Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulimba Mtima Chifukwa cha Chikhulupiriro ndi Kuopa Mulungu

Kulimba Mtima Chifukwa cha Chikhulupiriro ndi Kuopa Mulungu

Kulimba Mtima Chifukwa cha Chikhulupiriro ndi Kuopa Mulungu

“Khala wamphamvu, nulimbike mtima, . . . Yehova Mulungu wako ali ndi iwe.”​—YOSWA 1:9.

1, 2. (a) Malinga ndi kuona kwa munthu, kodi Israyeli akanatha kugonjetsa Akanani? (b) Kodi Yoswa analimbikitsidwa motani?

MU 1473 B.C.E., mtundu wa Israyeli unakonzekera kulowa Dziko Lolonjezedwa. Ponena za mavuto omwe anali m’tsogolo, Mose anakumbutsa anthuwo kuti: “Muli kuwoloka Yordano lerolino, kulowa ndi kulandira amitundu aakulu ndi amphamvu akuposa inu, midzi yaikulu ndi ya malinga ofikira kuthambo, anthu aakulu ndi atalitali, ana a Aanaki, . . . amene munamva mbiri yawo, ndi kuti, Adzaima ndani pamaso pa ana a Anaki?” (Deuteronomo 9:1, 2) Zoonadi zimphona zankhondo zimenezi zinali zotchuka kwambiri. Ndiponso, Akanani anali ndi ankhondo okhala ndi zida zonse. Iwo anali ndi akavalo ndi magaleta okhala ndi zikwakwa zachitsulo ku mawiro.​—Oweruza 4:13.

2 Koma Israyeli unali mtundu wa akapolo ndipo apa n’kuti atangomaliza zaka 40 ali m’chipululu. Motero, malinga ndi kuona kwa munthu, zinali zosatheka kuti iwo angagonjetse Akanani. Koma Mose anali ndi chikhulupiriro; iye ‘ankaona’ Yehova akuwatsogolera. (Ahebri 11:27) Ndipo anauza anthuwo kuti: “Yehova Mulungu wanu ndiye amene awoloka pamaso panu . . . Iye adzawawononga, iye adzawagwetsa pamaso panu.” (Deuteronomo 9:3; Salmo 33:16, 17) Mose atafa, Yehova analimbikitsa Yoswa mwa kumuuza kuti adzamuthandiza. Iye anati: “Tauka tsono, nuwoloke Yordano uyu, iwe ndi anthu awa onse, kulowa m’dzikomo ndili kuwapatsa, ndiwo ana a Israyeli. Palibe munthu adzatha kuima pamaso pako masiku onse a moyo wako; monga ndinakhala ndi Mose momwemo ndidzakhala ndi iwe.”​—Yoswa 1:2, 5.

3. Kodi n’chiyani chinathandiza Yoswa kuti akhale ndi chikhulupiriro ndiponso kulimba mtima?

3 Kuti Yehova amuthandize ndi kumutsogolera, Yoswa ankafunikira kuwerenga ndi kusinkhasinkha Chilamulo cha Mulungu ndi kuchitsatira. Yehova anati: “Ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru. Kodi sindinakulamulira iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.” (Yoswa 1:8, 9) Chifukwa choti Yoswa anamvera Mulungu, anali wolimba mtima, wamphamvu ndipo anachita zinthu mwanzeru. Koma anzake ambiri sanamvere. Chifukwa cha zimenezi, sanachite zinthu mwanzeru, ndipo anafa m’chipululu.

Anthu Opanda Chikhulupiriro Ndiponso Osalimba Mtima

4, 5. (a) Kodi maganizo a azondi khumi anali otani powayerekeza ndi a Yoswa ndi Kalebi? (b) Kodi Yehova anati chiyani chifukwa cha kupanda chikhulupiriro kwa anthuwa?

4 Zaka 40 m’mbuyomo pamene Israyeli anafika nthawi yoyamba pafupi ndi Kanani, Mose anatuma amuna 12 kuti akazonde dziko. Atabwerako, amuna 10 anali ndi mantha. Iwo anati: “Anthu onse tidaona pakati pake ndiwo anthu aatali misinkhu. Tinaonakonso Anefili, ana a Anaki, obadwa ndi Anefili; ndipo tinaoneka m’maso mwathu ngati zinsidzi.” Kodi “anthu onse,” kuwonjezera pa a Anaki, anali zimphona? Ayi. Kodi a Anaki anali mbadwa za Anefili omwe anakhalako Chigumula chisanachitike? Ayi. Koma chifukwa cha kukokomeza kumeneku, khamu lonse linachita mantha kwambiri. Anthu anafuna ngakhale kubwerera ku Igupto, m’dziko limene anali akapolo.​—Numeri 13:31–14:4.

