Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulemekeza Misonkhano Yathu Yopatulika

Kulemekeza Misonkhano Yathu Yopatulika

Kulemekeza Misonkhano Yathu Yopatulika

“Nawonso ndidzanka nawo ku phiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m’nyumba yanga yopemphereramo.”​—YESAYA 56:7.

1. Kodi tili ndi zifukwa ziti za m’Malemba zolemekezera moyenerera misonkhano yathu?

YEHOVA wasonkhanitsa anthu ake, Akhristu odzozedwa ndi anzawo, kuti amulambire pa ‘phiri lake lopatulika.’ Akuwasangalatsa ‘m’nyumba yake yopemphereramo,’ yomwe ndi kachisi wake wauzimu, kapena kuti “nyumba yopemphereramo mitundu yonse.” (Yesaya 56:7; Maliko 11:17) Zochitika zimenezi zikusonyeza kuti kulambira kwa Yehova n’koyera, kosadetsedwa, ndi kokwezeka. Mwa kulemekeza moyenerera misonkhano yathu yomwe timaphunzirako ndi kulambirako, timasonyeza kuti timaona zinthu zopatulika monga mmene Yehova amazionera.

2. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yehova ankaona kuti malo amene anawasankha kuti anthu azimulambirirako anali opatulika, ndipo Yesu anasonyeza bwanji kuti nayenso ankawaona motero?

2 Mu Isiraeli wakale, malo amene Yehova anasankha kuti anthu azimulambirirako anafunika kuonedwa kuti ndi opatulika. Chihema ndi ziwiya ndiponso zipangizo zake zinayenera kudzozedwa ndi kuyeretsedwa “kuti zikhale zopatulika ndithu.” (Eksodo 30:26-29) Zipinda ziwiri za chihemacho zinkatchedwa “Malo Oyera” ndi “Malo Oyera Kopambana.” (Aheberi 9:2, 3) Kenaka chihema chinadzalowedwa m’malo ndi kachisi wa ku Yerusalemu. Yerusalemu anali chimake cholambirira Yehova, motero ankatchedwa “mzinda woyera.” (Mateyo 27:53; Nehemiya 11:1) Panthawi ya utumiki wake wa padziko lapansi, Yesu nayenso analemekeza kachisi moyenerera. Anakwiya kwambiri chifukwa cha njira yachipongwe imene anthu ankagwiritsira ntchito malo a kachisi ngati ogulitsira malonda ndiponso ngati njira yachidule yodutsirapo.​—Maliko 11:15, 16.

3. Kodi ndi zochitika ziti zimene zikusonyeza kupatulika kwa misonkhano ya Aisiraeli?

3 Aisiraeli ankasonkhana nthawi ndi nthawi kuti alambire Yehova ndi kuti amvetsere Chilamulo chake chikuwerengedwa. Masiku ena a mapwando awo ankatchedwa misonkhano yopatulika, kusonyeza kuti misonkhanoyi inalidi yopatulika. (Levitiko 23:2, 3, 36, 37) Pa msonkhano wina waukulu m’masiku a Ezara ndi Nehemiya, Alevi “anadziwitsa anthu chilamulocho . . . Popeza anthu onse analira misozi pakumva mawu a chilamulo” Aleviwo “anatontholetsa anthu onse, ndi kuti, Khalani muli chete; pakuti lero ndi lopatulika.” Kenaka Aisiraeli anakondwerera phwando la misasa la masiku asanu ndi awiri ndi “chimwemwe chachikulu.” Komanso, “anawerenganso m’buku la chilamulo cha Mulungu tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lotsiriza. Nachita madyerero masiku asanu ndi awiri; ndi tsiku lachisanu ndi chitatu ndilo msonkhano woletsa, monga mwa malemba.” (Nehemiya 8:7-11, 17, 18) Zimenezi zinalidi zochitika zopatulika zofunika kuti anthu onse omwe analipo azimvetsera mwachidwi ndi kusonyeza ulemu.

Misonkhano Yathu Ndi Yopatulika

4, 5. Kodi pa misonkhano yathu pamachitika zinthu zotani zimene zimasonyeza kuti ndi yopatulika?

