Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungathe Kukhala ndi Moyo Wosatha

Mungathe Kukhala ndi Moyo Wosatha

Mungathe Kukhala ndi Moyo Wosatha

ANTHU m’matchalitchi ambiri padziko lonse lapansi amaganizira zodzakhala ndi moyo wosatha m’njira zosiyanasiyana. Inde, zoganiza zawo pankhaniyi zimasiyana mwina ndi mwina, malingana n’chipembedzo chimene iwowo ali, koma chiyembekezo chawo n’chofanana kwambiri. Onse amayembekeza kudzakhala moyo wosangalala, wokhala ndi zinthu zonse zofunikira komanso wopanda imfa. Mwinanso inuyo n’zimene mumafuna. Koma kodi zinatheka bwanji kuti zikhulupiriro zotere zifale chonchi? Ndipo kodi zidzathekadi kuti anthu akhale ndi moyo wosatha?

Malemba amasonyeza kuti pachiyambi, pamene Mulungu ankalenga mwamuna ndi mkazi woyamba, Iye anaika mumtima mwa anthufe chibadwa choti tizifuna kwambiri kukhala ndi moyo wosatha. Baibulo limati: “[Mulungu] waika zamuyaya m’mitima yawo.”​—Mlaliki 3:11.

Komabe kuti akwaniritse chilakolako chokhala ndi moyo wosathachi, anthu awiri oyambirirawo anayenera kumvera Mulungu pankhani yosankha zabwino ndi zoipa. Akanatero, Yehova akanawaona kuti n’ngoyenerera “kukhala ndi moyo nthawi zonse” m’malo amene anali atawakonzera, omwe anali munda wa Edene.​—Genesis 2:8; 3:22.

Kutaya Moyo Wosatha

Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anadzala m’mundamo “mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa,” ndipo analetsa Adamu ndi Hava kudya zipatso za mtengowo, n’kuwauza kuti ngati atatero adzafa. (Genesis 2:9, 17) Posadya zipatso za mtengowo, Adamu ndi Hava akanasonyeza kuti akumvera Mulungu. Komano kudya kukanasonyeza kuti iwo sakufuna kumvera Mulungu. Adamu ndi Hava sanamvere malangizo a Yehova ndipo anakhala ku mbali ya Satana, munthu wauzimu amene anali atapandukira Mulungu. Motero, Mulungu sanalakwe pogamula kuti Adamu ndi Hava sanali oyenerera kukhala ndi moyo wosatha.​—Genesis 3:1-6.

Mulungu anawauza kuti asankhe pakati pa moyo ndi imfa. Mapeto a kusamvera kwawo anali imfa ndi kusiyiratu kukhala ndi moyo. Sizikanatheka kuti Adamu ndi Hava kapena ana awo aliwonse apitirizebe kukhala ndi moyo pogwiritsa ntchito mankhwala enaake a mphamvu zapadera kapena pokhala ndi mzimu wosafa. *

Ana onse a Adamu anavutika chifukwa cha kupanduka kwake. Mtumwi Paulo ananena zotsatirapo zake. Iye anati: “Monga uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”​—Aroma 5:12.

Kupezanso Moyo Wosatha

Mtumwi Paulo anayerekezera ana a Adamu ndi akapolo a m’nthawi imeneyo. Chifukwa choti analowa uchimo, ana a Adamu ndi Hava anabadwa ali “akapolo a uchimo” wosathawika, woti adzafa nawo basi. (Aroma 5:12; 6:16, 17) Unali wosathawika pakanapanda njira youthetsera mwalamulo imene Yehova anakonza, kotero kuti agulire ufulu akapolo amenewa. Paulo analongosola kuti: “Chifukwa chake, monga mwa kulakwa kumodzi [kwa Adamu] kutsutsa kunafikira anthu onse; chomwechonso mwa chilungamitso chimodzi chilungamo cha moyo chinafikira anthu onse.” “Chilungamitso” chimenecho chinachititsa Yesu kupereka nsembe moyo wake wangwiro kuti ukhale “chiwombolo m’malo mwa onse.” Yehova anaona kuti dipoli lingathe kuwombola anthu ku “chiweruzo” cha “uchimo.”​—Aroma 5:16, [NW], 18, 19; 1 Timoteo 2:5, 6.

