Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Akhala Akufunafuna Moyo Wosatha

Anthu Akhala Akufunafuna Moyo Wosatha

Anthu Akhala Akufunafuna Moyo Wosatha

KUYAMBIRA kalekale, anthu akhala akulakalaka moyo wosatha. Koma mpaka pano chilakolako chimenechi sichinakwaniritsidwebe, chifukwa palibe munthu amene anapezapo njira yothetsera imfa. Komano zimene ofufuza zamankhwala apeza posachedwapa zachititsa anthu kukhalanso ndi chiyembekezo chakuti n’zothekadi kutalikitsa kwambiri moyo wa munthu. Taganizirani zimene asayansi osiyanasiyana akufufuza pankhaniyi.

Asayansi ya zamoyo akuyesa kupeza njira yoti munthu akamakalamba, thupi lake lizipangabe maselo atsopano. Asayansi akudziwa kuti thupi limachotsa maselo akale, omwe amakhala akutha ntchito, n’kupanga ena atsopano. Ndipotu, nthawi zingapo pa moyo wa munthu, mbali yaikulu ya thupi imakonzedwa m’njira imeneyi n’kukhala yatsopano. Ofufuza amati kukonza thupiku kutapitirira, ndiye kuti “thupi la munthu lingapitirize kukhala latsopano kwa nthawi yaitali kwambiri, mwinanso kosatha.”

Asayansi ena akufufuza njira yopangira ziwalo pogwiritsira ntchito maselo a mluza, ndipo njirayi anthu ambiri sakugwirizana nayo. Akuti mwa njira imeneyi n’zotheka kuti odwala amene akufunika ziwalo monga chiwindi, impso, kapena mtima angathe kuwapangira ziwalo zatsopano, zogwirizana ndendende ndi thupi lawo. Akuti angatero pogwiritsira ntchito maselo a wodwala yemweyo.

Asayansi ena akufufuza njira imene akuona kuti ingathe kudzachititsa kuti m’tsogolo muno madokotala adzakhale ndi tizipangizo tating’ono ngati selo ya m’thupi, tomwe azidzatilowetsa m’magazi a wodwala kuti tipeze ndi kuwononga maselo a khansa ndiponso tizilombo toyambitsa matenda. Anthu ena amakhulupirira kuti sayansi imeneyi, pamodzi ndi njira yochizira kapena kupewera matenda pokonza maselo enaake m’thupi, idzachititsa kuti thupi la munthu lizidzatha kumangopitirizabe kudzikonza.

Anthu ena amaumitsa mtembo pouziziritsa. Cholinga chawo n’chakuti ausunge mpaka nthawi imene ofufuza zamankhwala adzatulukire njira zothandiza madokotala kuchiza matenda osiyanasiyana, njira zothandiza thupi kuti lisakalambe, ndiponso zothandiza anthu akufa kukhalanso amoyo ndi athanzi. Magazini ya American Journal of Geriatric Psychiatry inanena kuti iyi ndi “njira yamakono yosungira mitembo ya anthu monga ankachitira Aigupto akale.”

Khama la anthu lofuna kukhala ndi moyo wosatha likusonyeza kuti imfa ndi yosatheka kuizolowera ngakhale pang’ono. Koma kodi n’zothekadi kuti anthu angakhale ndi moyo wosatha? Kodi Baibulo limati chiyani pankhaniyi? Nkhani yotsatirayi ipereka mayankho pa mafunso amenewa.