Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Monga Kumwamba Chomwecho Pansi Pano”

“Monga Kumwamba Chomwecho Pansi Pano”

“Monga Kumwamba Chomwecho Pansi Pano”

“Chikhulupiriro cha Akatolika n’chakuti pali Zinthu Zinayi Zotsiriza izi: Imfa, Chiweruzo, Gehena, ndi Kumwamba.”​—Linatero buku lakuti Catholicism, lolembedwa ndi George Brantl.

ONANI kuti pa mndandanda wa Zinthu Zinayi Zotsiriza zimene zingachitikire anthu, dziko lapansi silinatchulidwepo. Zimenezi n’zosadabwitsa m’pang’ono pomwe chifukwa chakuti Tchalitchi cha Katolika, mofanana ndi matchalitchi ena ambiri, chimakhulupirira kuti tsiku lina dziko lapansi lidzawonongedwa. Buku lina la matanthauzo a mawu lakuti Dictionnaire de Théologie Catholique, pa mawu akuti “Kutha kwa Dziko” limati: “Tchalitchi cha Katolika chimakhulupirira ndi kuphunzitsa kuti dziko limene lilipoli, monga mmene Mulungu analilengera ndi mmene lilili, silidzakhalapo kosatha.” Katekisima wa Chikatolika waposachedwapa amasonyezanso maganizo omwewa kuti: “Dziko lathuli . . . linapangidwa kuti lidzawonongedwe.” Koma ngati pulaneti yathuyi iti idzawonongedwe, nanga bwanji za malonjezo a m’Baibulo onena za paradaiso wa padziko lapansi?

Baibulo limanena momveka bwino za paradaiso wa m’tsogolo wa padziko lapansi pano. Mwachitsanzo, mneneri Yesaya anafotokoza za dziko ndi anthu ake motere: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja awo.” (Yesaya 65:21, 22) Ayuda, amene Mulungu anawalonjeza zimenezi, sankakayikira kuti dziko lawo, inde dziko lonse lapansi, tsiku lina lidzasanduka paradaiso amene anthu adzasangalale kukhalamo kwamuyaya.

Salmo 37 limatsimikizira za chiyembekezo chimenechi. Limati: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi.” (Salmo 37:11) Vesi limeneli silikunena za kubwezeretsedwa kwa kanthawi chabe kwa mtundu wa Aisrayeli ku Dziko Lolonjezedwa ayi. Salmo lomweli limanenanso momveka bwino kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) * Onani kuti salmoli likunena kuti moyo wosatha padziko lapansi udzakhala mphoto kwa anthu “ofatsa.” M’Baibulo lina la Chifalansa, ndemanga ya pavesili imanena kuti mawu akuti “wofatsa,” “ali ndi matanthauzo ambiri kuposa mmene amamvekera m’Mabaibulo osiyanasiyana; amaphatikizapo anthu osauka, amene akuzunzika chifukwa chofuna kukondweretsa Yahweh, anthu a mtima wodzichepetsa amene amagonjera Mulungu.”

Adzakhala Padziko Lapansi Kapena Kumwamba?

Mu ulaliki wa pa phiri, Yesu analonjeza zinthu zimene zikutikumbutsa malemba amene agwidwa mawu pamwambapa. Anati: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5) Kachiwirinso, dziko lapansi lidzakhala mphoto yosatha kwa anthu okhulupirika. Komabe, Yesu ananena momveka bwino kwa atumwi ake kuti akuwakonzera malo “m’nyumba ya Atate [wake]” ndipo akakhala kumwamba limodzi ndi iye. (Yohane 14:1, 2; Luka 12:32; 1 Petro 1:3, 4) Ndiyeno, kodi tizimva bwanji malonjezo a madalitso a padziko lapansi? Kodi malonjezowo akufunika masiku ano, ndipo kodi adzapita kwa ndani?

Akatswiri ambiri a maphunziro a Baibulo amati “dziko lapansi” limene linatchulidwa mu ulaliki wa pa phiri wa Yesu ndipo ngakhalenso mu Salmo 37 ndi lophiphiritsa chabe. Mu ndemanga zake za mu Bible de Glaire, F. Vigouroux anaona “chifanizo cha kumwamba ndi cha tchalitchi,” m’mavesi amenewa. Munthu wina wofufuza za Baibulo wa ku France, dzina lake M. Langrange, anati lonjezo limeneli, “si lonjezo lakuti ofatsa adzalandira dziko lapansi limene tikukhalali, kaya likhale dziko limene lilipoli kapena dziko latsopano limene lidzakhalepo m’tsogolo. Koma lonjezoli likutanthauza kuti ofatsa akakhala kulikonse kumene kudzakhala ufumu wa kumwamba.” Mogwirizana ndi wofufuza za Baibulo wina, lonjezo limeneli “amaligwiritsa ntchito mophiphiritsa ponena za kumwamba.” Komabe mogwirizana ndi ofufuza za Baibulo ena, “dziko lolonjezedwa la Kanani, mophiphiritsa limaimira dziko la kwawo kumwamba, ufumu wa Mulungu, malo amene adzaperekedwa kwa anthu ofatsa. Limenelonso ndi tanthauzo la chithunzithunzi chimenechi cha Salmo 37 ndi m’malo enanso omwe mawuwa amapezeka.” Koma kodi tiyenera kufulumira kuchotsa dziko lapansi pa malonjezo a Mulungu?

