Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yobu Anali Munthu Wopirira ndi Wosunga Umphumphu

Yobu Anali Munthu Wopirira ndi Wosunga Umphumphu

Yobu Anali Munthu Wopirira ndi Wosunga Umphumphu

“Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.”​—YOBU 1:8.

1, 2. (a) Kodi ndi mavuto adzidzidzi ati amene Yobu anakumana nawo? (b) Fotokozani mmene moyo wa Yobu unalili, mavuto asanam’gwere.

PANALI munthu wina amene anali wosasowa kanthu. Anali ndi chuma chambiri, anali munthu waulemu wake, wathanzi ndiponso anali ndi banja losangalala. Koma anakumana ndi mavuto aakulu maulendo atatu, motsatizanatsatizana. Chuma chonse chinatha mwadzidzidzi. Kenako, mphepo yamkuntho inapha ana ake onse. Pasanapite nthawi yaitali chichitikireni zimenezi, iye anayamba kudwala matenda ofooketsa amene anachititsa zironda zopweteka kwambiri thupi lake lonse. Mwina mwazindikira kuti munthuyu anali Yobu, mwininkhani m’buku la m’Baibulo limene limadziwika ndi dzina lake.​—Yobu, chaputala 1 ndi 2.

2 Yobu anadandaula kuti: “Ha! ndikadakhala monga m’miyezi yapitayi.” (Yobu 3:3; 29:2) Mavuto akafika, ndani amene safuna kuti zinthu zibwerere mwakale? Ponena za Yobu, iye anali ndi khalidwe labwino, losam’lowetsa m’mavuto. Anthu otchuka ankamulemekeza ndipo ankam’funsa uphungu. (Yobu 29:5-11) Anali ndi chuma chambiri, koma ankaona ndalama moyenerera. (Yobu 31:24, 25, 28) Akakumana ndi akazi amasiye kapena ana amasiye amene akufunikira thandizo, ankawathandiza. (Yobu 29:12-16) Ndipo anali wokhulupirika kwa mkazi wake.​—Yobu 31:1, 9, 11.

3. Kodi Yehova ankamuona motani Yobu?

3 Yobu ankakhala moyo wangwiro chifukwa ankalambira Mulungu. Yehova anati: “Palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.” (Yobu 1:1, 8) Koma ngakhale kuti Yobu anali wokhulupirika, mavuto anasokoneza moyo wake wosangalala. Zinthu zonse zomwe anapeza chifukwa cha ntchito yake zinatha, ndipo anasokonezeka maganizo chifukwa cha ululu, chisoni, ndi kugwiritsidwa mwala.

4. N’chifukwa chiyani kuli kothandiza kuganizira za mavuto amene Yobu anakumana nawo?

4 N’zoona kuti Yobu si mtumiki wa Mulungu yekhayo amene anakumana ndi mavuto. Akristu ambiri masiku ano akumana ndi mavuto ofanana ndi amene Yobu anakumana nawo. Chifukwa cha zimenezi, m’pofunika kuganizira mafunso awiri awa: Kodi kukumbukira mavuto amene Yobu anakumana nawo kungatithandize motani pamene tikukumana ndi mavuto? Ndipo mavuto akewo angatiphunzitse motani kuwamvera chifundo kwambiri anthu amene akuvutika?

Nkhani Yokhudza Kukhulupirika ndi Yoyesa Umphumphu

5. Kodi Satana anati Yobu ankatumikira Mulungu chifukwa chiyani?

5 Nkhani ya Yobu inali yapadera. Yobu sankadziwa kuti Mdyerekezi ankakayikira zolinga zimene anali nazo potumikira Mulungu. Pamsonkhano wina wakumwamba, Yehova anafotokoza za makhalidwe abwino a Yobu, ndipo Satana anayankha kuti: “Kodi simunam’tchinga iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pom’zinga ponse?” Choncho Satana anasonyeza kuti Yobu, ngakhalenso atumiki ena onse a Mulungu, amatumikira Mulungu chifukwa cha dyera. Satana anati kwa Yehova: “Mutambasule dzanja lanu ndi kum’khudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pankhope panu.”​—Yobu 1:8-11.