5 Koma azondi awiri, Yoswa ndi Kalebi, anali ofunitsitsa kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Iwo anati: Akanani “ndiwo mkate wathu; mthunzi wawo wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.” (Numeri 14:9) Kodi Yoswa ndi Kalebi anangotengeka maganizo? Ayi ndithu. Iwo limodzi ndi mtundu wonse anaona Yehova akuchititsa manyazi Igupto wamphamvu ndi milungu yake mwa kugwiritsa ntchito Miliri Khumi. Ndiyeno anaona Yehova akumiza Farao ndi gulu lake lankhondo m’Nyanja Yofiira. (Salmo 136:15) N’zoonekeratu kuti zifukwa zokhalira ndi mantha zomwe azondi khumi limodzi ndi anthu omwe anawatsatira anali nazo zinali zosamveka. Posonyeza kupwetekedwa mtima kwambiri, Yehova anati: “Adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pawo?”​—Numeri 14:11.

6. Kodi kulimba mtima kumayendera limodzi ndi chikhulupiriro motani, ndipo zimenezi zimachitika motani masiku ano?

6 Yehova anatchula vuto lenileni limene anthuwo anali nalo. Ndipo vutolo linali kupanda chikhulupiriro kwawo kumene kunaonekera chifukwa cha mantha amene anali nawo. Inde, chikhulupiriro ndi kulimba mtima zimayendera limodzi kwambiri moti ponena za mpingo wachikristu ndi nkhondo yake yauzimu, mtumwi Yohane analemba kuti: “Ichi ndi chilako tililaka nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu.” (1 Yohane 5:4) Masiku ano, chikhulupiriro chonga cha Yoswa ndi Kalebi chathandiza kuti uthenga wabwino wa Ufumu ulalikidwe padziko lonse ndi Mboni za Yehova zoposa sikisi miliyoni. Mboni zimenezi zimaphatikizapo ana ndi akulu, amphamvu ndi odwala. Palibe mdani yemwe watha kutseka pakamwa khamu lamphamvu ndi lolimba mtima limeneli.​—Aroma 8:31.

‘Musabwerere’ M’mbuyo

7. Kodi ‘kubwerera’ kumatanthauzanji?

7 Atumiki a Yehova masiku ano akulalikira uthenga wabwino molimba mtima chifukwa choti amagwirizana ndi mtumwi Paulo yemwe analemba kuti: “Ife si ndife a iwo akubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.” (Ahebri 10:39) ‘Kubwerera’ komwe Paulo anatchula sikutanthauza kuchita mantha nthawi yochepa chabe, chifukwa atumiki a Mulungu okhulupirika ambiri nthawi zina achitapo mantha. (1 Samueli 21:12; 1 Mafumu 19:1-4) M’malo mwake, buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo linafotokoza kuti, kumatanthauza “kufutuka,” “kutenga choonadi mopepuka.” Ndipo linawonjezera kuti, ‘kubwerera’ angakhale mawu okuluwika omwe anachokera pa “kutsitsa matanga a chombo n’kuchepetsa liwiro lake,” kumene kungakhale kuchepetsa changu potumikira Mulungu. Koma omwe ali ndi chikhulupiriro cholimba saganizira ‘zochepetsa liwiro lawo’ akakumana ndi mavuto kaya akhale chizunzo, kudwaladwala, kapena mayesero ena. M’malo mwake, amapitiriza kutumikira Yehova, podziwa kuti amawasamalira kwambiri ndiponso kuti Yehova amadziwa zomwe iwo angathe kuchita ndi zomwe sangathe. (Salmo 55:22; 103:14) Kodi muli ndi chikhulupiriro chotero?

8, 9. (a) Kodi Yehova analimbitsa motani chikhulupiriro cha Akristu oyambirira? (b) Kodi tingachite chiyani kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu?

