Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Anzeru mwa Kuopa Mulungu

Khalani Anzeru mwa Kuopa Mulungu

Khalani Anzeru mwa Kuopa Mulungu

“Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova.”​—MIYAMBO 9:10.

1. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amavutika kumvetsa nkhani ya kuopa Mulungu?

KALE, mukauza munthu kuti n’ngoopa Mulungu ankaona kuti mwamuyamikira. Koma masiku ano, ambiri amaona kuti zoopa Mulungu n’zachikale ndipo n’zovuta kuzimvetsa. N’kutheka kuti amadzifunsa kuti, ‘Ngati Mulungu ali chikondi n’chifukwa chiyani ndiyeneranso kumuopa?’ Iwo amaona kuti mantha n’chinthu chongolepheretsa munthu kuchita zinthu. Komatu kuopa Mulungu kwenikweni kumatanthauza zinthu zinanso zambiri, ndipo monga tionere sikutanthauza mantha okha ayi.

2, 3. Kodi kuopa Mulungu kwenikweni kumatanthauza zinthu zotani?

2 M’Baibulo kuopa Mulungu ndi khalidwe labwino. (Yesaya 11:3) Kumatanthauza kulemekeza Mulungu ndi mtima wonse ndi kum’patsa ulemu waukulu, ndiponso kukhala ndi mtima wosafuna kum’khumudwitsa. (Salmo 115:11) Kumatanthauzanso kuti munthuwe umavomereza mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino ndipo umayesetsa kuzitsatira ndiponso umagwirizana ndi zimene Mulungu amati n’zabwino kapena zoipa. Buku lina limati mantha oyenererawa amasonyeza kuti munthu “akuchitira Mulungu ulemu, moti amachita zinthu mwanzeru ndipo amapewa zoipa zamtundu wina uliwonse.” M’pake kuti Mawu a Mulungu amatiuza kuti: “Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova.”​—Miyambo 9:10.

3 Inde, kuopa Mulungu kumakhudza zochitika zathu zambiri. Sikuti kumangoyenderana ndi nzeru zokha ayi koma kumayenderananso ndi chimwemwe, mtendere, moyo wabwino, moyo wautali, chiyembekezo, kudalirika, ndi kusakayikira. (Salmo 2:11; Miyambo 1:7; 10:27; 14:26; 22:4; 23:17, 18; Machitidwe 9:31) Kumayenderana kwambiri ndi chikhulupiriro komanso chikondi. Kwenikweni, kumakhudza mbali zonse za ubwenzi wathu ndi Mulungu komanso ndi anthu anzathu. (Deuteronomo 10:12; Yobu 6:14; Ahebri 11:7) Kuopa Mulungu kumatanthauza kukhulupirira ndi mtima wonse kuti Atate wathu wakumwamba amatisamalira ndipo n’ngokonzeka kutikhululukira pa zolakwa zathu. (Salmo 130:4) Ndi anthu oipa komanso osalapa okha omwe ayenera kuchita naye mantha Mulungu. *​—Ahebri 10:26-31.

Kuphunzira Kuopa Yehova

4. Kodi n’chiyani chingatithandize ‘kuphunzira kuopa Yehova’?

4 Popeza kuti kuopa Mulungu n’kofunika pa moyo wathu kuti tizisankha zinthu mwanzeru ndi kudalitsidwa ndi Mulungu, kodi tingatani kuti ‘tiphunzire kuopa Yehova’ moyenerera? (Deuteronomo 17:19) M’Malemba muli zitsanzo zambiri za amuna ndi akazi oopa Mulungu zomwe “zinalembedwa kutilangiza.” (Aroma 15:4) Kuti timvetse tanthauzo lenileni la kuopa Mulungu, tiyeni tionepo nkhani ya Mfumu Davide ya Israyeli, yemwe ndi chitsanzo chimodzi mwa zitsanzo zimenezi.

