Yehova Anandithandiza Kupirira Mavuto pa Moyo Wanga
Mbiri ya Moyo Wanga
Yehova Anandithandiza Kupirira Mavuto pa Moyo Wanga
YOSIMBIDWA NDI DALE IRWIN
“ANA ACHITA KUKWANA EYITI! CHIFUKWA AWONJEZAPO ANAYI AMAPASA.” Uwu unali mutu wa nkhani m’nyuzipepala ina ya m’dziko lathu. Nkhaniyo inali yolengeza kubadwa kwa ana anayi amapasa m’banja lathu lomwe linali kale ndi ana anayi aakazi. Ndili mnyamata, sindinkaganiza zokwatira ndipo ndinalibiretu maganizo okhala ndi ana. Koma tsopano ndinali ndi ana eyiti!
NDINABADWA mu 1934 m’tauni ya Mareeba, ku Australia. Ndinali chitsirizira m’banja la ana atatu. Kenaka banja lathu linasamukira ku Brisbane, komwe mayi anayamba kuphunzitsa Sande sukulu kutchalitchi chinachake cha Methodist.
Kumayambiriro kwa m’ma 1938, nyuzipepala za m’dziko lathuli zinalemba nkhani yakuti Joseph F. Rutherford, wochokera ku likulu la Mboni za Yehova padziko lonse angathe kudzamuletsa kulowa m’dziko la Australia. Wamboni wina atafika pakhomo pathu, mayi anam’funsa kuti, “Kodi wawalakwira chiyani munthu ameneyu?” Wamboniyo anayankha kuti: “Kodi Yesu sananene kuti anthu adzavutitsa otsatira ake?” Kenaka mayi analandira kabuku kakuti Cure, kamene kanafotokoza mfundo zambiri zosonyeza mmene chipembedzo choona chimasiyanirana ndi chipembedzo chonyenga. * Bukuli linawakhudza mtima kwambiri mayi, moti Lamlungu lotsatira anayamba kutitenga anafe kumisonkhano ya Mboni za Yehova. Poyamba bambo anga analetsa zimenezi kwambiri, koma nthawi zina ankalemba mafunso a m’Baibulo kuti mayi akapereke kwa mmodzi wa abale. Kenaka, mbaleyo ankalemba yankho la m’Malemba la mafunsowo kuti mayi akapatse bambo.
Tsiku lina Lamlungu bambo anga anapita nafe
kumsonkhano, ndipo anatero pofuna kukauza Amboniwo kuti ziphunzitso zawo siziwafika pamtima. Koma atalankhula ndi woyang’anira woyendayenda amene anali kuyendera mpingowo panthawiyo, bambo anasintha maganizo awo moti mpaka analola kuti nyumba yathu izigwiritsidwa ntchito monga malo ochitirapo phunziro la Baibulo mlungu ndi mlungu, ndipo paphunziroli pamabwera anthu achidwi a m’dera lakwathu.Mu September 1938, makolo anga anabatizidwa. Ineyo ndi abale anga onse tinabatizidwa mu December 1941 pamsonkhano wa dziko lathu lonselo womwe unachitikira ku Hargreave Park mumzinda wa Sydney, ku New South Wales. Panthawiyi ndinali ndi zaka seveni. Kenaka, ndinayamba kulowa m’munda ndi makolo anga nthawi zonse. Masiku amenewo, Mboni zinkayenda nyumba ndi nyumba zitatenga magalamafoni a m’manja n’kumaikamo nkhani za m’Baibulo kuti eninyumba amvetsere.
Wamboni wina amene sindimuiwala ndi Bert Horton. Iyeyu anali ndi galimoto yamkuza mawu yomwe inali ndi sipika yaikulu padenga pake. Zinali zosangalatsa kwambiri kugwira ntchito ndi Bert, makamaka kwa mnyamata wamng’ono ngati ineyo. Mwachitsanzo, nthawi zambiri poulutsa nkhani ya m’Baibulo titaimitsa galimoto pa dera lokwera, tinkaona galimoto ya polisi ikulowera kumene tinaima. Bert ankazimitsa galamafoniyo mwamsanga, n’kuyendetsa galimotoyo kupita nayo kutali n’kukaiimitsa pa dera linanso lokwera. Akatero amaika nkhani ina mu galamafoniyo. Bert ndi abale ena okhulupirika ndiponso olimba mtima ngati iyeyo anandiphunzitsa zinthu zambiri zokhudza kudalira Yehova ndi kulimba mtima.—Mateyu 10:16.
