Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ikapita Siibweranso Choncho Igwiritseni Ntchito Bwino

Ikapita Siibweranso Choncho Igwiritseni Ntchito Bwino

Ikapita Siibweranso Choncho Igwiritseni Ntchito Bwino

NTHAWI ndi ndalama. Mawu amenewa amanenedwa kawirikawiri. Koma kwenikweni, nthawi n’njosiyana kwambiri ndi ndalama kapena zinthu zina zotere. Simungaike nthawi inayake padera kuti mudzaigwiritse ntchito m’tsogolo monga mmene mungachitire ndi ndalama, chakudya, zinthu monga mafuta kapena nkhuni, komanso zinthu zina zosiyanasiyana. Munthu sungapindule m’njira iliyonse poyesa kusunga nthawi mwa kusaigwiritsa ntchito. Kodi n’chiyani chimachitika ngati mutagona kwa maola eyiti n’kusachita chilichonse pa tsikulo pofuna kuti tsiku limenelo mulisunge? Tsikulo likamatha, ndiye kuti maola onse amene simunagwiritse ntchito aja apita basi mpaka kalekale.

Nthawi tingaiyerekezere ndi madzi othamanga mumtsinje waukulu. Nthawi zonse amayenda molowera kutsogolo. Simungaimitse mtsinjewo komanso simungagwiritse ntchito dontho lililonse la madzi amene akudutsawo. Panthawi ina kalekale, anthu anayamba kumanga magudumu oyendetsedwa ndi madzi n’kuwaika m’mphepete mwa mitsinje. Mphamvu zimene magudumuwa ankakhala nazo akamazungulira ankazigwiritsa ntchito pa mphero zawo, macheka awo, mapampu awo, ndiponso pa zipangizo zawo zosulira zitsulo. Chimodzimodzinso nthawi. Nthawi mungathe kuigwiritsa ntchito bwino osati poisunga penapake, koma pochita nayo zinthu zopindulitsa. Komabe kuti mutero, muyenera kulimbana ndi zinthu ziwiri zikuluzikulu zimene zimaba nthawi, zomwe ndi kuzengereza ndiponso kuunjika zinthu. Tiyeni tiyambe taona nkhani ya kuzengereza.

Pewani Kuzengereza

Pali mawu odziwika bwino akuti, Musaganize zodzachita mawa zinthu zimene mungathe kuchita lero. Koma pali anthu ena amene sagwiritsa ntchito mawuwa. Akakhala ndi ntchito yovuta, amaona kuti chidule n’kungozengereza kuchita ntchitoyo. Buku lina lotanthauzira mawu linati, “kuzerengereza” ndi “khalidwe ladala ndiponso lachizolowezi chosachita zinthu panthawi imene ziyenera kuchitidwa.” Munthu wakhalidwe lozengereza amafika pongozolowera kusachita ntchito yofunika pofuna kuti aichite nthawi ina. Ndiye akaona kuti ali pampanipani, amangoiika pambali ntchito ija ndipo amasangalala kuti tsopano wapeza “nthawi yopuma.” Koma patsogolo pake amadzakhalabe pampanipani.

Nthawi zina, timafunika kuika kaye pambali ntchito ina kapena ntchito yathu yonse chifukwa choti thanzi lathu kapena maganizo athu sali bwino. Komanso munthu aliyense amafunika kuti nthawi zina azipumako pa zinthu zimene amachita tsiku ndi tsiku. Ngakhale Mwana wa Mulungu ankapuma. Yesu ankakhala wotanganidwa kwambiri muutumiki, koma ankadzipatsanso nthawi yoti iyeyo ndi ophunzira ake apumeko. (Marko 6:31, 32) Kupuma kotereku n’kopindulitsa. Komatu kuzengereza ndi nkhani ina, ndipo nthawi zambiri kumalowetsa munthu m’mavuto. Taonani chitsanzo ichi.

