Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupembedza Komwe Kungakupindulitseni

Kupembedza Komwe Kungakupindulitseni

Kupembedza Komwe Kungakupindulitseni

ASAFU, wamasalmo anati: ‘Kundikomera kuyandikira kwa Mulungu.’ Panthawi ina iye anaganizapo zotsanzira anthu amene saganizira za Mulungu pofuna moyo wofewa. Koma kenaka Asafu anaganizira za ubwino woyandikira kwa Mulungu ndipo anaona kuti angapindule ngati atatero. (Salmo 73:2, 3, 12, 28) Kodi kupembedza koona kungakupindulitseni masiku ano? Nanga kungakupindulitseni motani?

Kupembedza Mulungu woona kumakuthandizani kusintha kaganizidwe kanu n’kusiya kukhala moyo wongoganizira zofuna zanu zokha. “Mulungu wa chikondi” anatipanga m’njira yoti sitingakhale osangalala ngati tikungochita zinthu zokomera ifeyo basi. (2 Akorinto 13:11) Yesu anaphunzitsa mfundo yofunika kwambiri ya makhalidwe pamene anati: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) N’chifukwa chake timasangalala tikamachitira zinthu anzathu ndiponso achibale athu. Koma timasangalala kwambiri tikamachitira zinthu Mulungu. Iye ndiye ali woyenera kum’konda kwambiri kuposa wina aliyense. Anthu osiyanasiyana ochuluka apeza kuti kupembedza Mulungu pochita zimene iye amafuna n’kosangalatsa kwambiri.​—1 Yohane 5:3.

Kukhala ndi Cholinga pa Moyo

Kupembedza koona kumakupindulitsaninso chifukwa choti kumakupatsani cholinga pa moyo wanu. N’zotheka kuti mwaona kuti nthawi zambiri munthu amakhala wosangalala akamaona kuti akuchita chinachake chaphindu. Anthu ambiri amakhala n’cholinga chinachake pa moyo wawo, kaya chokhudza banja lawo, anzawo, ntchito yawo, kapena kusangalala. Chifukwa choti moyo n’ngosapanganika, nthawi zambiri zinthu zimenezi siziwapatsa chimwemwe. (Mlaliki 9:11) Koma kupembedza koona kumakuthandizani kukhala ndi cholinga chapamwamba zedi, chomwe chimakhalabe chopindulitsa ngakhale zinthu zina pamoyo wanu zitapanda kuyenda bwino.

Kupembedza koona kumaphatikizapo kudziwa Yehova ndi kum’tumikira mokhulupirika. Amene amachita zimenezi amayandikira kwambiri kwa Mulungu. (Mlaliki 12:13; Yohane 4:23; Yakobo 4:8) Mwina zingakuvuteni kuganiza kuti mungathe kum’dziwa bwino Mulungu moti n’kukhala bwenzi lanu. Koma poganizira zimene wakhala akuchita ndi anthu ndiponso poganizira zimene walenga, mungathe kuona ena mwa makhalidwe ake. (Aroma 1:20) Komanso, powerenga Mawu a Mulungu, mungamvetse chifukwa chimene tilili padziko pano, chifukwa chimene Mulungu amalolera anthu kuvutika ndi mmene adzakuthetsere, ndiponso mwina chosangalatsa kwambiri n’chakuti mungamvetse udindo wanu pa zimene Mulungu akuchita. (Yesaya 43:10; 1 Akorinto 3:9) Mutamvetsa zimenezi, mungayambe kukonda kwambiri moyo.

Kukhala Munthu Wabwino

Kupembedza koona kungakupindulitseni chifukwa kumakuthandizani kukhala munthu wabwino. Mukamapembedza moonadi mumasintha khalidwe ndipo mumayamba kugwirizana ndi ena. Mumaphunzira kwa Mulungu ndiponso kwa Mwana wake za kukhala woona mtima, kulankhula mokoma mtima, ndi kukhala munthu wodalirika. (Aefeso 4:20–5:5) Mukam’dziwa bwino kwambiri Mulungu n’kufika pom’konda, mumaona kuti muyenera kum’tsanzira. Baibulo limati: “Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; ndipo yendani m’chikondi.”​—Aefeso 5:1, 2.

Kodi sizingakhale zosangalatsa kukhala ndi anthu amene amatsanzira chikondi cha Mulungu? N’zosangalatsa kuti munthu sapembedza Mulungu ali yekha. Kupembedza Mulungu kumachititsa kuti mukumane ndi anthu ena amene amakonda kuchita zinthu zoyenera ndi zabwino. N’zoona kuti mwina simungasangalale kukhala m’gulu linalake la chipembedzo. Komabe, monga taonera m’nkhani yoyamba ija, vuto la zipembedzo zambiri si loti zili m’magulumagulu ayi koma ndi loti dongosolo la magulu a zipembedzozo si labwino ndiponso linakhazikitsidwa pa zifukwa zosayenera. Zipembedzo zambiri zotere zimachita zinthu zosagwirizana ndi Chikristu. Dongosolo la gulu la anthu a Mulungu n’lokhazikitsidwa ndi Yehova ndipo n’lokhazikitsidwa pa zifukwa zabwino. Baibulo limati: “Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere.” (1 Akorinto 14:33) Pali anthu ochuluka zedi amene aona kuti kusonkhana ndi gulu lolinganizidwa bwino la Akristu kumawathandiza kukhala osangalala. Inunso mungathe kuona kuti kumathandizadi.

Kuyembekeza Tsogolo Labwino

Malemba Opatulika amasonyeza kuti Mulungu akukonzekeretsa olambira oona kuti adzapulumuke mapeto a dongosolo lino la zinthu ndi kulandira dziko latsopano mmene “mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13; Chivumbulutso 7:9-17) Motero kupembedza komwe kungakupindulitseni kumakupatsani chiyembekezo, chomwe n’chofunika kwambiri kuti mukhale wosangalala. Ena amaganiza kuti tsogolo lawo lingakhale labwino ngati maboma akuyenda bwino, ngati iwowo atapeza ntchito yabwino, kapena ngati atakhala ndi thanzi labwino ndiponso chiwongoladzanja chabwino chopumira pantchito. Komatu ndi zinthu zochepa chabe mwa zinthu zimenezi zomwe zingam’patse munthu chimwemwe pa moyo wake, ndipo mwina zonsezi sizingam’thandize ayi. Komano mtumwi Paulo analemba kuti: “Chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo.”​—1 Timoteo 4:10.

Ngati mutafufuza mozama, mungathe kupeza olambira oona. Ngakhale kuti masiku ano anthu agawanika kwambiri padzikoli, a Mboni za Yehova n’ngosiyana kwambiri ndi anthu ena chifukwa cha chikondi ndi mgwirizano wawo. Iwowa ndi anthu ochokera m’mitundu ndiponso mabanja osiyanasiyana; koma n’ngogwirizana chifukwa choti amakondana ndiponso amakonda Yehova. (Yohane 13:35) Angasangalale kwambiri ngati mutadzionera nokha zimene iwowo aona. Asafu analemba kuti: ‘Kundikomera kuyandikira kwa Mulungu.’​—Salmo 73:28.

[Chithunzi patsamba 7]

Mungathe kukhala bwenzi la Mulungu