Ndili ndi zaka 12, nthawi zambiri ndinkalalikira ndekha ndikaweruka kusukulu. Panthawi ina ndinakumana ndi banja la a Adshead. Patapita nthawi, mayi ndi bambo a m’banjalo, ana awo eyiti, ndi zidzukulu zawo zambiri zinaphunzira choonadi. Ndimathokoza Yehova chifukwa cholola kamnyamata kakang’ono ngati ineyo, kuuza banja labwino limeneli choonadi cha m’Baibulo.—Mateyu 21:16.
Mwayi Wotumikira Ndili Wamng’ono
Ndili ndi zaka 18, ndinakhala mpainiya wanthawi zonse ndipo ananditumiza ku Maitland, New South Wales. Mu 1956, anandiitana kukatumikira ku ofesi ya nthambi ya Australia, mumzinda wa Sydney. Pafupifupi anthu 7 pa anthu 20 ogwira ntchito panthambiyi, anali odzozedwa, okhala ndi chiyembekezo chodzalamulira ndi Kristu mu Ufumu wa kumwamba. Unali mwayi waukulu kwambiri kwa ine kugwira ntchito ndi anthu amenewa.—Luka 12:32; Chivumbulutso 1:6; 5:10.
Cholinga changa choti ndikhale wosakwatira chinatha pamene ndinakumana ndi Judy Helberg, mlongo wokongola yemwe ankachita upainiya, ndipo anali ataitanidwa kuti adzatumikire kwa kanthawi pa ofesi ya nthambi kudzandithandiza pa ntchito inayake yaikulu. Ine ndi Judy tinakondana, ndipo tinakwatirana patatha zaka ziwiri. Kenaka tinayamba ntchito ya utumiki wadera, yomwe inali ntchito yofunika kumayendera mpingo umodzi wa Mboni za Yehova mlungu uliwonse, kukalimbikitsa abale.
Mu 1960, Judy anabereka mwana wathu woyamba wamkazi, dzina lake Kim. Masiku ano, ukakhala ndi mwana chonchi nthawi zambiri umasiya ntchito ya dera n’kukakhazikika. Koma tinadabwa kwambiri atatiuza kuti tipitirizebe kuyendera mipingo. Titapemphera kwambiri, tinavomera ndipo pa miyezi seveni yotsatira, Kim anayenda nafe limodzi mtunda wa makilomita 13,000, pabasi, ndege, ndi sitima yapamtunda potumikira mipingo imene inali patalipatali m’chigawo cha Queensland ndi Northern Territory. Panthawiyi tinalibe galimoto.
Nthawi zonse tinkakhala m’nyumba za abale ndi alongo. Chifukwa cha nyengo yotentha ya m’derali, masiku amenewo zipinda zogona zambiri zinkakhala ndi makatani m’malo mwa zitseko, ndipo zimenezi zinkatiika pampanipani kwambiri Kim akamalira usiku. Patapita nthawi, zinafika poti sitikanatha kukwanitsa udindo wosamalira mwana n’kumachitanso ntchito yathu. Motero tinakhazikika ku Brisbane, ndipo ndinayamba ntchito yolemba zikwangwani. Patatha zaka ziwiri chibadwireni Kim, tinakhala ndi mwana wamkazi winanso, dzina lake Petina.
Kupirira Imfa
Mu 1972, ana athu ali ndi zaka 10 ndiponso 12, mkazi wanga Judy anamwalira ndi matenda otupa ziwalo zam’kati otchedwa Hodgkin. Imfa imeneyi inali yopweteka mosaneneka kwa banja langa. Komabe, pamatenda a Judy ndiponso pa imfa yake, Yehova anatitonthoza kudzera m’Mawu ake, mzimu wake, ndiponso abale auzimu. Tinalimbikitsidwanso ndi magazini ya Nsanja ya Olonda imene tinalandira zovutazi zitangochitika. Inali ndi nkhani yonena za kupirira mavuto pa moyo wathu, kuphatikizapo imfa, ndipo inasonyeza mmene ziyeso zingatithandizire kukhala ndi makhalidwe auzimu monga kupirira, chikhulupiriro, ndi kusunga umphumphu. *—Yakobo 1:2-4.
