Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zochita Zanu Zimatsimikizira Kuti Muli ndi Chikhulupiriro?

Kodi Zochita Zanu Zimatsimikizira Kuti Muli ndi Chikhulupiriro?

Kodi Zochita Zanu Zimatsimikizira Kuti Muli ndi Chikhulupiriro?

“Chikhulupiriro, chikapanda kukhala nazo ntchito, chikhala chakufa m’kati mwakemo.”​—YAKOBO 2:17.

1. N’chifukwa chiyani Akristu oyambirira ankafunika kuonetsetsa kuti chikhulupiriro ndi ntchito zawo ndi zabwino?

ZOCHITA za Akristu oyambirira, zinatsimikizira kuti iwo anali ndi chikhulupiriro. Wophunzira Yakobo analimbikitsa Akristu onse kuti: “Khalani akuchita mawu, osati akumva okha.” Ndipo anawonjezera kuti: “Monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.” (Yakobo 1:22; 2:26) Patatha zaka pafupifupi 35 chilembereni mawu amenewa, Akristu ambiri anali kupitiriza kutsimikizira kuti ali ndi chikhulupiriro mwa kuchita ntchito zabwino. Koma n’zomvetsa chisoni kuti ena sankatero. Yesu anayamikira mpingo wa ku Smurna; koma anauza Akristu ambiri a mu mpingo wa ku Sarde kuti: “Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.”​—Chivumbulutso 2:8-11; 3:1.

2. Kodi Akristu ayenera kumadzifunsa mafunso otani pankhani ya chikhulupiriro chawo?

2 Motero, Yesu analimbikitsa Akristu a ku Sarde, ndiponso onse owerenga mawu ake, kuti apitirize kukonda choonadi chachikristu monga momwe ankachitira poyamba ndiponso kuti akhale maso mwauzimu. (Chivumbulutso 3:2, 3) Aliyense wa ife angadzifunse kuti: ‘Bwanji za zochita zanga? Kodi zochita zanga zonse, ngakhale pazinthu zimene sizikhudzana mwachindunji ndi ntchito yolalikira kapena misonkhano ya mpingo, zimasonyezeratu kuti ndikuyesetsa kutsimikizira kuti ndili ndi chikhulupiriro?’ (Luka 16:10) Pankhaniyi, pali zambiri zimene zimachitika m’moyo mwathu zomwe tingathe kuziganizira, koma tiyeni tikambirane chinthu chimodzi chokha, chomwe ndi mapwando, kuphatikizapo mapwando amene nthawi zambiri amachitika pambuyo pa ukwati wachikristu.

Mapwando Ang’onoang’ono

3. Kodi Baibulo limati chiyani pankhani yopezeka pa phwando?

3 Ambirife timasangalala kuitanidwa ku phwando la Akristu anzathu. Yehova ndi ‘Mulungu wachisangalalo,’ yemwe amafuna kuti atumiki ake azisangalala. (1 Timoteo 1:11, NW) Iye anachititsa Solomo kulemba mfundo yoona iyi m’Baibulo, yakuti: “Ndinatama kusekaseka, pakuti munthu alibe kanthu kabwino pansi pano, koma kudya ndi kumwa, ndi kusekera; ndi kuti zimenezi zikhalebe naye m’vuto lake masiku onse a moyo wake.” (Mlaliki 3:1, 4, 13; 8:15) Kusangalala kumeneku kungachitike pa chakudya cha pabanja kapena pa phwando laling’ono la olambira oona.​—Yobu 1:4, 5, 18; Luka 10:38-42; 14:12-14.

4. Kodi munthu amene akukonza phwando ayenera kuganizira za chiyani?

4 Ngati mukukonza phwando loterolo, muyenera kuganizira mofatsa zimene mukukonzazo, ngakhale pa chakudya kapena kucheza komwe mukukonza zodzaitana okhulupirira anzanu ochepa chabe. (Aroma 12:13) Muyenera kudzaonetsetsa kuti ‘zonse zikuchitika koyenera,’ motsogoleredwa ndi “nzeru yochokera kumwamba.” (1 Akorinto 14:40; Yakobo 3:17) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu. Khalani osakhumudwitsa.” (1 Akorinto 10:31, 32) Kodi n’zinthu zina ziti zimene mufunikira kuziganizira mosamala? Kuganizira zinthu zimenezo nthawi idakalipo, kungakuthandizeni kuonetsetsa kuti zochita zanu ndiponso za anthu oitanidwa kuphwandolo zidzasonyeze kuti mumachita zinthu zogwirizana ndi chikhulupiriro chanu.​—Aroma 12:2.

