Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumanga Mogwirizana N’cholinga Chotamanda Mulungu

Kumanga Mogwirizana N’cholinga Chotamanda Mulungu

Kumanga Mogwirizana N’cholinga Chotamanda Mulungu

PA CHILUMBA china m’zilumba zotchedwa Solomon Islands, anthu ankachita chidwi ndi Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova yomangidwa chakumene. Mayi wina ananena kuti: “Kutchalitchi kwathu timakonza zochitika zambiri zopezera ndalama. Timapempha Akhristu athu kuti apereke ndalama, komabe sitikhala ndi ndalama zokwanira kumanga tchalitchi yatsopano. Kodi Amboninu mumapeza bwanji ndalama?” Wamboni amene ankalankhula naye anayankha kuti: “Timalambira Yehova monga banja la padziko lonse. Mpingo wathu ndi abale athu padziko lonse ndiwo anapereka ndalama ndi zinthu zina zofunika pomanga Nyumba ya Ufumu yatsopanoyi. Yehova watiphunzitsa kukhala ogwirizana m’zinthu zonse.”

Mungathe kuona kugwirizana pakati pa Mboni za Yehova m’zochita zawo zonse, ngakhale pomanga Nyumba za Ufumu, zomwe zilipo zochuluka kwabasi. Kugwirizana pochita ntchito zoterezi sikunayambe lero ayi. Kwakhalapo pakati pa anthu a Mulungu kwa zaka masauzande ambiri. Kodi kwakhalapo motani?

Kumanga Chihema ndi Kachisi

Ponena za mtundu wa Isiraeli, Yehova anauza Mose zaka zoposa 3,500 zapitazo mawu otsatirawa: “Andimangire malo opatulika.” (Eksodo 25:8) Pa za kamangidwe ka ntchito imeneyi, Yehova anapitiriza kunena kuti: “Monga mwa zonse ine ndili kuonetsa iwe [Mose], chifaniziro cha kachisi, ndi chifaniziro cha zipangizo zake zonse, momwemo uchimange,” kapena kuti, mtundu wonsewo uchimange. (Eksodo 25:9) Kenaka Yehova anapereka mapulani atsatanetsatane a kamangidwe ka malo opatulika, a zipangizo zake, ndi a zinthu zosiyanasiyana zoti zidzakhale m’kati mwake. (Eksodo 25:10–27:19) Chihema chimenechi chinadzakhala likulu la kulambira koona la Aisiraeli onse.

Sitikudziwa kuti ndi anthu angati amene anagwira nawo ntchito imeneyi, koma Aisiraeli onse anaitanidwa kukathandiza nawo pantchitoyo. Mose anawauza kuti: “Mum’tengere Yehova chopereka cha mwa zanu; aliyense wa mtima wom’funitsa mwini abwere nacho, ndicho chopereka cha Yehova.” (Eksodo 35:4-9) Kodi Aisiraeli anatani? Lemba la Eksodo 36:3 limanena kuti: “Analandira kwa Mose chopereka chonse, chimene ana a Israeli adabwera nacho chikhale cha machitidwe a ntchito ya malo opatulika, aipange nacho. Koma anawonjeza kubwera nazo kwa iye zopereka zofuna mwini, m’mawa ndi m’mawa.”

Posakhalitsa anthuwo anapereka katundu wambirimbiri, ndipo anapitirizabe kubweretsa wina. Potsiriza, amisiri amene ankagwira ntchitoyo anauza Mose kuti: “Anthu alinkubwera nazo zochuluka, zakuposera zoyenera ntchito imene Yehova anauza ichitike.” Motero Mose analamula kuti: “Asawonjezere ntchito ya ku chopereka cha malo opatulika, ngakhale mwamuna ngakhale mkazi.” Kodi zitatero chinachitika n’chiyani? “Zipangizo zinakwanira ntchito yonse ichitike, zinatsalakonso.”​—Eksodo 36:4-7.

Chifukwa cha kuwolowa manja kwa Aisiraeli, chihema anachimaliza chaka chimodzi chokha basi. (Eksodo 19:1; 40:1, 2) Pothandiza pa kulambira koona, anthu a Mulungu ankalemekeza Yehova. (Miyambo 3:9) M’tsogolo mwake, anadzayamba kumanga nyumba zazikulu kwambiri. Ndipo panthawi yachiwiriyinso, anthu onse ofuna kuthandizapo anali aufulu kutero, kaya anali ndi luso lomanga kapena ayi.

