Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Tingam’fikire “Wakumva Pemphero”

Mmene Tingam’fikire “Wakumva Pemphero”

Mmene Tingam’fikire “Wakumva Pemphero”

“Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.”​—SALMO 65:2.

1. Kodi n’chiyani chimene chimasiyanitsa anthu ndi zolengedwa zina padziko lapansi, ndipo chimatipatsa mwayi wotani?

PA ZAMOYO zambirimbiri zimene zili padziko lapansi, ndi anthu okha amene angathe kupembedza Mlengi. Ndi anthu okha amene amazindikira kuti akufunika zauzimu n’kumazifunadi. Zimenezi zimatipatsa mwayi patokhapatokha wokhala ndi ubwenzi wabwino ndi Atate wathu wa kumwamba.

2. Kodi uchimo unasokoneza bwanji ubwenzi wa anthu ndi Mlengi wawo?

2 Mulungu analenga anthu m’njira yoti angathe kum’fikira iyeyo monga Mlengi wawo. Adamu ndi Hava analengedwa opanda tchimo. Motero ankatha kum’fikira Mulungu momasuka monga mwana amachitira ndi atate ake. Koma uchimo unawalanda mwayi waukulu umenewu. Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu ndipo anataya ubwenzi wawo wapamtima ndi iye. (Genesis 3:8-13, 17-24) Kodi pamenepa ndiye kuti mbadwa zopanda ungwiro za Adamu sizingalankhulenso ndi Mulungu? Ayi si choncho, chifukwa Yehova amalola kuti zitero, malinga ngati zitakwaniritsa zinthu zinazake zofunikira. Kodi zinthu zake n’zotani?

Zofunika Kuti Tim’fikire Mulungu

3. Kodi anthu ochimwa ayenera kum’fikira motani Mulungu, ndipo n’chitsanzo chiti chimene chikusonyeza zimenezi?

3 Zimene zinachitika pakati pa ana awiri a Adamu zimatithandiza kuona zimene Mulungu amafuna kuti anthu opanda ungwiro, amene akufuna kum’fikira, azichita. Kaini ndi Abele onse anayesa kum’fikira Mulungu popereka nsembe. Nsembe ya Abele inali yolandirika, koma ya Kaini ayi. (Genesis 4:3-5) Kodi nsembe zimenezi zinasiyana bwanji? Lemba la Ahebri 11:4 limati: “Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, amene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama.” Motero n’zoonekeratu kuti chikhulupiriro n’chofunika kuti munthu am’fikire Mulungu. Chinthu chinanso chofunika timachiona m’mawu a Yehova amene anauza Kaini kuti: “Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi?” Inde, Mulungu akanavomera kuti Kaini am’fikire ngati Kainiyo akanayamba kuchita zabwino. Komabe Kaini anakana malangizo a Mulungu, n’kupha Abele, pamapeto pake anakanidwa ndi Mulungu. (Genesis 4:7-12) Motero, pachiyambi pomwe, Mulungu anagogomezera za kufunika kofika kwa iye mwa chikhulupiriro ndi ntchito zabwino.

4. Kodi tiyenera kuzindikira chiyani pankhani ya kum’fikira Mulungu?

4 Ngati tikufuna kum’fikira Mulungu m’pofunika kuzindikira kuti ndife ochimwa. Anthu onse ndi ochimwa, ndipo uchimo umalepheretsa munthu kum’fikira Mulungu. Mneneri Yeremiya analemba za Aisrayeli kuti: “Ife tilakwa . . . Mwadzikuta ndi mtambo kuti pemphero lathu lisapyolemo.” (Maliro 3:42, 44) Ngakhale zili choncho, m’mbuyo monsemu Mulungu wasonyeza kuti ndi wokonzeka kulandira mapemphero a anthu amene amafika kwa iye ndi chikhulupiriro ndiponso ndi mtima wowongoka, amenenso amamvera malamulo ake. (Salmo 119:145) Kodi ena mwa anthuwa anali ndani, ndipo tingaphunzirepo chiyani pa mapemphero awo?