6. Kodi Satana anayambitsa nkhani yaikulu iti?

6 Nkhaniyi inali yaikulu. Satana anatsutsa njira imene Yehova amalamulirira. Kodi n’zothekadi kuti Mulungu alamulire chilengedwe chonse mwachikondi? Kapena, monga mmene Satana anasonyezera, kodi dyera ndilo lidzapambane pamapeto pake? Yehova analola Mdyerekezi kuti ayese Yobu monga chitsanzo, ali ndi chikhulupiriro kuti mtumiki Wakeyo asunga umphumphu ndiponso akhalabe wokhulupirika. Choncho, Satanayo anachititsa mavuto amene Yobu anakumana nawo mongotsatizanatsatizana. Satana atalephera pakuukira kwake koyamba, anadwalitsa Yobu nthenda yowawa kwambiri. Mdyerekezi anati: “Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.”​—Yobu 2:4.

7. Kodi atumiki a Mulungu masiku ano amakumana ndi mayesero ofanana ndi a Yobu m’njira zotani?

7 Ngakhale kuti Akristu ambiri masiku ano savutika ngati mmene Yobu anavutikira, iwo amakumanabe ndi masautso osiyanasiyana. Ambiri amakumana ndi chizunzo kapena mavuto a m’banja. Umphawi kapena matenda zingakhale zinthu zothetsa nzeru kwambiri. Ena ataya moyo wawo chifukwa cha zimene amakhulupirira. N’zoona kuti sitiyenera kuganiza kuti Satana ndi amene amachititsa vuto lililonse limene takumana nalo. Kwenikweni, mavuto ena angayambe chifukwa chakuti talakwitsa zinthu zina kapena chifukwa cha chibadwa chomwe tinatengera kwa makolo athu. (Agalatiya 6:7) Ndipo tonse timavutika ndi ukalamba ndiponso masoka achilengedwe. Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti panthawi ino, Yehova sateteza atumiki ake mozizwitsa ku mavuto amenewa.​—Mlaliki 9:11.

8. Kodi Satana angapezerepo mwayi wotani pa mavuto amene timakumana nawo?

8 Komabe, Satana angagwiritse ntchito mavuto amene timakumana nawo kuti afooketse chikhulupiriro chathu. Mtumwi Paulo anatchula kuti anali kuvutika ndi “munga m’thupi, mngelo wa Satana” amene anakhala ‘akum’tundudza’ nthawi zonse. (2 Akorinto 12:7) Kaya limeneli linali vuto linalake la m’thupi, monga kusatha kupenya bwino kapena ayi, Paulo ankadziwa kuti Satana angathe kugwiritsa ntchito vutolo ndi zotsatirapo zake zokhumudwitsa, n’kum’landa chimwemwe ndi chikhulupiriro chake. (Miyambo 24:10) Masiku ano, Satana angachititse anthu a m’banja mwathu, anzathu a kusukulu, kapena maboma olamula mwankhanza, kuzunza atumiki a Mulungu m’njira inayake.

9. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa kwambiri ndi mavuto kapena chizunzo?

9 Kodi tingapambane motani tikakumana ndi mavuto amenewa? Tingatero poona mavutowo ngati mwayi wosonyeza kuti timakondadi Yehova ndipo timagonjera ulamuliro wake. (Yakobo 1:2-4) Kaya tivutike chifukwa cha chiyani, kumvetsa kuti kukhala okhulupirika kwa Mulungu n’kofunika, kungatithandize kuti tisasokonezeke mwauzimu. Mtumwi Petro analembera Akristu kuti: “Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu.” (1 Petro 4:12) Ndipo Paulo anafotokoza kuti: “Onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.” (2 Timoteo 3:12) Satana amakayikirabe umphumphu wa Mboni za Yehova, ngati mmene anachitira ndi Yobu. Ndipotu, Baibulo limasonyeza kuti Satana akuukira kwambiri anthu a Mulungu m’masiku otsiriza ano.​—Chivumbulutso 12:9, 17.

