Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalanibe M’chikondi cha Mulungu!

Khalanibe M’chikondi cha Mulungu!

Khalanibe M’chikondi cha Mulungu!

“Okondedwa, . . . khalanibe m’chikondi cha Mulungu, . . . pokhala ndi cholinga cha moyo wosatha.”​—YUDA 20, 21.

1, 2. Kodi muyenera kuchita chiyani kuti mukhalebe m’chikondi cha Mulungu?

YEHOVA amakonda kwambiri dziko la anthu moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha kuti onse okhulupirira iye angathe kukhala ndi moyo wosatha. (Yohane 3:16) Ndipotu n’zabwino kwambiri kukondedwa motere. Ngati ndinu mtumiki wa Yehova, mosakayikira mumafuna kuti akukondeni kosatha.

2 Wophunzira Yuda anafotokoza mmene mungakhalirebe m’chikondi cha Mulungu. Iye analemba kuti: “Podzimanga pa maziko a chikhulupiriro chanu choyera kopambana, ndi kupemphera m’mphamvu ya mzimu woyera, khalanibe m’chikondi cha Mulungu. Teroni pamene mukuyembekezera chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pokhala ndi cholinga cha moyo wosatha.” (Yuda 20, 21) Kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kulalikira uthenga wabwino kumakuthandizani kudzimanga pa ‘chikhulupiriro choyera kopambana,’ chimene ndi ziphunzitso zachikhristu. Kuti mukhalebe m’chikondi cha Mulungu, muyenera kupemphera “m’mphamvu ya mzimu woyera,” kapena kuti motsogoleredwa ndi mzimuwo. Kuti mukalandire moyo wosatha, muyeneranso kukhulupirira nsembe ya dipo la Yesu Khristu.​—1 Yohane 4:10.

3. N’chifukwa chiyani ena salinso Mboni za Yehova?

3 Anthu ena amene kale anali ndi chikhulupiriro, sanakhalebe m’chikondi cha Mulungu. Chifukwa chakuti anasankha njira yauchimo, salinso Mboni za Yehova. Kodi inu mungapewe bwanji zimenezi? Kusinkhasinkha mfundo zotsatirazi kungakuthandizeni kupewa tchimo n’kukhalabe m’chikondi cha Mulungu.

Sonyezani Kuti Mumam’konda Mulungu

4. N’chifukwa chiyani kumvera Mulungu n’kofunika kwambiri?

4 Sonyezani kuti mumam’konda Mulungu mwa kumvera iye. (Mateyo 22:37) Mtumwi Yohane analemba kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake; ndipo malamulo akewo si olemetsa.” (1 Yohane 5:3) Ngati muli ndi chizolowezi chomvera Mulungu, mudzakhala ndi nyonga yopewera ziyeso ndipo mudzasangalala. Wamasalmo anati: “Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, . . . komatu m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake.”​—Salmo 1:1, 2.

5. Kodi kukonda Yehova kudzakulimbikitsani kuchita chiyani?

5 Ngati mumakonda Yehova, mudzapewa kuchita tchimo lalikulu limene linganyozetse dzina lake. Aguri popemphera anati: “Musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera; ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.” (Miyambo 30:1, 8, 9) Onetsetsani kuti ‘simukutchula dzina la Mulungu pachabe’ mwa kupewa kubweretsa chitonzo pa iye. Koma nthawi zonse yesetsani kuchita zinthu zabwino zimene zimapereka ulemerero kwa iye.​—Salmo 86:12.

6. Kodi chingachitike n’chiyani ngati mungamachimwe dala?

6 Muzipemphera nthawi zonse kwa Atate wanu wakumwamba kuti akuthandizeni kulimbana ndi ziyeso zoti muchite tchimo. (Mateyo 6:13; Aroma 12:12) Pitirizani kutsatira uphungu wa Mulungu kuti mapemphero anu asatsekerezedwe. (1 Petulo 3:7) Ngati mungamachimwe dala, zotsatira zake zingakhale zoopsa, chifukwatu Yehova amatsekereza anthu opanduka ndi mtambo wophiphiritsa kuti mapemphero awo asadutse kufika kwa iye. (Maliro 3:42-44) Choncho khalani ndi mtima wodzichepetsa, ndipo muzipemphera kuti musachite chilichonse chimene chingaletse mapemphero anu kufika kwa Mulungu.​—2 Akorinto 13:7.

