Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zipembedzo Zili ndi Phindu Lanji?

Kodi Zipembedzo Zili ndi Phindu Lanji?

Kodi Zipembedzo Zili ndi Phindu Lanji?

“NDINGATHE kukhala munthu wabwino ngakhale popanda kupembedza.” Ambiri amaganiza choncho. Pali anthu ambiri oona mtima, achifundo komanso okhulupirika omwe sakonda zopembedza. Mwachitsanzo, anthu ambiri a kumadzulo kwa Ulaya amati amakhulupirira Mulungu, komano ndi anthu ochepa chabe a kumeneko amene amapita kutchalitchi. * Ngakhale kuti ku Latin America, pa Akatolika 100 alionse ndi Akatolika 15 kapena 20 okha amene amapita kutchalitchi nthawi zonse.

Monga anthu ambiri, mwina inunso mumaona kuti kupembedza sikuthandiza munthu kukhala ndi moyo wabwino. Komabe n’zotheka kuti mukudziwanso zoti kale, m’masiku a agogo anu, anthu ambiri ankakonda kwambiri zopembedza kusiyana ndi masiku ano. Kodi zinatani kuti anthu asiye kukopeka kwambiri ndi zopembedza? Kodi n’zotheka kuti munthu akhale wabwino popanda kukhala wopembedza? Kodi chilipo chipembedzo chimene chingakupindulitseni?

Chifukwa Chimene Ambiri Asiyira Zipembedzo

Kwa zaka zambiri m’mbuyomu, anthu ambiri m’Matchalitchi Achikristu ankakhulupirira kuti Mulungu amafuna kumumvera. Ankapita kutchalitchi kuti akasangalatse Mulungu pochita miyambo motsogozedwa ndi wansembe kapena pochita zinthu zina motsogozedwa ndi wolalikira. Inde, ambiri ankadziwa za chinyengo cha zipembedzo. Zipembedzo zinatchuka ndi nkhani yolimbikitsa nkhondo komanso khalidwe lachiwerewere la atsogoleri ake. Komabe ambiri ankaona kuti kupembedzako pakokha n’kwabwino. Ena ankasangalala ndi ulemerero umene amaumva akalowa m’tchalitchi, kapena miyambo ya kutchalitchi, ndiponso nyimbo zake. Ena ankakopeka ndi chiphunzitso choopseza anthu kuti akapsa kumoto wosazima, chomwe si cha m’Malemba ayi. Kenaka panachitika zinthu zambiri zimene zinasintha mmene anthu ambiri amaonera zipembedzo.

Chiphunzitso chakuti zamoyo zinakhalako mwa kuchita kusanduka kuchokera ku zinthu zina chinatchuka. Moti ena anafika pokhulupirira kuti zamoyo zinangokhalako mwangozi basi, osati mochita kulengedwa ndi Mulungu. Zipembedzo zambiri zinalephera kupereka umboni wogwira mtima wakuti Mulungu ndiye Chitsime cha moyo. (Salmo 36:9) Komanso, kupita patsogolo kwa zaumisiri, zachipatala, zamayendedwe ndiponso njira zolankhulirana kunachititsa anthu kuganiza kuti sayansi ingathetse vuto lililonse. Ndipo ena ankaona kuti akatswiri a zakhalidwe ndi a zamaganizo a anthu anali kuthandiza kwambiri anthu kusiyana ndi zipembedzo. Nazonso zipembedzo zinalephera kupereka umboni wogwira mtima woti moyo wotsatira malamulo a Mulungu ndiwo moyo wabwino kwambiri.​—Yakobo 1:25.

