Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachitatu ndi Chachinayi cha Masalmo

Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachitatu ndi Chachinayi cha Masalmo

Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachitatu ndi Chachinayi cha Masalmo

POPEMPHERA kwa Mulungu, wamasalmo anafunsa kuti: “Adzafotokozera chifundo chanu kumanda kodi, chikhulupiriko chanu ku malo a chiwonongeko?” (Salmo 88:11) N’zodziwikiratu kuti yankho lake n’loti ayi. Sitingatamande Yehova popanda moyo. Kutamanda Yehova n’chifukwa chokwanira chokhalira moyo, ndipo kukhala ndi moyo kuyenera kutilimbikitsa kum’tamanda.

Chigawo chachitatu ndi chachinayi cha Masalmo, kuyambira Salmo 73 mpaka 106, zimatipatsa zifukwa zambiri zoti titamande Mlengi ndi kulemekeza dzina lake. Kuganizira masalmo amenewa kungakulitse kuyamikira kwathu “Mawu a Mulungu” ndipo kungatilimbikitse kuti tiwonjezere ndi kuwongolera mawu athu otamanda Mulungu. (Ahebri 4:12) Tiyeni tione mosamala kwambiri zigawozi, kuyambira chigawo chachitatu cha Masalmo.

“KUNDIKOMERA KUYANDIKIZA KWA MULUNGU”

((Salmo 73:1–89:52)

Masalmo 11 oyambirira a chigawo chachitatuchi ndi nyimbo za Asafu kapena za anthu a nyumba ya Asafu. Nyimbo yoyamba ikufotokoza chomwe chinapulumutsa Asafu kuti asasokeretsedwe ndi maganizo olakwika. Iye anasankha bwino ndipo anaimba kuti: “Ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu.” (Salmo 73:28) Salmo 74 ndi nyimbo ya maliro a kuwonongedwa kwa Yerusalemu. Masalmo 75, 76, ndi 77 amafotokoza Yehova kukhala Woweruza wolungama, Mpulumutsi wa ofatsa ndiponso Womva pemphero. Salmo 78 limafotokoza mbiri ya Israyeli kuyambira nthawi ya Mose mpaka nthawi ya Davide. Salmo 79 limafotokoza kuwonongedwa kwa kachisi. Salmo 80 ndi pemphero lopempha kubwezeretsedwa kwa anthu a Mulungu. Salmo 81 lili ndi malangizo olimbikitsa anthu kumvera Yehova. Salmo 82 ndi pemphero losonyeza chiweruzo cha Mulungu kwa oweruza oipa. Ndipo Salmo 83 lilinso pemphero la chiweruzo cha Mulungu kwa adani ake.

Nyimbo ya ana a Kora imati: “Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova.” (Salmo 84:2) Salmo 85 ndi pempho lofuna madalitso a Mulungu pa anthu omwe anabwerako kuukapolo. Salmo limeneli limagogomezera kuti madalitso auzimu ndi abwino kwambiri kuposa madalitso akuthupi. Mu Salmo 86, Davide akupempha Mulungu kuti amuteteze ndi kumulangiza. Mu Salmo 87, muli nyimbo ya Ziyoni ndiponso ya anthu omwe anabadwira ku malowa. Ndiyeno Salmo 88 ndi pemphero kwa Yehova. Mu Salmo 89, anagogomezera kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova komwe kuli mu pangano la Davide. Salmo limeneli linalembedwa ndi Etani, amene mwina anali mmodzi mwa amuna anayi anzeru m’masiku a Solomo.​—1 Mafumu 4:31.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

73:9—Kodi ndi motani mmene anthu oipa ‘amanenera zam’mwamba, ndipo lilime lawo limayendayenda m’dziko lapansi’ motani? Popeza oipa saganizira munthu aliyense kaya wa kumwamba kapena wa padziko lapansi, iwo sazengereza kulankhulira Mulungu mwano. Ndipo amaneneranso anthu mabodza ndi lilime lawo.

74:13, 14—Kodi ndi liti pamene Yehova ‘anaswa mitu ya zoopsa za m’madzi ndi kuphwanya mitu ya Livyatanu’? “Farao mfumu ya Aigupto” ankatchedwa “ng’ona yaikulu yakugona m’kati mwa mitsinje yake.” (Ezekieli 29:3) Livyatanu angaimire amphamvu a Farao. (Salmo 74:14, NW, mawu a m’munsi.) N’kutheka kuti kuswedwa kwa mitu yawo kukutanthauza kugonjetsedwa kotheratu kwa Farao ndi magulu ake ankhondo nthawi imene Yehova analanditsa Aisrayeli muukapolo ku Igupto.