Sonyezani Kuti Mumakonda Mwana wa Mulungu

7, 8. Kodi kumvera uphungu wa Yesu kungakuthandizeni bwanji kukana njira yauchimo?

7 Sonyezani kuti mumakonda Yesu Khristu mwa kumvera malamulo ake, chifukwa kuchita zimenezi kudzakuthandizani kukana njira yauchimo. Yesu anati: “Ngati musunga malamulo anga, mudzakhalabe m’chikondi changa, mmenenso ine ndasungira malamulo a Atate ndi kukhalabe m’chikondi chake.” (Yohane 15:10) Kodi kutsatira mawu a Yesu kungakuthandizeni bwanji kukhalabe m’chikondi cha Mulungu?

8 Kumvera mawu a Yesu kungakuthandizeni kukhalabe ndi makhalidwe abwino. Chilamulo cha Mulungu kwa Isiraeli chinati: “Usachite chigololo.” (Eksodo 20:14) Koma Yesu anasonyeza mfundo ya lamulo limenelo ponena kuti: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.” (Mateyo 5:27, 28) Mtumwi Petulo ananena kuti ena mumpingo woyambirira anali ndi “maso odzala chigololo” ndipo ‘anakopa anthu a pendapenda.’ (2 Petulo 2:14) Mosiyana ndi amenewo, inuyo mungapewe machimo okhudzana ndi chiwerewere ngati mumakonda ndi kumvera Mulungu ndi Khristu ndiponso ngati mukufuna kuteteza ubwenzi wanu ndi iwo.

Lolani Mzimu wa Yehova Kukutsogolerani

9. Kodi n’chiyani chimene chingachitike ndi mzimu woyera ngati munthu angapitirize kuchimwa?

9 Muzipempherera mzimu woyera wa Mulungu, ndipo muziulola kukutsogolerani. (Luka 11:13; Agalatiya 5:19-25) Ngati mungapitirize kuchimwa, Mulungu angakuchotsereni mzimu wake. Davide atachimwa ndi Bateseba, anapempha Mulungu kuti: “Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere Mzimu wanu Woyera.” (Salmo 51:11) Chifukwa chochimwa mosalapa, Mfumu Sauli inataya mzimu wa Mulungu. Sauli anachimwa mwa kupereka nsembe ndi mwa kusawononga zina mwa nkhosa, mbuzi, ng’ombe, ndiponso mfumu ya Amaleki. Zitatero, Yehova anachotsa mzimu wake woyera pa Sauli.​—1 Samueli 13:1-14; 15:1-35; 16:14-23.

10. N’chifukwa chiyani muyenera kupeweratu chizolowezi chochimwa?

10 Peweranitu chizolowezi chochimwa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati timachita uchimo dala pambuyo podziwa choonadi molondola, sipatsalanso nsembe ina ya machimo athu.” (Aheberi 10:26-31) Ndiye ndi tsoka lalikulu ngati mungazolowere kuchimwa mpaka kufika pamenepa!

Sonyezani Ena Chikondi Chenicheni

11, 12. Kodi ndi motani mmene chikondi ndi ulemu zingaletsere munthu kuchita zachiwerewere?

11 Kukonda anthu anzanu kudzakuletsani kuchita zachiwerewere. (Mateyo 22:39) Chikondi chotero chidzakukakamizani kuteteza mtima wanu kuti usakunyengerereni kukopa mwamuna kapena mkazi wa wina kuti akukondeni. Mukalola mtima wanu kunyengedwa, mudzagwera m’tchimo la chigololo. (Miyambo 4:23; Yeremiya 4:14; 17:9, 10) Khalani monga Yobu, munthu wolungama, amene sanalole kukhumbira mkazi wina aliyense kusiyapo mkazi wake.​—Yobu 31:1.