Cholinga Chamuyaya Chokhudza Dziko Lapansi

Pachiyambi, dziko lapansi linkagwirizana mwachindunji ndi cholinga cha Mulungu kwa anthu. Wamasalmo analemba kuti: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.” (Salmo 115:16) Motero, cholinga choyambirira cha Mulungu kwa anthu chinali chogwirizana ndi dziko lapansi, osati kumwamba. Yehova analamula banja loyambirira la anthu kuti likuze munda wa Edene kuti ufike pa dziko lonse lapansi. (Genesis 1:28) Cholinga chimenechi sichinali cha nthawi yochepa chabe. Yehova amatsimikiza m’Mawu ake kuti dziko lapansi lidzakhalako kosatha. Amati: “Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse.”​—Mlaliki 1:4; 1 Mbiri 16:30; Yesaya 45:18.

Malonjezo a Mulungu sangokhala osakwaniritsidwa, pakuti iye ndi Wam’mwambamwamba, ndipo amaonetsetsa kuti akwaniritsidwa. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha kayendedwe ka madzi, Baibulo limafotokoza kuti palibe chimene chingalepheretse malonjezo a Mulungu kukwaniritsidwa: “Pakuti monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, . . . momwemo adzakhala mawu anga [mawu a Mulungu] amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.” (Yesaya 55:10, 11) Mulungu amalonjeza zinthu kwa anthu. Pangadutse nthawi malonjezowo asanakwaniritsidwe, koma salephera kukwaniritsidwa. ‘Amabwerera’ kwa iye atachita zonse zimene zinanenedwa.

Mosakayikira, Yehova ‘anafuna’ kulenga dziko lapansi kaamba ka anthu. Pamapeto pa tsiku lolenga lachisanu ndi chimodzi, iye ananena kuti zinthu zonse zinali “zabwino ndithu.” (Genesis 1:31) Kusintha kwa dziko lapansi kukhala paradaiso kwamuyaya ndi mbali ya cholinga cha Mulungu chimene sichinakwaniritsidwebe. Komabe, malonjezo a Mulungu ‘sadzabwerera kwa iye chabe.’ Malonjezo onse a moyo wangwiro padziko lapansi, pamene anthu adzakhale kosatha mu mtendere ndi chisungiko, adzakwaniritsidwa.​—Salmo 135:6; Yesaya 46:10.

Cholinga cha Mulungu Sichidzalephera Kukwaniritsidwa

Tchimo la makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava, linasokoneza kwa kanthawi cholinga choyambirira cha Mulungu, chopanga dziko lapansi kukhala paradaiso. Pambuyo pa kusamvera kwawo, anathamangitsidwa m’munda wa Edene. Choncho anataya mwayi wokwaniritsa nawo cholinga cha Mulungu choti anthu angwiro akhale m’paradaiso padziko lapansi. Komabe, Mulungu anakonza zinthu kuti akwaniritse cholinga chakecho. Motani?​—Genesis 3:17-19, 23.

Mmene zinthu zinalili mu Edene n’zofanana ndi munthu amene wayamba kumanga nyumba pamalo abwino kwambiri. Koma atangoyala maziko a nyumbayo, munthu wina akubwera n’kudzawononga mazikowo. M’malo mongolekera panjira ntchito yakeyo, munthuyo akuchita zinthu zosiyanasiyana pofuna kuonetsetsa kuti nyumbayo ithe. Ngakhale kuti ntchito yowonjezera imeneyo ingafunike ndalama zinanso zowonjezera, n’zosakayikitsa kuti ntchito yomanga nyumba imene anaiyamba poyambirira paja, inali yofunika.