Mtsikana wa pasukulu watsala ndi milungu itatu kuti akhale atakonzeka kulemba mayeso a masamu. Pali notsi ndiponso mabuku ambiri oti awerenge. Akuona kuti zinthu zamupanikiza. Akuganiza zozengereza ndipo akuterodi. M’malo momawerenga, iye akuonera TV. Masiku akutha koma iye akuzengerezabe kuchita zimene ayenera kuchita kuti akhoze mayesowo. Kenaka patsiku loti mayeso ali mawa, akuyenera kuwerenga zinthu zonsezo nthawi imodzi. Motero akukhala pansi n’kuyamba kuwerenga notsi ndi mabuku ake.

Akuwerenga kwa maola ambiri. Anthu ena pabanjapo akugona koma iyeyo akulimbana ndi masamu ovuta osiyanasiyana. Atapita kusukulu pa tsiku lotsatira, akuvutika kuyankha mafunso chifukwa chotopa. Akulephera kuchita bwino pamayesowo motero akulakwa. Ayenera kuwerenganso zinthuzo ndipo mwina sakhoza mayeso n’kukayamba kalasi lotsatira.

Apatu kuzengereza kunam’pweteketsa mtsikanayu. Koma pali mfundo ya m’Baibulo imene ingathandize anthu kupewa zinthu ngati zimenezi. Mfundo yake ndi imene Paulo analemba kuti: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi.” (Aefeso 5:15, 16) Pamenepa Paulo anali kulimbikitsa Akristu kuti azigwiritsa ntchito bwino nthawi yawo posamalira zinthu zauzimu, koma mfundoyi n’njothandizanso m’zinthu zambiri zofunikira pamoyo. Popeza kuti nthawi zambiri tingathe kusankha tokha nthawi yochitira ntchito inayake, ndi bwino kusankha nthawi yabwino kwambiri kuti ntchitoyo tiichite molongosoka ndiponso mwamsanga. Monga lembali likusonyezera, ichi n’chizindikiro cha anthu “anzeru.”

Kodi nthawi yabwino yoti mtsikana uja akonzekere mayeso ake ikanakhala iti? Mwina bwenzi atakonza zoti tsiku lililonse usiku aziwerenga kwa mphindi 15 kapena kuposa, ndipo potero akanatha kubwereramo pang’onopang’ono. Akanachita zimenezi sakanavutika n’kuwerenga zinthu zambirimbiri usiku, mayeso ali mawa lake, m’malo moti azigona. Pa tsiku la mayesolo, bwenzi akumva bwino kwambiri m’thupi ndipo bwenzi ali wokonzeka, motero mayesowo akanatha kukhoza bwino.

Ndiyetu mukapatsidwa ntchito yoti muchite, pezani nthawi yabwino kwambiri ndipo ichiteni nthawi imeneyo. Mukatero mungapewe msampha wopweteketsa wochita zinthu mozengereza. Mungakhalenso osangalala kuti mwachita bwino ntchito yanu. Zimenezi n’zofunika kwambiri makamaka ngati ntchitoyo ikukhudzanso anthu ena, monga mmene zimakhalira ndi ntchito za mumpingo wachikristu.

Musalole Zinthu Kuunjikana

Monga tanenera poyamba paja, chinthu chachiwiri chofunika kuti tigwiritse bwino ntchito nthawi yathu ndicho kusalola zinthu kuunjikana. Tonse tikudziwa kuti zimatenga nthawi kusamalira zinthu, kuzilongosola, kuzigwiritsa ntchito, kuziyeretsa, kuzisunga, ndi kuzipeza mukamazifuna. Tikakhala ndi zinthu zambiri pamafunikanso nthawi yambiri. Kuchita ntchito m’chipinda kapena m’nyumba yodzaza zinthu zambirimbiri kumawononga nthawi yambiri ndipo n’kovuta kwambiri kusiyana ndi kugwira ntchito m’malo osadzaza zinthu. Komanso zinthu zikamachuluka, pamafunikanso nthawi yochuluka kuti mupeze chinachake chimene mukufuna.