5. Kodi ntchito ya ubusa inam’thandiza bwanji Davide kuphunzira kuopa Yehova?

5 Yehova anakana Sauli, mfumu yoyamba ya Israyeli, chifukwa choti Sauli ankaopa anthu osati Mulungu. (1 Samueli 15:24-26) Koma moyo wa Davide ndiponso ubwenzi wake wapamtima ndi Yehova, zimaonetsa kuti anali munthu woopadi Mulungu. Kuyambira ali wamng’ono, Davide nthawi zambiri ankaweta nkhosa za atate wake kutchire. (1 Samueli 16:11) Davide ayenera kuti anaimvetsa bwino nkhani ya kuopa Yehova chifukwa choti nthawi zambiri ankaweta ziweto usiku n’kumaona nyenyezi kumwamba. Ngakhale kuti ankangoona mbali yochepa chabe ya thambo, zimene anazindikirazo zinali zoona chifukwa anazindikira kuti Mulungu n’ngoyenerera kumulemekeza ndi kumulambira. Pambuyo pake iye analemba kuti: “Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mum’kumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?”​—Salmo 8:3, 4.

6. Kodi Davide anamva bwanji atazindikira ukulu wa Yehova?

6 Davide anagoma kwambiri poganizira kuchepa kwake poyerekezera ndi kuchuluka kwa nyenyezi za kumwamba, ndipotu m’pake kugoma. Koma kudziwa zimenezi sikunamuopse ayi, m’malo mwake kunamuchititsa kutamanda Yehova ndi kunena kuti: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.” (Salmo 19:1) Kuopa Mulungu kumeneku kunachititsa Davide kuyandikira kwambiri kwa Yehova ndi kufuna kuphunzira komanso kutsatira njira Zake zangwiro. Taganizirani mmene Davide amamvera pamene ankaimba kwa Yehova kuti: “Pakuti Inu ndinu wamkulu, ndi wakuchita zodabwiza; inu ndinu Mulungu, nokhanu. Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m’choonadi chanu: Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.”​—Salmo 86:10, 11.

7. Kodi kuopa Mulungu kunathandiza bwanji Davide kumenyana ndi Goliati?

7 Afilisti atalanda dziko la Israyeli, Goliati, yemwe anali chimphona chawo chachitali pafupifupi mamita atatu, ananyoza Aisrayeli ndipo kwenikweni anali kunena kuti: ‘Sankhani munthu woti adzamenyane ndi ineyo! Ngati atapambana iyeyo, ndiye kuti tikhala akapolo anu.’ (1 Samueli 17:4-10) Sauli ndi asilikali ake onse anachita mantha kwambiri, koma Davide sanaope. Iye ankadziwa kuti Yehova ndiye ayenera kuopedwa, ndipo munthu sayenera kuopedwa, ngakhale atakhala wamphamvu zotani. Davide anauza Goliati kuti: “Ine ndafika kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu” ndipo “msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo.” Davide anapha chimphonacho ndi mwala umodzi wokha basi pogwiritsira ntchito choponyera mwala.​—1 Samueli 17:45-47.

8. Kodi zitsanzo za m’Baibulo za anthu oopa Mulungu zimatiphunzitsa chiyani?

8 Monga Davide, n’kutheka kuti ifenso tikukumana ndi mavuto kapena adani ochititsa mantha. Kodi tingatani? Tingathane nawo mwa kuopa Mulungu, monga anachitira Davide ndi anthu ena akale okhulupirika. Kuopa Mulungu kungathetse mantha oopa munthu. Nehemiya, yemwe anali mtumiki wokhulupirika wa Mulungu, analimbikitsa Aisrayeli anzake amene ankakumana ndi mavuto chifukwa cha anthu olimbana nawo. Iye anawauza kuti: “Musamawaopa iwo; kumbukirani Yehova wamkulu ndi woopsa.” (Nehemiya 4:14) Mothandizidwa ndi Yehova, Davide, Nehemiya, ndi atumiki a Mulungu ena okhulupirika anakwanitsa kuchita ntchito zimene Mulungu anawapatsa. Ifenso tingatero mwa kuopa Mulungu.

Kuthana ndi Mavuto mwa Kuopa Mulungu

9. Kodi Davide anasonyeza kuopa Mulungu pa nkhani zotani?

9 Davide atapha Goliati, Yehova anamuthandizanso kupambana nkhondo zambiri. Koma chifukwa cha nsanje, Sauli anayesa kupha Davide katatu konse. Koyambako anatero chifukwa zinangom’bwerera m’mutu kuti aphe Davideyo, kachiwiri anachita kum’konzekera mwachiwembu ndipo komalizako anachita kumusakasaka ali ndi gulu la nkhondo. Ngakhale kuti Yehova anamutsimikizira Davide kuti adzakhala mfumu, kwa zaka zambiri Davide anakhala akuthawa, kumenya nkhondo ndi kudikirira nthawi ya Yehova yodzamukhazika mfumu. Pa zochitika zonsezi Davide anasonyeza kuti akuopa Mulungu woona.​—1 Samueli 18:9, 11, 17; 24:2.