Kusamvetsa Ndiponso Malangizo Olakwika

10. Kodi Yobu analibe mwayi wodziwa chiyani?

10 Mosiyana ndi ifeyo, Yobu analibe mwayi wodziwa chifukwa chimene ankavutikira. Iye anaganiza molakwika kuti mwanjira inayake “Yehova anapatsa, [ndipo] Yehova watenga.” (Yobu 1:21) N’kutheka kuti Satana mwadala, ankafuna kuchititsa Yobu kuganiza kuti ndi Mulungu amene anali kuchititsa mavuto akewo.

11. Fotokozani zimene Yobu anachita ndi mavuto amene anakumana nawo.

11 Yobu anataya mtima kwambiri, ngakhale kuti anakana kuchitira Mulungu mwano, monga mmene mkazi wake anamuuzira. (Yobu 2:9, 10) Iye anati: ‘Anthu oipa amapambana pa zochita zawo kuposa ineyo.’ (Yobu 21:7-9) Ayenera kuti anadabwa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu akundilanga?’ Panali nthawi zina pamene ankafuna kuti angofa. Iye analira kuti: “Ha! mukadandibisa kumanda, mukadandisunga mtseri, mpaka wapita mkwiyo wanu.”​—Yobu 14:13.

12, 13. Kodi Yobu anakhudzidwa bwanji ndi zolankhula za anzake atatu aja?

12 Yobu anali ndi anzake atatu omwe anabwera kudzamuona, ngati kuti ‘akudzam’lirira ndi kum’sangalatsa.’ (Yobu 2:11) Komabe, anthuwa anasonyeza kuti anali ‘otonthoza mtima molemetsa.’ (Yobu 16:2) Yobu akanapindula ndi anzake amene akanam’chepetsera mavuto ake, koma anzake atatuwa anangowonjezera kum’sokoneza maganizo ndi kum’khumudwitsa kwambiri.​—Yobu 19:2; 26:2.

13 Sitingalakwitse kuganiza kuti Yobu ayenera kuti anadzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani ndikukumana ndi zimenezi? N’chiyani chimene ndalakwa kuti ndikumane ndi mavuto onsewa?’ Anzake aja ankafotokoza zinthu zimene zinali zosokoneza. Ankaganiza kuti Yobu wadzibweretsera yekha mavuto, pochita tchimo lalikulu. Elifazi anafunsa kuti: “Watayika ndani wosapalamula konse? . . . Monga umo ndaonera, olimira mphulupulu, nabzala vuto, akololapo zomwezo.”​—Yobu 4:7, 8.

14. N’chifukwa chiyani sitiyenera kufulumira kuganiza kuti mavuto abwera chifukwa cha khalidwe loipa?

14 N’zoona kuti tingakumane ndi mavuto ngati tifesera thupi m’malo mofesera mzimu. (Agalatiya 6:7, 8) Komabe, m’dongosolo lilipoli, tingakumane ndi mavuto ngakhale kuti tili ndi khalidwe labwino. Kuwonjezera apo, sitinganene kuti anthu osalakwa amatetezedwa ku mavuto onse ayi. Yesu Kristu, yemwe anali “wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa,” anafa imfa yowawa pamtengo wozunzirapo, ndipo mtumwi Yakobo anafa chifukwa cha chikhulupiriro chake. (Ahebri 7:26; Machitidwe 12:1, 2) Kuganiza molakwika kwa Elifazi ndi anzake awiri aja kunachititsa Yobu kuteteza dzina lake ndi kuumirira kunena kuti anali wosalakwa. Komabe, chifukwa chakuti anzake aja anapitirizabe kumuimba mlandu woti mavuto ake anabwera chifukwa chakuti anachimwa, mwina zinakhudza mmene Yobu ankaonera chilungamo cha Mulungu.​—Yobu 34:5; 35:2.