Kodi Phwandolo Lidzakhala Lotani?

5. N’chifukwa chiyani munthu akamakonza phwando ayenera kuganizira mosamala ngati akufuna kuti padzakhale mowa ndiponso nyimbo?

5 Anthu ambiri akamakonza phwando amafunika kuganizira bwino kuti paphwandopo padzakhale mowa kapena ayi. Kuti phwando likhale losangalatsa, sikuti pamachita kufunikira mowa ayi. Kumbukirani kuti Yesu anapatsa chakudya gulu lina lalikulu limene linabwera kwa iye. Anachulukitsa mkate ndi nsomba. Nkhaniyi sinena kuti anapanga vinyo mozizwitsa, ngakhale tikudziwa kuti iye akanatha kuchita zimenezo. (Mateyu 14:14-21) Mukasankha kuti paphwando padzakhale mowa, onetsetsani kuti pasadzakhale mowa wambiri, komanso padzakhale zakumwa zina zimene anthu angakonde kumwa m’malo mwa mowawo. (1 Timoteo 3:2, 3, 8; 5:23; 1 Petro 4:3) Musapangitse munthu kukakamizika kumwa chakumwa chimene chingathe kumuluma “ngati njoka.” (Miyambo 23:29-32) Nanga bwanji za nyimbo? Ngati paphwando lanulo padzakhale nyimbo, mosakayikira mungasankhe nyimbo zake mosamala, poganizira kaimbidwe ka zida ndiponso mawu ake. (Akolose 3:8; Yakobo 1:21) Akristu ambiri aona kuti kuimba nyimbo za Ufumu za Kingdom Melodies kapenanso kuimbira limodzi pakamwa nyimbo zimenezi, kumachititsa kuti phwando likhale losangalatsa kwambiri. (Aefeso 5:19, 20) Ndipo, m’pofunikanso kuonetsetsa kuti sizinakwere kwambiri kuti zisasokoneze kucheza kapena zisasokoneze anthu oyandikana nawo nyumba.​—Mateyu 7:12.

6. Kodi munthu amene wakonza phwando angasonyeze motani kuti ndi munthu wachikhulupiriro pankhani yocheza kapena pazochita zina?

6 Paphwando, Akristu angathe kukambirana nkhani zosiyanasiyana, kuwerengerana nkhani mokweza, kapena kufotokozerana zinthu zochititsa chidwi zimene zawachitikira m’moyo. Anthu akayamba kukambirana nkhani zosayenera Akristu, munthu wokonza phwandolo angathe kuchita zinthu mosamala kuti anthuwo azikambirana nkhani zabwino. Ayeneranso kukhala maso kuti munthu wina asamangolankhula yekha, osapatsa anzake mpata. Akaona kuti zimenezi zayamba kuchitika, iye angathe kufotokoza maganizo ake mwanzeru, ndi kupereka mpata kwa enanso kuti alankhulepo. Angachite zimenezi, mwina mwa kupempha ana kuti nawonso alankhulepo kapena kuyambitsa nkhani imene anthu osiyanasiyana angalankhulepo. Ana ndi akulu omwe angasangalale ndi kucheza kotereku. Ngati, inuyo monga wokonza phwando, muchita zinthu mwanzeru ndi mosamala, ‘kufatsa kwanu kudzazindikiridwa’ ndi anthu omwe abwera paphwandopo. (Afilipi 4:5) Adzazindikira kuti ndinu munthu wachikhulupiriro, ndipo chikhulupirirocho chimakhudza mbali zonse za moyo wanu.

Ukwati ndi Phwando Lake

7. N’chifukwa chiyani m’pofunika kuganizira mosamala za kukonzekera ukwati ndi phwando lake?

7 Ukwati wachikristu ndi chimodzi mwa zinthu zapadera zosangalatsa kwambiri. Atumiki a Mulungu akale, kuphatikizapo Yesu ndi ophunzira ake, ankasangalala kukhala nawo pa chisangalalo choterocho, ndiponso pa phwando lake. (Genesis 29:21, 22; Yohane 2:1, 2) Koma masiku ano, pakhala pakuchitika zinthu zimene zasonyeza kuti pokonzekera phwando la ukwati, pamafunika kusamala kwambiri ngati munthu akufuna kuti phwando lotero lidzakhale labwino ndiponso logwirizana ndi mfundo zachikristu. Komabe, mapwando amenewa si achilendo ndipo amapatsa Akristu mwayi wosonyeza chikhulupiriro chawo.