Judy atamwalira, chikondi cha pakati pa ine ndi ana angawo chinakula kwambiri. Koma kunena zoona, zinali zovuta kuchita ndekha udindo wa bambo ndi wa mayi. Koma ana anga awiri aakaziwo anali ana abwino kwambiri moti ntchitoyo siinandivute kwambiri.
Ndinakwatiranso Ndipo Banja Lathu Linakula
Patapita nthawi, ndinakwatiranso. Mkazi wanga wachiwiri Mary, anali wofanana ndi ine m’njira zambiri. Nayenso mwamuna wake anamwalira ndi matenda a Hodgkin. Nayenso anali ndi ana awiri aakazi, omwe mayina awo anali Colleen ndi Jennifer. Colleen anali mwana kwa Petina ndi zaka zitatu. Tsopano banja lathu linali ndi atsikana anayi, a zaka 14, 12, 9, ndi 7.
Ine ndi Mary tinagwirizana zoti kumayambiriro tizilangiza ana amene tinabereka tokha mpaka ana enawo atadzafika poti angathe kumvera malangizo a mayi kapena bambo wopeza. Awirifenso, monga mwamuna ndi mkazi, tinali ndi malamulo awiri aakulu. Loyamba linali lakuti tikasiyana maganizo sitinkatsutsana pamaso pa anawo, ndipo lachiwiri linali lakuti, mogwirizana ndi mfundo ya m’Baibulo ya pa Aefeso 4:26, tinkakambirana mpaka kuthetsa nkhaniyo, ngakhale zitatenga nthawi yaitali bwanji.
N’zodabwitsa kuti tonsefe tinazolowera mwamsanga kwambiri moyo wa m’banja lopeza, komabe zinatitengera nthawi kuti tiiwaleko za imfa zija. Mwachitsanzo, Lolemba lililonse usiku, Mary ankalira. Tikamaliza phunziro lathu la banja, atsikanawo akapita kogona, Mary ankalephera kudzigwira ndipo ankayamba kulira.
Mary ankafuna kuti tikhale ndi mwana wathuwathu. Koma n’zomvetsa chisoni kuti anapita padera. Ndiyeno Mary atakhalanso ndi pakati, sitinkadziwa kuti tiona zodabwitsa. Atamuunika kuchipatala anapeza kuti mimba yake siinali ya mwana mmodzi ayi, koma ana anayi! Zinandivuta kukhulupirira zimenezi. Sindinamvetse kuti posachedwa, munthu wa zaka 47 ngati ine, ndikhala ndi ana eyiti. Ana anayiwo anabadwa m’njira ya opaleshoni pa February 14, 1982, ali ndi miyezi eyiti. Anabadwa m’ndondomeko yotsatirayi:
Woyamba anali Clint, ndipo ankalemera makilogalamu 1.6, kenaka Cindy, 1.9; kenaka Jeremy, 1.4; ndi womaliza Danette, 1.7. Pa anawa panalibe aliyense wofanana ndi mnzake.Anawo atangobadwa, dokotala amene anathandiza mkazi wanga poberekapo anabwera kudzakhala pafupi nane.
Anandifunsa kuti: “Kodi ukuda nkhawa ndi zosamalira anawa?”
Ndiye ndinamuyankha kuti: “Inde, chifukwatu sindinachitepo zoterezi ayi.”
Mawu otsatira amene ananena anandidabwitsa ndi kundilimbikitsa kwambiri.
Iye anati: “Mpingo wako sungakusiye ayi. Uziti ukangoyetsemula pang’ono chabe, anthu azichita kukuunjirira kufuna kuti akuthandize!”
Patangotha miyezi iwiri, tinatuluka m’chipatalamo ndi ana athu anayi, onse ali athanzi. Izi zinatheka makamaka chifukwa cha luso la mzamba ameneyu, yemwe anali wodziwa bwino kwambiri ntchito yake, komanso chifukwa cha gulu lake la anthu om’thandiza.