Patatha zaka pafupifupi 500 chimangireni chihema, Aisiraeli anayamba kumanga kachisi ku Yerusalemu. (1 Mafumu 6:1) Iyi inali nyumba yaulemerero, yokhala ndi maziko, ndipo inali ya miyala komanso matabwa. (1 Mafumu 5:17, 18) Yehova anapereka kwa Davide “mwa mzimu” kapena kuti mouziridwa, mapulani a kamangidwe ka kachisi. (1 Mbiri 28:11-19) Koma anasankha Solomo, mwana wa Davide kuti atsogolere ntchito yomanga. (1 Mbiri 22:6-10) Davide anathandiza ntchito imeneyi ndi mtima wake wonse. Anapeza miyala, mitengo yomangira, ndi zipangizo zina ndipo anapereka golide komanso siliva wake wochuluka zedi. Analimbikitsanso Aisiraeli anzake kuti akhale owolowa manja, powafunsa kuti: “Ndani uyo afuna mwini kudzipatulira (“kupereka mphatso,” NW) kwa Yehova lero lino?” Kodi anthuwo anachitapo chiyani atamva funsoli?​—1 Mbiri 29:1-5.

Panthawi imene Solomo anayamba kumanga kachisi, anali atapatsidwa golide ndiponso siliva wokwana matani ambirimbiri. Panali miyala ya mkuwa ndiponso zitsulo zambiri zedi moti sakanatha kuziyeza. (1 Mbiri 22:14-16) Mothandizidwa ndi Yehova komanso Aisiraeli onse, ntchitoyo inatha zaka seveni ndi theka basi.​—1 Mafumu 6:1, 37, 38.

“Nyumba ya Mulungu”

Chihema komanso kachisi zinkatchedwa kuti “nyumba ya Mulungu” woona. (Oweruza 18:31; 2 Mbiri 24:7) Yehova safunikira kukhala m’nyumba kuti akhale wotetezeka. (Yesaya 66:1) Iye anamangitsa nyumba zimenezo n’cholinga chopindulitsa nazo anthu. Inde, mmene ankatsegulira kachisi, Solomo anafunsa kuti: “Kodi Mulungu adzakhala ndithu pa dziko lapansi? Taonani, thambo ndi m’Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.”​—1 Mafumu 8:27.

Kudzera mwa mneneri wake Yesaya, Yehova anati: “Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu onse.” (Yesaya 56:7) Nsembe ndi mapemphero operekedwa pa kachisi, komanso miyambo yochitika pamenepo, inathandiza kuti anthu oopa Mulungu, Ayuda ndi osakhala Ayuda, ayandikire kwa Mulungu woona. Yehova anayamba kuwayanja ndi kuwateteza chifukwa cholambira pa nyumba yake. Pemphero limene Solomo ananena popatulira kachisi limagogomezera mfundo imeneyi. Mungathe kuwerenga mawu okhudza mtima amenewa opita kwa Mulungu pa 1 Mafumu 8:22-53 ndi pa 2 Mbiri 6:12-42.

Nyumba ya Mulungu woona yakaleyi inawonongeka kalekale, koma Mawu a Mulungu anasonyeza kuti m’tsogolo, anthu a mitundu yonse adzasonkhanitsidwa kuti azilambira Yehova pakachisi wauzimu wofunika kwambiri kuposa wakaleyu. (Yesaya 2:2) Nsembe imodzi yangwiro ya Mwana wa Mulungu wobadwa yekha, yomwe inkafaniziridwa ndi nsembe za nyama zoperekedwa pakachisi zija, ndiyo inadzakhala njira yofikira kwa Yehova. (Yohane 14:6; Aheberi 7:27; 9:12) Mboni za Yehova masiku ano zikulambira Mulungu m’njira yapamwamba imeneyi, ndipo zikuthandiza anthu enanso ambiri kuchita chimodzimodzi.

Ntchito Zomanga Zamasiku Ano

Padziko lonse lapansi, Mboni za Yehova zimatumikira Mulungu woona. Mbonizi ndi “mtundu wamphamvu,” umene chiwerengero chake chikumka chikulirakulira. (Yesaya 60:22) Malo ofunika kwambiri amene Mboni za Yehova zimakumanapo ndiwo Nyumba ya Ufumu. * Pali nyumba zochuluka zedi zoterezi zimene zikugwiritsidwa ntchito, ndipo pali zinanso zambiri zimene zikufunika.