5, 6. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Abrahamu cha kufikira Mulungu?

5 Mmodzi wa anthuwa anali Abrahamu. Mulungu anavomera kuti iye am’fikire, chifukwa Mulungu anamutcha “bwenzi langa.” (Yesaya 41:8) Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Abrahamu cha kufikira Mulungu? Munthu wokhulupirikayu anafunsa Yehova zokhudza wolowa nyumba, ponena kuti: “Mudzandipatsa ine chiyani popeza ndine wopanda mwana?” (Genesis 15:2, 3; 17:18) Panthawi ina, iye anali ndi nkhawa ndipo anafuna kudziwa ngati pakhale opulumuka Mulungu akaweruza oipa mu Sodomu ndi Gomora. (Genesis 18:23-33) Abrahamu ankapemphereranso anthu ena. (Genesis 20:7, 17) Ndipo, monga anachitira Abele, nthawi zina Abrahamu ankafikira Mulungu popereka nsembe kwa Yehovayo.​—Genesis 22:9-14.

6 Panthawi zonsezi, Abrahamu ankalankhula ndi Yehova momasuka. Koma ngakhale kuti anali ndi ufulu wolankhula, ankazindikiranso kuti iyeyo n’ngochepa kwambiri poyerekezera ndi Mlengi wake. Taonani mawu ake aulemu a pa Genesis 18:27, akuti: “Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine fumbi ndi phulusa.” Uwutu ndi mtima wabwino kwambiri woyenera kuutsanzira.

7. Kodi ndi nkhani zotani zimene makolo akale anamuuza Yehova m’mapemphero awo?

7 Makolo akale ankapempherera nkhani zosiyanasiyana, ndipo Yehova anamva mapemphero awo. Mwachitsanzo, Yakobo ananenapo pemphero lomwe linali lumbiro. Atapempha kuti Mulungu am’thandize, iye polumbira analonjeza kuti: “Ndipo la zonse mudzandipatsa ine, ndidzakupatsani inu limodzi la magawo khumi.” (Genesis 28:20-22) Panthawi ina, atatsala pang’ono kukumana ndi mkulu wake, Yakobo anadandaulira Yehova kuti amuteteze ponena kuti: “Mundipulumutsetu ine m’dzanja la mkulu wanga, m’dzanja la Esau; chifukwa ine ndimuopa iye.” (Genesis 32:9-12) Yobu anapempherera anthu a m’banja mwake, ndipo anawaperekera nsembe kwa Yehova. Anzake atatu a Yobu atachimwa chifukwa cha zolankhula zawo, Yobu anawapempherera, ndipo “Yehova anavomereza Yobu.” (Yobu 1:5; 42:7-9) Zochitika zimenezi zikutithandiza kuona nkhani zimene tingamuuze Yehova popemphera. Zikutithandizanso kuona kuti Yehova ali wokonzeka kulandira mapemphero a anthu amene amam’fikira m’njira yoyenerera.

Njira Yom’fikira Yehova Yoperekedwa ndi Pangano la Chilamulo

8. Malinga ndi pangano la Chilamulo, kodi nkhani zokhudza anthu ankazipititsa bwanji kwa Yehova?

8 Yehova atapulumutsa mtundu wa Aisrayeli ku Aigupto, anawapatsa pangano la Chilamulo. Chilamulo chinafotokoza njira yom’fikira Mulungu kudzera mwa ansembe odzozedwa. Alevi ena anasankhidwa kuti akhale ansembe othandiza anthuwo. Pakabuka nkhani zokhudza mtundu wonsewo, nthumwi ya anthuwo, yomwe inkakhala mfumu kapena mneneri, inkapereka nkhaniyo kwa Mulungu kudzera m’pemphero. (1 Samueli 8:21, 22; 14:36-41; Yeremiya 42:1-3) Mwachitsanzo, popereka kachisi, Mfumu Solomo inam’fikira Yehova kudzera m’pemphero lochokera pansi pa mtima. Posonyeza kuti walandira pemphero la Solomolo, Yehova anadzaza kachisiyo ndi ulemerero wake ndipo ananena kuti: “Makutu anga [adzakhala] otchera, pemphero la m’malo ano.”​—2 Mbiri 6:12–7:3, 15.