Ntchito Yolera Ana Anayi a Mapasa
Pofuna kuchita zinthu mwadongosolo, ineyo ndi mkazi wanga Mary tinalemba ndandanda yochitira zinthu tsiku lililonse, masana ndi usiku. Ana anayi aakulupowo ankatithandiza kwambiri posamalira ana akhandawo. Ndipo mawu a dokotala aja analidi oona. “Kungoyetsemula” pang’ono chabe, anthu a kumpingo ankachita kuti unjiunji pofuna kutithandiza. Izi zisanachitike, mnzanga wina amene ndinadziwana naye kalekale, dzina lake John MacArthur, anapempha gulu la abale amene anali amisiri kuti litikulitsire nyumba yathu. Anawo atabadwa, gulu la alongo linkathandiza kuwasamalira. Kukoma mtima konseku kunkasonyeza chikondi chachikristu.—1 Yohane 3:18.
Makanda anayiwa anangokhala ngati ana a mpingo. Mpaka panopo, ana athuwa amaona abale ndi alongo ambiri amene anatithandiza, ngati mbali ya banja lathu. Mary ndi mkazi wabwino ndiponso mayi wabwino kwambiri yemwe wasamalira ana ake modzipereka zedi. Iye watsatiradi malangizo amene waphunzira m’Mawu a Mulungu ndi m’gulu lake. Palibe malangizo alionse oposa amenewa.—Salmo 1:2, 3; Mateyu 24:45.
Misonkhano yachikristu ndiponso ntchito yolalikira zinapitirizabe kukhala zinthu zofunika kwa ife mlungu ndi mlungu, ngakhale kuti kuchita zimenezi ndi ana akhanda anayi siinali nkhani yamasewera. Panthawiyi tinkaphunzira Baibulo ndi mabanja awiri, ndipo tinadalitsidwa chifukwa anthu anayi onsewa anakoma mtima moti ankadzaphunzirira kunyumba kwathu konko. Ngakhale kuti zimenezi zinatifewetsera zinthu, nthawi zina Mary ankakhala wotopa kwambiri moti ankangosinza m’kati mwa phunzirolo, kwinaku mwana akugona m’manja mwake. Patsogolo pake, mabanja awiri onsewo anadzakhala abale ndi alongo athu auzimu.
Kuwaphunzitsa Zauzimu Adakali Ana
Ineyo, mkazi wanga Mary, komanso ana athu aakulu aja, tinkatenga anawa tikamapita mu utumiki wa kumunda ndipo tinkatero anawo asanayambe n’komwe kuyenda. Atayamba kuyenda, ineyo ndi Mary tinkatenga ana awiri aliyense, ndipo sankavuta kuyenda nawo. Ndipotu tikakumana ndi eninyumba ansangala, anawa ndiwo ankakhala poyambira nkhani. Tsiku lina ndinakumana ndi munthu wina amene ananena kuti ngati pa tsiku limene munabadwa nyenyezi zinali zitayalana m’njira inayake kumwambaku, ndiye kuti zochitika zanu zizitsatira ndondomeko inayake. Sindinatsutsane naye, koma ndinangom’pempha kuti ndim’pezenso mawa lake m’mawa. Anavomera, ndipo ndinam’tengera ana anga anayi amapasa aja. Anayang’ana mosowa chonena kwinaku ndikuika anawo pamzere mogwirizana ndi mmene anabadwira. Kenaka tinayamba kucheza, ndipo tinakambirana za kusiyana kwa maonekedwe a anawo komanso zoti anawo anali osiyana kwambiri zochitika, ndipo
mfundo imeneyi inagonjetseratu mfundo yake ija. Iye anati: “Ayi, ndachita manyazi kuti ndinanena mfundo imeneyi kwa munthu ngati iweyo. Ndaona kuti m’pofunika kuti ndikafufuze kaye mokwanira.”Ana anayiwo atayamba kuyenda, sankafuna zoti tiziwalangira pamodzi akalakwitsa zinazake, motero tinkawalangiza pawokhapawokha. Komabe, anaphunzira kuti onse ayenera kutsatira malamulo omwewo. Kusukulu akawauza kuchita zinthu zosemphana ndi chikumbumtima chawo, onse ankakana mwamphamvu kuswa mfundo za m’Baibulo ndipo ankathandizana. Cindy ndiye anali kuwalankhulira. Posakhalitsa, anthu anadziwa kuti ana anayi amapasa si osewera nawo ayi.