8 Panthawi ina atumwi anaona kuti chikhulupiriro chawo chinali chosakwanira, motero anati kwa Yesu: “Mutiwonjezere chikhulupiriro.” (Luka 17:5) Pempho lawo lochokera m’mtima linayankhidwa, makamaka pa Pentekoste mu 33 C.E., pamene mzimu woyera womwe anawalonjeza unafika pa ophunzira ndipo unawathandiza kuzindikira mwakuya Mawu a Mulungu ndi cholinga chake. (Yohane 14:26; Machitidwe 2:1-4) Chikhulupiriro chawo chitalimbitsidwa, ophunzirawo anayamba ntchito yolalikira imene inapereka uthenga wabwino kwa “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo,” ngakhale kuti anali kutsutsidwa.​—Akolose 1:23; Machitidwe 1:8; 28:22.

9 Kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu ndi kupitirizabe mu utumiki wathu, ifenso tifunikira kuphunzira ndi kusinkhasinkha Malemba ndiponso kupempherera mzimu woyera. Mwa kuchita khama kuti choonadi cha Mulungu chikhazikike m’maganizo ndi m’mitima yathu, mofanana ndi mmene Yoswa, Kalebi ndi ophunzira achikristu oyambirira anachitira, tidzakhala ndi chikhulupiriro chomwe chidzatipatsa kulimba mtima komwe tikufunikira kuti tipirire pankhondo yathu yauzimu ndiponso kuti tipambane.​—Aroma 10:17.

Sitiyenera Kungokhulupirira Kuti Kuli Mulungu

10. Kodi chikhulupiriro chenicheni chimafuna chiyani?

10 Monga momwe anthu okhulupirika akale anachitira, chikhulupiriro chimene chingatilimbitse mtima ndi kupirira chimafuna zambiri osati kungokhulupirira kuti kuli Mulungu. (Yakobo 2:19) Chimafuna kuti tidziwe Yehova mmene alili ndi kum’dalira kwambiri. (Salmo 78:5-8; Miyambo 3:5, 6) Chimatanthauza kukhulupirira ndi mtima wonse kuti kumvera malamulo a Mulungu ndi mfundo zake kumatipindulitsa kwambiri. (Yesaya 48:17, 18) Chikhulupiriro chimafunanso kusakayika m’pang’ono pomwe kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake onse ndipo “ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.”​—Ahebri 11:1, 6; Yesaya 55:11.

11. Kodi Yoswa ndi Kalebi anadalitsidwa motani chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro ndi kulimba mtima?

11 Chikhulupiriro chotero sichimangokhala malo amodzi. Chimakula tikamagwiritsa ntchito choonadi m’moyo wathu, tikamalawa’ ubwino wake, ‘tikamaona’ mapemphero athu akuyankhidwa ndiponso tikamazindikira m’njira zina kuti Yehova ndi amene akutitsogolera. (Salmo 34:8; 1 Yohane 5:14, 15) Sitingakayikire kuti chikhulupiriro cha Yoswa ndi Kalebi chinakula atalawa ubwino wa Mulungu. (Yoswa 23:14) Taganizirani mfundo izi: Iwo anapulumuka ulendo wa zaka 40 m’chipululu, monga momwe Mulungu ananenera kuti adzatero. (Numeri 14:27-30; 32:11, 12) Iwo anachita ntchito yaikulu pa zaka zisanu ndi chimodzi zogonjetsa Kanani. Pomaliza, anakhala moyo wathanzi ndiponso wautali, ndipo aliyense analandira ngakhale cholowa chake. Yehova amaperekadi mphoto kwa anthu amene amam’tumikira mokhulupirika ndi molimba mtima.​—Yoswa 14:6, 9-14; 19:49, 50; 24:29.

12. Kodi Yehova ‘amakuza mawu ake’ motani?

12 Kukoma mtima kumene Mulungu anasonyeza kwa Yoswa ndi Kalebi kumatikumbutsa mawu a wamasalmo akuti: “Munakuzitsa mawu anu koposa dzina lanu lonse.” (Salmo 138:2) Yehova akalonjeza chinthu m’dzina lake, kukwaniritsidwa kwa lonjezolo ‘kumakuzika’ m’njira yakuti kumaposa zonse zimene timayembekezera. (Aefeso 3:20) Yehova sagwiritsa mwala anthu omwe ‘amakondwera’ mwa iye.​—Salmo 37:3, 4.

Munthu Amene “Anakondweretsa Mulungu”

13, 14. N’chifukwa chiyani Enoke anafunikira chikhulupiriro ndi kulimba mtima?

