“Chifukwa cha Mwana wa Zaka Naini”
“Chifukwa cha Mwana wa Zaka Naini”
AMBONI ZA YEHOVA akafika pakhomo pake, Wiesława, mayi yemwe akukhala m’chigawo chakum’mwera cha dziko la Poland, ankawathokoza mwaulemu koma ankawauza kuti sakufuna kumvetsera uthenga wawo. Tsiku lina, mwana wina wa zaka naini, dzina lake Samuel, anafika pakhomopo ali ndi mayi ake. Panthawiyi Wiesława anaganiza zomvetsera uthengawo ndipo analandira magazini ina yonena za dziko lapansi la paradaiso.
Chifukwa choti mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Yesu Kristu unali pafupi kuchitika, Samuel anafuna kuitana Wiesława ku mwambo wapaderawu. Motero iye anapitanso kwa mayiyu ali ndi mayi ake aja, ndipo panthawiyi anatenga kapepala koitanira anthu ku mwambowu. Poona kuti mwanayo anali atavala bwino, Wiesława anati am’dikire pang’ono kuti naye akasinthe zovala. Ndiye atabwerako, anamvetsera zimene Samuel anali kunena, n’kuvomera kupita ku mwambowo, ndipo anafunsa kuti: “Kodi ndibwere ndekha kapena ndibwere ndi amuna anga?” Kenaka anapitiriza kunena kuti: “Ngakhale amuna anga atapanda kubwera, ineyo ndibwera basi. Ndibwera chifukwa cha iweyo Samuel.” Mayiyu anasunga lonjezo lake ndipo Samuel anasangalala kwambiri.
Nkhani ya Chikumbutso ikukambidwa, Samuel anakhala pamodzi ndi Wiesława ndipo ankam’thandiza kutsegula malemba amene anali kuwerengedwa pankhaniyo. Wiesława anagoma kwambiri ndi zimenezi. Anasangalala kwambiri ndi mwambo wa Chikumbutsowo ndipo anayamikira kuti m’nkhaniyo analongosola mfundo zozama kwambiri koma m’njira yosavuta kumvetsa. Komanso anakhudzidwa mtima ndi mmene mpingo unam’landirira mokoma mtima. Kuyambira pamenepa, Wiesława wakhala akulimbikira kwambiri pa zinthu zauzimu ndipo anayamba kusonkhana ndi Mboni za Yehova nthawi zonse. Posachedwapa iye ananena kuti: “Ndimachita manyazi kuti m’mbuyomo ndinkakana kumva uthenga wanu mukafika pakhomo panga. Ndipo kunena zoona, ndinamvetsera uthenga wanu chifukwa cha mwana wa zaka naini, Samuel.”
Monga Samuel ku Poland, ana enanso ambiri a Mboni za Yehova amatamanda Mulungu pouza ena za iye ndiponso posonyeza makhalidwe abwino. Ngati inuyo ndinu mwana, dziwani kuti nanunso mungathandize anthu oona mtima kuchita chidwi ndi makhalidwe abwino auzimu.