Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi “Masiku Otsiriza” N’chiyani?

Kodi “Masiku Otsiriza” N’chiyani?

Kodi “Masiku Otsiriza” N’chiyani?

KODI mumadzifunsa kuti m’tsogolo mwanu pamodzi ndi achibale anu ndiponso mwa mabwenzi anu muli zotani? Anthu ambiri amamvetsera mwachidwi nkhani za pa TV, pa wailesi kapena kuwerenga manyuzipepala, kuti adziwe mmene zinthu zochitika padzikoli zingakhudzire moyo wawo. Koma timadziwa zoona zenizeni tikamawerenga m’Mawu ouziridwa a Mulungu. Zili choncho chifukwa chakuti kalekale Baibulo linaneneratu osati chabe za zinthu zimene zikuchitika tsopano lino komanso zinthu zimene zikubwera m’tsogolo.

Mwachitsanzo, pamene Yesu Kristu anali padziko lapansi, analankhula kwambiri za Ufumu wa Mulungu. (Luka 4:43) N’zoonekeratu kuti anthu amene ankamumvetsera ankafuna kudziwa nthawi imene Ufumu wabwino kwambiri umenewu udzabwere. Ndipo, patangotsala masiku atatu kuti Yesu aphedwe mopanda chilungamo, ophunzira ake anam’funsa kuti: “Chizindikiro cha kufika kwanu [kukhalapo kwanu m’mphamvu za Ufumu] n’chiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano?” (Mateyu 24:3) Yesu anawauza kuti Yehova Mulungu yekha ndi amene anali kudziwa za nthawi yeniyeni imene Ufumuwo udzayambe kulamulira padziko lonse lapansi. (Mateyu 24:36; Marko 13:32) Komabe, Yesu ndi anthu ena ananeneratu za zochitika zina padziko lapansi zimene zidzapereke umboni woti Kristu akulamulira m’mphamvu za Ufumu.

Tisanaone umboni umene ukuoneka woti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ a dongosolo la zinthu lilipoli, tiyeni tione mwachidule chinthu china chofunika kwambiri chimene chinachitika kumalo osaoneka a mizimu. (2 Timoteo 3:1) Yesu Kristu anakhala Mfumu kumwamba m’chaka cha 1914. * (Danieli 7:13, 14) Baibulo limatiuza zimene Yesu anachita atangolandira mphamvu za Ufumu. Limati: “Munali nkhondo m’mwamba. Mikayeli ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka; chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo.” (Chivumbulutso 12:7) “Mikayeli mkulu wa angelo” ndi Yesu Kristu pa udindo wake wakumwamba. * (Yuda 9; 1 Atesalonika 4:16) Chinjoka ndi Satana Mdyerekezi. Pankhondoyi, n’chiyani chomwe chinachitikira Satana ndi angelo omutsatira, omwe amatchedwa ziwanda? Anagonja ndipo ‘anaponyedwa pansi,’ kapena kuti anachotsedwa kumwamba, n’kuponyedwa kudziko lapansi. (Chivumbulutso 12:9) Chifukwa cha zimenezi, “miyamba ndi [iwo] akukhala momwemo,” amene ali ana auzimu okhulupirika a Mulungu, anakondwera. Koma anthu sanakondwere choncho. Baibulo linaneneratu kuti: “Tsoka mtunda . . . chifukwa mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziwa kuti kam’tsalira kanthawi.”​—Chivumbulutso 12:12.

Satana, mu mkwiyo wake, wabweretsa tsoka, zomwe zachititsa kuvutika ndi kuzunzika, kwa anthu a padziko lapansi. Komabe, tsoka limenelo ndi la “kanthawi.” Baibulo limatchula nthawi imeneyi kuti “masiku otsiriza.” Tingasangalale kuti posachedwapa mavuto amene Mdyerekezi akuchititsa padziko lapansi adzachotsedwa. Koma kodi ndi umboni wanji umene ukusonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Kuti mumve zambiri, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? tsamba 218 mpaka 219, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

COVER: Foreground: © Chris Stowers/​Panos Pictures; background: FAROOQ NAEEM/​AFP/​Getty Images