Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kayendedwe Panyanja Yaikulu

Kayendedwe Panyanja Yaikulu

Kayendedwe Panyanja Yaikulu

MU ZILUMBA zotchedwa Marshall muli tizilumba topitirira 1,200, ndipo tambiri n’tatitali mosapitirira mamita sikisi, kuchokera pothera madzi a nyanja. Mukangoyenda pang’ono kuchoka ku tizilumbati kupita m’nyanja, tizilumbati sitionekanso. Koma amalinyero akale a ku Marshall ankayenda bwinobwino pabwato ulendo wopita m’tizilumba tambirimbiriti, tomwe tinayalana m’dera lalikulu makilomita 2 miliyoni m’nyanja ya Pacific. Kodi ankachita zimenezi motani? Iwo ankayenda motsogozedwa ndi “mapu” osacholowana koma othandiza kwambiri, otchedwa matchati a timitengo.

Chifukwa choyendayenda m’derali, amalinyero a ku Marshall anadziwa kuti nthaka ya pa chilumba imachititsa kuti mafunde aziyenda m’ndondomeko inayake yomwe imasonyeza kumene kuli chilumbacho, ngakhale chitakhala kutali pamtunda wa makilomita mpaka 30. Popeza kuti mafundewo anali kuyenda m’ndondomeko zambirimbiri, matchati a timitengo ankawathandiza kukumbukira ndondomekozo. Kodi matchatiwa anali otani? Monga mukuonera pachithunzichi, timitengo todulidwa ku mitsitsi ya payini kapena ku timitengo ta pakati pa masamba a kokonati ankatimangirira pamodzi mopingasa, kuimira dongosolo la kayendedwe ka mafunde. Ndiye ankamangiriranso tizigoba ta nkhono, kuimira malo amene pali kachilumba kalikonse.

Kwa zaka zambiri, kuyenda panyanja mogwiritsa ntchito tchati cha timitengo chinali chinsinsi chodziwidwa ndi anthu omwe anachita kusankhidwa basi. Nangano kodi mwana amene wangoyamba kumene kuyenda panyanja ankaphunzira bwanji kugwiritsa ntchito tchati cha timitengochi? Ankatero pophunzitsidwa ndi kugwiritsa ntchito zimene waphunzirazo. Munthu amene akudziwa bwino kuyenda panyanja, ankaphunzitsa m’malinyero wamng’onoyo mwamseri, mwina poyenda naye ulendo wopita m’tizilumba tapafupi. Wophunzirayo akayamba kudziwa ndondomeko ya kayendedwe ka mafunde, ankayamba kudzidalira pa luso lake logwiritsa ntchito tchati cha timitengo. Kenaka amafika poyenda yekha panyanja.

Chimodzimodzinso, Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, lingatitsogolere pa ulendo wa pamoyo wathu. Poyamba, munthu wina angatithandize kudziwa mfundo zikuluzikulu za m’Malemba. Kenaka, tikapitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kugwiritsa ntchito mfundo zake, timayamba kudalira zimene mawuwa amanena. Mulungu anauza Yoswa, yemwe anali mtsogoleri wa Aisrayeli, kuti apitirize kuwerenga Mawu a Mulungu kotero kuti ‘asamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo.’ Ndipo Mulungu anauzanso Yoswa kuti “ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.” (Yoswa 1:8) Inde, Baibulo lingathe kutitsogolera njira ya moyo yomwe ili yodalirika ndiponso yopindulitsa.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

© Greg Vaughn