Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Wachibale Akasiya Yehova

Wachibale Akasiya Yehova

Wachibale Akasiya Yehova

MARK ndi Louise ndi a Mboni za Yehova. * Iwo mwachikondi ndipo mosamala, anaphunzitsa ana awo Malemba mogwirizana ndi zimene Baibulo limalangiza makolo achikristu. (Miyambo 22:6; 2 Timoteo 3:15) Koma n’zomvetsa chisoni kuti ena mwa ana awo sanapitirize kutumikira Yehova atakula. Louise anati: “Ndikaganiza za ana anga amene analowerera, mtima wanga umandipweteka kwambiri. Sindinganame kuti ndimakhala bwinobwino tsiku lililonse osamva kupweteka. Ena akamalankhula za ana awo, chinthu chinachake chimandigwira pakhosi ndipo misozi imalengeza m’maso.”

Zoonadi, munthu akasankha kusiya Yehova ndiponso moyo umene Malemba amanena, anthu okhulupirika m’banjamo amazunzika mtima kwambiri. Irene akuti: “Ndimam’konda kwambiri mkulu wanga. Ndingachite zonse zotheka kuti abwerere kwa Yehova.” Maria, amene mlongo wake anasiya Yehova n’kutsata moyo wachiwerewere, akuti: “Zimenezi zakhala zovuta kwambiri kupirira chifukwa pambali zina, iye anali munthu wabwino. Ndimam’sowa kwambiri pamacheza a banja lathu.”

N’chifukwa Chiyani Zimapweteka Kwambiri?

Kodi n’chifukwa chiyani mwana kapena wachibale wina akatayika mwauzimu, zimawapweteka kwambiri achibale ake amene ndi Akristu? Chifukwa chakuti iwo amadziwa zimene Malemba amalonjeza kuti munthu wokhulupirika kwa Yehova adzapeza moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. (Salmo 37:29; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3-5) Amayembekeza kulandira madalitso amenewa ali limodzi ndi akazi kapena amuna awo, ana awo, makolo awo, akulu kapena ang’ono awo, ndi adzukulu awo. Choncho zimawapweteka kwambiri akaganiza zoti achibale awo amene anasiya kutumikira Yehova angaphonye madalitso amenewo. Akristu amazindikira kuti malamulo ndi mfundo za Yehova zimathandiza ngakhale pa moyo uno. N’chifukwa chake amasweka mtima akaona achibale awo akufesa m’njira yoti adzakolola zoipa zokhazokha.​—Yesaya 48:17, 18; Agalatiya 6:7, 8.

Ena amene zimenezi sizinawachitikirepo angavutike kumvetsa mmene nkhaniyi imapwetekera. Vuto limeneli limakhudza moyo wonse wa munthu. Louise akuti: “Zimandivuta kwambiri kukhala pamisonkhano yachikristu kwinaku ndikuona makolo ndi ana awo akulankhulana ndi kuseka. Panthawi yosangalala, ndimachita chisoni chifukwa chakuti ana anga palibe.” Mkulu wina wachikristu amakumbukira zaka zinayi zimene mwana wamkazi wake wopeza, anasiya kuyanjana nawo. Mkuluyo anati: “Nthawi zambiri, zinkachitika kuti nthawi imene tinayenera kuti tisangalale, zinthu zinali kuvuta. Ndikapatsa mkazi wanga mphatso kapena ndikapita naye kokasangalala, mkazi wangayo anali kulira akaganiza zoti mwana wake wamkazi sitinali kusangalala naye limodzi.”

Kodi tingati Akristu amenewa angokhala oti sachedwa kumva chisoni? Si zimenezo ayi. Kunena zoona, iwo angakhale akuonetsa makhalidwe amenenso Yehova ali nawo popeza munthu analengedwa m’chifanizo chake. (Genesis 1:26, 27) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Kodi Yehova anamva bwanji anthu ake Aisrayeli atam’pandukira? Pa lemba la Salmo 78:38-41, timaphunzirapo kuti Yehova zinam’pweteka kwambiri. Ngakhale zinatero, iye moleza mtima anawachenjeza ndi kuwalanga, ndipo anawakhululukira maulendo angapo atalapa. N’zodziwikiratu kuti Yehova amakonda kwambiri zolengedwa zake, zimene zili ‘ntchito ya manja ake,’ ndipo sazisiya msanga. (Yobu 14:15; Yona 4:10, 11) Iye anapatsa anthu mtima ngati wake wokondana kwambiri, ndipo n’chifukwa chake anthu pabanja amakondana kwambiri. Ndiye si zachilendo kuti anthu amachita chisoni kwambiri wachibale wawo akatayika mwauzimu.