9. Kodi n’chiyani chimene chinali kufunika kuti afikire Yehova m’njira yoyenera pakachisi?

9 M’Chilamulo chimene anapatsa Aisrayeli, Yehova anaikamo lamulo lofotokoza njira yoyenera imene akanam’fikira pakachisi. Kodi njira yake inali yotani? M’mawa ndi madzulo aliwonse, kuphatikiza pa kupereka nsembe za nyama, mkulu wa ansembe anayenera kufukiza zonunkhira pamaso pa Yehova. Kenaka ansembe aang’ono anayambanso kuchita nawo ntchito imeneyi, koma osati pa Tsiku la Chitetezo. Ansembewo akanapanda kupereka ulemu kwa Mulungu m’njira imeneyi, Yehova sakanasangalala ndi utumiki wawo.​—Eksodo 30:7, 8; 2 Mbiri 13:11.

10, 11. Kodi tili ndi umboni wanji wakuti Yehova analandira mapemphero a anthu paokhapaokha?

10 Ku Israyeli wakale, kodi anthu ankafikira Mulungu kudzera mwa nthumwi zoikidwa zokhazokha? Ayi, Malemba amasonyeza kuti Yehova ankasangalala kulandira mapemphero a anthu paokhapaokha. M’pemphero lake loperekera kachisi, Solomo anachonderera Yehova ponena kuti: “Pemphero ndi pembedzero lililonse likachitika ndi munthu aliyense, kapena ndi anthu anu onse Aisrayeli, . . . nakatambasulira manja ake kuloza ku nyumba iyi; pamenepo mumvere m’Mwamba.” (2 Mbiri 6:29, 30) Nkhani ya Luka imatiuza kuti pamene Zakariya, bambo ake a Yohane Mbatizi, ankapereka nsembe yofukiza m’kachisi, gulu la anthu olambira omwe sanali ansembe anali “kupemphera kunja.” Zikuoneka kuti anthu anayamba kusonkhana n’kumapemphera panja pa kachisi panthawi imene nsembe yofukiza inali kuperekedwa kwa Yehova paguwa la nsembe lagolide.​—Luka 1:8-10.

11 Motero, akam’fikira Yehova m’njira yoyenera, iye ankalandira mapemphero a anthu amene ankaimira mtundu wonsewo ndiponso a anthu amene ankam’fikira paokha. Masiku ano, sititsatira pangano la Chilamulo. Komabe, tingaphunzire zinthu zofunika zokhudza pemphero poona njira zimene Aisrayeli akale ankafikira Mulungu.

Njira Yachikristu Yom’fikira Yehova

12. Kodi Akristu ali ndi njira yotani yom’fikira Yehova?

12 Njira imene timatsatira pano ndi yachikristu. Kulibenso kachisi weniweni wokhala ndi ansembe ochita zinthu m’malo mwa anthu onse a Mulungu kapena kachisi yemwe tingamayang’aneko popemphera kwa Mulungu. Ngakhale zili choncho, Yehova adakali ndi njira imene tingam’fikire. Kodi njira yake ndi iti? M’chaka cha 29 C.E., Kristu atadzozedwa n’kukhala Mkulu wa Ansembe, panakhazikitsidwa kachisi wauzimu. * Kachisi wauzimu ameneyu anali njira yatsopano yom’fikira Yehova pom’lambira kudzera m’nsembe yophimba machimo yomwe anapereka Yesu Kristu.​—Ahebri 9:11, 12.

