Kodi Baibulo Lili ndi Malamulo Okhwima Kwambiri?
Kodi Baibulo Lili ndi Malamulo Okhwima Kwambiri?
“NDILI mwana, sindinaphunzitsidwe mfundo zilizonse za m’Baibulo. Sitinkakambirana n’komwe za Mulungu,” anatero mnyamata wina wa ku Finland. Anthu oleredwa motere si osowa masiku ano. Anthu ambiri, makamaka ana, amaona kuti Baibulo ndi buku lachikale kwambiri ndiponso kuti malamulo ake n’ngokhwima kwambiri. Anthu ofuna kutsatira Baibulo amaonedwa ngati opanikizika ndipo amangovutika kutsatira malamulo ambirimbiri okhwima. Motero, anthu ambiri amaona kuti ndi bwino kupeza nzeru m’njira ina kusiyana ndi kuvutika n’kuwerenga Baibulo.
Chifukwa chachikulu chimene chimachititsa anthu kuona Baibulo m’njira imeneyi n’chakuti, kale, kwa nthawi yaitali, Matchalitchi Achikristu anali ndi mbiri yozunza anthu. Mwachitsanzo, m’nyengo imene akatswiri ena a mbiri yakale anaitcha kuti Nyengo Yamdima, tchalitchi cha Katolika ku Ulaya chinkalamulira pafupifupi mbali iliyonse ya moyo wa anthu. Munthu aliyense amene akanayesa kutsutsana ndi tchalitchicho akanatha kuzunzidwa mwinanso kuphedwa kumene. Matchalitchi a Chipolotesitanti, amene anabwera pambuyo pake, nawo anachititsa kuti ufulu wa anthu ukhale wochepa. Masiku ano anthu amene akudziwa bwino zipembedzo za Chipolotesitanti amaganizira za chilango choopsa chimene magulu amenewa ankapatsa anthu. Motero chifukwa choti matchalitchiwa anali ankhanza, anthuwa amangoganiza kuti ndiye kutinso ziphunzitso za m’Baibulo n’zolimbikitsa nkhanza.
Chaposachedwapa, m’mayiko ena matchalitchi achikristu ataya kwambiri mphamvu zimene anali nazo pa moyo wa anthu. Anthu ambiri atasiya zikhulupiriro za matchalitchiwa anayamba kukhulupirira kuti anthu ali ndi ufulu wosankha okha zabwino ndi zoipa. Kodi zotsatirapo n’zotani? Ahti Laitinen, yemwe ndi pulofesa wa maphunziro apamwamba okhudza zamalamulo, analongosola kuti: “Anthu ambiri asiya kulemekeza anthu aulamuliro, ndipo ayamba kuvutika kumvetsa zimene zili zabwino ndi zimene sizili zabwino.” Chodabwitsa n’chakuti ngakhale atsogoleri azipembedzo ayamba kuganiza choncho. Bishopu wina wotchuka wa mpingo wa Lutheran anati: “Ine ndimatsutsa mfundo yakuti nkhani zokhudza khalidwe labwino tingazimvetse mothandizidwa ndi Baibulo kapena atsogoleri achipembedzo.”
Kodi Ufulu Wopanda Malire N’ngwabwino?
Anthu ena, makamaka achinyamata, amasangalala ndi zokhala ndi ufulu wopanda malire. Ambiri safuna zoti winawake aziwauza zochita kapena kuti azichita chilichonse motsatira malamulo enaake. Komabe kodi ndi bwino kuti aliyense azingochita zimene akufuna? Kuti tiyankhe funso limeneli, taganizirani chitsanzo ichi. Ganizirani kuti mzinda winawake ulibe malamulo alionse a pamsewu. Mumzindawu, munthu safunika laisensi kuti ayendetse galimoto. Anthu amaloledwa kuyendetsa galimoto mulimonse mmene akufunira, ngakhale ataledzera, ndipo mulibe malire a liwiro lovomerezeka, mulibe zikwangwani zolamula magalimoto kuima, magetsi olamulira magalimoto pamsewu, misewu yongoyenda
galimoto zolowera kumodzi, kapena malo owolokera msewu a oyenda pansi. Kodi umenewu ungakhale ufulu wabwino? Ayi ndithu. Zimenezi mapeto ake zingachititse chisokonezo ndiponso ngozi zoopsa. Ngakhale kuti malamulo a pamsewu amachepetsa ufulu wa anthu, tikudziwa kuti malamulowa amateteza woyendetsa galimoto komanso anthu oyenda pansi.Chimodzimodzinso, Yehova amatipatsa malangizo a mmene tiyenera kukhalira. Zimenezi zimatipindulitsa. Popanda malangizo otere, bwenzi tikuphunzira zinthu mochita kuyesa izi ndi izi kuti tione zimene zingatithandize. Mapeto ake tingathe kudzivulaza ndiponso kuvulaza anthu ena. Kukhala ndi chisokonezo chotere pa nkhani ya khalidwe n’koopsa mofanana ndi kukhala mumzinda wopanda malamulo apamsewu. Chifukwatu timafunikira malamulo enaake ndithu, ndipo anthu ambiri amavomereza mfundo imeneyi.