Zipembedzo zambiri zitaona zimenezi, zinasintha uthenga wawo. Ansembe ndi olalikira anasiya kuphunzitsa anthu kuti Mulungu amafuna kumumvera. M’malo mwake, ambiri ankaphunzitsa kuti munthu aliyense ayenera kusankha yekha zabwino ndi zoipa. Pofuna kukondedwa ndi anthu ambiri, atsogoleri ena azipembedzo ankanena kuti Mulungu amavomereza munthu aliyense ngakhale atakhala wa khalidwe lotani. Ziphunzitso zimenezi zimatikumbutsa zimene Baibulo linalosera kuti: “Pakuti idzafika nthawi imene anthu sadzafunanso chiphunzitso chopindulitsa, koma mogwirizana ndi zilakolako za iwo eni, adzadzipezera okha aphunzitsi kuti amve zowakomera m’khutu.”​—2 Timoteo 4:3, NW.

Ziphunzitso zimenezi sizinakope anthu koma zinawaingitsira kutali. Iwo anayamba kudzifunsa kuti: ‘Ngati zipembedzo zikukayikira mphamvu ya Mulungu yolenga ndiponso nzeru zake zopanga malamulo, kodi kupita kutchalitchi kungandipindulitse bwanji? Komanso ndivutikirenji n’kuphunzitsa ana anga zachipembedzo?’ Motero anthu amene ankafuna kukhala moyo wabwino anayamba kuona kuti zipembedzo sizingawapindulire. Anasiya zipembedzo zawo, ndipo zopembedza anathana nazo. Kodi zinatani kuti chinthu choyenera kupindulitsa anthu chifike potha ntchito chonchi? Baibulo limafotokoza nkhaniyi mogwira mtima kwambiri.

Kugwiritsa Ntchito Zipembedzo ndi Zolinga Zoipa

Mtumwi Paulo anachenjeza Akristu oyambirira kuti anthu ena adzagwiritsa ntchito Chikristu ndi zolinga zoipa. Iye anati: “Adzalowa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo; ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.” (Machitidwe 20:29, 30) Mmodzi mwa anthu “olankhula zokhotakhota” anali Mkatolika wamaphunziro apamwamba a zaumulungu, dzina lake Augustine. Yesu anaphunzitsa anthu om’tsatira kuti aziphunzitsa ena powafotokozera mfundo za m’Malemba mogwira mtima. Koma Augustine anakhotetsa mawu a Yesu pa Luka 14:23 akuti, “Nuwaumirize anthu alowe,” ponena kuti mawuwa akutanthauza kuti sikulakwa kuumiriza anthu pantchito yowatembenuza. (Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 28:23, 24) Motero, Augustine anagwiritsa ntchito chipembedzo polamulira anthu.

Satana, yemwe ndi mngelo wopanduka, ndiye akulimbikitsa khalidwe logwiritsa ntchito zipembedzo molakwika ndiponso ndiye akuipitsa nkhani yopembedza. Iye anachititsa kuti anthu achipembedzo m’nthawi ya atumwi ayese kuipitsa mipingo yachikristu. Za anthu amenewo, Baibulo limati: “Otere ali atumwi onyenga, ochita ochenjerera, odzionetsa ngati atumwi a Kristu. Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika. Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adzionetsa monga atumiki a chilungamo; amene chimaliziro chawo chidzakhala monga ntchito zawo.”​—2 Akorinto 11:13-15.

Satana akugwiritsabe ntchito zipembedzo zomwe zimanamizira kuti n’zachikristu, n’zamakhalidwe abwino, ndiponso n’zodziwa kuphunzitsa. Iye akutero n’cholinga choti anthu azichita zinthu mogwirizana ndi makhalidwe ake osati a Mulungu. (Luka 4:5-7) N’kutheka kuti mwaona kuti atsogoleri ambiri azipembedzo masiku ano amagwiritsa ntchito kupembedza kuti adzikweze mwa kudzipatsa mayina aulemerero ndiponso potenga ndalama kwa nkhosa zawo. Maboma akhalanso akugwiritsa ntchito zipembedzo pofuna kukopa nzika zawo kuti zilolere kulowa usilikali n’kukafera kunkhondo.