10. Kodi Davide anasonyeza bwanji kuopa Mulungu panthawi imene moyo wake unali pangozi?

10 Panthawi ina, Davide anapita kwa Akisi, mfumu ya mzinda wa Afilisti wa Gati, kwawo kwa Goliati. (1 Samueli 21:10-15) Atumiki a mfumuyo ananena kuti Davide ndi mdani wa mtundu wawo. Kodi Davide anatani zinthu zitafika poopsa chonchi? Iye anapemphera kwa Yehova mwamtima wonse. (Salmo 56:1-4, 11-13) Ngakhale kuti anachita kufika ponamizira misala, Davide ankadziwa kuti kwenikweni Yehova ndiye anamuwombola podalitsa nzeru imeneyi. Davide anadalira Yehova ndi mtima wonse, kusonyeza kuti analidi munthu woopa Mulungu.​—Salmo 34:4-6, 9-11.

11. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaopa Mulungu tikakumana ndi chiyeso monga anachitira Davide?

11 Monga Davide, ifenso tingasonyeze kuti timaopa Mulungu podalira lonjezo lake lakuti atithandiza kuthana ndi mavuto athu. Davide anati: “Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita.” (Salmo 37:5) Zimenezi sizikutanthauza kuti mavuto athuwo timangomusiyira Yehova kuti iyeyo ndiye athane nawo ifeyo n’kungopinda manja basi, osachitapo chilichonse. Davide sanangopemphera kuti Mulungu amuthandize n’kulekera pomwepo basi. Koma anagwiritsa ntchito mphamvu ndiponso nzeru zimene Yehova anam’patsa n’kuthana ndi vuto lakelo. Komatu Davide ankadziwa kuti zochita za munthu payekha sizingakhale zodalirika. Ifenso tizidziwa zimenezi. Tikachita mbali yathu ndi mphamvu zathu zonse, tiyenera kusiya zonse m’manja mwa Yehova. Kwenikweni, nthawi zambiri sipakhala chilichonse choti tingachite kupatulapo kudalira Yehova basi. Imeneyi ndiyo nthawi yoti ifeyo patokha tionetse kuti timaopadi Mulungu. Tingalimbikitsidwe ndi mawu amene Davide ananena mochoka pansi pa mtima akuti: “Chinsinsi cha Yehova chili kwa iwo akumuopa Iye.”​—Salmo 25:14.

12. N’chifukwa chiyani mapemphero athu tiyenera kuwaona kuti n’ngofunika kwambiri, ndipo kodi tiyenera kupewa mtima wotani?

12 Motero, mapemphero athu ndiponso ubwenzi wathu ndi Mulungu tiziziona kuti n’zinthu zofunikira kwambiri. Tikamapemphera kwa Yehova, tiyenera “kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” (Ahebri 11:6; Yakobo 1:5-8) Ndipo iye akatithandiza, tiyenera ‘kukhala akuyamika,’ monga mtumwi Paulo anatilangizira. (Akolose 3:15, 17) Tisakhale ngati anthu amene Mkristu wina wachikulire wodzozedwa anawalongosola motere: “Mulungu amamutenga ngati wantchito wokhala kumwamba. Akafuna chinachake amangoganiza zom’kodola kuti adzawatumikire. Akangowapatsa chimene akufunacho, basi athana naye.” Mtima woterewu umasonyeza kusaopa Mulungu.

