Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mudamva za Chipiriro cha Yobu”

“Mudamva za Chipiriro cha Yobu”

“Mudamva za Chipiriro cha Yobu”

“Mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.”​—YAKOBO 5:11.

1, 2. Kodi banja lina la ku Poland linakumana ndi chiyeso chotani?

HARALD ABT anali atakhala Mboni ya Yehova kwa nthawi yosakwana chaka chimodzi pamene asilikali a Hitler anagonjetsa mzinda wa Danzig (tsopano Gdańsk), kumpoto kwa dziko la Poland. Kenako zinthu zinafika povuta kumeneko, ndiponso poopsa, makamaka kwa Akristu oona. Apolisi a gulu la Gestapo anayesetsa kukakamiza Harald kuti asaine pepala losonyeza kuti wasiya zimene ankakhulupirira, koma iye anakana. Patapita masabata angapo ali m’ndende, Harald anatumizidwa ku ndende yozunzirako anthu ya Sachsenhausen kumene ankamuopseza nthawi zonse ndiponso kum’menya. Ofesala wina anauza Harald uku akuloza chumuni cha nyumba imene ankawotcheramo mitembo ya anthu kuti: “Ngati uumirirabe pa zimene umakhulupirirazo, m’masiku 14 akubwerawa udzakwera mmenemo kupita kwa Yehova wakoyo.”

2 Pamene Harald ankamangidwa n’kuti mkazi wake Elsa ali ndi mwana wa miyezi teni, yemwe anali adakayamwa. Koma a gulu la Gestapo sanamvere chisoni Elsa. Posapita nthawi, anam’landa mwana wake uja, ndipo anam’tumiza ku ndende yopherako anthu ku Auschwitz. Komabe, Elsa anakhalabe ndi moyo kundendeko kwa zaka zambiri ngati mmene anachitiranso Harald. Mungawerenge zambiri za mmene anapiririra mu Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya April 15, 1980. Harald analemba kuti: “Ndinakhala zaka 14 m’ndende zosiyanasiyana chifukwa cha chikhulupiriro changa pa Mulungu. Ndakhala ndikufunsidwa kuti: ‘Kodi mkazi wako ankakuthandiza kupirira zinthu zonsezi?’ Indedi wakhala akundithandiza! Ndinkadziwa kuyambira pachiyambi kuti sangasiye chikhulupiriro chake, ndipo kudziwa zimenezi, kunandilimbikitsa. Ndinali kudziwa kuti angakonde kundiona nditamwalira, koposa kudziwa kuti ndatuluka kundende chifukwa chakuti ndasiya chikhulupiriro changa. . . . Elsa anapirira zovuta zambiri pa zaka zimene anali ku ndende zozunzirako anthu ku Germany.”

3, 4. (a) Kodi n’chitsanzo cha ndani chimene chingalimbikitse Akristu kupirira? (b) N’chifukwa chiyani Baibulo limatilimbikitsa kuganizira zimene Yobu anakumana nazo?

3 Ndithudi, kuvutika sikophweka ayi, ndipo Mboni zambiri zingavomereze mfundo imeneyi. Pachifukwa chimenechi, Baibulo limapereka uphungu kwa Akristu onse kuti: “Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m’dzina la Ambuye.” (Yakobo 5:10) Kwa zaka zambiri, atumiki ambiri a Mulungu akhala akuzunzidwa popanda chifukwa. Zitsanzo zoperekedwa ndi ‘mtambo waukulu wa mboni’ umenewu, zingatilimbikitse kuti tithamangebe mwachipiriro mpikisano wathu wachikristu.​—Ahebri 11:32-38; 12:1.

4 M’Baibulo, Yobu ndi chitsanzo chapadera kwambiri cha kupirira. Yakobo analemba kuti: “Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Zimene Yobu anakumana nazo zimatisonyeza za mphoto imene anthu okhulupirika, amene Yehova akuwadalitsa adzalandire. Chofunika kwambiri n’chakuti, zimasonyeza mfundo za choonadi zimene zingatipindulitse panthawi ya mavuto. Buku la Yobu limatithandiza kuyankha mafunso awa: Tikamayesedwa, n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kumvetsa nkhani zikuluzikulu zimene zikulowetsedwamo? Kodi ndi makhalidwe ndiponso maganizo otani amene angatithandize kupirira? Kodi tingalimbikitse motani Akristu anzathu amene akuvutika?