Mdyerekezi amagwiritsa ntchito kwambiri zipembedzo kuposa mmene anthu ambiri amaganizira. Mwina mukuganiza kuti Satana akugwiritsa ntchito magulu ochepa chabe a zipembedzo omwe akuchita zinthu monyanyira. Koma Baibulo limati, ‘iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, akunyenga dziko lonse.’ Baibulo limanenanso kuti: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (Chivumbulutso 12:9; 1 Yohane 5:19) Kodi Mulungu amamva bwanji akaona zipembedzo zimene zikugwiritsidwa ntchito ndi atsogoleri amene akungofuna kukopa anthu kuti awatsate iwowo?

“Ndili Nazo Ntchito Yanji?”

Ngati zochita za matchalitchi ena achikristu zimakuipirani inuyo, kuli bwanji Mulungu Wamphamvuyonse? Ndithu, zimamuipira kwambiri. Matchalitchi Achikristu amanena kuti anachita pangano ndi Mulungu; Aisrayeli akale ankanenanso chimodzimodzi. Koma magulu awiri onsewa achita zinthu zosakhulupirika. Motero zimene Yehova ananena posasangalala ndi Aisrayeli aja zikusonyeza kuti Yehova adzachitanso chimodzimodzi ndi Matchalitchi Achikristu masiku ano. Iye anati: “Sanamvere mawu anga ndipo akana chilamulo changa. Ndili nazo ntchito yanji nsembe za ku Seba? . . . Nsembe zanu sizindisangalatsa.” (Yeremiya 6:19, 20, New International Version) Mulungu sanavomereze kulambira kwa anthu achiphamaso amenewo. Analibe nayo ntchito miyambo yawo ndiponso mapemphero awo. Iye anauza Aisrayeliwo kuti: “Masiku anu okhala mwezi ndi nthawi za mapwando anu mtima wanga uzida; zindivuta Ine; ndalema ndi kupirira nazo. Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva.”​—Yesaya 1:14, 15.

Kodi Yehova amasangalala ndi mapwando amene matchalitchi amati ndi mapwando achikristu koma amene poyamba ankalemekeza milungu yabodza? Kodi Yehova amamvetsera mapemphero a abusa amene amaipitsa ziphunzitso za Kristu? Kodi Mulungu amavomereza zipembedzo zilizonse zimene zimakana lamulo lake? Iye sanasangalale ndi nsembe za Aisrayeli akale aja n’chifukwa chake anati: “Ndili nazo ntchito yanji?” Mosakayika, amamva chimodzimodzi akaona miyambo ya matchalitchi ya masiku anoyi.

Komabe, Yehova amakondwera kwambiri anthu oona mtima akamam’pembedza moona. Mulungu amasangalala anthu akamayamikira zinthu zonse zimene amalandira kwa iye. (Malaki 3:16, 17) Ndiye kodi n’zotheka kuti mukhale munthu wabwino popanda kupembedza Mulungu? Munthu amene sawachitira chilichonse makolo ake, ngakhale kuti iwo amam’konda, sangadzione kuti n’ngwabwino. Angatero ngati? Nanga munthu amene sam’chitira chilichonse Mulungu anganene bwanji kuti n’ngwabwino? Motero, n’zomveka kuti tiyenera kumachita zinthu moganizira kwambiri Mulungu woona, amene anayambitsa moyo. M’nkhani yotsatirayi, tiona mmene kupembedza koona kumapatsira Mulungu ulemu ndiponso mmene kumatipindulitsira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Buku la The Decline of Christendom in Western Europe, 1750-2000 linati: “Cha m’ma 1960 . . . m’mayiko ambiri anthu anayamba kusakonda zopembedza.”

[Zithunzi patsamba 4]

Kodi matchalitchi asonyeza anthu umboni wakuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse?

[Chithunzi pamasamba 4, 5]

Kodi munthu woimira Mulungu angapezeke uku?

[Chithunzi patsamba 5]

Kodi miyambo ngati uwu Mulungu amaiona motani?

[Mawu a Chithunzi]

AP Photo/​Georgy Abdaladze