Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Wokalamba Koma Wosasungulumwa

Wokalamba Koma Wosasungulumwa

Wokalamba Koma Wosasungulumwa

AMBIRI akamakalamba, amalumala, n’kumakhala kwaokha. Koma umu si mmene zinalili ndi Fernand Rivarol, amene anamwalira ali ndi zaka 95 ku Geneva, m’dziko la Switzerland. Iye ankakhala yekhayekha, chifukwa mkazi wake anali atamwalira ndipo mwana wake wamkazi yemwe anali pabanja, anali ndi nyumba yake. Ngakhale kuti nthawi zambiri ankabindikira kunyumba kwake, Fernand sankakhala wosungulumwa. Kawirikawiri ankakhala patebulo la pabalaza ndi telefoni m’manja, n’kumaimbira anthu kuti alankhule nawo zinthu zauzimu.

Fernand anatsekeredwapo m’ndende nthawi ina. Chifukwa chiyani? Fernand ndi mkazi wake atangokhala Mboni za Yehova zachangu mu 1939, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inayambika ku Ulaya. Fernand anakhalabe mogwirizana ndi chosankha chake chochokera m’Baibulo, chosafuna kuvulaza aliyense. Chifukwa cha zimenezo, anam’chotsa ntchito ndipo anam’tsekera m’ndende maulendo angapo, moti nthawi yonse yomwe anakhala m’ndendeyo inakwana zaka zisanu ndi theka, ndipo panthawiyi anasiyana ndi mkazi wake ndiponso mwana wake yemwe anali wamng’ono.

Ataganizira zimenezi, Fernand anati: “Kwa anthu ambiri, zinkaoneka ngati kuti ndasiya ntchito yodalirika, n’kusiya banja langa lili losowa thandizo. Anthu ankandinyoza ndiponso ankanditenga ngati chigawenga. Komabe, ndikaganiza za zaka zovuta zimenezo, chimene ndimakumbukira bwino kwambiri ndi mmene Yehova anatichirikizira ndi kutithandiza. Zaka zambiri zadutsa chichitikireni zimenezo, koma chikhulupiriro changa mwa Yehova n’cholimbabe monga mmene chinalili nthawi imeneyo.”

Chikhulupiriro chimenechi n’chimene chinam’pangitsa Fernand kuuza ena patelefoni za chiyembekezo chake cha m’Malemba. Munthu wina akasangalala ndi chiyembekezochi, ankam’tumizira buku lofotokoza za m’Baibulo. Kenako, ankamuimbiranso telefoni kuti aone ngati wasangalala ndi bukulo. Nthawi zina anthu ankayankha mwa kulemba kalata yoyamikira, ndipo zimenezi zinkamusangalatsa kwambiri.

Mwina mungakumane ndi munthu wonga Fernand komwe mumakhalako. Bwanji osamvetsera zimene akufuna kulankhula kuti mudziwe zimene iye amakhulupirira? Mboni za Yehova zimasangalala nthawi zonse kukuuzani zimene zimakhulupirira.