Akatswiri osamalira m’nyumba amati pafupifupi theka la nthawi yonse imene anthu amatha poyeretsa m’nyumba imathera “ponyamula, polambalala, ndi posuntha zinthu zongopezeka paliponse m’nyumbamo komanso zinyalala.” N’kuthekanso kuti zili chimodzimodzi ndi zochitika zina pamoyo. Motero ngati mukufuna kugwiritsa ntchito bwino nthawi yanu, taonani bwinobwino mmene zinthu zakhalira pa malo anupo. Kodi pali zinthu zambirimbiri zimene zikungotha malo, moti zimakulepheretsani kuyenda momasuka, komanso zimakuwonongerani nthawi yanu? Ngati ndi choncho, chepetsani zinthu zotere.

Kuchotsa zinthu zotere si kophweka. Ngakhale zitakhala zopanda ntchito, koma kutaya zinthu zomwe mumazikonda kumawawa, mwinanso mofanana ndi ululu wolekana ndi mnzanu wapamtima. Ndiye kodi mungasankhe bwanji kuti chinthu chinachake muchisunge kapena muchitaye? Ena amagwiritsa ntchito lamulo losunga chinthu kwa chaka chimodzi. Kutanthauza kuti ngati chinachake simunachigwiritse ntchito kwa chaka chimodzi, chitayeni. Nanga mungatani ngati patha chaka koma simukufunabe kuchitaya chinthucho? Chiikeni pa malo osungira zinthu kwa miyezi ina sikisi. Mwina simungadzavutike kwambiri kutaya chinthucho ngati mutaona kuti patha chaka ndi miyezi sikisi musanachigwiritse ntchito. Mulimonsemo, cholinga chanu chizikhala chochepetsa kuunjikana kwa zinthu kuti nthawi yanu muigwiritse ntchito bwino.

Inde, sikuti zinthu zimangounjikana kunyumba ndi kuntchito kokha. Yesu ananenapo za “kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma,” zimene zingathe ‘kutsamwitsa mawu’ a Mulungu n’kuchititsa kuti munthu akhale “wopanda chipatso” pankhani ya uthenga wabwino. (Mateyu 13:22) Moyo wa munthu ungathe kuunjikana ndi zochita zambirimbiri moti angalephere kupeza nthawi yoti apititse patsogolo moyo wake wauzimu, womwe uli wofunika koposa. Zimenezi zingamuwonongere moyo wake wauzimu ndipo pamapeto pake angatayiretu mwayi wodzalowa m’dziko latsopano limene Mulungu analonjeza. M’dziko limenelo anthu adzakhala ndi nthawi yosatha yochitira zinthu zokhutiritsa ndiponso zosangalatsadi.​—Yesaya 65:17-24; 2 Petro 3:13.

Kodi nthawi zambiri mumapezeka kuti muli ndi zinthu zambirimbiri zoyenera kuti muchite pakanthawi kochepa, kaya n’zokhudza ntchito yanu, pakhomo panu, galimoto yanu, zosangalatsa zimene mumachita, maulendo anu, zolimbitsa thupi, macheza, kapenanso zinthu zina zosiyanasiyana? Ngati n’choncho, mwina ndi bwino kuganizira mmene mungachepetsere kuunjika zinthu mwauzimu.

Mawu enanso odziwika bwino n’ngakuti, Zengerezu analinda kwawukwawu. Inde, nthawi siima koma imapita m’tsogolo ngati madzi a mumtsinje. Siingabwezedwe kapena kusungidwa; ikapita yapita basi mpaka kalekale. Komabe, potsatira mfundo zosavuta za m’Baibulo ndiponso pochita zinthu zingapo zothandiza, tingathe kugwiritsa ntchito bwino nthawi imene timafunikira kuti tichite “zinthu zofunika kwambiri” zomwe tingapindule nazo kosatha ndipo potero ‘Mulungu angalemekezedwe ndi kutamandidwa.’​—Afilipi 1:10, 11, NW.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Monga mtsinje wa madzi othamanga kwambiri, nthawi ingathe kugwiritsidwa ntchito mwaphindu

[Chithunzi patsamba 9]

Kodi nthawi yabwino yoti mtsikanayu akonzekere mayeso ake ndi iti?

[Chithunzi patsamba 10]

Kugwira ntchito pa malo odzadza zinthu zambirimbiri kumawonongetsa nthawi ndiponso n’kovuta