Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi timadziwa bwanji kuti mawu ofotokoza nzeru pa Miyambo 8:22-31 amanena za Yesu Kristu asanabadwe padziko monga munthu?

Mawu ouziridwa ofotokoza nzeru m’buku la Miyambo amati: “Mulungu anali nane [anandipanga, NW] poyamba njira yake, asanalenge zake zakale. . . . Mapiri asanakhazikike, zitunda zisanapangidwe, ndinabadwa . . . Pamene anakhazika mlengalenga ndinali pompo; . . . ndinali pa mbali pake ngati mmisiri; ndinam’sekeretsa tsiku ndi tsiku ndi kukondwera pamaso pake nthawi zonse, . . . ndi kusekerera ndi ana a anthu.”

Lemba limeneli silikunena za nzeru za Mulungu kapena nzeru chabe ayi. N’chifukwa chiyani silikutero? Chifukwa chakuti nzeru imene ikutchulidwa apa ‘inapangidwa’ monga poyambira njira ya Yehova. Yehova Mulungu alibe chiyambi ndipo wakhala wanzeru kuyambira kalekale. (Salmo 90:1, 2) Nzeru zake zilibe chiyambi; sizinachite kupangidwa ayi. Sizinachite ‘kubadwa.’ Komanso, akuti nzeru imeneyi ikulankhula ndi kuchita zinthu, zimene zikutanthauza kuti nzeruyi ikuimira munthu.​—Miyambo 8:1.

Buku la Miyambo limati, kale nzeru inali pambali pa Yehova, yemwe ndi Mlengi, ndipo inali pamenepo “ngati mmisiri.” Mawu amenewa akugwirizana zedi ndi Yesu. Kwa nthawi yaitali asanabwere padziko lapansi, Yesu ankagwira ntchito mogwirizana kwambiri ndi Yehova moti Mawu a Mulungu amati: “Ndipo iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa iye [zinakhalapo kudzera mwa iye, NW].”​—Akolose 1:17; Chivumbulutso 3:14.

Kufotokoza Mwana wa Mulungu ngati nzeru n’koyenera, chifukwa iye ndiye anavumbula zolinga ndiponso malamulo anzeru a Yehova. Asanabwere padziko pano n’kudzakhala munthu, Yesu anali Mawu a Mulungu, kapena kuti Wolankhulira Mulungu. (Yohane 1:1) Baibulo limalongosola kuti iye ndi “mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu.” (1 Akorinto 1:24, 30) Awatu ndi mawu osangalatsa kwambiri ofotokoza Mwana wa Mulungu, amene amakonda kwambiri anthu moti mpaka anapereka moyo wake kukhala dipo lowawombola.​—Yohane 3:16.

[Chithunzi patsamba 31]

“Mapiri asanakhazikike . . . ndinabadwa”