu m’Israyeli wakale anachita zolakwa zazikulu. Mwachitsanzo, Davide adakali wachinyamata anapemphedwa kuti azikaimbira nyimbo Mfumu Sauli n’cholinga chomukhazika mtima pansi pamavuto ake. Patapita nthawi, Sauli ankafuna kupha Davide, ndipo Davide anathawa kuti apulumutse moyo wake.​—1 Samueli 16:14-23; 18:10-12; 19:18; 20:32, 33; 22:1-5.

9 Aisrayeli ena anachita zinthu mwachinyengo. Mwachitsanzo, Yoabu mkulu wa ankhondo a Davide, anapha Abineri wachibale wa Sauli. Abisalomu anachitira chiwembu bambo ake, Davide, chifukwa chofuna ufumu. Ndipo Ahitofeli, phungu wokhulupirika wa Davide ndiye anam’pereka. (2 Samueli 3:22-30; 15:1-17, 31; 16:15, 21) Koma Davide sanakhale wodandaula kwambiri kapena kusiya kulambira koona. Ndipotu, Davide anachita zinthu mosiyana kwambiri. Mavuto anapangitsa Davide kudalira kwambiri Yehova ndiponso kukhala ndi maganizo abwino omwe anali nawo nthawi imene ankathawa chifukwa cha Sauli. Panthawi imeneyo, Davide anaimba kuti: “Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu: Ndipo ndithawira ku mthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita.”​—Salmo 57:1.

10, 11. Kodi Gertrud anakumana ndi zotani ali wachitsikana, ndipo ananena chiyani za kupanda ungwiro kwa Akristu anzake?

10 Palibe chifukwa chodandaulira tikamaona chinyengo chikuchitika m’gulu la Mulungu masiku ano. Yehova, angelo ndiponso abusa auzimu sangalekerere anthu achinyengo ndi oipa mumpingo wachikristu. Komabe ife tonse timayang’anizana ndi kupanda ungwiro kwathu ndiponso kwa atumiki ena a Mulungu.

11 Nthawi ina ali wachitsikana, Gertrud yemwe wakhala wolambira Yehova kwa nthawi yaitali, anam’namizira kuti anali munthu wachinyengo osati wolengeza Ufumu wa nthawi zonse. Kodi anatani? Kodi Gertrud anang’ung’udza chifukwa cha zimene anam’chitirazi? Ayi. Atatsala pang’ono kumwalira mu 2003 ali ndi zaka 91, iye anakumbukira zomwe zinam’chitikira ndipo anati: “Pamoyo wanga wonse zochitika zimenezi zandiphunzitsa kuti ngakhale anthu ena alakwitse zinthu, Yehova amatsogolera ntchito yake yofunika, ndipo pantchitoyi amagwiritsa ntchito anthu opanda ungwirofe.” Pamene Gertrud ankakhudzidwa ndi kupanda ungwiro kwa atumiki ena a Mulungu, iye ankapemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima.

12. (a) Kodi n’chitsanzo choipa chotani chomwe Akristu ena a m’nthawi ya atumwi anasonyeza? (b) Kodi tiyenera kuika maganizo athu pa chiyani?

12 Popeza kuti ngakhale Akristu omwe ndi okhulupirika ndiponso odzipereka kwambiri ndi opanda ungwiro, mtumiki woikidwa akalakwitsa, tiyeni tipitirize kuchita “zinthu zonse kopanda madandaulo.” (Afilipi 2:14) Zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri ngati tingatsatire chitsanzo choipa cha anthu ochepa a mumpingo wachikristu wa m’nthawi ya atumwi. Malinga n’kunena kwa wophunzira Yuda, aphunzitsi onyenga a m’nthawiyi ananyalanyaza ulamuliro ndipo ankalankhula monyoza aulemerero. Ndiponso, ochita zoipa amenewa anali ong’ung’udza, okonda kudandaula za moyo wawo. (Yuda 8, 16) Tiyeni tipewe moyo wa anthu ong’ung’udza ndipo tiike maganizo athu pa zinthu zabwino zimene timalandira kudzera mwa “kapolo wokhulupirika.” Tiyeni tikhale oyamikira ubwino wa gulu la Yehova ndipo ‘tichite zinthu zonse kopanda madandaulo.’