75:4, 5, 10—Kodi mawu akuti “nyanga” amaimira chiyani? Nyanga za nyama ndi chida champhamvu. Motero, mawu akuti “nyanga” mophiphiritsa amaimira mphamvu kapena nyonga. Yehova amanyamula nyanga za anthu ake, kuwaika pokwezeka, koma ‘amatseteka nyanga zonse za oipa.’ Tikuchenjezedwa kuti ‘tisamakwezetse nyanga yathu kuti tisakhale onyada kapena odzikweza. Popeza Yehova ndiye amakweza anthu, tiyenera kuona udindo pampingo kuti umachokera kwa iye.​—Salmo 75:7.

76:10—Kodi “kuzaza kwake kwa munthu” kungalemekeze bwanji Yehova? Mulungu akamalola anthu kutikwiyira chifukwa choti ndife atumiki ake, pangakhale zotsatirapo zabwino. Vuto lililonse limene tingakumane nalo lingatipatse phunziro linalake. Yehova amalola kuvutika n’cholinga choti kuvutikako kutiphunzitse kanthu kena. (1 Petro 5:10) ‘Chotsalira cha kuzaza kwa munthu, Mulungu adzachiletsa.’ Bwanji ngati tivutika mpaka kumwalira? Izinso zingalemekeze Yehova chifukwa anthu omwe ankationa tikupirira mokhulupirika iwonso angayambe kupembedza Mulungu.

78:24, 25—N’chifukwa chiyani mana amatchedwa “tirigu wa kumwamba” ndiponso “mkate wa omveka” kapena kuti angelo? Mawu onsewa satanthauza kuti mana chinali chakudya cha angelo. Mana anali “tirigu wa kumwamba” chifukwa chakuti ankachokera kumwamba. (Salmo 105:40) Popeza angelo, kapena kuti “omveka,” amakhala kumwamba, mawu akuti “mkate wa omveka” angatanthauze kuti mana anaperekedwa ndi Mulungu, amene amakhala kumwamba. (Salmo 11:4) Yehova angakhale kuti analinso kugwiritsa ntchito angelo kupereka mana kwa Aisrayeli.

82:1, 6—Kodi ndani amene amatchedwa kuti “milungu” ndiponso “ana a Wam’mwambamwamba”? Mawu onse awiriwa amatanthauza oweruza omwe anali m’Israyeli. Mawu amenewa anali owayenera chifukwa oweruzawa ankatumikira monga olankhulira Mulungu ndiponso omuimira.​—Yohane 10:33-36.

83:2—Kodi ‘kuweramutsa mutu’ kumatanthauzanji? Kuchita zimenezi kumasonyeza kukhala wokonzeka kuonetsa mphamvu kapena kuchitapo kanthu, ndipo nthawi zambiri mwa kutsutsa, kumenya, kapena kutsendereza.

Zimene Tikuphunzirapo:

73:2-5, 18-20, 25, 28. Tisamasirire chuma cha oipa ndi kutsatira njira zawo zoipa. Anthu oipa ali poterera. Ndithudi iwo ‘adzayesedwa bwinja.’ Ndiponso, popeza kuti kuipa sikungathetsedwe ndi ulamuliro wa munthu wopanda ungwiro, kuyesayesa kwathu kothetsa kuipa sikungapambane. Mofanana ndi Asafu, tingachite bwino ngati tingapirire kuipa mwa “kuyandikiza kwa Mulungu” ndiponso kukhala ndi ubwenzi wolimba ndi Iye.

73:3, 6, 8, 27. Tifunikira kupewa kudzitamandira, kudzikuza, kuchita zaphwete, ndi kulanda ena zinthu. Kupewa zimenezi n’kofunika ngakhale kuti kukhala ndi makhalidwe amenewa kungaoneke ngati kopindulitsa.

73:15-17. Tikasokonezeka poganizira zinthu zina, tizipewa kuuza anthu ena maganizo athu osokonezekawo. Chifukwa chakuti kuuza anthu ena maganizo oterowo kungangowalefula. Tifunikira kuganizira bwinobwino nkhawa zathu ndi kuzithetsa mwa kugwirizana ndi Akristu anzathu.​—Miyambo 18:1.