Ndithudi, kutayika mwauzimu kwa wachibale kumakhala chimodzi mwa ziyeso zovuta kwambiri kuzipirira zimene olambira oona amakumana nazo. (Machitidwe 14:22) Yesu ananena kuti chifukwa chokhulupirira uthenga wake, mabanja ena adzagawanika. (Mateyu 10:34-38) Izi zimachitika osati chifukwa chakuti uthenga wa m’Baibulo paokha umagawanitsa mabanja ayi. M’malo mwake, kugawanika kumeneko kumachitika chifukwa chakuti ena pabanja amene si Mboni, kapena amene ataya chikhulupiriro amakana, kusiya, kapena ngakhale kutsutsa njira ya Chikristu. Koma tithokoze kuti Yehova sasiya anthu ake okhulupirika ali opanda njira yopirira nayo ziyeso zimene amakumana nazo. Ngati panopa muli ndi chisoni chifukwa chakuti wachibale wanu anatayika mwauzimu, ndi mfundo ziti za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kupirira ndi kukhalabe osangalala?

Zimene Zingakuthandizeni Kupirira

“Podzimanga . . . , khalanibe m’chikondi cha Mulungu.” (Yuda 20, 21, NW) Malinga ndi mmene zinthu zilili kwa inu panopa, zingakhale zoti palibe chimene mungachite kuti muthandize wachibale amene wasiya kutumikira Yehova. Ngakhale zili choncho, mungathe ndipo muyenera kudzimanga inuyo limodzinso ndi ena okhulupirika otsala m’banja. Veronica, amene anaona awiri mwa ana ake atatu akusiya choonadi, anati: “Ine ndi mwamuna wanga tinakumbutsidwa kuti ngati tikhalabe olimba mwauzimu, tidzakhala pamalo abwino kulandira ana athu akasintha maganizo awo. Kodi mwana wosakaza akanapita kuti atate ake akanakhala oti sanali okhoza kum’landira?”

Kuti mukhale olimba, limbikirani kuchita zinthu zauzimu. Zimenezi zikuphatikizapo kukhala ndi chizolowezi chophunzira Baibulo mozama ndi kupezeka pamisonkhano yachikristu. Dziperekeni kuthandiza ena mumpingo malinga ndi mpata umene muli nawo. N’zoona kuti zimenezi zingakhale zovuta poyamba. Veronica akukumbukira kuti: “Zimenezi zitachitika, chimene ndinali kufuna ndi kungokhala kwandekha ngati nyama yoti yavulala. Koma mwamuna wanga anaonetsetsa kuti tikuchita zinthu zauzimu. Anatsimikiza kuti tikupita ku misonkhano. Itakwana nthawi yopita ku msonkhano wachigawo, ndinafunika kulimba mtima kwambiri kuti ndipite ndi kukakumana ndi anthu. Ngakhale zinali choncho, msonkhanowo unatithandiza kum’konda kwambiri Yehova. Komanso unalimbikitsa kwambiri mwana wathu amene anali wokhulupirika.”

Maria, amene tatchula poyamba uja, amaona kuti zimam’thandiza kwambiri akamatangwanika ndi utumiki wa kumunda ndipo panopa akuthandiza anthu anayi kuphunzira Baibulo. Nayenso Laura akuti: “Ngakhale kuti ndimalira masiku onse, ndikuthokoza Yehova kuti ngakhale sindinathe kulera ana anga monga mmene makolo ena achitira, ndili ndi uthenga wangwiro wa m’Baibulo, umene umathandiza mabanja masiku ano otsiriza.” Ken ndi Eleanor, amene ana awo achikulire anachoka mu mpingo, anasintha moyo wawo kuti asamukire kumene kukufunika ofalitsa Ufumu ambiri ndipo anakayamba utumiki wa nthawi zonse. Zimenezi zawathandiza kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani imeneyi ndi kupewa kuthedwa nzeru ndi chisoni.