13 Tingaphunzire zambiri zokhudza chikhulupiriro ndi kulimba mtima mwa kuona chitsanzo cha Enoke, Mboni inanso yomwe inakhalako Chikhristu chisanayambe. Ngakhale nthawi imene Enoke anali asanayambe kulosera, n’kutheka kuti ankadziwa kuti chikhulupiriro ndi kulimba mtima kwake zidzayesedwa. Akanadziwa bwanji zimenezi? Chifukwa chakuti Yehova anali atanena m’munda wa Edene kuti padzakhala chidani pakati pa otumikira Mulungu ndi otumikira Satana Mdyerekezi. (Genesis 3:15) Enoke ankadziwanso kuti chidani chimenechi chinali chitayamba kale m’mbiri ya anthu nthawi imene Kaini anapha mbale wake Abele. Ndithudi, pambuyo poti Enoke wabadwa, Adamu, tate wawo, anakhala moyo zaka pafupifupi 310.​—Genesis 5:3-18.

14 Koma ngakhale zinali choncho, Enoke molimba mtima “anayendabe ndi Mulungu” ndipo anadana ndi zinthu zonse zonyoza koopsa zimene anthu ankanenera Yehova. (Genesis 5:22; Yuda 14, 15) Zikuoneka kuti chifukwa cha kulimba mtima kotereku pochirikiza kulambira koona, Enoke anakhala ndi adani ambiri ndipo anaika moyo wake pangozi. Zitatero, Yehova anateteza mneneri wake ku ululu wa imfa. Atauza Enoke kuti “anakondweretsa Mulungu,” Yehovayo ‘anam’tenga’ kuchoka ku moyo kupita ku imfa, mwina panthawi imene anali kuona masomphenya olosera zam’tsogolo.​—Ahebri 11:5, 13; Genesis 5:24.

15. Kodi n’chitsanzo chabwino chotani chomwe Enoke anasonyeza atumiki a Yehova masiku ano?

15 Atangotchula za kutengedwa kwa Enoke, Paulo anagogomezeranso kufunika kwa chikhulupiriro, ndipo anati: ‘Koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kukondweretsa Mulungu.’ (Ahebri 11:6) Inde, chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro Enoke analimba mtima kuyenda ndi Yehova ndipo anatha kulengeza uthenga Wake wa chiweruzo kwa anthu osapembedza. Pochita zimenezi, Enoke anatisonyeza chitsanzo chabwino. Ifenso tili ndi ntchito yofanana yoti tichite m’dziko limene limatsutsa kulambira koona ndipo ndi loipa mwamtundu uliwonse.​—Salmo 92:7; Mateyu 24:14; Chivumbulutso 12:17.

Kulimba Mtima Chifukwa Choopa Mulungu

16, 17. Kodi Obadiya anali yani, ndipo anakumana ndi zinthu zotani?

16 Kusiyapo chikhulupiriro, palinso khalidwe lina lomwe limathandiza kukhala olimba mtima. Khalidwe limeneli ndi kuopa Mulungu mosonyeza ulemu. Tiyeni tikambirane chitsanzo chabwino kwambiri cha munthu woopa Mulungu amene anakhalako m’nthawi ya mneneri Eliya ndi ya Mfumu Ahabu, imene inkalamulira ufumu wa kumpoto wa Israyeli. Panthawi ya kulamulira kwa Ahabu, kulambira Baala kunaipitsa ufumu wonse wa kumpoto kuposa kale lonse. Ndipotu, aneneri a Baala okwana 450 ndi aneneri okwana 400 a chifanizo, chomwe chinali chizindikiro cha ziwalo za mwamuna, ‘ankadya pa gome la Yezebeli,’ mkazi wa Ahabu.​—1 Mafumu 16:30-33; 18:19.

17 Yezebeli, mdani wa Yehova wopanda chifundo, anafuna kuthetsa kulambira koona m’dzikolo. Iye anapha aneneri ena a Yehova ndipo anafuna ngakhale kupha Eliya, amene motsogoleredwa ndi Mulungu anathawa kuwoloka Yordano. (1 Mafumu 17:1-3; 18:13) Kodi mukuona mmene kukanakhalira kovuta kuchirikiza kulambira koyera mu ufumu wa kumpoto m’nthawi imeneyo? Ndipo bwanji ngati munali kugwira ntchito panyumba ya mfumu, kodi sizikanakhala zovuta kwambiri? Izi n’zomwe munthu woopa Mulungu, Obadiya, * amene ankayang’anira nyumba ya Ahabu, anakumana nazo.​—1 Mafumu 18:3.