8, 9. Kodi zochitika pa maukwati ambiri zimatsimikizira motani zimene timawerenga pa 1 Yohane 2:16, 17?

8 Anthu ambiri amene sadziwa ndiponso alibe ntchito ndi mfundo za Mulungu amaona kuti phwando la ukwati ndi nthawi yochita zinthu mopyola malire kapena yomwe anthu angaloledwe kuchita zinthu motero. M’magazini ina ya ku Ulaya, mkazi wina yemwe anali atangolowa kumene m’banja anafotokoza izi pankhani ya ukwati wake womwe anati unali waulemerero kwambiri. Anati: ‘Tinayenda pa ngolo ya akavalo anayi yomwe m’mbuyo mwake munali ngolo zina 12 za kavalo mmodzimmodzi ndiponso ngolo ina yaikulu, momwe munali bandi ikuimba nyimbo. Kenako tinadya chakudya chapamwamba kwambiri ndipo panali nyimbo zabwino kwambiri; zonse zinali zapamwamba kwambiri. Zimenezo n’zimene ndinkafuna, ndipo panalibenso munthu wondiposa.’

9 Ngakhale kuti kachitidwe ka zinthu kangasiyane malinga ndi malo, maganizo amenewa akungotsimikizira zimene mtumwi Yohane analemba, kuti: “Chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.” Kodi mungayembekezere Akristu okhwima maganizo kufuna kukhala ndi ukwati waulemerero kwambiri ndiponso phwando lopambanitsa? Ayi. M’malo mwake, pokonzekera ukwati wawo afunika kuganizira malangizo akuti “iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi zonse.”​—1 Yohane 2:16, 17.

10. (a) Kuti ukwati ukhale wabwino, n’chifukwa chiyani kukonzekera n’kofunika? (b) Kodi kusankha anthu oti aitanidwe kuyenera kuchitika motani?

10 Mwamuna ndi mkazi wachikristu afunika kuchita zinthu molingalira bwino, ndipo Baibulo lingathe kuwathandiza pamfundoyi. Ngakhale kuti tsiku la ukwati n’lapadera, iwo amadziwa kuti langokhala chiyambi cha moyo wabanja wa Akristu awiri omwe akuyembekezera moyo wosatha. Sayenera kukakamizika kuchita phwando lalikulu la ukwati. Akasankha kuchita phwando, ayenera kuganizira mtengo wake ndiponso mtundu wa phwandolo. (Luka 14:28) M’banja lawo lachikristu, mwamuna adzakhala mutu mogwirizana ndi Malemba. (1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:22, 23) Motero, mkwati ndiye amene ali ndi udindo waukulu pa phwando la ukwati. N’zoona kuti poganizira munthu amene adzakhale mkazi wakeyo, iye angakambirane naye nkhani monga ya anthu amene akufuna kuwaitana kapena anthu amene angakwanitse kuwaitana ku phwando la ukwatilo. Mwina sangakwanitse kapena sizingakhale bwino kuitana anzawo ndi achibale onse; motero ayenera kusankha zochita zina modzichepetsa. Mwamuna ndi mkaziyo ayenera kuzindikira kuti ngati satha kuitana ena mwa Akristu anzawo, iwo adzamvetsa zimenezo ndipo sadzakhumudwa.​—Mlaliki 7:9.

“Mkulu wa Phwando”

11. Kodi “mkulu wa phwando” angagwire ntchito yotani pa ukwati?

11 Ngati mwamuna ndi mkazi asankha kukhala ndi phwando lokondwerera ukwati wawo, kodi angatani pofuna kuonetsetsa kuti mwambowo udzakhale wopatsa ulemu? Kwa zaka zambiri tsopano, Mboni za Yehova zaona kufunika kokhala ndi munthu amene anatchulidwa m’nkhani ya phwando lomwe Yesu anachita nawo ku Kana. Paphwandolo panali “mkulu wa phwando,” amene mosakayikira ankalambirira limodzi mokhulupirika ndi eni ukwatiwo. (Yohane 2:8-10) Mofanana ndi zimenezi, mkwati wanzeru angapereke ntchito yofunika imeneyi kwa mbale wachikristu wokhwima maganizo. Atadziwa zofuna ndi zokonda za mkwati, mkulu wa phwandoyo angaonetsetse kuti zonsezo zikutsatiridwa, pokonzekera ndi pochita phwandolo.