Ichi n’chifukwa chake asayansi sangapeze chinsinsi cha moyo wosatha mwa kufufuza maselo a anthu. Chinsinsi cha moyo wosatha sichili mmenemo ayi. Baibulo limati chimene chinachititsa kuti anthu azifa ndi nkhani yokhudza khalidwe ndiponso lamulo, osati maselo ayi. Moteronso, njira yothandiza kuti adzakhalenso ndi moyo wosatha, yomwe ndi nsembe ya dipo ya Yesu, n’njokhudza lamulo. Nsembe ya dipo imasonyezanso kulungama kwa Mulungu ndi chifundo chake. Komano kodi ndani amene adzapindule ndi dipo n’kudzalandira moyo wosatha?

Mphatso ya Moyo Wosafa

Yehova Mulungu wakhalako “kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha.” Ali ndi moyo wosafa. (Salmo 90:2) Munthu woyamba amene Yehova anam’patsa mphatso ya moyo wosafa anali Yesu Kristu. Mtumwi Paulo analongosola kuti: “Kristu anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siichitanso ufumu pa iye.” (Aroma 6:9) Inde, poyerekezera Yesu woukitsidwa ndi olamulira a padziko pano, Paulo anati Yesu yekha ndi amene ali ndi moyo wosafa. Yesu “akhala Iye nthawi yosatha.” Moyo wake ndi “wosawonongeka.”​—Ahebri 7:15-17, 23-25; 1 Timoteo 6:15, 16.

Si Yesu yekha amene analandira mphatso yotereyi. Kuukitsidwa kwa Akristu odzozedwa ndi mzimu omwe anasankhidwa kukalamulira monga mafumu mu ulemerero wa kumwamba n’kofanana ndi kuukitsidwa kwa Yesu. (Aroma 6:5) Mtumwi Yohane anasonyeza kuti mwayi umenewu unaperekedwa kwa anthu 144,000. (Chivumbulutso 14:1) Nawonso amapatsidwa moyo wosafa. Paulo ananena izi pankhani ya kuuka kwa anthu amenewa: “Thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu . . . Lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika. Pakuti chovunda ichi chiyenera kuvala chosafa.” Imfa ilibe mphamvu iliyonse pa anthu oukitsidwa pa kuuka kumeneku.​—1 Akorinto 15:50-53; Chivumbulutso 20:6.

Vumbulutso la Mulungu limeneli n’lodabwitsa kwambiri. Ngakhale kuti angelo ndi anthu auzimu, iwonso sanalengedwe ndi moyo wosafa. Timadziwa zimenezi chifukwa choti angelo amene anatsatira Satana popandukira Mulungu adzawonongedwa. (Mateyu 25:41) Koma anthu amene adzalamulire pamodzi ndi Yesu mphatso yawo ndi ya moyo wosafa, kutsimikizira kuti Yehova sakayikira ngakhale pang’ono za kukhulupirika kwawo.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti pa anthu mabiliyoni ambirimbiri amene akhalako chilengedwereni dziko, pali anthu 144,000 okha amene adzakhale ndi moyo wosatha? Ayi. Tiyeni tione chifukwa chake?

Moyo Wosatha M’Paradaiso Padziko Lapansi

Buku la m’Baibulo la Chivumbulutso limapereka chithunzithunzi chokongola cha anthu osawerengeka amene adzapatsidwe moyo wosatha padziko lapansi m’paradaiso. Pagululi padzakhalanso anthu amene anafa koma anaukitsidwa n’kupatsidwanso moyo wathanzi ndiponso wamphamvu. (Chivumbulutso 7:9; 20:12, 13; 21:3, 4) Iwowa akupatsidwa “mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati klustalo, wotuluka ku mpando wachifumu wa Mulungu.” M’mphepete mwa mtsinjewo muli “mtengo wa moyo . . . ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nawo amitundu.” Mwakukoma mtima kwake, Yehova Mulungu akuitanira anthu kuti: “Wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.”​—Chivumbulutso 22:1, 2, 17.

Mitengo ndi madzi amenewa sikuti ndi mankhwala enaake opatsa moyo wosatha kapena akasupe opatsa unyamata omwe anthu ena ofufuza mankhwala otalikitsira moyo ndiponso anthu ena oyenda maulendo aatali pofufuza malo atsopano ankafunafuna. M’malo mwake mitengo ndi madziwa akuimira mphatso za Mulungu kudzera mwa Yesu Kristu, zothandiza anthu kupezanso moyo wangwiro umene anali nawo pachiyambi.

