Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yembekezani Yehova Kuti Mukhale Olimba Mtima

Yembekezani Yehova Kuti Mukhale Olimba Mtima

Yembekezani Yehova Kuti Mukhale Olimba Mtima

“Yembekeza Yehova: limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.”​—SALMO 27:14.

1. Kodi n’chifukwa chiyani chiyembekezo n’chofunika, ndipo mawu amenewa agwiritsidwa ntchito motani m’Malemba?

CHIYEMBEKEZO chenicheni chili monga kuwala kwakukulu. Chimatithandiza kuti tisamangoona chabe mayesero omwe tili nawo komanso kuti tiyang’ane kutsogolo molimba mtima ndi mwachimwemwe. Yehova yekhayo ndi amene angatipatse chiyembekezo chodalirika, ndipo amachita zimenezi mwa kugwiritsa ntchito Mawu ake ouziridwa. (2 Timoteo 3:16) Ndipotu, mawu akuti “chiyembekezo,” “anayembekeza,” ndi “kuyembekezera” amapezeka m’Baibulo nthawi zambiri. Amatanthauza kudikirira mwachidwi ndi motsimikiza zinthu zabwino ndiponso cholinga cha zinthuzo. * Chiyembekezo chotero sindicho kungolakalaka zinazake, kumene kungakhale kopanda maziko kapena sikungakwaniritsidwe.

2. Kodi chiyembekezo chinam’thandiza bwanji Yesu pa moyo wake?

2 Pamene ankakumana ndi mayesero ndi mavuto, Yesu anayang’ana kupyola pa zimene zinkam’chitikira panthawiyo ndipo anayembekeza Yehova. “Chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira [mtengo wozunzirapo], nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” (Ahebri 12:2) Chifukwa choti Yesu ankaganizira kwambiri za mwayi woti asonyeze kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndiponso za kuyeretsa dzina la Lake, iye sanapatuke panjira yake yomvera Mulungu ngakhale anakumana ndi zinthu zotani.

3. Kodi chiyembekezo chimathandiza motani atumiki a Mulungu pamoyo wawo?

3 Mfumu Davide anatchula za kugwirizana kwa chiyembekezo ndi kulimba mtima. Iye anati: “Yembekeza Yehova: limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.” (Salmo 27:14) Ngati tikufuna kuti mtima wathu ukhale wolimba, tisalole chiyembekezo chathu kuzirala koma nthawi zonse chizikhala mu maganizo ndiponso mu mitima yathu. Zimenezi zidzatithandiza kutsanzira Yesu mwa kukhala olimba mtima ndi achangu pantchito imene analamula ophunzira ake kuchita. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Ndithudi, chiyembekezo chimatchulidwa limodzi ndi chikhulupiriro ndiponso chikondi monga khalidwe lofunika ndipo lokhalitsa limene atumiki a Mulungu amadziwika nalo pamoyo wawo.​—1 Akorinto 13:13.

Kodi Muli ndi Chiyembekezo Chochuluka?

4. Kodi Akristu odzozedwa limodzi ndi anzawo a “nkhosa zina” akuyembekezera chiyani mwachidwi?

4 Atumiki a Mulungu ali ndi tsogolo labwino kwambiri. Akristu odzozedwa amayembekezera mwachidwi kutumikira limodzi ndi Kristu kumwamba, pamene “nkhosa zina” zimayembekezera ‘kumasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu [apadziko lapansi].’ (Yohane 10:16; Aroma 8:19-21; Afilipi 3:20) “Ufulu wa ulemerero” umenewo umaphatikizapo kumasuka ku uchimo ndi zotsatirapo zake zoipa. Ndithudi, Yehova, Wopatsa “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro” adzapatsa anthu ake okhulupirika zabwino zokhazokha.​—Yakobo 1:17; Yesaya 25:8.

5. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale ndi chiyembekezo chochuluka?