Kupeza Thandizo Panthawi ya Mavuto

15. Kodi ndi maganizo otani amene angatithandize ngati takumana ndi mavuto?

15 Kodi pamenepa pali phunziro lililonse kwa ife? Panthawi ya mavuto, matenda, kapena chizunzo, munthu angaone kuti sichilungamo kuti iye akumane ndi zimenezo. Anthu ena amaoneka ngati sakumana ndi mavuto ambiri oterewa. (Salmo 73:3-12) Nthawi zina, tingafunike kudzifunsa mafunso ofunika awa: ‘Kodi chikondi changa pa Mulungu chimandichititsa kum’tumikirabe ngakhale nditakumana ndi vuto lina lililonse? Kodi ndimalakalaka kum’patsa Yehova “yankho kwa yemwe akumutonza?”’ (Miyambo 27:11; Mateyu 22:37) Sitiyenera kulola ndemanga zopanda pake za anthu ena kutikayikitsa kuti Atate wathu wakumwamba adzatithandiza. Mkristu wina wokhulupirika amene anadwala matenda aakulu kwa zaka zambiri, nthawi ina anati: “Ndikudziwa kuti chilichonse chimene Yehova walola, ndidzatha kuchipirira. Ndimadziwa kuti adzandipatsa nyonga zimene ndikufunikira. Ndipo wakhala akutero.”

16. Kodi Mawu a Mulungu amathandiza motani anthu amene akuvutika?

16 Ife timamvetsa bwino za machenjerero a Satana kusiyana ndi Yobu. “Pakuti sitikhala osadziwa machenjerero ake,” kapena kuti ziwembu zake. (2 Akorinto 2:11) Kuwonjezera apo, pali nzeru zambiri zabwino zimene tingagwiritse ntchito. M’Baibulo, timapezamo nkhani za amuna ndi akazi okhulupirika amene anapirira zovuta zosiyanasiyana. Mtumwi Paulo, amene anavutika kuposa Akristu ambiri, analemba kuti: “Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Wamboni wina wa ku Ulaya amene panthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse anaikidwa m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chake, anasinthanitsa chakudya chake cha masiku atatu ndi Baibulo. Iye anati: “Kusinthana kumeneku kunali kwaphindu kwabasi. Ngakhale kuti ndinakhala ndi njala yakuthupi, ndinalandira chakudya chauzimu chimene chinandithandiza ineyo ndiponso anthu ena kupirira ziyeso panthawi yovuta imeneyo. Ndinasunga Baibulo limenelo mpakana lero.”

17. Kodi ndi zinthu ziti zomwe Mulungu amapereka zimene zingatithandize kupirira?

17 Kuwonjezera pa chitonthozo chimene chimapezeka m’Malemba, tili ndi mabuku ambiri ofotokoza za m’Baibulo amene amatithandiza kwambiri kuti tithe kupirira mavuto. Mutafufuza m’buku la Watch Tower Publications Index, mosakayikira mudzapeza zimene Mkristu mnzanu anakumana nazo zofanana ndi zimene inuyo mukukumana nazo. (1 Petro 5:9) Zingakhalenso zothandiza kukambirana zimene mukukumana nazo ndi akulu amene amamvetsetsa bwino kapena Akristu ena okhwima mwauzimu. Koma koposa zonse, mwa kupemphera mungadalire thandizo la Yehova ndi mzimu wake woyera. Kodi Paulo anatani kuti asagonje ‘potundudzidwa’ ndi Satana? Anatero mwa kuphunzira kudalira mphamvu ya Mulungu. (2 Akorinto 12:9, 10) Analemba kuti: “Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.”​—Afilipi 4:13.