12 Ukwati n’ngopatulika. Kulemekeza mfundo imeneyi kungakuthandizeni kupewa tchimo lalikulu. Mulungu anafuna kuti ukwati wolemekezeka ndi kugonana kolemekezeka zikhale njira yoberekera kuti moyo upitirire. (Genesis 1:26-28) Muzikumbukira kuti ziwalo zoberekera ntchito yake ndi kupatsira ana moyo, umene ndi wopatulika. Adama ndi achigololo samvera Mulungu, amanyoza kugonana, salemekeza ukwati womwe ndi wopatulika, ndipo amachimwira matupi awo. (1 Akorinto 6:18) Koma kukonda Mulungu ndi mnansi, kuphatikizapo kumvera Mulungu kumateteza munthu kuti asachite zinthu zimene zingamuchotsetse mu mpingo wachikhristu.

13. Kodi munthu wachigololo ‘amamwaza chuma’ m’njira yotani?

13 Tifunikira kuletsa maganizo oipa kuti tisapweteke mtima anthu amene timawakonda. Lemba la Miyambo 29:3 limati: “Wotsagana ndi akazi adama amwaza chuma.” Munthu wachigololo amene salapa amawononga ubwenzi wake ndi Mulungu ndipo amapasula banja. Mkazi wake amakhala ndi chifukwa chomusudzulira. (Mateyo 19:9) Kaya wochimwayo ndi mwamuna kapena mkazi, kusweka kwa banja kumapweteka kwambiri wosachimwayo, ana, ndi anthu ena. Kodi simukuvomereza kuti kudziwa kuti khalidwe lachiwerewere limawononga zambiri kuyenera kutilimbikitsa kukana, tikayesedwa kuchita chiwerewere?

14. Kodi tikupezapo phunziro lotani pa Miyambo 6:30-35 lokhudza kulakwa?

14 Popeza kuti palibe njira imene munthu angalipirire mlandu wa chigololo, m’pofunika kupeweratu khalidwe loipa ndi ladyera limeneli. Lemba la Miyambo 6:30-35 limasonyeza kuti ngakhale kuti anthu angachitire chifundo munthu amene waba chifukwa cha njala, iwo amadana ndi wachigololo chifukwa chakuti zolinga za munthuyo n’zoipa. ‘Amawononga moyo wakewake.’ Malinga ndi Chilamulo cha Mose, munthu wotero ankayenera kuphedwa. (Levitiko 20:10) Munthu amene amachita chigololo amalolera kupweteka anzake kuti angokhutiritsa chilakolako chake, ndipo wachigololo amene salapa sakhalabe m’chikondi cha Mulungu koma amachotsedwa mu mpingo woyera wachikhristu.

Khalanibe ndi Chikumbumtima Chabwino

15. Kodi chikumbumtima cholochedwa “ngati ndi chitsulo chamoto” chimakhala chotani?

15 Ngati tikufuna kukhalabe m’chikondi cha Mulungu, tisalole chikumbumtima chathu kufa mpaka kusiya kuzindikira uchimo. Mwachidziwikire, sitiyenera kutengera makhalidwe a dzikoli ochititsa manyazi, ndipo tifunikira kusamala pamene tikusankha mabwenzi, mabuku owerenga, ndi zosangalatsa. Paulo anachenjeza kuti: “M’nthawi zam’tsogolo, ena adzagwa pa chikhulupiriro, posamalira mawu ouziridwa osocheretsa, ndi ziphunzitso za ziwanda, komanso pomvera chinyengo cha anthu olankhula mabodza, okhala ndi chikumbumtima cholochedwa ngati ndi chitsulo chamoto.” (1 Timoteyo 4:1, 2) Chikumbumtima cholochedwa “ngati ndi chitsulo chamoto” chimakhala ngati pakhungu pamene pali chipsera ndiponso m’pakufa moti sipamva kupweteka. Chikumbumtima chotero chimasiya kutichenjeza kuti tipewe ampatuko ndi zochitika zimene zingatigwetse pa chikhulupiriro chathu.