5 Kodi chiyembekezo chachikristu chiyenera kutithandiza motani pamoyo wathu? Pa lemba la Aroma 15:13, timawerenga kuti: ‘Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m’kukhulupira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya mzimu woyera.’ Inde, chiyembekezo tingachiyerekezere, osati ndi kandulo yomwe ili mu mdima, koma ndi kuwala kwa dzuwa m’mawa, komwe kumathandiza munthu kukhala ndi mtendere, chimwemwe, cholinga, ndi kulimba mtima pamoyo wake. Onani kuti timakhala ndi chiyembekezo chochuluka tikakhulupirira Mawu olembedwa a Mulungu ndi kulandira mzimu wake woyera. Lemba la Aroma 15:4, limati: “Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.” Motero dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimasunga chiyembekezo changa kukhala chamoyo mwa kuphunzira bwino Baibulo, kuliwerenga tsiku ndi tsiku? Kodi ndimapempha mzimu wa Mulungu nthawi zambiri?’​—Luka 11:13.

6. Kodi tiyenera kupewa chiyani kuti chiyembekezo chathu chikhalebe chamoyo?

6 Yesu, Chitsanzo chathu, analimbikitsidwa ndi Mawu a Mulungu. Mwa kum’tsanzira kwambiri, timapewa kutopa ndi kuti moyo wathu usalefuke. (Ahebri 12:3) N’zomveka kunena kuti, ngati chiyembekezo chathu chimene Mulungu watipatsa chizirala mu maganizo ndi mu mtima wathu kapena tikayamba kuika kwambiri maganizo athu pa zinthu zina, mwina zinthu zakuthupi kapena zolinga za kudziko, tingayambe kugona mwauzimu. Pomaliza pake, tingamalephere kukhala olimba mtima ndiponso kusunga khalidwe lathu labwino. Tikakhala ndi maganizo otero, ‘chikhulupiriro chathu chingatayike.’ (1 Timoteo 1:19) Koma chiyembekezo chenicheni chimalimbitsa chikhulupiriro chathu.

Chiyembekezo N’chofunika pa Chikhulupiriro

7. Kodi chiyembekezo n’chofunika motani pa chikhulupiriro?

7 Baibulo limati: “Chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.” (Ahebri 11:1) Chotero, chiyembekezo n’chofunika kwambiri pa chikhulupiriro. Inde, zimayendera limodzi. Taganizirani za Abrahamu. Malinga ndi kuona kwa anthu, iye ndi mkazi wake, Sara, anali atadutsa kale msinkhu woti angakhale ndi mwana pamene Yehova anawalonjeza mwana. (Genesis 17:15-17) Kodi Abrahamu anachita motani? Ngakhale kuti analibe chiyembekezo, anakhulupirira atapatsidwa chiyembekezo kuti iye adzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu. (Aroma 4:18) Inde, chiyembekezo cha Abrahamu chopatsidwa ndi Mulungu chinathandiza kuti chikhulupiriro chake choti adzakhala ndi mwana chikhale ndi maziko olimba. Kenako, chikhulupiriro chake chinalimbitsa chiyembekezo chake. Ndipo Abrahamu ndi Sara analimba mtima kusiya nyumba yawo ndi achibale awo n’kukakhala moyo wawo wonse mu mahema m’dziko lachilendo.

8. Kodi kupirira mokhulupirika kumalimbitsa motani chiyembekezo?

8 Abrahamu anakhala ndi chiyembekezo cholimba mwa kumvera Yehova m’zonse, ngakhale pamene kuchita zimenezo kunali kovuta. (Genesis 22:2, 12) Mofananamo, mwa kumvera Yehova ndi kupirira mu utumiki wake, tingakhale ndi chidaliro choti adzatipatsa mphoto. Paulo analemba kuti: ‘Chipiriro’ chimabala ‘chivomerezo,’ ndipo chivomerezocho chimabala chiyembekezo, ‘ndipo chiyembekezocho sichigwiritsa mwala.’ (Aroma 5:4, 5, NW) N’chifukwa chake Paulo analembanso kuti: ‘Tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga ku chiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro.’ (Ahebri 6:11) Kukhala ndi maganizo abwino amenewa, ozikidwa pa unansi wabwino ndi Yehova, kungatithandize kukumana ndi mavuto alionse molimba mtima ndiponso mwachimwemwe.