“Katundu Wanga Ali Wopepuka”
Malamulo apamsewu amakhala ndi mfundo zambiri zatsatanetsatane ndipo m’madera ena muli malamulo ambirimbiri ongokhudza kaimitsidwe ka galimoto basi. Koma Baibulo silitchula malamulo ambirimbiri. M’malo mwake limatchula mfundo zikuluzikulu za makhalidwe abwino, ndipo mfundo zimenezi si zokhwima kwambiri kapena zopanikiza ayi. Yesu Kristu anauza anthu a m’nthawi yake mawu olimbikitsa kwambiri owaitana, akuti: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” (Mateyu 11:28, 30) M’kalata yopita ku mpingo wachikristu wa ku Korinto, mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.”—2 Akorinto 3:17.
Komatu ufulu umenewu uli ndi malire. Yesu anasonyezeratu kuti pa zinthu zimene Mulungu amafuna kuti tizichita palinso malamulo osiyanasiyana osavuta kutsatira. Mwachitsanzo, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu.” (Yohane 15:12) Tangoganizirani mmene moyo ukanakhalira aliyense akanati azitsatira lamulo limeneli. Motero, ufulu umene Akristu ali nawo si wopanda malire. Mtumwi Petro analemba kuti: “Monga mfulu, koma osakhala nawo ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu.”—1 Petro 2:16.
Motero, ngakhale kuti Akristu sali pansi pa malamulo ambirimbiri atsatanetsatane, iwo sayendera maganizo awo pankhani ya zabwino ndi zoipa. Anthu amafunikira malangizo amene Mulungu yekha ndiye angapereke. Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Tikamamvera malangizo a Mulungu, timapindula kwambiri.—Salmo 19:11.
Phindu lake limodzi ndilo kukhala wosangalala. Mwachitsanzo, mnyamata amene tam’tchula kumayambiriro kwa nkhani ino uja, poyamba anali mbava ndiponso wabodza. Iye ankakondanso kwambiri zachiwerewere. Komano ataphunzira mfundo zapamwamba za m’Baibulo, anasintha moyo wake kuti azichita zinthu mogwirizana ndi zimenezo. Panthawi ina, iye anati: “Ngakhale kuti sindinayambe kutsatira mfundo za m’Baibulo
zonse panthawi imodzi, ndinkadziwa kuti zinali zothandiza. Moyo wanga wakale sunandipatse chimwemwe chimene ndili nacho panopo. Ukamatsatira mfundo za m’Baibulo, moyo wako umakhala wabwino. Umadziwa kumene ukulowera ndiponso umadziwa kuti izi n’zabwino, izi n’zoipa.”Anthu ochuluka zedi aonanso zoterezi pa moyo wawo. Mwa zinthu zina, malangizo a m’Baibulo awathandiza kukhala bwino kwambiri ndi anthu, kuona ntchito m’njira yoyenera, kupewa makhalidwe oipa, ndi kukhala moyo wosangalala kuposa kale. Mnyamata wina dzina lake Markus, * yemwe wakhalapo moyo wosatsatira miyezo ya m’Baibulo ananena za moyo wake motere: “Chifukwa chokhala moyo wotsatira mfundo za m’Baibulo, ndinayamba kudzipatsa ulemu kwambiri.” *
Inuyo Mutsatira Ziti?
Ndiye kodi tingati Baibulo lili ndi malamulo okhwima? Inde, lili ndi malamulo okhwima otipindulitsa. Koma kodi Baibulo lili ndi malamulo okhwima kwambiri? Ayi. Chifukwatu ufulu wopanda malire umabweretsa mavuto basi. Mfundo za m’Baibulo si zokhwima kwambiri ayi, ndipo zimatithandiza kukhala moyo wabwino ndi kusangalala. Markus anati: “M’kupita kwa nthawi ndaona kuti kutsatira Mawu a Mulungu pa moyo n’chinthu chanzeru. Ngakhale kuti moyo wanga n’ngosiyana kwambiri ndi moyo wa anthu ambiri, sindiganiza kuti ndamanidwa zinazake zofunikira pa moyo.”
Mukayamba kupeza madalitso obwera chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo, mumamvetsa kwambiri kufunika kwa Mawu a Mulungu. Zimenezi zimabweretsa madalitso aakulu kuposa apa, chifukwa mudzayamba kukonda Mwini wa mfundo zimenezi, yemwe ndi Yehova Mulungu. “Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.”—1 Yohane 5:3.
Yehova ndi Mlengi wathu komanso ndi Tate wathu wakumwamba. Iye amadziwa zinthu zimene zingatithandize kwambiri. Satikhwimitsira zinthu ayi, koma amatilangiza mwachikondi kuti tizikhala moyo wabwino. M’mawu a ndakatulo, Yehova akutilimbikitsa kuti: “Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”—Yesaya 48:18.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 13 Dzinali talisintha.
^ ndime 13 Kuti mudziwe zambiri zokhudza moyo umene Baibulo limati tizikhala, onani mutu 12 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 9]
Yesu ananena kuti malamulo a Mulungu n’ngopumulitsa
[Chithunzi patsamba 10]
Munthu akamamvera malangizo a Mulungu amakhala wachimwemwe ndi wodzilemekeza