13. Pankhani ya pemphero, kodi pali kufanana kotani pakati pa kachisi wa ku Yerusalemu ndi kachisi wauzimu?

13 Zinthu zambiri zokhudza kachisi ku Yerusalemu zinali chithunzi chabwino kwambiri cha zinthu zosiyanasiyana za m’kachisi wauzimu, kuphatikizapo zinthu zokhudza pemphero. (Ahebri 9:1-10) Mwachitsanzo, kodi zofukiza zimene ankafukiza m’mawa ndi madzulo pa guwa la nsembe la m’Malo Opatulika a m’kachisi, zinaimira chiyani? Buku la Chivumbulutso limati zofukiza “ndizo mapemphero a oyera mtima.” (Chivumbulutso 5:8; 8:3, 4) Davide anauziridwa kulemba kuti: “Pemphero langa liikike [“likonzedwe,” NW] ngati chofukiza pamaso panu.” (Salmo 141:2) Motero, pa Chikristu, zofukiza zonunkhira zimaimira mapemphero ndiponso zitamando zolandirika kwa Yehova.​—1 Atesalonika 3:10.

14, 15. Kodi tinganene chiyani pankhani ya kum’fikira Yehova komwe amachita (a) Akristu odzozedwa? (b) a “nkhosa zina”?

14 Kodi ndani amene angam’fikire Mulungu pakachisi wauzimu ameneyu? Pakachisi wakale uja, ansembe ndi Alevi anali ndi mwayi wotumikira m’bwalo la m’kati, koma ndi ansembe okha amene ankaloledwa kulowa m’Malo Opatulika. Bwalo la m’kati ndiponso Malo Opatulikawa zinali kuimira mwayi wapadera wauzimu umene Akristu odzozedwa okhala ndi chiyembekezo chopita kumwamba ali nawo, womwe umawatheketsa kupemphera ndi kutamanda Mulungu.

15 Nanga bwanji anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi, a “nkhosa zina”? (Yohane 10:16) Mneneri Yesaya anasonyeza kuti anthu a m’mitundu yambiri adzabwera kudzalambira Yehova “masiku otsiriza.” (Yesaya 2:2, 3) Analembanso kuti “alendo” adzadziphatika kwa Yehova. Posonyeza kuti ali wokonzeka kuwalandira anthuwa akafika kwa iye, Mulungu anati: ‘Ndidzawasangalatsa m’nyumba yanga yopemphereramo.’ (Yesaya 56:6, 7) Lemba la Chivumbulutso 7:9-15 limatiuzanso zinthu zina ndipo limafotokoza za “khamu lalikulu” lochokera mwa “mtundu uliwonse,” lomwe likusonkhana popembedza ndi popemphera kwa Mulungu “usana ndi usiku,” litaima m’bwalo la panja la kachisi wauzimu. N’zolimbikitsa kwambiri kuti atumiki onse a Mulungu masiku ano angathe kum’fikira Mulungu momasuka, osakayika n’komwe kuti akuwamva.

Kodi Mulungu Amamva Mapemphero Otani?

16. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Akristu oyambirira pankhani ya pemphero?

16 Akristu oyambirira ankakonda kupemphera. Kodi ankapemphera pa nkhani zotani? Akulu achikristu ankapempha nzeru posankha abale pa maudindo okhudza kayendetsedwe ka zinthu m’gulu. (Machitidwe 1:24, 25; 6:5, 6) Epafra anapempherera okhulupirira anzake. (Akolose 4:12) Anthu a mumpingo wa ku Yerusalemu anapempherera Petro pamene iye anali m’ndende. (Machitidwe 12:5) Akristu oyambirira anapempha Mulungu kuti awalimbitse mtima panthawi imene anali kuzunzidwa. Iwo anati: “Ambuye, penyani mawu awo akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mawu anu ndi kulimbika mtima konse.” (Machitidwe 4:23-30) Wophunzira Yakobo analimbikitsa Akristu kuti akakhala pachiyeso, azipemphera kwa Mulungu kuti awapatse nzeru. (Yakobo 1:5) Kodi inuyo mumatchula nkhani ngati zimenezi mukamapemphera kwa Yehova?