Kumvetsa Bwino Nkhani Yonse

5. Tikakumana ndi ziyeso, kodi nthawi zonse tiyenera kuganizira nkhani yaikulu iti?

5 Kuti tikhalebe olimba mwauzimu tikakumana ndi mavuto, timafunika kumvetsa nkhani yonse. Ngati sititero, mavuto amene timakumana nawo angatichititse kuti tisamaone bwino mwauzimu. Nkhani yokhala wokhulupirika kwa Mulungu ndi yofunika kwambiri. Atate wathu wakumwamba akutiuza motere zinthu zimene tiyenera kuganizira: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) Umenewu ndi mwayi wapadera. Ngakhale kuti ndife anthu ofooka ndiponso opanda ungwiro, tingakondweretse Mlengi wathu. Tingachite zimenezo ngati chikondi chathu pa Yehova chimatichititsa kupirira ziyeso. Chikondi choona cha Akristu chimapirira zinthu zonse, ndipo sichilephera.​—1 Akorinto 13:7, 8.

6. Kodi Satana amatonza motani Yehova, ndipo kodi zitonzo zake zafika pati?

6 Buku la Yobu limatchula momveka bwino kuti Satana ndi amene amatonza Yehova. Limavumbulanso mtima woipa wa mdani wosaoneka ameneyu ndiponso cholinga chake chofuna kuwononga unansi wathu ndi Mulungu. Monga mmene nkhani ya Yobu imasonyezera, Satana makamaka amaimba mlandu atumiki onse a Yehova kuti amam’tumikira ndi zolinga zadyera ndipo amafuna atatsimikizira kuti atumikiwa angasiye kukonda Mulungu. Wakhala akutonza Mulungu kwa zaka masauzande ambiri. Satana atagwetsedwa kuchokera kumwamba, mawu ochokera kumwamba anam’fotokoza kuti ndi “wonenera wa abale athu” ndipo anati amawanenera “pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.” (Chivumbulutso 12:10) Mwa kupirira mokhulupirika, tingasonyeze kuti zimene amanena Satanazo n’zabodza.

7. Kodi tingalimbane motani ndi kufooka kwa thupi?

7 Tiyenera kukumbukira kuti Mdyerekezi angapezerepo mwayi pachisautso chilichonse chimene tingakumane nacho poyesa kutichititsa kuti titalikirane ndi Yehova. Kodi ndi liti pamene anayesa Yesu? Inali nthawi imene Yesu anali ndi njala, pambuyo posala kudya kwa masiku ambiri. (Luka 4:1-3) Komabe, mphamvu yauzimu imene Yesu anali nayo, inam’thandiza kukana zolimba mayesero a Mdyerekezi. Choncho n’kofunika kulimbana ndi zofooka zina zilizonse zimene zingayambe, mwina chifukwa cha matenda kapena ukalamba, pogwiritsa ntchito mphamvu yauzimu. Ngakhale kuti “umunthu wathu wakunja uvunda,” sitigonja chifukwa umunthu “wa mkati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.”​—2 Akorinto 4:16.

8. (a) Kodi ndi motani mmene mavuto angatifooketsere? (b) Kodi Yesu anali ndi mtima wotani?

8 Kuwonjezera apo, mavuto angawononge munthu mwauzimu. Mwina munthu ungadabwe kuti: ‘N’chifukwa chiyani Yehova akulola zimenezi?’ Munthu wina angafunse pambuyo pochitiridwa nkhanza kuti: ‘Mbale angachite bwanji zimenezi?’ Kuganiza motero kungatichititse kunyalanyaza nkhani zikuluzikulu, n’kumangoganiza za zimene tikukumana nazozo basi. Kukhumudwa kwa Yobu ndi anzake atatu onyenga aja kunamuwononga maganizo kwambiri ngati mmene matenda ake aja anawonongera thupi lake. (Yobu 16:20; 19:2) Mofanana ndi zimenezo, mtumwi Paulo anasonyeza kuti kukhala wokwiya kwa nthawi yaitali ‘kungapatse malo [kapena kuti mwayi] Mdyerekezi.’ (Aefeso 4:26, 27) M’malo mosonyeza kukhumudwa kapena kukwiya ndi munthu winawake, kapena kuganizira kwambiri za kupanda chilungamo komwe kwachitika, Akristu angapindule kwambiri mwa kutsanzira Yesu ‘popereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama,’ Yehova Mulungu. (1 Petro 2:21-23) Mwa kukhala ndi “mtima” wa Yesu, tingatetezedwe kwambiri pamene Satana akutiukira.​—1 Petro 4:1.

