Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tingam’dziwedi mulungu?

Kodi Tingam’dziwedi mulungu?

Kodi Tingam’dziwedi mulungu?

“Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe . . . Mulungu woona yekha.”​—Yohane 17:3.

“HA! KUYA kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa [zinthu, NW] kwake kwa Mulungu!” Anatero mtumwi Paulo, ndipo anapitiriza kuti: “Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake n’zosalondoleka!” (Aroma 11:33) Kuchokera pa mawu amenewa, kodi tinganene kuti n’zosatheka kuti munthu akhale wodziwa zinthu ndi wanzeru ngati Mulungu, kapena kuti n’zosatheka kum’dziwa Mulungu ndiponso zolinga zake?

Akatswiri ena oganizira kwambiri nkhani za zipembedzo, amayankha kuti inde. Ponena za maganizo amenewa, The Encyclopedia of Religion imati: “Mulungu n’ngosayerekezereka. . . . Mulungu sangapatsidwe dzina kapena kufotokozedwa. Dzina lililonse kapena kafotokozedwe kalikonse kali ndi malire, ndipo Mulungu . . . alibe malire. . . . Sangadziwike, chifukwa sitingathe kum’dziwa.” *

Mogwirizana ndi magazini ya Newsweek, mabungwe ambiri omwe si achipembedzo amatsatira “maganizo atsopano” omwe kwenikweni ndi akuti “pali mfundo imodzi yokha yoona, ndipo mfundo yake n’njakuti palibe choonadi.”

Komabe, anthu ambiri amafuna kudziwa cholinga cha moyo, koma sanapeze mayankho ake. Amawawidwa mtima kuona mavuto osaneneka a umphawi, matenda ndiponso chiwawa. Amatha kukhumudwa kwambiri akaona kusinthasintha kumene kumachitika pamoyo. Amalakalaka atadziwa chifukwa chake zinthu zimenezi zimachitika, koma ngati sakupeza mayankho, amangoganiza kuti nkhani zimenezi zilibe mayankho. Motero, anthu ambiri otere achoka m’magulu a zipembedzo ndipo ngati akukhulupirirabe kuti Mulungu aliko, iwo akufunafuna njira yoti am’fikire okha Mulunguyo.

Zimene Baibulo Limanena

Anthu amene amakhulupirira Baibulo ndi kuvomereza kuti Yesu Kristu ndi Wolankhulira wa Mulungu, ayenera kukhala ndi chidwi chofuna kudziwa zimene Baibulo limanena. Mwina mukukumbukira kuti Yesu ananenapo za njira ziwiri, ‘njira yotakata, yomuka nayo kukuwonongeka’ ndi ‘njira yochepetsetsa, yomuka nayo kumoyo.’ Anafotokoza mmene tingadziwire anthu amene akuyenda m’njira zonse ziwirizi kuti: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.” Kodi zipatso zake n’zotani? Tingazidziwe mwa zochita zawo, osati mwa zonena zawo. Yesu ananena momveka bwino kuti: “Siyense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.” Kungonena kuti ndimakhulupirira Mulungu sikokwanira. Tiyenera kuchita chifuniro cha Mulungu. N’zosatheka kuchita chifuniro cha Mulungu tisanadziwe molondola kuti chifuniro chakecho n’chotani.​—Mateyu 7:13-23.

Yesu ananena momveka bwino kuti n’zotheka kuti anthu am’dziwe Mulungu. Iye anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Pokhapokha ngati tachita khama, tingapeze nzeru ndiponso tingadziwe zinthu zimene Mulungu amadziwitsa anthu. Mulungu adzapereka mphatso ya moyo wosatha kwa anthu amene amachita zimenezo. Choncho, kufunafuna nzeru ndi kudziwa zinthu zimenezi, n’kofunikadi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Maganizo otere amapezekanso m’miyambo ya zipembedzo za Kum’mawa za Chihindu, Chitao, ndi Chibuda.

[Chithunzi patsamba 4]

Yesu anati njira yopita nayo ku moyo n’njochepetsetsa