12. Kodi mkwati ayenera kuganizira chiyani pankhani yokhala ndi mowa pa ukwati?

12 Mogwirizana ndi zomwe taona m’ndime 5, amuna ndi akazi ena amasankha kuti asakhale ndi mowa paphwando la ukwati wawo poopa kuti anthu angathe kusokoneza mwambowo ngati atamwa kwambiri. (Aroma 13:13; 1 Akorinto 5:11) Koma ngati akonza zodzakhala ndi mowa, mkwati ayenera kuonetsetsa kuti anthu asadzapatsidwe mowa wambiri, komanso kuti paphwandopo pasadzakhale mowa wambiri. Ku ukwati wa ku Kana komwe Yesu anapita, kunali vinyo ndipo iye anapanga vinyo wina wabwino kwambiri. N’zochititsa chidwi kumva zimene mkulu wa phwandolo ananena, kuti: “Munthu aliyense amayamba kuika vinyo wokoma; ndipo anthu atamwatu [“ataledzera,” NW], pamenepo wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino.” (Yohane 2:10) Zoona zake n’zakuti Yesu sanalimbikitse anthu kuledzera, chifukwa ankadana nako. (Luka 12:45, 46) Podabwa ndi vinyo wabwino uja, mkuluyo anasonyeza kuti anaonapo nthawi zina pamene anthu obwera ku ukwati analedzera. (Machitidwe 2:15; 1 Atesalonika 5:7) Motero, mkwati ndiponso Mkristu wodalirika amene wasankhidwa kukhala mkulu wa phwando, ayenera kuonetsetsa kuti onse ofika pa phwandolo akutsatira malangizo omveka bwino awa, akuti: “Musaledzere naye vinyo, mmene muli chitayiko.”​—Aefeso 5:18; Miyambo 20:1; Hoseya 4:11.

13. Kodi mwamuna ndi mkazi ayenera kuganizira chiyani ngati akukonza zoti adzakhale ndi nyimbo paphwando la ukwati, ndipo n’chifukwa chiyani?

13 Mofanana ndi phwando lina lililonse, ngati padzakhale nyimbo, m’pofunika kusamala kuti voliyumu yake isadzalepheretse anthu kumvana. Mbale wina yemwe ndi mkulu mumpingo wachikristu anati: “Kukamada, kucheza kukayamba kukoma kwambiri kapena kuvina kukayamba, nthawi zina voliyumu ya nyimbo imakwera. Nyimbo zimene poyamba zinali kumveka chapansipansi, zimatha kukhala zaphokoso, mpaka anthu osatha kumvana. Phwando la ukwati limapereka mpata wabwino kwambiri wocheza. Zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri ngati nyimbo zingasokoneze mwayi umenewu!” Apanso, mkwati limodzi ndi mkulu wa phwando amafunika kuchita zinthu mwanzeru. Sayenera kusiyira abandi, kaya ndi olipidwa kapena ayi, kuti ndiwo asankhe mtundu wa nyimbo ndiponso voliyumu yake. Paulo analemba kuti: “Chilichonse mukachichita m’mawu kapena muntchito, chitani zonse m’dzina la Ambuye Yesu.” (Akolose 3:17) Anthu akabwerera kwawo pambuyo pa phwando (kapena madyerero) a ukwati ndi kukumbukira nyimbo za paphwandopo, kodi adzaona kuti mwamuna ndi mkaziyo achita chilichonse m’dzina la Yesu? Umu ndi mmene ziyenera kukhalira.

14. Kodi n’zinthu ziti zokhudzana ndi ukwati zimene zimakhala zosaiwalika?

14 Zoonadi, ukwati wokonzedwa bwino umakhala wosaiwalika. Adam ndi Edyta, omwe akhala m’banja zaka 30, anafotokozapo za ukwati wina kuti: “Zinkachita kuonekeratu kuti ndi mwambo wachikristu. Panali nyimbo zotamanda Yehova komanso zosangalatsa zina zabwino. Nyimbo ndi kuvina sizinali zofunika kwenikweni. Unali ukwati wabwino ndi wosangalatsa, ndipo chilichonse chinali chogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo.” Kunena zoona, pali zambiri zimene mkwati ndi mkwatibwi angachite pa ukwati wawo posonyeza kuti ndi anthu achikhulupiriro.

