Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Mulungu Wathu Akhoza Kutilanditsa’

‘Mulungu Wathu Akhoza Kutilanditsa’

“Tiyenera Kumvera Mulungu Koposa Anthu”

‘Mulungu Wathu Akhoza Kutilanditsa’

MWAMBO wogwadira fano lagolidi anaukonza kuti ukhale wochititsa mantha. Ndipo fano lalikulu lagolidi analiimika pa chidikha cha Dura, mwachionekere pafupi ndi mzinda wa Babulo. Anthu ankafunika kuyamba kulambira fanoli pa mwambo wapadera wa akuluakulu olemekezeka. Ndipo ankafunika kuligwadira atamva kulira kwa zida zosiyanasiyana zoimbira. Nebukadinezara, Mfumu ya Babulo analamula kuti aliyense amene sadzapembedza fanoli adzaphedwa mwa kuponyedwa m’ng’anjo yotentha koopsa. Kodi ndani amene akanakhala wolimba mtima n’kukana kumvera lamuloli?

Anthu omwe ankaonerera anadabwa kwambiri kuona kuti anthu atatu omwe ankaopa ndi kupembedza Yehova, omwe mayina ndi Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, sanagwadire fanoli. Iwo ankadziwa kuti kuchita zimenezi kukanakhala kuswa lamulo lopembedza Yehova Mulungu yekha. (Deuteronomo 5:8-10) Atapemphedwa kufotokoza chifukwa chake sanagwadire fanoli, iwo mopanda mantha anauza Nebukadinezara kuti: “Taonani, Mulungu wathu amene tim’tumikira akhoza kutilanditsa m’ng’anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m’dzanja lanu, mfumu. Koma akapanda kutero, dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira fano lagolidi mudaliimikalo.”​—Danieli 3:17, 18.

Ahebri atatuwa ataponyedwa m’ng’anjo yotentha ya moto, iwo anapulumutsidwa mozizwitsa. Mulungu anatumiza mngelo kuti akateteze atumiki ake okhulupirikawa. Koma Ahebriwa anali atalolera kale kufa m’malo mwa kuswa lamulo la Yehova. * Iwo anachita zofanana ndi zomwe atumwi a Yesu Kristu anachita, patapita zaka zoposa mazana asanu ndi limodzi. Iwo ataonekera pamaso pa khoti lalikulu la Ayuda, anati: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”​—Machitidwe 5:29.

Maphunziro Ofunika kwa Ife

Sadrake, Mesake, ndi Abedinego anasonyeza chitsanzo chabwino cha kukhala okhulupirika ndi omvera. Ahebri atatuwa anakhulupirira Yehova. Popeza ankaphunzira Malemba, chikumbumtima chawo sichinawalole kuchita nawo mbali iliyonse ya kulambira konyenga kapena kusonyeza kukonda dzikolo. Akristu nawonso masiku ano amakhulupirira kwambiri Mulungu woona. Chifukwa choti amaphunzira Baibulo, chikumbumtima chawo n’chimene chimawatsogolera ndipo amakana kutenga nawo mbali m’miyambo ya kulambira konyenga imene imasemphana ndi malamulo a Mulungu.

Ahebri atatu okhulupirika aja anakhulupirira Yehova ndipo anakana kuti asiye kumvera Yehova chifukwa cha zinthu monga kutchuka, malo apamwamba, ulemerero, zimene Ufumu wa Babulo ukanawapatsa. Achinyamata amenewa anali okonzeka kuvutika ndi kufa m’malo moti awononge ubwenzi wawo ndi Mulungu. Mofanana ndi Mose yemwe anakhalako iwo asanabadwe, iwonso “anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.” (Ahebri 11:27) Kaya Yehova akanasankha kuwapulumutsa ku imfa kapena ayi, amuna atatuwa anatsimikiza mtima kukhalabe okhulupirika kwa iye m’malo momvera Nebukadinezara kuti apulumutse moyo wawo. Zikuoneka kuti mtumwi Paulo anatchula za okhulupirika amene ‘anazima mphamvu ya moto,’ pofotokoza chitsanzo chawo. (Ahebri 11:34) Atumiki a Yehova masiku ano amasonyeza chikhulupiriro ndi kumvera kofanana ndi kumeneku akakumana ndi ziyeso zachikhulupiriro.

Pa zimene zinachitikira Sadrake, Mesake, ndi Abedinego timaphunziraponso kuti Mulungu amapatsa mphoto anthu omwe amakhala okhulupirika kwa iye. Wamasalmo anaimba kuti: ‘Yehova sadzataya okondedwa ake.’ (Salmo 37:28) Masiku ano, sitingayembekezere Mulungu kutipulumutsa mozizwitsa, monga momwe anachitira kwa Ahebri atatu aja. Koma tingakhale ndi chikhulupiriro choti pa mavuto aliwonse amene tingakumane nawo, Atate wathu wa kumwamba adzatithandiza. Mulungu angathetse vutolo, angatipatse mphamvu zoti tilipirire, kapena kutiukitsa kwa akufa ngati tikhalabe okhulupirika mpaka imfa. (Salmo 37:10, 11, 29; Yohane 5:28, 29) Nthawi zonse tikamayesedwa, chikhulupiriro ndi kumvera zimapambana ndipo timasankha kumvera Mulungu koposa anthu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani Kalendala ya 2006 ya Mboni za Yehova, pa mwezi July ndi August.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 9]

KODI MUKUDZIWA?

• Panthawi imene ankayesedwa, Ahebri onse atatu anali atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 30.

• Kutentha kwa ng’anjo ya moto kunawonjezedwa mowirikiza.​—Danieli 3:19.