Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Daniel ndi Baji Yake ya Msonkhano

Daniel ndi Baji Yake ya Msonkhano

Daniel ndi Baji Yake ya Msonkhano

YESU anadzudzula atsogoleri a chipembedzo odzilungamitsa amene anakwiya ataona anyamata ang’onoang’ono akutamanda Mulungu poyera. Moyenerera, Yesu anawafunsa kuti: “Kodi simunawerenge zimenezi kuti, ‘M’kamwa mwa tiana ndi makanda oyamwa mwaikamo mawu otamanda’?”​—Mateyo 21:15, 16.

Nkhani ya mnyamata wa zaka sikisi dzina lake Daniel, amene amasonkhana mu mpingo wachinenero cha Chirasha ku Germany, ikupereka umboni woti achinyamata akutamandabe Yehova. Iye limodzi ndi mayi ake ndi mchemwali wake anapita ku msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova ku Duisburg. Aka kanali koyamba kuti iwo apite ku msonkhano waukulu chonchi. Chilichonse chinali chachilendo: kungoyambira kukhala ku hotela, kuona anthu ambiri ali pa msonkhano, kungokhala phee kwa masiku atatu, kuonerera ubatizo, ngakhalenso sewero limene. Ndipo Daniel anasonyeza khalidwe labwino kwambiri.

Daniel atabwerera kwawo msonkhanowo utatha, Lolemba anadzuka m’mamawa kuti azipita ku sukulu yamkaka. Koma pa jekete yake panali pakadali baji imene imasonyeza kuti anapita ku msonkhano. Mayi ake anamufotokozera kuti: “Msonkhano watha. Lero ukhoza kuchotsa bajiyo.” Koma Daniel anati: “Ndikufuna aliyense aone komwe ndinali ndiponso adziwe zomwe ndaphunzira.” Choncho tsiku lonse kumkaka kuja, anavala baji yake monyadira. Aphunzitsi ake atamufunsa za bajiyo, anawafotokozera za msonkhanowo.

Pochita zimenezi, Daniel anali kutsatira chitsanzo cha anyamata ndi atsikana ambiri amene akhala akutamanda Yehova poyera pa zaka zambiri m’mbuyo monsemu.