9. Kodi Mulungu akutitsimikizira chiyani ponena za mavuto amene angatigwere kapena mayesero amene tingakumane nawo?

9 Koposa zonse, sitiyenera kuganiza kuti mavuto athu ndi umboni wotsimikizika woti Mulungu sakukondwera nafe. Kusamvetsa bwino kumeneko n’kumene kunapweteka Yobu panthawi imene anthu omwe ankafunika kum’limbikitsa ankamunenera mawu opweteka. (Yobu 19:21, 22) Baibulo limatitsimikizira mawu awa: “Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu.” (Yakobo 1:13) Mosiyana ndi zimenezi, Yehova akulonjeza kuti adzatithandiza kupirira zovuta zilizonse zimene zingatigwere ndipo adzapereka populumukira chiyeso chilichonse chimene tingakumane nacho. (Salmo 55:22; 1 Akorinto 10:13) Mwa kuyandikira kwa Mulungu panthawi ya mavuto, tingathe kuona zinthu bwinobwino ndipo tingathe kukaniza Mdyerekezi.​—Yakobo 4:7, 8.

Zinthu Zotithandiza Kupirira

10, 11. (a) Kodi n’chiyani chinathandiza Yobu kupirira? (b) Kodi kukhala ndi chikumbumtima chabwino kunam’thandiza motani Yobu?

10 Mosasamala kanthu za mmene Yobu analili, kuphatikizapo mawu achipongwe ochokera kwa anthu amene anayenera kumutonthoza, ndiponso kusokonezeka maganizo posadziwa chenicheni chimene chinayambitsa mavutowo, Yobu anasungabe umphumphu wake. Kodi tingaphunzire chiyani pa kupirira kwake? Mosakayikira, kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndicho chinthu chachikulu chimene chinam’chititsa kupambana. ‘Anaopa Mulungu ndi kupewa zoipa.’ (Yobu 1:1) Umu ndi mmene ankakhalira. Yobu anakana kusiya Yehova, ngakhale pamene sanamvetse chomwe chinachititsa kuti zinthu zisinthe mwadzidzidzi. Yobu ankakhulupirira kuti ayenera kutumikira Mulungu pamtendere ndiponso pamavuto.​—Yobu 1:21; 2:10.

11 Yobu anatonthozedwanso chifukwa chokhala ndi chikumbumtima chabwino. Panthawi imene zinkaoneka ngati kuti watsala pang’ono kumwalira, iye analimbikitsidwa podziwa kuti anayesetsa kuthandiza ena, ndi kuti anakhala akusunga miyezo yolungama ya Yehova, ndiponso kuti anapewa kulambira konyenga kwa mtundu wina uliwonse.​—Yobu 31:4-11.

12. Kodi Yobu anachita motani ndi thandizo limene Elihu anam’patsa?

12 N’zoona kuti Yobu ankafunikira thandizo kuti asinthe kaonedwe kake ka zinthu zina. Ndipo analandira thandizo limenelo modzichepetsa, ndipo chimenecho chinali chinthu china chimene chinam’thandiza kuti athe kupirira. Yobu anamvetsera mwaulemu uphungu wanzeru wa Elihu, ndipo anachita mogwirizana ndi mmene Yehova anam’dzudzulira. Iye anavomereza kuti: “Ndinafotokozera zimene sindinazizindikira . . . Ndekha ndidzinyansa, ndi kulapa m’fumbi ndi mapulusa.” (Yobu 42:3, 6) Ngakhale kuti matenda anali akumusautsabe, Yobu anasangalala kuti kusintha kwa zimene ankaganiza kunam’thandiza kuyandikira kwa Mulungu. Yobu anati: “Ndidziwa kuti [inu Yehova] mukhoza kuchita zonse.” (Yobu 42:2) Yehova atafotokoza za ukulu wake, Yobu anamvetsa bwino kwambiri malo ake poyerekezera ndi a Mlengi.

