Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
ANTHU anakumana ndi vuto loopsa kwambiri kuchiyambi kwenikweni kwa mbiri yawo. Mngelo wina anapandukira ulamuliro wa Mlengi wake. Mngelo wopandukayu ananyengerera mkazi woyambirira, Hava, kuti adye chipatso choletsedwa. Pofotokoza zomwe zidzachitikire mkaziyo limodzi ndi mwamuna wake, Adamu, mngeloyo anati: “Kufa simudzafai; chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 2:16, 17; 3:1-5) M’kupita kwa nthawi, mngelo wopandukayo anayamba kutchedwa Mdyerekezi ndi Satana.—Chivumbulutso 12:9.
Kodi Hava anamvera Satana? Baibulo limatiuza kuti: “Anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m’maso, mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene ali naye, nadya iyenso.” (Genesis 3:6) Inde, anthu awiri oyambirirawa, Adamu ndi Hava, anagwirizana ndi Satana pa kupanduka kwake. Motero, anataya mwayi woti iwo ndi ana awo akhale m’Paradaiso. Ana awo, omwe akanabadwa ali angwiro ndipo ali ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya, anatengera uchimo ndi imfa kuchokera kwa makolo awo.—Aroma 5:12.
Kodi Yehova Mulungu, yemwe ndi Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse, anachitapo chiyani? Anakonza zokhazikitsa dongosolo lokhululukira anthu machimo. (Aroma 5:8) Yehova Mulungu anakhazikitsanso dongosolo la boma loti lithane ndi vutoli. Dongosolo limeneli limatchedwa “Ufumu wa Mulungu.” (Luka 21:31) Ufumu umenewu, womwe unakhazikitsidwa monga nthambi ya ulamuliro wa chilengedwe chonse wa Mulungu, uli ndi cholinga choti ukwaniritse.
Kodi cholinga cha Ufumu wa Mulungu n’chiyani? Kodi zina mwa mbali zake n’zotani, ndipo n’zosiyana motani ndi ulamuliro wa anthu? Kodi anakonza zoti Ufumu umenewu udzayambe liti kulamulira? Mafunso amenewa ayankhidwa m’nkhani yotsatirayi.