Mboni za Yehova ‘zimadzipereka zokha’ kumanga Nyumba za Ufumu m’madera amene zikufunika. (Salmo 110:3) Komabe nthawi zambiri, Mboni za m’madera otere sizikhala ndi luso la zomangamanga, ndipo madera ena amene Mboni zikuwonjezeka kwambiri n’ngosauka zedi. Mu 1999 Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linakhazikitsa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu kuti lithetse mavuto amenewo. Kudzera m’ntchito imeneyi, Mboni zimene zili ndi luso losiyanasiyana la zomangamanga zapita ku madera akutali kukaphunzitsa abale ndi alongo kumanga Nyumba za Ufumu. Ndiyeno abale ndi alongo ophunzitsidwawo apitiriza ntchito yomanga m’chigawo chimenecho. Kodi ntchito yapadera imeneyi yadzetsa zotani?

Pofika mwezi wa February 2006, Mboni za Yehova m’madera osauka zamanga Nyumba za Ufumu 13,000. Werengani mawu otsatirawa a anthu ena amene akugwiritsira ntchito Nyumba za Ufumu zatsopanozo.

“Kumpingo kunkabwera anthu pafupifupi 160. Pamsonkhano woyamba, atangomanga kumene Nyumba ya Ufumu yoyamba, chiwerengero cha anthu chinakwera n’kufika pa 200. Tsopano, patatha miyezi sikisi, pakubwera anthu 230. N’zoonekeratu kuti Yehova akudalitsa malowa, omwe amagwira ntchito yake bwinobwino ngakhale kuti n’ngomangidwa m’njira yosavuta.”​—Kuchokera kwa woyang’anira dera wina ku Ecuador.

“Kwa zaka zambiri anthu akhala akutifunsa kuti, ‘Kodi mudzamanga liti Nyumba ya Ufumu yofanana ndi zimene timaona m’mabuku anu?’ Tikuthokoza Yehova, kuti tsopano tili ndi malo ooneka bwino olambirirapo. Tinkachita misonkhano m’nyumba ya mbale wina, ndipo nthawi zambiri kunkabwera mwina anthu 30 basi. Koma pa msonkhano woyamba m’Nyumba ya Ufumu yatsopanoyo panabwera anthu 110.”​—Kuchokera ku mpingo wina ku Uganda.

“Apainiya ena awiri okhazikika ananena kuti kugwira ntchito m’gawo kunayamba kusangalatsa kwambiri chimangireni Nyumba ya Ufumu. Anthu ambiri anayamba kumvetsera muutumiki wa khomo ndi khomo komanso pa ulaliki wamwamwayi. Alongo amenewa tsopano akuchititsa maphunziro a Baibulo 17, ndipo ophunzira Baibulo ambiri pagululi anayamba kubwera kumisonkhano.”​—Kuchokera ku ofesi ya nthambi ya ku Solomon Islands.

“Mbusa wina amene amakhala chapafupi ananena kuti Nyumba ya Ufumu yatsopano inachititsa kuti dera lonselo lizilemekezeka ndiponso anati anthu a m’deralo amanyadira nyumbayo. Anthu ambiri amene amadutsa chapafupi amatchula za kukongola kwa nyumbayo. Zimenezi zimapatsa abalewo mpata wabwino kwambiri wochitira umboni. Anthu ambiri ayamba kufuna kudziwa za ubale wathu wa padziko lonse. Ambiri amene atha zaka zambiri osapita kumisonkhano alimbikitsidwa kuyambanso kusonkhana mokhazikika.”​—Kuchokera ku ofesi ya nthambi ya Myanmar.

“Mlongo wina anaitana munthu wachidwi kuti apite kumene anali kumanga Nyumba ya Ufumu m’deralo. Pambuyo pake munthuyo ananena kuti: ‘Ndinkaganiza kuti anthuwo akana kundilowetsa. Koma ndinadabwa kuona Amboniwo akundipatsa moni mosangalala. Amuna ndi akazi anali kugwira ntchito molimba, osataya nthawi. Ankachita zinthu mogwirizana ndiponso mosangalala.’ Munthuyo anavomera kuphunzira Baibulo n’kuyamba kupita kumisonkhano. Pambuyo pake iye ananena kuti: ‘Ndasintha maganizo. Sindisiya Mulungu panopo chifukwa ndam’peza.’”​—Kuchokera ku ofesi ya nthambi ya dziko la Colombia.