4 N’zoona kuti masiku ano Yehova alibe mzinda woyera weniweni pa dziko lapansi, wokhala ndi kachisi wapadera woperekedwa kuti anthu azimulambiriramo. Komabe, sitiyenera kuiwala kuti misonkhano yolambirira Yehova ndi yopatulika. Katatu pamlungu timakumana kuti tiwerenge ndi kuphunzira Malemba. Mawu a Yehova ‘amawerengedwa momveka’ ndipo mofanana ndi mu nthawi ya Nehemiya, ‘amatanthauziridwa.’ (Nehemiya 8:8) Misonkhano yathu yonse imayamba ndi kutha ndi pemphero, ndipo pa misonkhano yambiri timaimba nyimbo zotamanda Yehova. (Salmo 26:12) Misonkhano ya mpingo ilidi mbali ya kulambira kwathu ndipo imafunika kuti tizikhalapo ndi kumvetsera mwachidwi komanso kusonyeza ulemu.

5 Yehova amadalitsa anthu ake akamakumana kuti amulambire, aphunzire Mawu ake, ndi kusangalala ndi mayanjano abwino achikhristu. Nthawi yoti tikhale ndi msonkhano ikakwana, tingakhale otsimikiza kuti pa msonkhanopo ‘m’pamene Yehova amalamula kuti pakhale dalitso.’ (Salmo 133:1, 3) Timalandira nawo dalitso limenelo ngati tilipo ndipo tikumvetsera mwachidwi pulogalamu yauzimuyo. Kuwonjezera apo, Yesu anati: “Kulikonse kumene awiri kapena atatu asonkhana m’dzina langa, ine ndidzakhala pakati pawo.” Mawu amenewa akunena za akulu achikhristu amene akumana kuti athetse mavuto aakulu amene abuka pakati pa anthu awiri kapena angapo, koma mfundo yake imakhudzanso misonkhano yathu. (Mateyo 18:20) Ngati Khristu, mwa mzimu woyera, amakhalapo Akhristu akakumana m’dzina lake, kodi sitiyenera kuona kuti misonkhano yoteroyo ndi yopatulika?

6. Kodi tinganene chiyani za malo athu ochitira misonkhano, yaikulu ndi yaing’ono yomwe?

6 N’zoona kuti Yehova sakhala m’makachisi omangidwa ndi anthu. Komabe, Nyumba zathu za Ufumu ndi malo a kulambira koona. (Machitidwe 7:48; 17:24) Timakumana kumeneko kuti tiphunzire Mawu a Yehova, tipemphere kwa iye, ndi kumuimbira zitamando. N’chimodzimodzinso ndi Malo athu a Misonkhano. Malo akuluakulu amene timachita lendi kuti tichitireko misonkhano ikuluikulu, monga maholo ndi masitediyamu, amasanduka malo a kulambira panthawi imene tikuchitiramo misonkhano yathu yopatulika. Pa misonkhano yolambirira imeneyi, kaya yaing’ono kapena yaikulu, timafunika kusonyeza ulemu, ndipo tiyenera kusonyeza zimenezi m’maganizo ndi khalidwe lathu.

Njira Zolemekezera Misonkhano Yathu

7. Kodi tingalemekeze misonkhano yathu m’njira yoonekeratu iti?

7 Pali njira zoonekeratu zimene tingalemekezere misonkhano yathu. Njira imodzi ndiyo kuimba nawo nyimbo za Ufumu. Zambiri mwa nyimbo zimenezi zinalembedwa ngati mapemphero, choncho tiyenera kuziimba mwaulemu. Pogwira mawu Salmo 22, mtumwi Paulo analemba za Yesu kuti: “Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga, pakati pa mpingo ndidzakutamandani ndi nyimbo.” (Aheberi 2:12) Choncho tiziyesetsa kukhala pansi tcheyamani asanatchule nyimbo imene tiimbe kenaka n’kuimba moganizira kwambiri tanthauzo la mawu a nyimboyo. Kuimba kwathu kuzisonyeza mmene wamasalmo ankamvera, amene analemba kuti: “Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.” (Salmo 111:1) Zoonadi, kuimbira Yehova zitamando n’chifukwa chimodzi chabwino kwambiri choti tizifikira mwamsanga pa misonkhano yathu n’kukhalapo mpaka pamapeto.