Ana athu atakula n’kukhala atsikana, ineyo ndi Mary tinakumana ndi vuto limene limakhalapo polera ana a msinkhu umenewu kuti akhale okhulupirika kwa Yehova. Mwachidule, tingati ntchito imeneyi ikanativuta kwambiri tikanapanda kuthandizidwa mwachikondi ndi mpingo komanso ndi chakudya chauzimu cha mwanaalirenji chomwe tinali kulandira kuchokera ku mbali yooneka ya gulu la Yehova. Tinkayesetsa kuchita phunziro la Baibulo la banja nthawi zonse ndi kukambirana zinthu momasuka, ngakhale kuti nthawi zina kuchita zimenezi kunali kovuta. Komabe, khama lathu lapindula chifukwa choti panopo ana athu onse eyiti anasankha kutumikira Yehova.
Kupirira Mavuto Aukalamba
Kwa zaka zambiri m’mbuyomu, ndakhala ndi mwayi wotumikira m’njira zosiyanasiyana monga mkulu, woyang’anira mzinda, ndiponso woyang’anira dera wogwirizira. Ndatumikiraponso monga mmodzi wa anthu a mu Komiti Yolankhulana ndi Achipatala, omwe ntchito yawo ndiyo kuthandiza madokotala kuti athandize odwala a Mboni pakabuka nkhani yoika odwalawo magazi. Kwa zaka 34 ndakhalanso ndi mwayi wokhala munthu wovomerezeka mwalamulo kukwatitsa anthu. Ndachititsapo maukwati 350, kuphatikizapo maukwati sikisi a ana anga.
Ndimathokoza Yehova nthawi zonse chifukwa chothandizidwa mokhulupirika ndi Judy komanso panopo ndi Mary. (Miyambo 31:10, 30) Akaziwa anandichirikiza pantchito yanga monga mkulu, komanso anali zitsanzo zabwino muutumiki ndipo anathandiza kuphunzitsa makhalidwe auzimu mwakhama kwa ana athu.
Mu 1996, anandipeza ndi matenda okhudza ubongo amene amachititsa kuti manja anga azinjenjemera ndi kuti ndiziyenda mwapendapenda. Motero sindikanathanso kuchita ntchito yolemba zikwangwani ija. Komabe, ndimasangalala kwambiri potumikira Yehova, ngakhale kuti tsopano ndayamba kuchita zinthu mwapang’onopang’ono. Cholimbikitsa n’chakuti zimenezi zandithandiza kumvetsetsa anthu okalamba.
Ndikaganizira za moyo wanga, ndimathokoza Yehova kuti nthawi zonse wakhala akundithandiza ndiponso kuthandiza banja langa kukhala lachimwemwe pothana ndi mavuto athu ambirimbiri. (Yesaya 41:10) Ine ndi Mary, pamodzi ndi ana athu eyiti, timayamikiranso kwambiri kuti tili ndi banja labwino kwambiri lotichirikiza la abale ndi alongo auzimu. Onsewa atisonyeza chikondi m’njira zoti sitingathe kuzisimba.—Yohane 13:34, 35.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma tsopano anasiya kulisindikiza.
^ ndime 17 Onani Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya March 15, 1972, masamba 174 mpaka 180.
[Chithunzi patsamba 12]
Ndili ndi mayi anga, mkulu wanga Garth, ndi mchemwali wanga Dawn, titakonzeka kuyamba ulendo wopita ku msonkhano ku Sydney mu 1941
[Chithunzi patsamba 13]
Ndili ndi Judy ndi Kim ali mwana pamene ndinali mu ntchito ya dera ku Queensland
[Chithunzi patsamba 15]
Ana athu anayi amapasa atabadwa, ana athu anayi aakulu aja ndiponso anthu a mumpingo wathu anatithandiza mosaneneka