73:21-24. ‘Kuwawidwa mtima’ chifukwa cha anthu oipa omwe akuoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino n’kofanana ndi kuchita zinthu monga nyama zimene siziganiza. Kuchita motero ndiko kuchita zinthu mwaphuma, mosaganizira. M’malo mwake tifunika kulola malangizo a Yehova kutitsogolera, tili ndi chikhulupiriro chonse choti ‘adzatigwira dzanja lathu lamanja’ ndipo adzatithandiza. Kuwonjezera apa, Yehova ‘adzatilandira mu ulemerero’ kutanthauza kuti tidzakhala naye paubwenzi wolimba kwambiri.

77:6. Kukhala ndi nthawi yophunzira ndi kusinkhasinkha choonadi chauzimu kudzatithandiza kuchiganizira mochokera pansi pamtima ndi kuchifunafuna mosamalitsa. Ndipo n’kofunika kuti tizipeza nthawi ina yokhala patokha.

79:9. Yehova amamvetsera mapemphero athu, makamaka ngati ndi okhudza kuyeretsedwa kwa dzina lake.

81:13, 16. Tikamvera Yehova ndi kuyenda m’njira zake tingapeze madalitso ochuluka.​—Miyambo 10:22.

82:2, 5Kuweruza mosalungama kumachititsa “maziko onse a dziko lapansi” kugwedezeka. Kuchita zinthu mosalungama kumasokoneza mtendere wa anthu.

84:1-4, 10-12. Kulemekeza malo olambirira Yehova ndiponso kukhala okhutira ndi mwayi wotumikira kumene olemba masalmo anali nako kumatipatsa chitsanzo chabwino.

86:5. Tikuyamikira kwambiri chifukwa choti Yehova ndi “wokhululukira.” Iye nthawi zonse amafuna kuona umboni uliwonse umene ungakhale maziko oti asonyezere chifundo kwa munthu wochimwa amene walapa.

87:5, 6Kodi anthu omwe adzakhale ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi adzatha kudziwa mayina a anthu omwe anaukitsidwa kukakhala ndi moyo kumwamba? Mavesi amenewa akusonyeza kuti zimenezi zingakhale zotheka.

88:13, 14. Kuyankha mochedwa mapemphero athu okhudza vuto linalake kungatanthauze kuti Yehova akufuna kuti tisonyeze kuti ndife odziperekadi kwa iye.

“M’YAMIKENI; LILEMEKEZENI DZINA LAKE”

(Salmo 90:1–106:48)

Taonani zifukwa zosiyanasiyana zotamandira Yehova zomwe zatchulidwa m’chigawo chachinayi cha masalmo. Mu Salmo 90, Mose anafotokoza kusiyana kwa moyo wa “Mfumu yosatha” ndi moyo wa munthu wosakhalitsa. (1 Timoteo 1:17) Malinga ndi kunena kwa Salmo 91:2, Mose anatcha Yehova kukhala ‘pothawirapo pake ndi linga lake,’ Gwero la chitetezo chake. Masalmo angapo otsatira akufotokoza makhalidwe abwino a Mulungu, maganizo ake apamwamba ndi ntchito zake zodabwitsa. Masalmo atatu amayamba ndi mfundo yosonyeza kuti “Yehova achita ufumu.” (Salmo 93:1; 97:1; 99:1) Popeza wamasalmo akufotokoza Yehova kukhala Wotipanga, akutipempha kuti ‘timuyamike; tilemekeze dzina lake.’​—Salmo 100:4.

Kodi wolamulira amene amaopa Yehova ayenera kuyendetsa bwanji zinthu zake? Salmo 101, lolembedwa ndi Mfumu Davide, likupereka yankho. Salmo lotsatira likutiuza kuti Yehova ‘adzasamalira pemphero la iwo akusowa konse, osapeputsa pemphero lawo.’ (Salmo 102:17) Salmo 103 likunena za kukoma mtima kwachikondi ndiponso chifundo cha Yehova. Pofotokoza zinthu zambiri zomwe Mulungu wazipanga padziko lapansi, wamasalmo anati: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru.” (Salmo 104:24) Nyimbo ziwiri zomaliza za chigawo chachinayi cha Salmo zimayamika Yehova chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa.​—Salmo 105:2, 5; 106:7, 22.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

91:1, 2—Kodi “ngaka yake ya Wam’mwambamwamba” n’chiyani, ndipo tingakhalemo bwanji? Ndi malo ophiphiritsa omwe ali otetezeka mwauzimu, malo omwe palibe chimene chingatiwononge mwauzimu. Malowa ndi ngaka chifukwa ndi obisika kwa anthu amene sakhulupirira Mulungu. Timaona Yehova kukhala malo athu okhalamo mwa kuyang’ana kwa iye monga pothawirapo pathu ndi linga lathu, mwa kumuyamika monga Wolamulira Wamkulu m’chilengedwe chonse, ndiponso mwa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Timaona kuti ndife otetezeka mwauzimu chifukwa timadziwa kuti Yehova ndi wokonzeka nthawi zonse kutithandiza.​—Salmo 90:1.