13. Kodi kusonyeza chifundo kunam’thandiza motani Yobu?

13 Pomaliza, Yobu anakhala chitsanzo chapadera kwambiri cha chifundo. Omutonthoza ake onyenga aja anavulaza kwambiri maganizo ake, koma Yehova atapempha Yobu kuti awapempherere, iye anawapemphereradi. Kenako, Yehova anachiritsa Yobu. (Yobu 42:8, 10) Mwachionekere, kuipidwa sikungatithandize kuti tipirire, koma chikondi ndi chifundo zingatithandize. Kuleka kuipidwa kungatitsitsimule mwauzimu, ndipo Yehova amadalitsa mtima woterowo.​—Marko 11:25.

Alangizi Anzeru Amene Amatithandiza Kupirira

14, 15. (a) Kodi ndi makhalidwe otani amene angathandize alangizi kulimbikitsa ena? (b) Fotokozani chimene chinachititsa Elihu kuti athe kuthandiza Yobu.

14 Phunziro lina limene tingaphunzire kuchokera m’nkhani ya Yobu ndi lakuti timafunika alangizi anzeru. Amenewo ndi abale amene ‘anabadwira kuti atithandize pooneka tsoka.’ (Miyambo 17:17) Komabe, monga mmene tikuonera pa zimene Yobu anakumana nazo, alangizi ena angavulaze m’malo molimbikitsa. Mlangizi wabwino amafunika kuganizira ena, kusonyeza ulemu, ndi kukoma mtima, monga mmene anachitira Elihu. Akulu ndiponso Akristu ena okhwima angafunike kusintha kaganiziridwe ka abale amene apsinjika ndi mavuto, ndipo pankhani imeneyi, alangizi oterowo angaphunzire zochuluka kuchokera m’buku la Yobu.​—Agalatiya 6:1; Ahebri 12:12, 13.

15 Pali maphunziro ambiri abwino a mmene Elihu anachitira ndi nkhaniyo. Anamvetsera kwa nthawi yaitali asanayambe kulankhula za zolakwika zimene anzake a Yobu atatu aja ankanena. (Yobu 32:11; Miyambo 18:13) Elihu anagwiritsa ntchito dzina la Yobu ndipo anam’chonderera ngati mnzake. (Yobu 33:1) Mosiyana ndi otonthoza onyenga atatu aja, Elihu sanadziyese wopambana kwa Yobu. Iye anati: “Inenso ndinaumbidwa ndi dothi.” Sanafune kuwonjezera mavuto a Yobu mwa kulankhula zopanda pake. (Yobu 33:6, 7; Miyambo 12:18) M’malo monyoza khalidwe limene Yobu anali nalo poyamba, Elihu anam’yamikira chifukwa cha chilungamo chake. (Yobu 33:32) Chofunika kwambiri chinali chakuti, Elihu anali kuona zinthu mmene Mulungu amaonera, ndipo anam’thandiza Yobu kuona kuti Yehova sangachite zinthu mopanda chilungamo. (Yobu 34:10-12) Analimbikitsa Yobu kuti adikire Yehova, m’malo moyesa kusonyeza kuti iye anali wolungama. (Yobu 35:2; 37:14, 23) Ndithudi, akulu achikristu ndiponso anthu ena angapindule ndi maphunziro amenewa.

16. Kodi ndi motani mmene otonthoza onyenga a Yobu atatu aja anakhalira atumiki a Satana?

16 Uphungu wanzeru wa Elihu ukusiyana ndi mawu ovulaza a Elifazi, Bilidadi, ndi Zofari. Yehova anawauza kuti: “Simunandinenera choyenera.” (Yobu 42:7) Ngakhale ngati akanati anali ndi zolinga zabwino, iwo anakhala ngati atumiki a Satana m’malo mokhala mabwenzi okhulupirika. Kuyambira pachiyambi, onse atatu anaganiza kuti Yobu anayambitsa yekha mavuto ake. (Yobu 4:7, 8; 8:6; 20:22, 29) Mogwirizana ndi zimene ananena Elifazi, Mulungu sakhulupirira atumiki ake, ndipo sasamala zoti ndife olungama kapena ayi. (Yobu 15:15; 22:2, 3) Ndipo Elifazi anayimba mlandu Yobu pa zophophonya zimene sanazichite n’komwe. (Yobu 22:5, 9) Koma, Elihu analimbikitsa Yobu mwauzimu, ndipo zimenezi n’zimene mlangizi wachikondi amafunika kuchita nthawi zonse.

