Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ha! Ndikondadi Chilamulo Chanu”

“Ha! Ndikondadi Chilamulo Chanu”

“Ha! Ndikondadi Chilamulo Chanu”

SALMO 119 ndi nyimbo yonena za mmene munthu amene analilemba ankamvera ponena za uthenga, kapena kuti mawu, ouziridwa a Mulungu. Wolemba salmoli anaimba kuti: ‘Ndinawabisa mawu anu mumtima mwanga.’ ‘Ndidzadzikondweretsa nawo malemba anu.’ ‘Mtima wanga wasweka ndi kukhumba maweruzo anu nyengo zonse.’ ‘Mboni zanu . . . ndizo zondikondwetsa.’ ‘Ndinalira malangizo anu.’ ‘Ndidzadzikondweretsa nawo malamulo anu, amene ndiwakonda.’ ‘Ndipo ndidzalingalira pa malemba anu.’ ‘Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.’​—Salmo 119:11, 16, 20, 24, 40, 47, 48, 97.

Wamasalmo ameneyu anayamikira kuchokera pansi pa mtima mawu omwe Mulungu anadziwitsa anthu. Kodi inu mumamvanso chimodzimodzi ndi uthenga wa m’Mawu a Mulungu, Baibulo? Kodi mumafuna kuti muziwakonda kwambiri choncho? Ngati n’choncho, choyamba mukufunikira kukhala ndi chizolowezi chowerenga Baibulo nthawi zonse, tsiku lililonse ngati kungakhale kotheka. Yesu Kristu anati: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Chachiwiri, muyenera kusinkhasinkha zimene mwawerenga. Kuganizira za choonadi chonena za Mulungu, makhalidwe ake, chifuniro chake, ndiponso cholinga chake kungachititse kuti muzikonda kwambiri Baibulo. (Salmo 143:5) Ndipo chofunika kwambiri, muyenera kugwiritsa ntchito malangizo ake ogwira mtima m’moyo wanu wa tsiku ndi tsiku.​—Luka 11:28; Yohane 13:17.

Kodi mungapindule motani ngati mumakonda kwambiri zimene Baibulo limanena? “Odala iwo akusunga mboni [za Mulungu],” limatero lemba la Salmo 119:2. Mboni, kapena kuti zikumbutso, zimene zimapezeka m’Baibulo zingakuthandizeni kupirira mavuto m’moyo. (Salmo 1:1-3) Mudzapeza nzeru, luntha, ndi kuzindikira, zimene zingakuthandizeni ‘kuletsa mapazi anu njira iliyonse yoipa.’ (Salmo 119:98-101) Kudziwa choonadi chonena za Mulungu ndi cholinga chake cha dziko lapansi, kudzachititsa moyo wanu kukhala watanthauzo kwambiri ndipo kudzalimbitsa chiyembekezo chanu cham’tsogolo.​—Yesaya 45:18; Yohane 17:3; Chivumbulutso 21:3, 4.

Mboni za Yehova zimasangalala kwambiri kuthandiza ena kuti alidziwe bwino Baibulo ndiponso kuti azikonda uthenga wake. Tidzakhala osangalala ngati mutavomera pempho lathu lili m’munsimu.