Mofanana ndi zimenezo, Mulungu anapanga makonzedwe otsimikizira kuti cholinga chake chikwaniritsidwe. Makolo athu oyamba atangochimwa, iye analengeza za chiyembekezo cha ana awo, “mbewu” imene idzachotseratu mavuto onse. Pokwaniritsa ulosi umenewu, mbali yoyamba ya mbewu imeneyi inadzakhala Mwana wa Mulungu, Yesu, amene anabwera padziko lapansi ndi kupereka moyo wake monga nsembe kuti awombole anthu. (Agalatiya 3:16; Mateyu 20:28) Ataukitsidwira kumwamba, Yesu anadzakhala Mfumu ya Ufumuwo. Kwenikweni, Yesu ndi munthu wofatsa amene analandira dziko lapansi pamodzi ndi osankhidwa okhulupirika ena oukitsidwira kumwamba kuti akalamulire limodzi ndi Yesu mu Ufumu umenewu. (Salmo 2:6-9) M’kupita kwa nthawi, boma limeneli lidzayamba kulamulira dziko lonse lapansi pofuna kukwaniritsa cholinga choyambirira cha Mulungu ndi kusandutsa dziko lapansi kukhala paradaiso. Anthu ambiri ofatsa “adzalandira dziko lapansi” m’njira yakuti iwo adzapindula ndi ulamuliro wa Ufumu umenewu wolamulidwa ndi Yesu Kristu limodzi ndi olamulira anzake.​—Genesis 3:15; Danieli 2:44; Machitidwe 2:32, 33; Chivumbulutso 20:5, 6.

“Monga Kumwamba Chomwecho Pansi Pano”

M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona magulu awiri opulumutsidwa, la anthu okhala kumwamba ndi gulu lina la anthu okhala padziko lapansi. Anaona mafumu ali pa mipando yachifumu kumwamba, amene anasankhidwa kuchokera mwa ophunzira okhulupirika a Kristu. Baibulo limafotokoza za anzake a Kristu amenewa kuti “achita ufumu padziko.” (Chivumbulutso 5:9, 10) Taonani mbali ziwiri za kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Mulungu, dziko lapansi lokonzedwanso ndi kulamulidwa ndi Ufumu wa kumwamba wopangidwa ndi Yesu Kristu ndi olowa m’nyumba anzake. Makonzedwe a Mulungu onsewa akuchititsa kuti zikhale zotheka kukonzanso dziko lapansi komaliza mogwirizana ndi cholinga choyambirira cha Mulungu.

M’pemphero lake lachitsanzo, Yesu anauza ophunzira ake kuti azipemphera kuti chifuniro cha Mulungu chichitike “monga kumwamba, chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Kodi mawu amenewa angakhale ndi tanthauzo ngati dziko liti lidzawonongedwe kapena ngati linangophiphiritsa kumwamba? Komanso, kodi zingakhale zomveka ngati olungama onse adzapite kumwamba? Chifuniro cha Mulungu cha dziko lapansili chafotokozedwa momveka bwino m’Malemba, kuyambira m’nkhani yonena za chilengedwe mpaka kufika ku masomphenya a m’buku la Chivumbulutso. Dziko lapansi lidzakhala paradaiso, mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu. Chimenechi ndi chifuniro chimene Mulungu akulonjeza kuti chidzakwaniritsidwa. Anthu okhulupirika amene ali padziko lapansi amapempherera kukwaniritsidwa kwa chifuniro chimenechi.

Cholinga choyambirira cha Mlengi, Mulungu amene ‘sanasinthe’ n’chakuti anthu akhale ndi moyo wosatha padziko lapansi. (Malaki 3:6; Yohane 17:3; Yakobo 1:17) Kwa zaka zoposa 100, magazini ino, ya Nsanja ya Olonda, yakhala ikufotokoza mbali ziwiri zimenezi za kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Mulungu. Zimenezi zimatithandiza kumvetsa malonjezo a m’Malemba a kukonzedwanso kwa dziko lapansi. Tikukupemphani kuti mumve mfundo zina zowonjezeka za nkhani imeneyi, pokambirana ndi Mboni za Yehova kapena polemba kalata kwa ofalitsa magazini ino.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Ngakhale kuti Mabaibulo ambiri amamasulira mawu a Chihebri akuti ‘eʹrets kuti “malo,” m’malo mwa “dziko lapansi,” palibe chifukwa chilichonse chonenera kuti mawu akuti ‘eʹrets amene ali pa Salmo 37:11, 29 amangotanthauza dziko limene mtundu wa Aisrayeli unapatsidwa. Buku lakuti Old Testament Word Studies limene analemba William Wilson limatanthauzira mawu akuti ‘eʹrets kuti “kwenikweni ndi dziko lonse lapansi, kutanthauza malo okhalidwa ndi anthu ndiponso amene alibe anthu; koma nthawi zina malinga ndi mmene agwiritsidwira ntchito amatanthauza malo enaake padziko lapansi, kapena dziko.” Choncho tanthauzo loyamba la mawu a Chihebri omwe anagwiritsidwa ntchito m’malo mwa “malo,” ndi pulaneti lathuli, dziko lapansi.​—Onani Nsanja ya Olonda ya May 15, 1986, tsamba 31.

[Chithunzi patsamba 4]

Baibulo limanena momveka bwino za kukhazikitsidwa kwa dziko lapansi la Paradaiso m’tsogolo

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi pemphero lachitsanzo la Yesu lingakhale ndi tanthauzo ngati dziko lapansili liti lidzawonongedwe?