18. Kodi Akristu anzathu angatilimbikitse motani?

18 Choncho, thandizo lilipo, ndipo musachedwe kulifunafuna. Buku la Miyambo limati: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” (Miyambo 24:10) Kutaya mtima kungafooketse kukhulupirika kwa Mkristu, mofanana ndi mmene chiswe chingagwetsere nyumba. Kuti tithane ndi ngozi imeneyi, Yehova watipatsa thandizo kudzera mwa atumiki anzathu. Mngelo anaonekera kwa Yesu ndipo anam’limbikitsa usiku umene iye anagwidwa. (Luka 22:43) Akupita ku Roma monga mkaidi, Paulo “anayamika Mulungu, nalimbika mtima” atakumana ndi abale pabwalo la Apiyo ndi ku Nyumba za Alendo Zitatu. (Machitidwe 28:15) Mboni ina ya ku Germany imakumbukirabe thandizo limene inalandira ili mtsikana itafika ku ndende yozunzirako anthu ya Ravensbrück, pomwe inkachita mantha kwambiri. Mboniyi imakumbukira kuti: “Mkristu mnzanga anandipeza nthawi yomweyo n’kundilandira mwachikondi. Mlongo wina wokhulupirika anayamba kundisamalira ndipo anakhala monga mayi wanga wauzimu.”

‘Khalani Wokhulupirika’

19. Kodi n’chiyani chinathandiza Yobu kuti asagonje pa zoyesayesa za Satana?

19 Yehova anam’fotokoza Yobu monga munthu amene ‘anaumirirabe kukhala wangwiro.’ (Yobu 2:3) Ngakhale kuti anataya mtima ndipo sanazindikire chifukwa chimene ankavutikira, Yobu sanasunthike pankhani yofunika kwambiri ya kukhulupirika. Yobu anakana kutayiratu zonse pamoyo wake. Iye anaumirira kuti: “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.”​—Yobu 27:5.

20. N’chifukwa chiyani kupirira kuli kopindulitsa?

20 Kutsimikiza mtima ngati kumeneku kudzatithandiza kusunga umphumphu wathu ngakhale titakumana ndi zinthu zotani, kaya ndi mayesero, chitsutso, kapena mavuto. Yesu anauza mpingo wa ku Smurna kuti: “Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, Mdyerekezi adzaponya ena a inu m’nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso [mavuto, kapena kuponderezedwa] masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.”​—Chivumbulutso 2:10.

21, 22. Kodi tingalimbikitsidwe ndi nkhani iti popirira chiyeso?

21 M’dongosolo lino limene likulamulidwa ndi Satana, kupirira ndi kukhulupirika kwathu kudzayesedwa. Komabe, Yesu akutitsimikizira kuti tikamayang’ana za m’tsogolo, tilibe chifukwa chilichonse chochitira mantha. Chinthu chofunikira ndicho kusonyeza kuti ndife okhulupirika. Paulo anati: ‘Chisautso chathu n’chakanthawi’ pamene “kulemera,” kapena kuti mphoto imene Yehova watilonjeza, ndi ‘yoposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero.’ (2 Akorinto 4:17, 18) Ngakhale chisautso cha Yobu chinali chakanthawi poyerekezera ndi zaka zambiri zimene anakhala akusangalala, asanakumane ndi chiyeso komanso pambuyo pake.​—Yobu 42:16.

22 Komabe, pangakhale nthawi zina m’moyo wathu, pamene mayesero angaoneke ngati sakutha ndipo tingaone ngati sitingathe kupirira mavuto amene tikukumana nawo. M’nkhani yotsatirayi, tiona mmene zimene Yobu anakumana nazo zingatiphunzitsire zinthu zinanso zokhudzana ndi kupirira. Tionanso njira zimene tingalimbikitsire ena amene akukumana ndi mavuto.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ndi nkhani yaikulu iti imene Satana anayambitsa malinga ndi kusunga umphumphu kwa Yobu?

• N’chifukwa chiyani mavuto sayenera kutidabwitsa kwambiri?

• Kodi Yehova amatithandiza motani kupirira?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 23]

Kufufuza m’mabuku, kulankhula ndi Akristu okhwima mwauzimu, ndi kumuuza Yehova m’pemphero zimene tikuganiza, zingatithandize kupirira