Atabwerera M’mbuyo pa Kuopa Mulungu

13. Kodi ndi panthawi iti pamene Davide sanalemekeze Chilamulo cha Mulungu?

13 Chifukwa chothandizidwa ndi Yehova panthawi ya mavuto, Davide anakulitsa khalidwe la kuopa Mulungu ndi kum’dalira. (Salmo 31:22-24) Komabe katatu konse Davide anabwerera m’mbuyo pa kuopa Mulungu ndipo anagwa m’mavuto oopsa. Nthawi yoyamba iye anakonza zoti likasa la chipangano cha Yehova lipite ku Yerusalemu pa galeta m’malo moti Alevi alinyamule pa mapewa pawo, monga mmene Chilamulo cha Mulungu chinanenera. Uza, yemwe ankatsogolera galetalo, atagwira likasa lija kuti alikhazike bwinobwino, anafera pomwepo chifukwa cha ‘kusalingalira kwakeko.’ Inde, Uza anachimwa kwambiri, komatu kwenikweni iye analangidwa chifukwa choti Davide anachita zosalemekeza Chilamulo cha Mulungu. Kuopa Mulungu kumatanthauza kuchita zinthu mogwirizana ndi njira imene Mulungu amachitira zinthu.​—2 Samueli 6:2-9; Numeri 4:15; 7:9.

14. Kodi chinachitika n’chiyani Davide atawerenga Aisrayeli?

14 Patsogolo pake, Davide mosonkhezeredwa ndi Satana anawerengetsera amuna a Israyeli omenya nkhondo. (1 Mbiri 21:1) Pochita zimenezi, Davide anasonyeza kuti anabwerera m’mbuyo pa kuopa kwake Mulungu, ndipo zimenezi zinaphetsa Aisrayeli 70,000. Ngakhale kuti Davide analapa kwa Yehova, iyeyo pamodzinso ndi anthu ake anavutika kwambiri.​—2 Samueli 24:1-16.

15. Kodi n’chiyani chinachititsa Davide tchimo la chigololo?

15 Panthawi inanso, Davide anabwerera m’mbuyo mwakanthawi pa kuopa Mulungu ndipo zinachititsa kuti achite chigololo ndi Bateseba, mkazi wa Uriya. Davide ankadziwa kuti n’kulakwa kuchita chigololo ngakhalenso kungokhumbira chabe mkazi wa mwini. (Eksodo 20:14, 17) Vuto linayamba Davide ataona Bateseba akusamba. Akanakhala kuti akuopa Mulungu moyenerera, nthawi yomweyo Davide akanachotsa maso ake ndiponso maganizo ake pa zomwe anali kuonazo. Koma zikuoneka kuti Davide anapitiriza ‘kuyang’ana’ mkazi uja mpaka kufika poti chilakolako chake chinaposa kuopa kwake Mulungu. (Mateyu 5:28; 2 Samueli 11:1-4) Davide anasiya kuona kuti Yehova amakhudzidwa ndi mbali iliyonse ya moyo wake.​—Salmo 139:1-7.

16. Kodi Davide anakumana n’zotani chifukwa cha tchimo limene anachita?

16 Davide atachita chigololo ndi Bateseba anabereka mwana wamwamuna. Posakhalitsa, Yehova anatumiza mneneri wake Natani kuti akavumbule tchimo la Davide. Atazindikira kulakwa kwake, Davide anayambanso kuopa Mulungu ndipo analapa. Iye anapempha Yehova kuti asamutaye kapena kum’chotsera mzimu wake woyera. (Salmo 51:7, 11) Yehova anam’khululukira Davide ndipo anam’chepetsera chilango chake, koma sanam’teteze ku zotsatirapo zonse zoipa za zochita zakezo. Mwana wa Davide uja anamwalira, ndipo kuyambira pamenepo banja lake linakumana ndi mavuto aakulu. Apatu Davide analangika kwambiri chifukwa chobwerera m’mbuyo pa kuopa Mulungu.​—2 Samueli 12:10-14; 13:10-14; 15:14.

17. Taperekani chitsanzo chosonyeza mavuto amene kuchimwa kumabweretsa.

17 Masiku ano, kusalemekeza Mulungu pa nkhani za makhalidwe abwino kungathenso kutibweretsera mavuto oopsa komanso okhalitsa. Taganizirani mmene mkazi wina wachitsikana anamvera atamva kuti mwamuna wake, yemwe ndi Mkristu, anachita zosakhulupirika atapita kunja kukagwira ntchito. Pothedwa nzeru ndiponso posakhulupirira, mkaziyu anangowerama n’kuyamba kulira atabisa nkhope yake ndi manja. Sitingadziwe kuti zidzatenga nthawi yaitali bwanji kuti mkaziyu adzayambenso kukhulupirira ndi kulemekeza mwamuna wakeyo. Tingathe kupewa zosautsa ngati zimenezi poopadi Mulungu.​—1 Akorinto 6:18.