18. Kodi n’chiyani chinathandiza Obadiya kukhala wolambira Yehova wapadera kwambiri?

18 Mosakayika, Obadiya anali wosamala ndi wochenjera polambira Yehova. Koma sanagonje. Ndipotu, lemba la 1 Mafumu 18:3, limatiuza kuti: ‘Obadiya anaopa ndithu Yehova.’ Inde, kuopa Mulungu kwa Obadiya kunali kwapadera kwambiri. Chifukwa choopa Mulungu, Obadiya anali wolimba mtima kwambiri, ndipo zimenezi zinaonekera kwambiri nthawi imene Yezebeli anali atangopha kumene aneneri a Yehova.

19. Kodi Obadiya anachita chiyani chimene chinasonyeza kulimba mtima kwake?

19 Timawerenga kuti: “Pamene Yezebeli anapulula aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri zana limodzi, nawabisa makumi asanuasanu m’phanga, nawadyetsa mkate ndi madzi.” (1 Mafumu 18:4) Monga momwe mukuonera, kudyetsa anthu zana limodzi mwachinsinsi inali ntchito yoopsa kwambiri. Obadiya sanafunikire chabe kupewa Ahabu ndi Yezebeli kuti asamugwire koma anafunikiranso kupewa kudziwika ndi aneneri onyenga 850 omwe nthawi zambiri ankabwera ku nyumba ya mfumu. Kusiyapo zimenezi, panalinso olambira onyenga ambiri osiyanasiyana m’Israyeli, omwe mosakayikira akanakonda kuulula Obadiya kuti mfumu ndi mkazi wake awakonde. Koma ngakhale panali olambira mafano onsewa, Obadiya molimba mtima anasamalira zosowa za aneneri a Yehova. Kuopa Mulungu kumathandizadi kuti munthu akhale wolimba mtima.

20. Kodi kuopa Mulungu kunamuthandiza motani Obadiya, ndipo chitsanzo chake chimakuthandizani motani inuyo?

20 Popeza kuti Obadiya anali wolimba mtima chifukwa choopa Mulungu, mwachionekere anatetezedwa ndi Yehova kwa adani ake. Lemba la Miyambo 29:25, limati: “Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.” Obadiya anali munthu wamba; iye ankaopa kugwidwa ndi kuphedwa, monga momwe tikanachitira. (1 Mafumu 18:7-9, 12) Koma kuopa Mulungu kunam’thandiza kukhala wolimba mtima moti anathetsa mantha oopa munthu omwe angakhale anali nawo. Obadiya n’chitsanzo chabwino kwambiri kwa tonsefe, makamaka omwe amalambira Yehova mwa kuika ufulu wawo kapena ngakhale moyo wawo pangozi. (Mateyu 24:9) Tiyeni tonse tiyesetse kutumikira Yehova mwa “kum’chitira ulemu ndi mantha.”​—Ahebri 12:28.

21. Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

21 Chikhulupiriro ndiponso kuopa Mulungu si makhalidwe okhawa amene amathandiza kukhala wolimba mtima. Chikondi nachonso chingatithandize koposa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.” (2 Timoteo 1:7) Mu nkhani yotsatira tidzaona mmene chikondi chingatithandizire kutumikira Yehova molimba mtima m’masiku otsiriza owawitsawa.​—2 Timoteo 3:1.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Ameneyu si mneneri Obadiya.

Kodi Mungayankhe?

• Kodi n’chiyani chinathandiza Yoswa ndi Kalebi kukhala olimba mtima?

• Kodi chikhulupiriro chenicheni chimafuna chiyani?

• N’chifukwa chiyani Enoke analibe mantha polengeza uthenga wa Mulungu wa chiweruzo?

• Kodi kuopa Mulungu kumathandiza motani kuti tikhale olimba mtima?

[Mafunso]

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Yehova analamula Yoswa kuti: “Khala wamphamvu, nulimbike mtima”

[Chithunzi patsamba 18]

Obadiya anasamalira ndi kuteteza aneneri a Mulungu

[Zithunzi patsamba 19]

Enoke analankhula mawu a Mulungu molimba mtima