“Mawu Awa Ndi Osautsa”

13. Kodi anthu ena anachita chiyani atamva ziphunzitso zina za Yesu Kristu?

13 M’nthawi ya atumwi anthu ena ankadandaula zochita za atumiki oikidwa, koma ena anadandaula ndi zomwe Yesu ankaphunzitsa. Monga momwe lemba la Yohane 6:48-69 likunenera, Yesu anati: “Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nawo moyo wosatha.” Atamva mawu amenewa, “ambiri a akuphunzira ake . . . anati, Mawu awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani?” Yesu anadziwa kuti “akuphunzira ake alikung’ung’udza chifukwa cha ichi.” Kuwonjezera apo, chifukwa cha zimenezi “ambiri a [iwo] anabwerera m’mbuyo, ndipo sanayendayendanso ndi Iye.” Koma si ophunzira onse omwe ankang’ung’udza. Taonani zimene zinachitika Yesu atafunsa atumwi khumi ndi awiri aja kuti: “Nanga inunso mufuna kuchoka?” Mtumwi Petro anayankha kuti: “Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha. Ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziwa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu.”

14, 15. (a) N’chifukwa chiyani anthu ena amakhumudwa ndi mbali zina za ziphunzitso zachikristu? (b) Kodi tingaphunzirepo chiyani pa zimene zinachitikira Emanuel?

14 Masiku ano, anthu ochepa kwambiri pakati pa anthu a Mulungu akhumudwa ndi mbali zina za ziphunzitso zachikristu ndipo adandaula ndi zochita za mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova. N’chifukwa chiyani zimenezi zimachitika? Kudandaula kotero nthawi zambiri kumachitika chifukwa chosadziwa mmene Mulungu amachitira zinthu. Mlengi amauza anthu ake choonadi pang’onopang’ono. Chotero, kamvedwe kathu ka Malemba nthawi zina kangathe kusintha. Atumiki ambiri a Yehova amasangalala ndi kusintha koteroko. Ochepa ‘amapambanitsa kukhala olungama’ ndipo amakhumudwa pakakhala kusintha. (Mlaliki 7:16) Mwina kunyada n’kumene kumachititsa zimenezi ndipo ena agwidwa m’msampha wa kuyendera maganizo awo. Kaya tili ndi zifukwa zotani zochitira zimenezi, kung’ung’udza kotero n’koopsa, chifukwa kungatipangitse kubwerera kudzikoli ndi njira zake.

15 Mwachitsanzo, Emanuel anali Mboni yomwe inkatsutsa zinthu zina zopezeka m’zofalitsa za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Iye anasiya kuwerenga zofalitsa zathu zachikristu ndipo m’kupita kwa nthawi anauza akulu a pa mpingo umene ankasonkhana kuti sakufuna kukhalanso wa Mboni za Yehova. Koma patapita nthawi yochepa, Emanuel anazindikira kuti ziphunzitso za gulu la Yehova zinali zolondola. Iye anakumana ndi Mboni, n’kuvomereza kulakwa kwake ndipo anabwezeretsedwa kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Chifukwa cha zimenezi, anakhalanso munthu wosangalala.

16. Kodi n’chiyani chomwe chingatithandize kuthetsa kukayikira ziphunzitso zina zachikristu?

16 Kodi tingachite chiyani tikakumana ndi chiyeso chofuna kung’ung’udza chifukwa chokayikira ziphunzitso zina za gulu la Yehova? Tisachite zinthu mopupuluma. M’kupita kwa nthawi “kapolo wokhulupirika” angathe kufalitsa zinthu zina zimene zingayankhe mafunso athu ndi kuthetsa kukayikira kwathu konse. Ndi nzeru yabwino kupempha akulu achikristu kuti atithandize. (Yuda 22, 23) Pemphero, phunziro laumwini ndiponso kucheza ndi Akristu anzathu okonda zauzimu kungatithandizenso kuthetsa kukayikira kulikonse. Ndipo zingatipangitsenso kuyamikira kwambiri choonadi cha m’Baibulo cholimbitsa chikhulupiriro chathu chimene taphunzira kudzera m’njira yomwe Yehova akulankhulira nafe.