17. Kodi n’chiyani chimene tiyenera kukumbukira tikakumana ndi chiyeso?

17 Palinso phunziro lina la kupirira limene tingapeze kuchokera m’buku la Yobu. Mulungu wathu wachikondi amaona zimene zikutichitikira, ndipo amafuna komanso angathe kutithandiza m’njira zosiyanasiyana. Poyamba taona zimene Elsa Abt anakumana nazo. Taganizirani mawu awa amene iye ananena: “Asanandimange, ndinali nditawerenga kalata ya mlongo wina imene inati, ukakhala pachiyeso chachikulu, mzimu wa Yehova umakukhazikitsa mtima m’malo. Ndinkaganiza kuti ankakokomeza pang’ono. Koma nditakumana ndi chiyeso, ndinazindikira kuti zimene mlongoyu ananena zinali zoona. Zimachitikadi momwemo. N’zovuta kungoziganizira, ngati sunakumanepo nazo. Koma zinandichitikiradi. Yehova amathandiza.” Elsa sankalankhula za zimene Yehova akanachita kapena anachita zaka zambiri zapitazo, m’nthawi ya Yobu ayi. Iye ankalankhula za m’nthawi yathu ino. N’zoonadi, “Yehova amathandiza”!

Munthu Wopirira Amakhala Wachimwemwe

18. Kodi Yobu anapindula motani chifukwa cha kupirira?

18 Ndi ochepa a ife amene tingakumane ndi masautso aakulu monga amene Yobu anakumana nawo. Koma ziyeso zilizonse zimene zingatigwere m’dongosolo la zinthu lilipoli, tili ndi zifukwa zomveka zosungira umphumphu wathu monga mmene Yobu anachitira. Ndipotu, kupirira kunam’thandiza kwambiri Yobu. Kunam’pangitsa kukhala wangwiro, ndi wopanda chirema. (Yakobo 1:2-4) Ndipo kunalimbikitsa unansi wake ndi Mulungu. Yobu anatsimikiza kuti: “Kumva ndidamva mbiri yanu, koma tsopano ndikupenyani maso.” (Yobu 42:5) Satana anaoneka kuti n’ngwabodza chifukwa sanathe kuwononga umphumphu wa Yobu. Patapita zaka zambirimbiri, Yehova analankhulabe za mtumiki wake Yobu kuti ndi chitsanzo cha munthu wolungama. (Ezekieli 14:14) Nkhani yake ya kukhulupirika ndi kupirira, imalimbikitsa anthu a Mulungu ngakhale masiku ano.

19. N’chifukwa chiyani mukuganiza kuti kupirira n’kofunika?

19 M’kalata imene Yakobo analembera Akristu oyambirira, ananenamo za mmene kupirira kumakhutiritsira. Ndipo anagwiritsa ntchito chitsanzo cha Yobu powakumbutsa kuti Yehova amapereka mphoto yaikulu kwa atumiki ake okhulupirika. (Yakobo 5:11) Timawerenga pa Yobu 42:12 kuti: “Ndipo Yehova anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake.” Mulungu anapereka kwa Yobu zinthu zowirikiza kawiri pa zimene anataya, ndipo anakhala ndi moyo wautali, ndiponso wosangalala. (Yobu 42:16, 17) Mofanana ndi zimenezo, chisoni, mavuto, kapena masautso alionse amene tingapirire panthawi ya mapeto a dongosolo la zinthu lilipoli, zidzachotsedwa ndi kuiwalika m’dziko latsopano la Mulungu. (Yesaya 65:17; Chivumbulutso 21:4) Tamva za kupirira kwa Yobu, ndipo tatsimikiza mtima kutsanzira chitsanzo chake, mothandizidwa ndi Yehova. Baibulo limalonjeza kuti: “Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumukonda Iye.”​—Yakobo 1:12.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tingakondweretse motani mtima wa Yehova?

• N’chifukwa chiyani sitiyenera kugamula kuti mavuto athu ndi umboni woti Mulungu sakukondwera nafe?

• Ndi zinthu ziti zimene zinathandiza Yobu kupirira?

• Kodi tingatsanzire motani Elihu polimbikitsa okhulupirira anzathu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 28]

Mlangizi wabwino amaganizira ena, amasonyeza ulemu, ndi kukoma mtima

[Zithunzi patsamba 29]

Elsa ndi Harald Abt