Musataye mtima. Chikondi “chiyembekeza zinthu zonse.” (1 Akorinto 13:7) Ken, amene tamutchula kale uja, anati: “Ana athu atasiya njira ya choonadi, ndinaona ngati kuti amwalira. Koma mlongo wanga atamwalira, ndinasintha maganizo. Ndikuthokoza kuti ana anga sanafe imfa yeniyeni ndipo Yehova wasiyabe khomo lili lotseguka kuti iwo abwerere kwa iye.” Zoonadi, zimene zimachitika n’zoti ambiri amene asiya choonadi amabwerera patapita nthawi.​—Luka 15:11-24.

Musamadziimbe mlandu. Makolo makamaka amati akakumbukira za kale, amamva chisoni poganiza kuti sanayendetse bwino zinthu polera ana awo. Komabe, mfundo yaikulu imene ili pa Ezekieli 18:20 n’njakuti Yehova amaona wochimwayo kukhala wamlandu, osati makolo ake ayi. Mfundo ina yochititsa chidwi n’njakuti ngakhale kuti buku la Miyambo limanena zambiri zokhudza udindo wa makolo wolera ana awo m’njira yabwino, lili ndi uphungu wowirikiza kanayi kuposa pamenepo wouza ana kumvera makolo awo. Inde, ana ali ndi udindo wolabadira malangizo a m’Baibulo amene makolo awo opanda ungwiro amawapatsa. Mosakayika inuyo kholo munachita zonse zotheka nthawi imeneyo. Ngakhale ngati mukuganizabe kuti munalakwitsa zina n’zina, sindiye kuti basi zimene munalakwitsazo n’zimene zachititsa kuti mwana wanu asiye choonadi. Mulimonsemo, sizipindula kungokhalira kumati “chipanda zakuti, zakuti sizikanachitika.” Tengeranipo phunziro pa zimene munalakwitsazo, yesetsani kusazibwereza, ndipo pempherani kwa Yehova kuti akukhululukireni. (Salmo 103:8-14; Yesaya 55:7) Kenako siyani kuyang’ana za m’mbuyozo n’kumayang’ana za kutsogolo.

Lezani mtima ndi anthu ena. Anthu ena, makamaka oti zimenezi sizinawachitikirepo, angavutike ndi zoti anene pofuna kukulimbikitsani kapena kukutonthozani. Chinanso, anthufe timasiyana pa zimene timaona kukhala zolimbikitsa ndi zotonthoza. Ndiye, ena akanena zinthu zoti inu n’kukhumudwa nazo, tsatirani uphungu wa Paulo wopezeka pa Akolose 3:13, NW, umene umati: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana wina ndi mnzake ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaula za mnzake.”

Zindikirani njira ya Yehova yoperekera chilango. Wachibale wanu akalandira chilango ku mpingo, kumbukirani kuti imeneyi ndiyo njira imene Yehova wakhazikitsa ndipo n’njothandiza onse, kuphatikizapo wolakwayo. (Ahebri 12:11) Choncho, pewani mtima wopeza zifukwa akulu amene anasamalira nkhaniyo kapena wotsutsa zimene anagamula. Kumbukirani kuti zinthu zimakhala bwino kwambiri tikamatsatira njira imene Yehova anakhazikitsa, koma tikamatsutsa timangowonjezera mavuto.

Aisrayeli atalanditsidwa ku Igupto, Mose anali woweruza wawo. (Eksodo 18:13-16) Popeza kuti mlandu ukakomera munthu wina umatsutsa mnzake amene ali naye mlandu, n’zosavuta kuona kuti ena anakhumudwa ndi zimene Mose anagamula. Mwina iwo anapeza zifukwa ndi kaweruzidwe ka Mose ndipo zimenezi zinalimbikitsa ena kupandukira utsogoleri wake. Ngakhale zinali choncho, Yehova anali kugwiritsabe ntchito Mose potsogolera anthu Ake, ndipo sanalange Moseyo koma apanduwo ndi mabanja awo amene anagwirizana nawo. (Numeri 16:31-35) Pamenepa tikuphunzirapo kuti tizilemekeza ndi kugwirizana ndi zimene abale amene Mulungu wawapatsa udindo masiku ano, agamula.

