Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mwala Wina Wosema Umatchula za Anthu Otchedwa Israyeli

Mwala Wina Wosema Umatchula za Anthu Otchedwa Israyeli

Mwala Wina Wosema Umatchula za Anthu Otchedwa Israyeli

M’NYUMBA yosungiramo zinthu zakale zochititsa chidwi ya ku Cairo, m’dziko la Egypt, muli mwala umene uli ndi mawu ozokotedwa osimba mbiri ya kupambana kwa Farao Merneptah. Akatswiri ena ophunzira amati Merneptah anali mwana wa khumi ndi chitatu wa Ramses Wachiwiri, ndipo amamuganizira kuti anali wolamulira kuyambira m’chaka cha 1212 mpaka mu 1202 B.C.E, chakumapeto kwa nthawi ya ulamuliro wa Oweruza mu Israyeli wakale. Mizere iwiri yomalizira ya mawu ozokotedwa pa mwala umenewu wa Merneptah imati: “Talanda Kanani, titalimbana naye kwambiri. Talanda Asikeloni, tagonjetsa Gezeri, Yanoamu tam’gonjetseratu. Israyeli tam’sandutsa bwinja, ana ake sadzapezekanso.”

Kodi pamenepa liwu lakuti “Israyeli” likutanthauzanji? Pa kalembedwe kakale ka zizindikiro ka ku Igupto, panali zizindikiro zina zimene amati akaziwonjezera ku zizindikiro zotanthauza dzina la chinthu, chinthucho chinkadziwikiratu gulu lake. Buku lakuti The Rise of Ancient Israel limafotokoza kuti: ‘Mayina atatu osemedwa pa mwalawu, Asikeloni, Gezeri, ndi Yanoamu, ali ndi zizindikiro zowonjezera zosonyeza kuti amenewa ndi mayina a mizinda. . . . Koma dzina la Israyeli lili ndi chizindikiro chowonjezera chosonyeza kuti limeneli ndi dzina la mtundu wa anthu.’

Kodi mawu ozokotedwa pa mwala amenewa ali ndi tanthauzo lotani? Mlembi komanso mkonzi wa buku tatchula lija, dzina lake Hershel Shanks anati: “Mwala wa Merneptah umasonyeza kuti anthu otchedwa Israyeli, analipo m’chaka cha 1212 B.C.E., ndi kuti farao wa ku Igupto sanangowadziwa chabe anthu amenewa komanso ankadzitamandira kuti anawagonjetsa pankhondo.” William G. Dever, yemwe ndi katswiri wa mbiri ya zinthu zakale zokumbidwa pansi za kumayiko ozungulira dziko la Israel, anathirirapo ndemanga kuti: “Mwala wa Merneptah umatitsimikizira mosapita m’mbali kuti: Ku Kanani kunkakhala anthu amene ankadzitcha kuti ‘Israyeli.’ Ndiponso anthu a ku Igupto amene sankakhulupirira n’komwe Baibulo, amenenso sakanatha kungotchula dzinali n’cholinga chofuna kutchuka, ankawatchanso kuti ‘Israyeli.’”

Baibulo limatchula koyamba liwu lakuti Israyeli monga dzina la Yakobo, kholo lakale. N’chifukwa chake mbadwa za ana 12 a Yakobo zinayamba kutchedwanso kuti “ana a Israyeli.” (Genesis 32:22-28, 32; 35:9, 10) Patapita zaka zambiri pambuyo pake, mneneri Mose ndi Farao wa ku Igupto anagwiritsa ntchito liwuli “Israyeli” potchula mbadwa za Yakobo. (Eksodo 5:1, 2) Kupatula pa Baibulo, umboni wina wakale kwambiri wosonyeza kuti kunali mtundu wa anthu wotchedwa Israyeli ndi mwala umenewu wa Merneptah.

[Zithunzi patsamba 24]

Mwala wa Merneptah

Kuphatikiza zizindikiro zomalizira zitatu (kuchokera kumanja kupita kumanzere)​—kamtengo, mwamuna ndi mkazi atakhala pansi​—kukusonyeza kuti Israyeli unali mtundu wa anthu wa kunja kwa Igupto

[Mawu a Chithunzi]

Egyptian National Museum, Cairo, Egypt/​Giraudon/​The Bridgeman Art Library