“Kondwerani M’chiyembekezo”

9. Kodi tiyenera kuchita chiyani nthawi zonse chomwe chingatithandize ‘kukondwera m’chiyembekezo’?

9 Chiyembekezo chathu chopatsidwa ndi Mulungu sitingachiyerekezere ndi chinthu china chilichonse chomwe dziko lingatipatse. Lemba la Salmo 37:34 limati: “Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko: pakudulidwa oipa udzapenya.” Tili ndi zifukwa zabwino zokhalira ‘okondwera m’chiyembekezo.’ (Aroma 12:12) Koma kuti tichite zimenezi, tifunikira nthawi zonse kuganizira za chiyembekezo chathu. Kodi nthawi zonse mumaganizira za chiyembekezo chanu chopatsidwa ndi Mulungu? Kodi mumadziona muli m’Paradaiso, muli athanzi labwino, opanda nkhawa, limodzi ndi anthu amene mumawakonda, ndipo mukuchita ntchito zosangalatsa kwambiri? Kodi mumasinkhasinkha zithunzi zosonyeza Paradaiso zomwe zimapezeka m’mabuku athu? Kuganizira zimenezi nthawi zonse tingakuyerekezere ndi kupukuta galasi la pawindo limene munthu angaonerepo bwino zinthu. Ngati tinyalanyaza kupukuta galasilo, posapita nthawi fumbi lingatilepheretse kuona bwino zinthu zokongola. Ndiyeno tingayambe kuyang’ana zinthu zina. Tisalole zimenezo kutichitikira.

10. N’chifukwa chiyani tikamayang’ana mphoto timasonyeza kuti tili ndi unansi wabwino ndi Yehova?

10 N’zoona kuti chifukwa chachikulu chotumikira Yehova n’choti timamukonda. (Marko 12:30) Ngakhale zili choncho, tiyenera kuyang’ana mwachidwi pa mphoto. Ndipotu, Yehova amafuna kuti tichite zimenezi. Lemba la Ahebri 11:6, limati: “Wopanda chikhulupiriro sikutheka kum’kondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” N’chifukwa chiyani Yehova akufuna kuti tizimuona kuti ndi wobwezera mphoto? Chifukwa tikatero, timasonyeza kuti timadziwa bwino Atate wathu wakumwamba. Iye ndi wowolowa manja ndipo amakonda ana ake. Taganizirani mmene tikanakhalira osasangalala ndiponso otaya mtima mosavuta tikanakhala kuti tinalibe tsogolo ndi chiyembekezo.​—Yeremiya 29:11.

11. Kodi chiyembekezo chake chopatsidwa ndi Mulungu chinam’thandiza motani Mose kusankha bwino?

11 Chitsanzo chabwino kwambiri cha munthu amene anaikirapo mtima kwambiri pa chiyembekezo chake chopatsidwa ndi Mulungu anali Mose. Pokhala “mwana wake wa mwana wamkazi wa Farao,” Mose anali ndi mphamvu, moyo wapamwamba, ndi chuma cha dziko la Igupto zomwe akanagwiritsa ntchito. Kodi anasankha zinthu izi, kapena kutumikira Yehova? Molimba mtima Mose anasankha kutumikira Yehova. Chifukwa chiyani? Chifukwa ‘anapenyerera chobwezera cha mphoto.’ (Ahebri 11:24-26) Inde, Mose sanaone mopepuka chiyembekezo chimene Yehova anam’patsa.

12. N’chifukwa chiyani chiyembekezo chachikristu chili monga chisoti?

12 Mtumwi Paulo anayerekeza chiyembekezo ndi chisoti. Chisoti chathu chophiphiritsa chimateteza maganizo athu, chimatithandiza kusankha zinthu mwanzeru, kuika zinthu zofunika patsogolo, ndi kukhala okhulupirika. (1 Atesalonika 5:8) Kodi nthawi zonse mumavala chisoti chanu chophiphiritsa? Ngati n’choncho, ndiye kuti mofanana ndi Mose ndi Paulo, mudzaika chiyembekezo chanu osati pa “chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo.” N’zoona kuti kupewa zinthu zomwe anthu ambiri amakonda mwa kukana kuchita zinthu zokomera ife tokha, kumafuna kulimba mtima. Koma ndi bwino kutero. Ndipotu, n’kukonderanji zinthu zomwe sizingafanane ndi “moyo weniweniwo” umene anthu omwe amayembekeza ndi kukonda Yehova adzalandira?​—1 Timoteo 6:17, 19.