16. N’chifukwa chiyani kukhala ndi chikumbumtima chabwino kuli kofunika kwambiri?

16 Chipulumutso chathu chimadalira kukhala ndi chikumbumtima chabwino. (1 Petulo 3:21) Popeza kuti timakhulupirira magazi okhetsedwa a Yesu, chikumbumtima chathu chayeretsedwa ku ntchito zakufa, “kuti tichite utumiki wopatulika kwa Mulungu wamoyo.” (Aheberi 9:13, 14) Ngati tichimwira dala, chikumbumtima chathu chingaipe ndipo sitingakhalenso anthu oyera, oyenera kutumikira Mulungu. (Tito 1:15) Koma mothandizidwa ndi Yehova, tingakhale ndi chikumbumtima chabwino.

Njira Zina Zopewera Khalidwe Loipa

17. Kodi ‘kulimbika ndi kutsata Yehova’ mokwanira kuli ndi phindu lanji?

17 ‘Limbikani ndi kutsata Yehova’ mokwanira, ngati mmene Kalebi wa ku Isiraeli wakale anachitira. (Deuteronomo 1:34-36) Chitani zimene Mulungu akufuna kuti muchite, ndipo musayerekeze m’pang’ono pomwe kudya pa “tebulo la ziwanda.” (1 Akorinto 10:21) Kanani mpatuko. Idyani ndi mtima woyamikira chakudya chauzimu chimene chimapezeka pa tebulo la Yehova lokha basi, ndipo sadzakusocheretsani aphunzitsi onyenga kapena makamu a mizimu yoipa. (Aefeso 6:12; Yuda 3, 4) Limbikirani zinthu zauzimu, monga kuphunzira Baibulo, kupezeka pamisonkhano, ndi utumiki wa kumunda. Mukalimbika ndi kutsata Yehova mokwanira, mudzasangalala ndipo mudzakhala ndi zochita zochuluka m’ntchito ya Ambuye.​—1 Akorinto 15:58.

18. Kodi kuopa Yehova kumakhudza bwanji khalidwe lanu?

18 Musasiye ‘kuchitira Mulungu utumiki wopatulika moopa iye ndi mwaulemu waukulu.’ (Aheberi 12:28) Kuopa Yehova kudzakulimbikitsani kukana njira iliyonse yopulupudza. Kudzakuthandizani kutsatira uphungu wa Petulo kwa odzozedwa anzake wakuti: “Ngati mukuitana pa Atate amene amaweruza mopanda tsankho malinga ndi ntchito za aliyense, chitani zinthu ndi mantha panthawi imene muli ngati alendo m’dziko.”​—1 Petulo 1:17.

19. N’chifukwa chiyani nthawi zonse muyenera kugwiritsa ntchito zimene mukuphunzira m’Mawu a Mulungu?

19 Nthawi zonse gwiritsani ntchito zimene mukuphunzira m’Mawu a Mulungu. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kupewa machimo aakulu chifukwa mudzakhala pakati pa anthu “amene pogwiritsa ntchito luntha lawo la kuzindikira, aphunzitsa lunthalo kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika.” (Aheberi 5:14) M’malo motayirira pa kalankhulidwe ndi khalidwe lanu, muzisamala kuti muziyenda monga munthu wanzeru, amene ‘amawombola nthawi yoyenerera’ m’masiku ano oipa. “Pitirizani kuzindikira chifuniro cha Yehova,” ndipo osasiya kuchita chifunirocho.​—Aefeso 5:15-17; 2 Petulo 3:17.

20. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kusirira kwa nsanje?

20 Musalole m’pang’ono pomwe kusirira kwa nsanje, komwe ndi kulakalaka zinthu za eni mwadyera. Limodzi mwa Malamulo Khumi limati: “Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng’ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.” (Eksodo 20:17) Lamulo limeneli linateteza nyumba ya munthu, mkazi wake, antchito ake, ziweto zake, ndi zina zotero. Koma mfundo yofunika kwambiri ndi imene Yesu ananena kuti kusirira kwa nsanje kumaipitsa munthu.​—Maliko 7:20-23.