Mphatso za pa Ukwati

15. Kodi ndi uphungu wa m’Baibulo wotani womwe ungagwiritsidwe ntchito pankhani ya mphatso za pa ukwati?

15 M’mayiko ambiri mabwenzi ndiponso achibale amakonda kupereka mphatso kwa anthu amene akukwatirana. Ngati mukufuna kuchita zimenezi, kodi muyenera kukumbukira chiyani? Musaiwale mfundo ya mtumwi Yohane yonena za “matamandidwe a moyo.” Iye anagwirizanitsa kudzionetsera koteroko ndi ‘dziko lapansi limene likupita,’ osati ndi Akristu amene zochita zawo zimasonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro. (1 Yohane 2:16, 17) Malinga ndi mfundo youziridwa yomwe Yohane anatchula, kodi anthu omwe angokwatirana kumene ayenera kulengeza mayina a anthu amene apereka mphatso ndiponso mphatso zawo? Akristu a ku Makedoniya ndi ku Akaya anapereka chithandizo kwa abale awo ku Yerusalemu, koma palibe pamene pamasonyeza kuti mayina awo analengezedwa. (Aroma 15:26) Akristu ambiri amene apereka mphatso pa ukwati angakonde kuti anthu asadziwe mayina awo, m’malo mofuna kudzionetsera. Pamfundoyi, onani uphungu wa Yesu womwe uli pa Mateyu 6:1-4.

16. Kodi anthu omwe angokwatirana kumene angatani kuti asakhumudwitse anthu ena pankhani ya mphatso za pa ukwati?

16 Kudziwitsa anthu mayina a amene apereka mphatso kungalimbikitse mpikisano wofuna kupereka mphatso yabwino ndi yokwera mtengo kwambiri. Motero, Akristu anzeru omwe angokwatirana kumene salengeza mayina a anthu amene apereka mphatso. Kulengeza mayinawo kungachititse manyazi anthu ena amene mwina sanathe kupereka mphatso. (Agalatiya 5:26; 6:10) N’zoona kuti palibe cholakwika kuti mkwati ndi mkwatibwi adziwe amene wapereka mphatso inayake. Iwo angathe kudziwa zimenezo kudzera pa khadi labwino lomwe munthu waperekera limodzi ndi mphatsoyo, koma osati n’cholinga choti awerengere anthu ayi. Pogula, popereka, ndi polandira mphatso za ukwati, tonse timakhala ndi mwayi wotsimikizira ngakhale pankhani yaing’ono ngati imeneyi, kuti ndife achikhulupiriro chomwe chimakhudza zochita zathu. *

17. Kodi Akristu ayenera kukhala ndi cholinga chotani pankhani ya chikhulupiriro ndi ntchito zawo?

17 Kutsimikizira kuti tili ndi chikhulupiriro kumafuna zambiri kuwonjezera pa kukhala akhalidwe labwino, kupita ku misonkhano yachikristu, ndiponso kugwira nawo ntchito yolalikira. Tiyeni tonse tikhale ndi chikhulupiriro champhamvu chomwe chimakhudza zonse zimene timachita. Inde, tingasonyeze chikhulupiriro chathu, mwa ntchito ‘zochitidwa mokwanira,’ kuphatikizapo mbali zosiyanasiyana zokhudza moyo wathu zomwe takambirana m’nkhani ino.​—Chivumbulutso 3:2, NW.

18. Kodi mawu a pa Yohane 13:17 angagwire ntchito motani pankhani ya ukwati ndi phwando lachikristu?

18 Yesu atasonyeza ophunzira ake okhulupirika chitsanzo chabwino mwa kugwira ntchito yonyozeka yosambitsa mapazi awo, anati: “Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzichita.” (Yohane 13:4-17) Mwina kumadera omwe tikukhala masiku ano, kulibe mwambo wosambitsa mapazi a alendo panyumba pathu. Komabe monga momwe taonera m’nkhaniyi, nthawi zina timasonyeza chikhulupiriro chathu mwa kukhala achikondi, oganizira ena, kuphatikizapo pankhani zokhudza ukwati wachikristu kapena phwando lina lililonse. Tingachite zimenezi kaya tikukwatira, taitanidwa ku ukwati kapena phwando la ukwati wa Akristu omwe amasonyeza chikhulupiriro chawo mwa ntchito zawo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 16 Nkhani yotsatirayi yakuti, “Zomwe Mungachite Kuti Tsiku la Ukwati Wanu Likhale Losangalatsa ndi Lolemekezeka Kwambiri” yafotokoza mbali zina za ukwati ndiponso phwando lake.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi mungatsimikizire motani chikhulupiriro chanu

• pokonzekera phwando laling’ono?

• pokonzekera ukwati kapena phwando la ukwati?

• popereka kapena polandira mphatso za pa ukwati?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 24]

Ngakhale poitana anthu ochepa chabe, lolani “nzeru yochokera kumwamba” kuti ikutsogolereni