“Sindidzakusiya Konse”

13. Kodi n’chiyani chimene Yehova akulonjeza atumiki ake okhulupirika?

13 Anthu amene amaika chiyembekezo chawo pa dongosolo lino la zinthu amakhala ndi nkhawa akamaganiza za zinthu zimene zikuchitika pamene dzikoli likupitiriza kukumana ndi “zowawa” zambiri. (Mateyu 24:8) Koma amene amayembekeza Yehova alibe mantha ngati amenewo. Iwo adzapitirizabe kukhala “osatekeseka, nadzakhala phe osaopa zoipa.” (Miyambo 1:33) Popeza saika chiyembekezo chawo pa dongosolo lino, iwo mosangalala amalabadira uphungu wa Paulo wakuti: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.”​—Ahebri 13:5.

14. N’chifukwa chiyani Akristu safunikira kuda nkhawa kwambiri ndi zosowa za pamoyo wawo?

14 Mawu akuti “konse,” “ndithu” akutsimikizira kuti Mulungu adzatisamalira. Yesu nayenso anatitsimikizira kuti Mulungu adzatisamalira mwachikondi. Iye anati: “Muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo [zofunika pa moyo] zidzawonjezedwa kwa inu. Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha.” (Mateyu 6:33, 34) Yehova amadziwa kuti zimativuta kukhala achangu pochirikiza Ufumu wake ndipo panthawi imodzimodzi kukwaniritsa udindo wathu wonse woti tipeze zofunika pa moyo. Chotero tiyeni tidalire kwambiri mphamvu zake ndi mtima wake wofuna kusamalira zosowa zathu.​—Mateyu 6:25-32; 11:28-30.

15. Kodi Akristu amakhala bwanji ndi ‘diso la kumodzi’?

15 Timasonyeza kuti timadalira Yehova ngati tili ndi ‘diso la kumodzi.’ (Mateyu 6:22, 23) Munthu wa diso la kumodzi amakhala woona mtima, wa zolinga zabwino ndipo sakhala waumbombo kapena kulakalaka zinthu zapamwamba. Kukhala ndi diso la kumodzi sikutanthauza kuti tikhale pa umphawi wadzaoneni kapena tisaikirepo mtima posamalira maudindo athu achikristu. Koma kumatanthauza kukhala wodziletsa pamene tikuika utumiki wa Yehova patsogolo.​—2 Timoteo 1:7.

16. N’chifukwa chiyani chikhulupiriro ndi kulimba mtima n’zofunika kuti tikhale ndi diso la kumodzi?

16 Kukhala ndi diso la kumodzi kumafuna chikhulupiriro ndi kulimba mtima. Mwachitsanzo, ngati okulembani ntchito amakukakamizani nthawi zonse kugwira ntchito panthawi ya misonkhano yachikristu, kodi molimba mtima mudzachitabe zinthu zanu zauzimu zomwe mufunika kuchita? Ngati munthu akukayikira zoti Yehova adzakwaniritsa lonjezo Lake losamalira atumiki Ake, ndiye kuti Satana adzangowonjezera ziyeso zake ndipo munthu wotero angasiye kupezeka ngakhale pamisonkhano. Inde, ngati tilibe chikhulupiriro, tingalole Satana kutilamulira moti iye angamatiuze zochita m’malo moti Yehova atero. Imeneyo ingakhale ngozi yaikulu kwambiri.​—2 Akorinto 13:5.

‘Yembekezani Yehova’

17. Kodi anthu omwe amakhulupirira Yehova amadalitsidwa motani ngakhale panopo?

17 Malemba mobwerezabwereza amasonyeza kuti omwe amayembekeza ndi kukhulupirira Yehova salephera. (Miyambo 3:5, 6; Yeremiya 17:7) N’zoona kuti nthawi zina ayenera kukhala okhutira ndi zochepa zomwe ali nazo, koma amaona kuti zinthu zomwe adzimana n’zochepa poyerekeza ndi madalitso omwe awasungira m’tsogolo. Motero, iwo amasonyeza kuti ‘amayembekeza Yehova’ ndipo amakhulupirira kuti pomaliza pake iye adzapatsa anthu ake okhulupirika zinthu zonse zabwino zimene mtima wawo umafuna. (Salmo 37:4, 34) Chotero, ndi osangalala kwambiri ngakhale panopo. “Chiyembekezo cha olungama ndicho chimwemwe; koma chidikiro cha oipa chidzawonongeka.”​—Miyambo 10:28.