92:12—Kodi ndi motani mmene olungama ‘amaphukira ngati mgwalangwa’? Mtengo wa mgwalangwa umadziwika kukhala mtengo wobala kwambiri. Munthu wolungama ali ngati mtengo wa mgwalangwa chifukwa chakuti amachita zolungama pamaso pa Yehova ndipo amabalabe “zipatso zokoma,” zimene zimaphatikizapo ntchito zabwino.​—Mateyu 7:17-20.

Zimene Tikuphunzirapo:

90:7, 8, 13, 14. Nthawi zonse zolakwa zathu zimawononga ubwenzi wathu ndi Mulungu woona. Ndipo machimo amene timabisa sangakhale obisika kwa Iye. Koma ngati tilapadi ndi kusiya njira yathu yolakwika, Yehova adzatiyanjanso, ‘adzatikhutitsa ndi chifundo chake.’

90:10, 12. Popeza tili ndi moyo waufupi, tiyenera “kuwerenga masiku athu.” Motani? Mwa kukhala ndi “mtima wanzeru,” kapena kukhala anzeru kotero kuti tisawawanye masiku athu omwe atsala koma kuti tiwagwiritse ntchito m’njira imene idzakondweretsa Yehova. Zimenezi zikutanthauza kukhala ndi zolinga zauzimu ndi kugwiritsa ntchito nthawi yathu mwanzeru.​—Aefeso 5:15, 16; Afilipi 1:10.

90:17. N’koyenera kupemphera kuti Yehova ‘akhazikitse ntchito ya manja athu’ ndipo adalitse kuyesetsa kwathu muutumiki.

92:14, 15. Okalamba akamawerenga mwakhama Mawu a Mulungu ndi kugwirizana nthawi zonse ndi anthu a Yehova, amakhalabe “abiriwiri,” amphamvu mwauzimu ndipo amakhala othandiza kwambiri pa mpingo.

94:19. Kaya n’zinthu zotani zimene zachititsa nkhawa zathu, kuwerenga ndi kusinkhasinkha “zotonthoza” zomwe zili m’Baibulo kudzatilimbikitsa.

95:7, 8Kumvetsera malangizo a m’Malemba, ndipo mwamsanga kuchita zimene akunena kudzatithandiza kupewa kuumitsa mitima yathu.​—Ahebri 3:7, 8.

106:36, 37. Mavesiwa akusonyeza kuti kulambira mafano kumagwirizana ndi nsembe zoperekedwa ku ziwanda. Zimenezi zikutanthauza kuti, munthu amene amapembedza mafano angayambe kugwiritsidwa ntchito ndi ziwanda. Baibulo limatilangiza kuti: “Dzisungireni nokha kupewa mafano.”​—1 Yohane 5:21.

Tamandani Ya, Anthu Inu!

Nyimbo zitatu zomaliza za chigawo chachinayi cha Masalmo zimatha ndi mawu akuti: “Haleluya” kutanthauza kuti tamandani Ya, anthu inu. Salmo lomaliza la chigawo chachinayichi limayambanso ndi mawu omwewa. (Salmo 104:35; 105:45; 106:1, 48) Ndipotu, mawu akuti “Haleluya” amapezeka nthawi zambiri m’chigawo chachinayi cha masalmo.

Ndithudi tili ndi zifukwa zambiri zotamandira Yehova. Masalmo 73 mpaka 106 atifotokozera zinthu zambiri zoti tiziganizire, ndipo mitima yathu ikuyamikira kwambiri Atate wathu wa kumwamba. Tikaganizira zinthu zonse zimene Yehova watichitira kale ndiponso zimene adzatichitire, kodi sizoona kuti zimatilimbikitsa kumuyamikira ndi mphamvu zathu zonse?

[Chithunzi patsamba 10]

Mofanana ndi Asafu, tingapirire kuipa mwa “kuyandikiza kwa Mulungu”

[Chithunzi patsamba 11]

Farao anagonjetsedwa pa Nyanja Yofiira

[Chithunzi patsamba 11]

Kodi mumadziwa chifukwa chake mana amatchedwa kuti “mkate wa omveka”?

[Chithunzi patsamba 13]

Kodi n’chiyani chimatithandiza kuthetsa nkhawa zathu?