Pa mfundoyi, Delores amakumbukira kuti zinamuvuta kwambiri kuvomereza, mwana wake wamkazi atalangidwa ndi mpingo. Iye akuti: “Chimene chinandithandiza ndi kuwerenga mobwerezabwereza nkhani zofotokoza ubwino wa mmene Yehova amayendetsera zinthu. Ndinapanga kabuku kamene ndinalembamo mfundo zimene ndinamva m’nkhani ndi zimene ndinawerenga, zimene zinandithandiza kupirira ndi kusabwerera m’mbuyo.” Zimenezi zikutifikitsa pa mfundo ina yofunika imene ingakuthandizeni kupirira.

Nenani zakukhosi kwanu. Zingakuthandizeni kukhala ndi bwenzi limodzi kapena awiri achifundo amene mumawakhulupirira oti muziwauza zakukhosi kwanu. Ngati mukufuna zimenezi, sankhani mabwenzi amene angakuthandizeni kuganiza zinthu zolimbikitsa. Ndiponso zidzakuthandizani kwambiri ‘kutsanulira mtima wanu’ kwa Yehova mwa kupemphera. * (Salmo 62:7, 8) N’chifukwa chiyani zimenezi zidzakuthandizani? Chifukwa chakuti iye ndi amene amamvetsetsa mavuto anu. Mwachitsanzo, zingachitike kuti inu n’kuganiza kuti si chilungamo kuti muzivutika mtima choncho popeza inuyo simunasiye Yehova. Pamenepo muuzeni Yehova zakukhosi kwanu, ndipo m’pempheni kuti akuthandizeni kuganiza za nkhaniyo m’njira yosapweteka kwambiri.​—Salmo 37:5.

Pakapita nthawi, mudzatha kupirira bwinobwino chisoni chanu. Koma pakadali pano, musasiye kusangalatsa Atate wanu wakumwamba, ndipo musaganize kuti khama lanu lipita pachabe. (Agalatiya 6:9) Muzikumbukira kuti tikasiya Yehova, mavuto athu tidzakhalabe nawo. Koma tikakhala okhulupirika kwa iye, adzatithandiza pa ziyeso zimene tikukumana nazo. Choncho, dziwani kuti Yehova akumvetsa vuto lanu lonse ndipo adzapitiriza kukupatsani mphamvu yofunikira panthawi yake kuti mupirire.​—2 Akorinto 4:7; Afilipi 4:13; Ahebri 4:16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mayina ena asintha.

^ ndime 19 Kuti mumve zopempherera wachibale wochotsedwa, onani Nsanja ya Olonda ya December 1, 2001, masamba 30 ndi 31.

[Bokosi patsamba 19]

Kupirira Kwake

“Podzimanga . . . , khalanibe m’chikondi cha Mulungu.”​—Yuda 20, 21, NW.

Musataye mtima.​—1 Akorinto 13:7.

Musadziimbe mlandu.​—Ezekieli 18:20.

Lezani mtima ndi anthu ena.​—Akolose 3:13.

Zindikirani njira ya Yehova yoperekera chilango.​—Ahebri 12:11.

Nenani zakukhosi kwanu.​—Salmo 62:7, 8.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 21]

Kodi Inuyo Mwasiya Yehova?

Ngati mwatero, kaya zifukwa zake zikhale zotani, ubwenzi wanu ndi Yehova ndiponso chiyembekezo chanu chokhala ndi moyo wosatha, zasokonekera. Mwina mukufuna kubwerera kwa Yehova. Kodi mukuyesetsa kuchita zimenezo panopa? Kapena kodi mukuzengereza poganiza kuti “nthawi yake” sinafike? Kumbukirani kuti Armagedo, imene ili ngati chigumula, ikubwera mofulumira. Ndiponso, moyo m’dongosolo lino n’ngwaufupi ndi wosapanganika. Simungadziwe ngati mawa mukhala ndi moyo. (Salmo 102:3; Yakobo 4:13, 14) Munthu wina amene anapezeka ndi matenda akupha anati: “Matendawa andipeza ndikutumikira Yehova nthawi zonse, popanda zinthu zamanyazi zimene ndikubisa. Ndipo panopo mtima wanga uli pamtendere.” Koma taganizani kuti iye akanamva bwanji ngati matenda akewo anakam’peza akuganiza kuti, “Tsiku lina, ndidzabwerera kwa Yehova”? Choncho, ngati inuyo mwasiya Yehova, nthawi yake ndi ino yakuti mubwerere kwa iye.

[Zithunzi patsamba 18]

Kulimbikira kuchita zinthu zauzimu kungakuthandizeni kukhala ndi maganizo oyenera