8. Kodi ndi chitsanzo chiti cha m’Baibulo chimene chikusonyeza kuti mapemphero a pamisonkhano yathu amafunika kuti tiziwalemekeza pomvetsera mwachidwi ndi kusonyeza ulemu?

8 Chinthu china chimene chimalemeretsa mwauzimu misonkhano yathu yonse ndicho pemphero lochokera pansi pa mtima limene limaperekedwa m’malo mwa anthu onse osonkhana. Panthawi inayake, Akhristu oyambirira a ku Yerusalemu anasonkhana ndipo “onse pamodzi anakweza mawu awo kwa Mulungu” m’pemphero lochokera pansi pa mtima. Chifukwa chochita zimenezi, anapitiriza “kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima,” ngakhale anali kuzunzidwa. (Machitidwe 4:24-31) Kodi tikuganiza kuti nthawi imeneyo alipo amene anayamba kuganiza zina pempherolo lili m’kati? Ayi, anapemphera “onse pamodzi.” Mapemphero amene amapempheredwa pa misonkhano yathu amasonyeza mmene onse opezekapo akumvera. N’ngofunika kuti tiziwalemekeza pomvetsera mwachidwi ndi kusonyeza ulemu.

9. Kodi tingalemekeze bwanji misonkhano yathu yopatulika mwa kavalidwe ndi khalidwe lathu?

9 Chinanso, tingasonyeze kuti timalemekeza kwambiri kupatulika kwa misonkhano yathu m’njira imene timavalira. Kaonekedwe kathu, kaya zovala zathu ndi sitayilo yathu ya tsitsi, zingathandizire kwambiri kulemekeza misonkhano yathu. Mtumwi Paulo anatilangiza kuti: “Ndimafuna kuti kulikonse amuna apitirize kupemphera, kukweza manja awo okhulupirika m’mwamba popanda mkwiyo ndi kutsutsana. Mofananamo, ndimafunanso kuti akazi azidzikongoletsa mwa kuvala moyenera, mwaulemu ndi mwanzeru, osati mwa masitayilo a malukidwe a tsitsi, golide, ngale, kapena zovala zamtengo wapatali, koma moyenera akazi amene amati amalemekeza Mulungu.” (1 Timoteyo 2:8-10) Tikapita ku misonkhano ikuluikulu yochitikira m’masitediyamu osatseka pamwamba, kavalidwe kathu kakhoza kukhala kogwirizana ndi nyengo komabe kolemekezeka. Komanso, ngati tikulemekeza msonkhanowo sitingadye chakudya kapena kutafuna chingamu nkhani zili m’kati. Kavalidwe ndiponso khalidwe loyenera pa misonkhano yathu zimalemekeza Yehova Mulungu, kulambira kwake, ndi olambira anzathu.

Khalidwe Loyenera pa Nyumba ya Mulungu

10. Kodi mtumwi Paulo anasonyeza bwanji kuti pa misonkhano yathu yachikhristu pamafunika khalidwe labwino kwambiri?

10 M’buku la 1 Akorinto, chaputala 14, timapezamo malangizo anzeru a mtumwi Paulo a mmene misonkhano yachikhristu iyenera kuchitikira. Anamaliza n’kunena kuti: “Zinthu zonse zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.” (1 Akorinto 14:40) Misonkhano yathu ndi mbali yofunika ya ntchito za mpingo wachikhristu, ndipo imafunika kuti anthu amene ali pamenepo azisonyeza khalidwe loyenera nyumba ya Yehova.

11, 12. (a) Kodi n’chiyani chimene chiyenera kutsindikidwa m’maganizo mwa ana amene amabwera ku misonkhano yathu? (b) Kodi ana anganene za chikhulupiriro chawo m’njira yoyenera iti pa misonkhano yathu?

