Kodi Mukukumbukira?
Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:
• Monga mmene lemba la Salmo 72:12 limanenera, kodi Yesu “adzapulumutsa waumphawi,” motani?
Muulamuliro wake, chilungamo chidzakhalapo kwa aliyense, ndipo sikudzakhalanso ziphuphu. Kawirikawiri nkhondo imabweretsa umphawi, koma Kristu adzabweretsa mtendere pena paliponse. Iye amachita chifundo ndi anthu ndipo adzagwirizanitsa anthu onse, ndiponso adzaonetsetsa kuti anthu ali ndi chakudya chokwanira. (Salmo 72:4-16)—5/1, tsamba 7.
• Ndi motani mmene ife monga Akristu tingasonyezere “ufulu wa kulankhula”? (1 Timoteo 3:13; Filemoni 8; Ahebri 4:16)
Tingatero mwa kulalikira kwa ena mwachangu ndi molimba mtima, mwa kuphunzitsa ndi kupereka uphungu mwamsanga ndi mogwira mtima, ndiponso mwa kumuuza Mulungu zakukhosi kwathu popemphera, tili ndi chikhulupiriro kuti iye akumva mapemphero athuwo ndipo atiyankha.—5/15, tsamba 14 mpaka 16.
• N’chifukwa chiyani m’Chilamulo zinthu zina zochitika mwachibadwa zokhudza kugonana zinkachititsa munthu kukhala ‘wodetsedwa’?
Malamulo amene ankanena za zinthu zodetsa munthu zokhudza mwamuna akagona kuipa, mkazi akakhala kumwezi, ndiponso akabereka, ankathandiza kuti anthu azikhala ndi moyo wathanzi ndiponso makhalidwe abwino kwambiri. Malamulowa ankagogomezeranso kupatulika kwa magazi ndi kufunika koteteza mtunduwo kumachimo.—6/1, tsamba 31.
• Ngati munthu akufuna kukhala wachimwemwe, n’chifukwa chiyani angachite bwino kuganizira buku la Masalmo?
Olemba Masalmo ankadziwa kuti chimwemwe chimabwera chifukwa chokhala ndi ubwenzi wabwino ndi Mulungu. (Salmo 112:1) Anagogomezera kuti palibe ubwenzi ndi munthu wina aliyense, kaya kukhala ndi katundu wotani, kapena kukwanitsa kuchita chinthu chinachake kumene kungabweretse chimwemwe ngati chimene chimabwera chifukwa chokhala m’gulu la “anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.” (Salmo 144:15)—6/15, tsamba 12.
• Kodi Aisrayeli akale anali pa ubwenzi wapadera wotani ndi Yehova?
Mu 1513 B.C.E., Yehova anakhala pa unansi watsopano ndi Aisrayeli, analowa m’pangano. (Eksodo 19:5, 6; 24:7) Kenako, Aisrayeli ankabadwira mu mtundu wopatulika wa anthu a Mulungu odzipereka kwa iye. Komabe, aliyense payekha anayenera kusankha yekha kutumikira Mulungu.—7/1, tsamba 21 mpaka 22.
• N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zonse “kopanda madandaulo,” kapena kuti kung’ung’udza? (Afilipi 2:14)
Zitsanzo zambiri za m’Malemba zimasonyeza kuti kung’ung’udza kunachititsa mavuto pakati pa anthu a Mulungu. Tiyenera kuganiza mozama ponena za mavuto amene kung’ung’udza kungachititse masiku ano. Anthu opanda ungwiro ali ndi chizolowezi chodandaula, ndipo tiyenera kusamala kuti tithe kuona chizindikiro chilichonse cha khalidweli mwa ifeyo, n’kuchipewa.—7/15, tsamba 16 mpaka 17.
• Kodi timadziwa bwanji kuti nzeru imene inafotokozedwa pa Miyambo 8:22-31 si nzeru chabe?
Nzeru imeneyi ‘inapangidwa,’ kapena kulengedwa monga poyambira njira ya Yehova. Mulungu alibe chiyambi ndipo wakhala wanzeru kuyambira kalekale. Nzeru zake sizinachite kulengedwa ayi. Nzeru ya pa Miyambo 8:22-31 inali pambali pa Mulungu ngati “mmisiri,” zimene zikugwirizana ndi cholengedwa chauzimu chimene chinadzakhala Yesu amene anagwira ntchito mogwirizana ndi Mulungu polenga zinthu. (Miyambo 8:22-31; Akolose 1:17; Chivumbulutso 3:14)—8/1, tsamba 31.