“N’chifukwa Chiyani Tili ndi Moyo?”
“N’chifukwa Chiyani Tili ndi Moyo?”
MUNTHU yemwe anapatapo mphoto ya Nobel, yemwenso anapulumuka nkhanza zoopsa za Anazi, Elie Wiesel, ananena kuti limeneli ndi “funso lofunika kwambiri limene munthu aliyense ayenera kuliganizira.” Lakuti chiyani? “N’chifukwa chiyani tili ndi moyo?”
Kodi munayamba mwaganizapo za funso limeneli? Ambiri atero, koma sapeza yankho lake. Pofuna kudziwa tanthauzo la moyo, katswiri wina wolemba mbiri wa ku Britain, Arnold Toynbee analemba kuti: “Cholinga chenicheni cha munthu ndicho kulemekeza Mulungu ndi kusangalala Naye kosatha.”
N’zochititsa chidwi kuti, zaka masauzande atatu apitawo, munthu wina amene ankadziwika chifukwa cha chidwi chake pa zochitika m’moyo, anali atadziwa kale yankho lofunika la funsoli. Mfumu yanzeru Solomo inati: “Mawu atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”—Mlaliki 12:13.
Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu ananenaponso mfundo yomweyi. Ali padziko lapansi pano, Yesu anachita zonse zomwe akanatha kuti alemekeze Atate wake wakumwamba. Kutumikira Mlengi wake kunachititsa Yesu kusangalala ndi moyo wake. Kunamuthandiza kwambiri, n’chifukwa chake ananena kuti: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine.”—Yohane 4:34.
Nanga kodi n’chifukwa chiyani tili ndi moyo? Monga Yesu, Solomo, ndi atumiki ena ambiri a Mulungu, tingakhale ndi moyo watanthauzo ndi wachimwemwe mwa kuchita chifuniro cha Mulungu. Kodi mukufuna kudziwa zambiri za mmene mungalambirire Mulungu “mumzimu ndi m’choonadi”? (Yohane 4:24) Mboni za Yehova za m’dera lanu zidzakhala zosangalala kukuthandizani kuyankha funso lakuti, “N’chifukwa chiyani tili ndi moyo?”