11 Makamaka ana ayenera kuphunzitsidwa khalidwe loyenera pa misonkhano yathu. Makolo achikhristu ayenera kufotokozera ana awo kuti ku Nyumba ya Ufumu ndiponso ku malo ochitira Phunziro la Buku la Mpingo si kosewerera. Ndi malo amene timalambirira Yehova ndi kuphunzirako Mawu ake. Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Samalira phazi lako popita ku nyumba ya Mulungu; [ndipo pakhale] kuyandikira kumvera.” (Mlaliki 5:1) Mose anaphunzitsa Aisiraeli kuti asonkhanitse akulu ndi “ana.” Anati: ‘Sonkhanitsani anthu . . . kuti amve, ndi kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kuchita mawu onse a chilamulo ichi; ndi kuti ana awo osadziwa amve, naphunzire kuopa Yehova.’​—Deuteronomo 31:12, 13.

12 Chimodzimodzinso masiku ano, ana amapita ku misonkhano ndi makolo awo makamaka kuti akamve ndi kuphunzira. Akayamba kutsatira zimene zikukambidwa n’kumvetsa mfundo zoyambirira za choonadi cha m’Baibulo, ana akhozanso ‘kulengeza poyera’ chikhulupiriro chawo mwa kutenga nawo mbali popereka mayankho achidule. (Aroma 10:10) Mwana wamng’ono angayambe n’kunena mawu ochepa poyankha funso lomwe walimvetsa. Poyamba, angafunikire kuwerenga yankholo, koma m’kupita kwa nthawi, angathe kuyankha mosachita kuwerenga. Zimenezi n’zothandiza ndi zosangalatsa kwa mwanayo, ndiponso zimasangalatsa achikulire amene akumva mwanayo akufotokoza chikhulupiriro chake kuchokera mumtima. Mwachidziwikire, makolo amapereka chitsanzo chabwino ngati iwowo paokha amayankha pa misonkhano. Ngati zingatheke, ndi bwino kuti ana akhale ndi Baibulo, nyimbo, ndi buku kapena magazini awoawo amene akuphunziridwa. Ayenera kuphunzira kulemekeza mabuku amenewa. Zonsezi zimatsindika m’maganizo a anawo kuti misonkhano yathu ndi yopatulika.

13. Kodi timalakalaka chiyani kwa anthu obwera pa misonkhano yathu kwa nthawi yoyamba?

13 Komabe, sitikufuna kuti misonkhano yathu izifanana ndi mapemphero a matchalitchi a Chikhristu. Mapemphero amenewa amakhala ongochita mwamwambo kuti anthuwo aoneke ngati opembedza kwambiri, kapena amakhala aphokoso ngati madansi. Timafuna kuti misonkhano ya ku Nyumba za Ufumu izikhala yosangalatsa ndipo anthu azikhala omasuka, koma osafika pokhala ngati malo achisangalalo. Timakumana n’cholinga choti tilambire Yehova, choncho misonkhano yathu nthawi zonse iyenera kukhala yolemekezeka. Timalakalaka kuti anthu obwera pa misonkhanoyi kwa nthawi yoyamba akamvera nkhani zokambidwa kumeneko ndi kuona khalidwe lathu ndi la ana athu, azinena kuti: “Zoonadi Mulungu ali pakati panu.”​—1 Akorinto 14:25.

Mbali Yosatha ya Kulambira Kwathu

14, 15. (a) Kodi tingapewe bwanji ‘kunyalanyaza nyumba ya Mulungu wathu’? (b) Kodi lemba la Yesaya 66:23 likukwaniritsidwa motani?

14 Monga tanenera kale, Yehova akusonkhanitsa anthu ake n’kuwasangalatsa m’kati mwa ‘nyumba yake yopempherera,’ yomwe ndi kachisi wake wauzimu. (Yesaya 56:7) Munthu wokhulupirika Nehemiya anakumbutsa Ayuda anzake kuti azilemekeza kachisi weniweni mwa kupereka ndalama zawo kuti zizithandiza pa kachisiyo. Iye anati: “Tisasiye (“tisanyalanyaze,” NW) nyumba ya Mulungu wathu.” (Nehemiya 10:39) Komanso, tisamanyalanyaze pempho la Yehova loti timulambire m’kati mwa ‘nyumba yake yopempherera.’