Mulungu sanasinthe cholinga chake chopereka moyo wosatha padziko lapansi kwa anthu omvera. Yehova adzakwaniritsa cholinga chimenecho chifukwa choti n’ngokhulupirika. Lemba la Salmo 37:29 limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Lonjezo limeneli limalimbikitsa ifeyo pamodzi ndi anthu amene apatsidwa mwayi wa moyo wosafa kumwamba, kunena kuti: “Ntchito zanu n’zazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu n’zolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha. Ndani adzakhala wosawopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera.”​—Chivumbulutso 15:3, 4.

Kodi inuyo mumalakalaka mphatso yamtengo wapatali ya moyo wosafa? Ngati n’choncho muyenera kukhulupirika ndiponso kumvera ‘Mfumu ya nthawi zosatha.’ Muyenera kuphunzira za Yehova ndiponso za munthu amene moyo wosatha unakhala wotheka kudzera mwa iyeyo. Munthuyu ndi Yesu Kristu. Anthu onse amene akufuna kutsatira mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino adzapatsidwa mphatso ya “moyo wosatha.”​—Yohane 17:3.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Kuti mumve zambiri pankhani ya zimene zimachitika munthu akafa, onani mutu 6 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lomwe limafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 5]

Anthu Anayamba Kale Kufunafuna Moyo Wautali

Nkhani ya Gilgamesh, yomwe ndi nthano yotchuka ya ku Mesopotamia, akuti mwina inachitika m’zaka za m’ma 1000 B.C.E., ndipo imalongosola zimene munthu wotchuka ameneyu anachita pofunafuna njira yokhalira ndi thanzi launyamata kwa moyo wosatha. Anthu akale a ku Igupto ankaumitsa mitembo ya anthu akufa chifukwa chokhulupirira kuti mzimu sufa, motero udzabwereranso m’thupilo m’tsogolo. Moti m’manda ena ku Igupto ankaikamo zinthu zonse zimene akufa angakafune m’moyo umene ankaganiza kuti adzakhala nawo pambuyo pa imfa.

Zikuoneka kuti pakati pa anthu ofufuza mankhwala otalikitsira moyo ku China, zokhulupirira kuti thupi silifa zinayamba kale mwina cha m’ma 700 B.C.E. Ndipo kukhulupirira kuti n’zotheka kuchita zimenezi pogwiritsira ntchito mankhwala amphamvu zapadera kunayamba m’ma 300 B.C.E. Ofufuza oterewa a ku Ulaya ndi ku Arabia, m’zaka za m’ma 500 mpaka m’ma 1500 anayesa kupeza njira zawo zopangira mankhwala otalikitsira moyo. Ena mwa mankhwalawo ankasanganizamo poizoni wa mtundu wosiyanasiyana. Motitu n’zotheka kuti anthu ambiri anadzipha poyesa mankhwala ofuna kutalikitsira moyowa.

Panthawi ina kunkamvekanso nkhani zambiri zonena kuti kuli kasupe wopatsa unyamata, yemwe ankanena kuti ali ndi madzi oti munthu akamwa ankakhala ndi thanzi labwino kwambiri.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 7]

Kodi Moyo Wosatha Udzakhala Wosasangalatsa?

Anthu ena amanena kuti moyo wosatha udzakhala wosasangalatsa, chifukwa “nthawi yake izidzangothera n’kuchita zosangalatsa” mobwerezabwereza mpaka kutopa nazo. Mwina anthu amenewa amaganiza kuti moyo wosatha udzakhala wofanana ndi moyo wa anthu enaake masiku ano, womwe ambiri amaona kuti n’ngosasangalatsa ndiponso n’ngosapindulitsa. Komatu, Mulungu walonjeza kuti m’Paradaiso amene iye adzabweretsenso, anthu ‘adzakondwera nawo mtendere wochuluka.’ (Salmo 37:11) Moyo umenewu udzapatsa anthu mwayi wodziwa za chilengedwe cha Yehova ndi kukhala ndi nthawi yophunzira chilichonse kapena zonse zokhudza luso, maphunziro, ndiponso ntchito zosangalatsa zimene panopo timangozilakalaka.

Dr. Aubrey de Grey, katswiri wa sayansi ya zachibadwa wa ku Cambridge University, yemwe akufufuza njira yotalikitsira moyo wa anthu, anati: “Anthu amene ali ophunzira ndithu ndipo ali ndi nthawi yogwiritsira ntchito maphunziro awowo safika poona kuti moyo sukusangalatsa masiku ano ndipo saganiza kuti nthawi inayake adzasowa zinthu zatsopano zochita.” Komabe Mawu ouziridwa a Mulungu amati, ‘palibe munthu adzathe kulondola ntchito zimene Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.’​—Mlaliki 3:11.