18, 19. (a) Kodi ndi mawu olimbikitsa otani omwe Yehova akutiuza? (b) Kodi tingaike motani Yehova ‘pa dzanja lathu lamanja’?

18 Mwana wamng’ono akamayenda ndi bambo ake atamugwira dzanja, amamva kukhala wotetezeka kwambiri. Ifenso timamva chimodzimodzi tikamayenda ndi Atate wathu wa kumwamba. Yehova anati kwa Israyeli: “Usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; . . . inde ndidzakuthangata. . . . Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.”​—Yesaya 41:10, 13.

19 Kugwira dzanja la munthu kwa Yehova kumasonyezadi chikondi! Davide analemba kuti: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse: popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.” (Salmo 16:8) Kodi tingaike motani Yehova ‘pa dzanja lathu lamanja’? Timachita zimenezi m’njira ziwiri. Yoyamba, timalola Mawu ake kutitsogolera pamoyo wathu wonse; ndipo yachiwiri, timayang’ana pa mphoto ya ulemerero imene Yehova waika patsogolo pathu. Wamasalmo Asafu anaimba kuti: “Ndikhala ndi Inu chikhalire: mwandigwira dzanja langa la manja. Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu, ndipo mutatero, mudzandilandira mu ulemerero.” (Salmo 73:23, 24) Chifukwa cha mawu olimbikitsa amenewa tingayang’ane kutsogolo molimba mtima.

“Chiwomboledwe Chanu Chayandikira”

20, 21. Kodi amene ayembekeza Yehova adzakhala ndi tsogolo lotani?

20 Tsiku lililonse likamapita, timafunika kuchita changu kuti tiike Yehova pa dzanja lathu la manja. Posachedwapa, dziko la Satana lidzakumana ndi chisautso chimene silinakumanepo nacho, ndipo zipembedzo zonyenga zidzakhala zoyamba kuwonongedwa. (Mateyu 24:21) Anthu opanda chikhulupiriro adzakhala ndi mantha. Koma panthawi yovuta imeneyi, atumiki a Yehova olimba mtima adzakondwera m’chiyembekezo. Yesu anati: “Poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.”​—Luka 21:28.

21 Chotero tiyeni tikondwere m’chiyembekezo chathu chopatsidwa ndi Mulungu ndipo tisanyengedwe kapena kuyesedwa ndi machenjera a Satana. Panthawi imodzimodzi, tiyeni tichite khama kukhala ndi chikhulupiriro, chikondi ndi kuopa Mulungu. Tikachita zimenezi, tidzakhala olimba mtima ndipo tidzamvera Yehova kaya zinthu zikhale zotani ndiponso tidzakaniza Mdyerekezi. (Yakobo 4:7, 8) Inde, “limbikani ndipo Iye adzalimbitsa mtima wanu, inu nonse akuyembekeza Yehova.”​—Salmo 31:24.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Ngakhale kuti m’Malemba Achigiriki Achikristu mawu akuti “chiyembekezo” nthawi zambiri amatanthauza mphoto yakumwamba ya Akristu odzozedwa, m’nkhani ino tikambirana mawuwa mmene anthu ambiri amawadziwira.

Kodi Mungayankhe?

• Kodi chiyembekezo chomwe Yesu anali nacho chinam’thandiza bwanji kuti akhale wolimba mtima?

• Kodi chikhulupiriro ndi chiyembekezo n’zogwirizana motani?

• Kodi chiyembekezo ndi chikhulupiriro zingathandize motani Mkristu kukhala wolimba mtima poika zinthu zofunika patsogolo m’moyo?

• N’chifukwa chiyani anthu omwe ‘amayembekeza Yehova’ amayang’ana kutsogolo molimba mtima?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 28]

Kaya ndife ana kapena akulu, kodi timadziona tili m’Paradaiso?