15 Posonyeza kufunika kosonkhana nthawi zonse polambira, Yesaya ananeneratu kuti: “Kudzakhala kuti kuyambira pa mwezi wokhala kufikira ku unzake, ndi kuyambira pa Sabata lina kufikira ku linzake, anthu onse adzafika kudzapembedzera pamaso pa Ine, ati Yehova.” (Yesaya 66:23) Zimenezi zikuchitika masiku ano. Nthawi zonse, mlungu uliwonse ndi mwezi uliwonse, Akhristu odzipereka amasonkhana kuti alambire Yehova. Mwa zina, amachita zimenezi mwa kupezeka pa misonkhano yachikhristu ndi kuchita nawo utumiki wolalikira. Kodi ndinu mmodzi wa anthu amene nthawi zonse ‘amafika kudzapembedza pamaso pa Yehova’?

16. N’chifukwa chiyani kupezeka pa misonkhano nthawi zonse kuyenera kukhala mbali yosatha ya moyo wathu panopa?

16 Lemba la Yesaya 66:23 lidzakwaniritsidwa mokwanira m’dziko latsopano limene Yehova walonjezedwa. Panthawi imeneyo, “anthu onse” mlungu ndi mlungu, ndiponso mwezi ndi mwezi, “adzafika kudzapembedzera” kapena kuti kudzalambira, Yehova, ndipo adzatero kwa umuyaya wonse. Popeza kusonkhana pamodzi kuti tilambire Yehova kudzakhala mbali yosatha ya moyo wathu wauzimu m’dongosolo latsopano la zinthu, kodi sitiyenera kuonetsetsa kuti kupezeka pa misonkhano yathu yopatulika kukhale mbali yosatha ya moyo wathu panopa?

17. N’chifukwa chiyani misonkhano yathu ili yofunika “makamaka pamene [tikuona] kuti tsikulo likuyandikira”?

17 Pamene mapeto akuyandikira, tiyenera kutsimikiza kuposa kale lonse kupezeka pa misonkhano yathu yachikhristu yolambirira. Polemekeza kupatulika kwa misonkhano yathu, sitilola kuti ntchito, homuweki ya ku sukulu, kapena makalasi a madzulo atilepheretse kusonkhana nthawi zonse ndi okhulupirira anzathu. Timafunikira mphamvu zimene timapeza chifukwa chosonkhana pamodzi. Misonkhano yathu ya mpingo imatipatsa mpata wodziwana bwino ndi kulimbikitsana pa “chikondi ndi ntchito zabwino.” Tifunika kuchita zimenezi “makamaka pamene [tikuona] kuti tsikulo likuyandikira.” (Aheberi 10:24, 25) Choncho tiyeni tizilemekeza misonkhano yathu yopatulika mwa kupezekapo nthawi zonse, kuvala moyenera, ndi kusonyeza khalidwe labwino. Tikatero, timasonyeza kuti timaona zinthu zopatulika monga mmene Yehova amazionera.

Kubwereza

• N’chiyani chikusonyeza kuti misonkhano ya anthu a Yehova iyenera kuonedwa kuti ndi yopatulika?

• Kodi pa misonkhano yathu pamachitika zinthu zotani zosonyeza kuti ndi yopatulika?

• Popeza misonkhano yathu ndi yopatulika, kodi ana angasonyeze bwanji kuti amailemekeza?

• N’chifukwa chiyani kupezeka nthawi zonse pa misonkhano kuyenera kukhala mbali yosatha ya moyo wathu?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 28]

Misonkhano yolambirira Yehova imakhala yopatulika kulikonse komwe ikuchitikira

[Chithunzi patsamba 31]

Ana athu amapita ku misonkhano kuti akamve ndi kuphunzira