Khalani ndi Maganizo Abwino

17, 18. M’malo mong’ung’udza, kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani, ndipo n’chifukwa chiyani?

17 Kunena zoona, anthu opanda ungwiro ali ndi chibadwa chofuna kuchita tchimo, ndipo anthu ena amakonda kwambiri kudandaula popanda zifukwa zomveka. (Genesis 8:21; Aroma 5:12) Koma ngati tingakhale ndi chizolowezi chodandaula, tingaike pangozi ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu. Chotero, tifunika kuthetsa kung’ung’udza kulikonse komwe kungayambe mwa ife.

18 M’malo modandaula chifukwa cha mmene zinthu zikuyendera mumpingo, tifunika kukhala ndi maganizo abwino ndiponso ndandanda yomwe idzatipangitsa kukhala ndi zinthu zambiri zochita, kukhala achimwemwe, opembedza, osamala pochita zinthu komanso kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. (1 Akorinto 15:58; Tito 2:1-5) Yehova ndi yemwe akuyendetsa zinthu zonse m’gulu lake, ndipo Yesu amadziwa zimene zikuchitika mumpingo uliwonse, monga momwe ankadziwira m’nthawi ya atumwi. (Chivumbulutso 1:10, 11) Moleza mtima, dikirirani Mulungu ndi Kristu, Mutu wa mpingo. Abusa otsogolera angagwiritsidwe ntchito kukonza zinthu zomwe zingafunikire kusintha.​—Salmo 43:5; Akolose 1:18; Tito 1:5.

19. Kodi tiyenera kuyang’ana pa chiyani mpaka nthawi imene Ufumu udzayendetse zochita zonse za anthu?

19 Posachedwapa dongosolo loipali lidzatha, ndipo Ufumu wa Mesiya udzayamba kulamulira zochita zonse za anthu. Mpaka pamene nthawi imeneyo idzakwane, n’kofunika kuti aliyense wa ife akhale ndi maganizo abwino. Zimenezi zidzatithandiza kuzindikira makhalidwe abwino a Akristu anzathu, m’malo mongoyang’ana zolakwa zawo. Kuyang’ana mbali zabwino za umunthu wawo kudzatithandiza kukhala osangalala. M’malo moti kung’ung’udza kutitopetse, tidzalimbikitsidwa ndipo tidzakhala olimba mwauzimu.

20. Kodi kukhala ndi maganizo abwino kungatithandize kuti tikhale ndi madalitso otani?

20 Kukhala ndi maganizo abwino kudzatithandizanso kukumbukira madalitso ambiri amene tili nawo chifukwa chogwirizana ndi mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova. Padziko lonse lapansi ndi gulu lokhali lomwe lili lokhulupirika kwa Mfumu ya chilengedwe chonse. Kodi mumamva bwanji za mfundo imeneyi ndiponso mwayi wolambira Mulungu woona yekha, Yehova? Maganizo anu akhale monga a Davide yemwe anaimba kuti: “Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu. Wodala munthuyo mum’sankha, ndi kum’yandikizitsa, akhale m’mabwalo anu: Tidzakhuta nazo zokoma za m’nyumba yanu.”​—Salmo 65:2, 4.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oyamikira chifukwa cha anthu omwe akutsogolera mumpingo?

• Kodi tiyenera kuchita chiyani abale omwe akutsogolera akamalakwitsa zinthu?

• Kodi tiyenera kuona bwanji kusintha kwa kamvedwe ka Malemba?

• Kodi n’chiyani chomwe chingathandize Mkristu kuthetsa kukayikira?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 20]

Davide anapatsa Solomo mapulani omangira kachisi ndipo anachirikiza kulambira koona ndi mtima wonse

[Chithunzi patsamba 23]

Akulu achikristu amasangalala kuthandiza ena mwauzimu