17. Kodi Yehova amamvera mapemphero a ndani?

17 Mulungu samva mapemphero onse. Ndiye kodi tingatani kuti tizipemphera popanda kukayikira kuti iye amva mapemphero athu? Anthu okhulupirika amene Mulungu ankawamvera kale ankafika kwa iye mokhulupirika ndiponso ndi mtima wowongoka. Iwo anaonetsa chikhulupiriro ndipo anatero pochita ntchito zabwino. Tikutsimikiza kuti masiku ano Yehova amamvera mapemphero a anthu amene amam’fikira m’njira imeneyi.

18. Kodi chofunika n’chiyani kuti mapemphero a Akristu amvedwe?

18 Pali chinthu chinanso chofunika. Mtumwi Paulo analongosola chinthu chimenechi ponena kuti: “Mwa Iye . . . tili nawo malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi.” Kodi Paulo ankanena za ndani ponena kuti, “mwa Iye”? Ankanena za Yesu Kristu. (Aefeso 2:13, 18) Inde, tili omasuka kufikira Atate kudzera mwa Yesu basi.​—Yohane 14:6; 15:16; 16:23, 24.

19. (a) Kodi ndi liti pamene Yehova ananyansidwa ndi zofukiza zimene Aisrayeli ankapereka? (b) Kodi tingatani kuti mapemphero athu akhale ngati zofukiza zonunkhira bwino kwa Yehova?

19 Monga tanenera kale, zofukiza zimene ansembe mu Israyeli anali kupereka zikuimira mapemphero olandirika a atumiki okhulupirika a Mulungu. Komabe, nthawi zina zofukiza zimene Aisrayeliwo ankapereka zinali zoipa pamaso pa Yehova. Umu ndi mmene zinthu zinalili panthawi imene Aisrayeli anali kuwotcha nsembe zofukiza m’kachisi, koma n’kumagwadiranso mafano. (Ezekieli 8:10, 11) N’chimodzimodzinso masiku ano. Mapemphero a anthu amene amati amalambira Yehova, koma n’kumachitanso zinthu zotsutsana ndi malamulo ake, ali ngati fungo lonyansa kwa iye. (Miyambo 15:8) Motero tiziyesetsa kukhala oyera pa moyo wathu wonse kuti, kwa Mulungu, mapemphero athu azikhala ngati zofukiza zonunkhira bwino. Yehova amasangalala ndi mapemphero a anthu amene amatsatira njira zake zolungama. (Yohane 9:31) Komabe, pali mafunso ena awa ofunika kuwayankha: Kodi tiyenera kupemphera motani? Kodi tingapempherere zinthu ziti? Ndipo kodi Mulungu amayankha bwanji mapemphero athu? Nkhani yathu yotsatira idzayankha mafunso amenewa ndi mafunso enanso.

[Mawu a M’munsi]

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi anthu opanda ungwiro angam’fikire bwanji Mulungu movomerezeka?

• Kodi tingatsanzire bwanji makolo akale pa mapemphero athu?

• Kodi timaphunzira chiyani pa mapemphero a Akristu oyambirira?

• Kodi mapemphero athu amakhala ngati zofukiza zonunkhira bwino ngati tikutani?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 23]

N’chifukwa chiyani Mulungu analandira nsembe ya Abele koma osati ya Kaini?

[Chithunzi patsamba 24]

“Ine ndine fumbi ndi phulusa”

[Chithunzi patsamba 25]

“Ndidzakupatsani Inu limodzi la magawo khumi”

[Chithunzi patsamba 26]

Kodi mapemphero anu ali ngati zofukiza zonunkhira bwino kwa Yehova?