Kuopa Mulungu Kumatiletsa Kuchimwa

18. Kodi cholinga cha Satana n’chiyani ndipo ndi njira iti imene iye amagwiritsa ntchito?

18 Satana akuyesetsa kuipitsa makhalidwe a anthu padzikoli ndipo akufunitsitsa kuti makamaka aipitse makhalidwe a Akristu oona. Kuti atero, amagwiritsa ntchito njira yachidule kwambiri yofikira mumtima ndi m’maganizo athu, yomwe makamaka ili maso ndi makutu athu. (Aefeso 4:17-19) Kodi mungatani ngati mosayembekezera mutaona zithunzi zolaula, kumva mawu olaula, mwinanso kuona kapena kukumana ndi anthu okonda zinthu zoterezi?

19. Kodi kuopa Mulungu kunathandiza bwanji Mkristu wina kuthana ndi chiyeso?

19 Taganizirani zomwe zinam’chitikira André, * yemwe ndi mkulu mumpingo, ndi bambo wa ana ake, ndiponso ndi dokotala ku Ulaya. André akamagwira ntchito usiku wonse kuchipatala, akazi amene ankagwira nawo ntchito m’chipatalamo nthawi zambiri ankamata timapepala pa pilo wake atajambulapo chizindikiro chosonyeza chikondi, tomuitana kuti akagonane nawo. André anakanitsitsa kuchita zimene akaziwa ankafuna. Komanso, pofuna kuti achoke pa chiyeso chimenechi, iye anakapeza ntchito kwina. Anachita zanzeruzi chifukwa cha kuopa Mulungu ndipo anadalitsidwa, chifukwa tikunena pano André ali ndi mwayi wakuti panthawi yake ina amatumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lake.

20, 21. (a)  Kodi kuopa Mulungu kungatithandize bwanji kupewa kuchimwa? (b) Kodi nkhani yotsatirayi yalongosola chiyani?

20 Kuganizira kwambiri zinthu zoipa kungachititse munthu kuti m’maganizo mwake akhale wokonzeka kutaya ubwenzi wamtengo wapatali umene ali nawo ndi Yehova pofuna kupeza chinthu chinachake chimene sali woyenerera kukhala nacho. (Yakobo 1:14, 15) Komano tikamaopa Yehova, timapewa anthu, malo, zochitika, ndiponso zosangalatsa zimene zingatiiwalitse makhalidwe athu abwino ndipo pena timachita kuzithawa zinthu zoterezi. (Miyambo 22:3) Kaya tichite manyazi kapena tivutike motani, zonsezi n’zochepa poyerekezera ndi kuti Yehova asiye kutiyanja. (Mateyu 5:29, 30) Kuopa Mulungu kumatanthauza kuti tisamaziike dala pa ngozi yotha kukumana ndi zoipa, monga kuona zithunzi zolaula za mtundu wina uliwonse, koma m’malo mwake ‘tichititse mlubza maso athu kuti asapenye zachabe.’ Tikamatero, sitingakayike kuti Yehova ‘adzatipatsa moyo’ ndi zinthu zonse zimene timafunikira.​—Salmo 84:11; 119:37.

21 N’zoona kuti nthawi zonse kuchita zinthu moopadi Mulungu n’chinthu chanzeru. Komanso kumatipatsa chimwemwe chenicheni. (Salmo 34:9) Zimenezi zalongosoledwa bwino m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Onani nkhani yakuti “Lingaliro la Baibulo: Kodi Mungamuope Bwanji Mulungu Wachikondi?” mu Galamukani! ya January 8, 1998, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 19 Dzinali talisintha.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi kuopa Mulungu kumaphatikizapo makhalidwe achikristu ati?

• Kodi kuopa Mulungu kumathetsa bwanji kuopa anthu?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaona pemphero m’njira yoyenera?

• Kodi kuopa Mulungu kumatiletsa bwanji kusachimwa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Davide anaphunzira kuopa Mulungu poona ntchito za Yehova

[Zithunzi patsamba 24]

Kodi mungatani ngati mutakumana ndi chiyeso chinachake mosayembekezeka?