21, 22. Kodi njira zodzitetezera zimene Mkhristu angatsatire kuti apewe kuchimwa n’zotani?

21 Tsatirani njira zodzitetezera kuti chilakolako chisakutsogolereni ku uchimo. Wophunzira Yakobe analemba kuti: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako cha iye mwini. Ndiye chilakolako chikatenga pathupi, chimabala tchimo; nalonso tchimo likakwaniritsidwa, limabweretsa imfa.” (Yakobe 1:14, 15) Mwachitsanzo, ngati munthu kale anali ndi vuto la kumwa mowa, angasankhe kusakhala ndi mowa m’nyumba mwake. Pofuna kupewa chiyeso chokopeka ndi mkazi kapena mwamuna wina, Mkhristu angafunikire kusintha malo amene amagwirira ntchito kupita pena kapena kusiya ntchito kumene n’kukalowa kwina.​—Miyambo 6:23-28.

22 Pewani ngakhale chiyambi cha tchimo. Chifukwa cha kukopana ndi kuganizira zachiwerewere, munthu angachite dama kapena chigololo. Kunama pang’ono kungalimbitse munthu mtima kuti azilankhula mabodza akuluakulu n’kukhala ndi chizolowezi chonena mabodza, chimene ndi tchimo. Kuba tinthu ting’onoting’ono kungaphe chikumbumtima cha munthu mpaka kufika poti angayambe kuba zazikulu. Ngakhale kulolera maganizo ampatuko pang’ono kungachititse kuti munthu m’kupita kwa nthawi akhale wampatuko weniweni.​—Miyambo 11:9; Chivumbulutso 21:8.

Nanga Bwanji Ngati Mwachimwa?

23, 24. Kodi ndi chilimbikitso chotani chimene tingapeze pa 2 Mbiri 6:29, 30 ndiponso pa Miyambo 28:13?

23 Anthu onse ndi opanda ungwiro. (Mlaliki 7:20) Koma ngati mwachimwa kwambiri, mungapeze chitonthozo m’pemphero la Mfumu Solomo limene anapereka potsegulira kachisi wa Yehova. Popemphera kwa Mulungu, Solomo anati: “Pemphero ndi pembedzero lililonse likachitika ndi munthu aliyense, kapena ndi anthu anu onse Aisiraeli, akadziwa yense chinthenda chake, ndi chisoni chake, nakatambasulira manja ake kuloza ku nyumba iyi; pamenepo mumvere m’Mwamba mokhala Inumo, nimukhululukire, ndi kubwezera aliyense monga mwa njira zake zonse, monga mudziwa mtima wake; pakuti Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana a anthu.”​—2 Mbiri 6:29, 30.

24 Inde, Mulungu amadziwa mtima wa munthu ndipo amakhululuka. Lemba la Miyambo 28:13 limati: “Wobisa machimo ake sadzaona mwayi; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.” Mukaulula tchimolo n’kulapa, kenako n’kulisiya, Mulungu angakuchitireni chifundo. Koma bwanji ngati mwafooka mwauzimu? N’chiyani china chimene chingakuthandizeni kukhalabe m’chikondi cha Mulungu?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhalebe m’chikondi cha Mulungu?

• Kodi kukonda Mulungu ndi Khristu kumatithandiza bwanji kukana njira yauchimo?

• N’chifukwa chiyani kukhala ndi chikondi chenicheni pa ena kumatiletsa kuchita zachiwerewere?

• Kodi zina mwa njira zopewera khalidwe loipa n’zotani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Yuda amatisonyeza mmene tingakhalirebe m’chikondi cha Mulungu

[Chithunzi patsamba 23]

Kusweka kwa banja kumapweteka kwambiri wosachimwayo ndi ana

[Chithunzi patsamba 24]

Mofanana ndi Kalebi, kodi ‘mukulimbika ndi kutsata Yehova’ mokwanira?

[Chithunzi patsamba 25]

Muzipemphera nthawi zonse kuti mupeze thandizo polimbana ndi chiyeso