Thandizo Lathu N’lofunika

Kumanga Nyumba za Ufumu ndi mbali yofunika ya utumiki wathu wopatulika. Ndi chinthu choyamikika kwambiri kuona mmene Mboni za Yehova padziko lonse zathandizira pa ntchito imeneyi, popereka ndalama ndiponso pothandiza m’njira zina. Komabe tizikumbukira kuti mbali zina za utumiki wopatulika n’zofunikiranso. Nthawi ndi nthawi, Akhristu amakumana ndi mavuto a zachilengedwe ndipo amafunika thandizo lathu. Ntchito yopanga mabuku ofotokoza Baibulo imathandiza kwambiri pa utumiki wopatulika. Ambirife taonapo mphamvu ya magazini kapena buku lofotokoza za m’Baibulo tikalipereka kwa munthu wa maganizo oyenera. Komanso, ntchito yothandiza amishonale ndi anthu ena ochita utumiki wa nthawi zonse n’njofunika kwambiri. Akhristu amenewa, omwe amalolera kuvutikira ena, akuchita mbali yofunika kwambiri yokulitsa ntchito yolalikira m’masiku otsiriza ano.

Anthu amene anathandiza pomanga kachisi anasangalala kwambiri. (1 Mbiri 29:9) Masiku anonso, tingapeze chimwemwe pochirikiza kulambira koona ndi zopereka zathu. (Machitidwe 20:35) Timapeza chimwemwe chimenechi tikamaika zopereka zathu m’bokosi la Thumba la Nyumba za Ufumu ndiponso la ntchito ya padziko lonse, chifukwa potero timakhala tikuthandiza ntchito zina zokhudzana ndi kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. M’njira yodabwitsa, Mboni za Yehova masiku ano n’zogwirizana pa kulambira koona. Tiyeni tonse tipeze chimwemwe chifukwa chothandiza nawo pa kulambira kumeneku.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 16 Kuti mudziwe chiyambi cha mawu akuti “Nyumba ya Ufumu,” onani buku la Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom, tsamba 319, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi pamasamba 20, 21]

NJIRA ZIMENE ENA AMAPEREKERA

ZOPEREKA ZA NTCHITO YA PADZIKO LONSE

Ambiri amaika padera ndalama, kapena kuti amachita bajeti kuti aziponya ndalama mwakutimwakuti m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse​—Mateyu 24:14.”

Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova imene imayang’anira ntchito ya m’dziko lawo. N’zothekanso kutumiza ndalama zimene mwapereka ku Accounting Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, P. O. Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu. Mukamatumiza macheke ku adiresi yomwe ili pamwambayi, musonyeze kuti ndalamazo zipite ku “Watch Tower.” Mungathenso kupereka zinthu ngati ndolo, mphete, zibangili, kapena zinthu zina zamtengo wapatali. Potumiza zinthu zimenezi, mulembe kalata yachidule yofotokoza kuti zimene mukutumizazo ndi mphatso basi.

MPHATSO ZINA

Kuwonjezera pa kupereka mphatso za ndalama, pali njira zinanso zoperekera zinthu zopititsira patsogolo utumiki wa Ufumu padziko lonse. Zina mwa njirazi ndi izi:

Inshuwalansi: Mungalembetse kuti Watch Tower Society ndiyo idzapatsidwe phindu la inshuwalansi kapena ndalama za penshoni.

Maakaunti a ku Banki: Mukhoza kuikiza m’manja mwa Watch Tower Society maakaunti anu a ku banki, zikalata zosungitsira ndalama, kapena maakaunti a ndalama zimene mukusunga kuti mudzagwiritse ntchito mukadzapuma pantchito. Mukhozanso kukonza zoti mukadzamwalira a Watch Tower Society adzatenge zinthu zimenezi. Pochita zimenezi, mutsatire malamulo amene mabanki a m’dziko lanu amayendera.

Masheya: Mungapereke masheya amene muli nawo mu kampani ku Watch Tower Society monga mphatso basi.

Malo ndi Nyumba: Mungapereke monga mphatso, malo ndi nyumba zoti zingagulitsidwe, kapena ngati ili nyumba yoti mukukhalamo mukhoza kuipereka komabe n’kupitiriza kukhalamo panthawi yonse imene muli ndi moyo. Musanakonze zopereka malo kapena nyumba iliyonse, lankhulani kaye ndi ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu.

Chuma Chamasiye: Mukhoza kulemba mu wilo yovomerezeka ku boma kuti Watch Tower Society idzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu inuyo mukadzamwalira.

Ngati mukufuna kudziwa zambiri za mmene mungaperekere mphatso zimenezi, lankhulani ndi a ku Accounting Office pa telefoni kapena alembereni kalata pa adiresi imene ili pansipa kapena mungalembe kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu.

Accounting Office

Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

P. O. Box 30749

Lilongwe 3

Malawi

Telefoni: 01 762 111

[Chithunzi patsamba 18]

Khama ndi mgwirizano wathu umachititsa kuti tithe kumanga Nyumba za Ufumu zokongola padziko lonse

[Chithunzi patsamba 18]

Nyumba ya Ufumu yatsopano ku Ghana