Kuvala Malaya Aubweya Pofuna Kukhala Wauzimu
Kuvala Malaya Aubweya Pofuna Kukhala Wauzimu
MFUMU LOUIS YACHISANU NDI CHINAYI ya ku France inkavala malaya otere. Adakali mnyamata, Sir Thomas More, ankaphunzira za malamulo ndipo ankakhala maso kwa maola 19 kapena 20 tsiku lililonse kwa miyezi ingapo, mothandizidwa ndi malaya otere. Akuti mbali yaikulu ya moyo wake, More ankavala malaya otere. Thomas Becket, yemwe anali bishopu wamkulu wa ku Canterbury, ataphedwa m’tchalitchi ku Canterbury komweko, anapeza kuti anavala malaya amenewa m’kati, ndipo izi zinali zosayembekezereka. Kodi n’chinthu chimodzi chiti chimene anthu onsewa ankachita? Iwowa ankadzizunza pogwiritsa ntchito malaya aubweya n’cholinga choti athetse zikhumbo zoipa.
Malayawa ankawapanga ndi ubweya wa mbuzi ndipo ankawavala m’kati kuti azibayabaya khungu n’kumalinyerenyetsa kwambiri. Komanso nsabwe zinkaswana kwambiri m’malaya amenewa. Akuti Thomas Becket ankavala malaya aubweyawa, pamodzi ndi kabudula wam’kati waubweyanso, mpaka kufika poti malayawa “anadzaza nsabwe zokhazokha.” Pambuyo pa zaka za m’ma 1700, m’malo mwa ubweya wa mbuzi, nthawi zina ankagwiritsa ntchito mawaya osongoka ang’onoang’ono akuthwa kutsogolo ndipo ankawaimika m’njira yoti azibaya khungu. Kukonza malayawa m’njira imeneyi kunkachititsa kuti wovalayo azunzike kwambiri.
Buku lina limati, cholinga cha malaya amenewa, mofanana ndi njira zina zodzizunzira motere, chinali “choletsa zikhumbo zoipa za thupi n’kulimbikitsa munthu kuti aziganizira kwambiri zinthu zauzimu pa moyo wake.” Si anthu okhala moyo wodzimana okha amene ankavala malaya amenewa; ngakhale anthu wamba, kuphatikizapo anthu a maudindo akuluakulu, akuti ankavalanso malayawa. Ngakhale panopo, pali zipani zosiyanasiyana za zipembedzo zimene anthu awo ena amavala malaya otere.
Kodi kuvala malaya aubweya kapena kukhala dala moyo wodzimana zofunikira pa moyo kungam’pangitse munthu kukhala wauzimu? Ayi, kuti munthu akhale wauzimu safunika kuchita zinthu zodzizunza ngati zimenezi. Kwenikweni, mtumwi Paulo analetsa khalidwe la “kuzunza thupi.” (Akolose 2:23, NW) * M’malo mwake, moyo wauzimu weniweni umabwera chifukwa chofuna kudziwa Mulungu pophunzira Mawu ake mwakhama ndi kugwiritsa ntchito zimene tikudziwazo m’moyo wathu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Kuti mudziwe zina zokhudza nkhaniyi, onani nkhani yakuti, “Lingaliro la Baibulo: Kodi Kudzimana Konyanya Ndiyo Njira Yopezera Nzeru?” yomwe ili mu Galamukani! ya October 8, 1997.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
King Louis IX, top: From the book Great Men and Famous Women; Thomas Becket, center: From the book Ridpath’s History of the World (Vol. IV); Thomas More, bottom: From the book Heroes of the Reformation, 1904