Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yuda Anakhaladi Bwinja?

Kodi Yuda Anakhaladi Bwinja?

Kodi Yuda Anakhaladi Bwinja?

BAIBULO linaneneratu kuti dziko la ufumu wa Yuda lidzawonongedwa ndi Ababulo ndipo lidzakhala labwinja mpaka Ayuda amene anali kundende atabwerera kwawo. (Yeremiya 25:8-11) Chifukwa chachikulu chokhulupirira kuti ulosi umenewu unakhaladi woona ndi mbiri youziridwa imene inalembedwa zaka 75 gulu loyamba la Ayuda andende litabwerera ku dziko la kwawo. Mbiriyi imanena kuti, mfumu ya Ababulo inatenga ‘amene adapulumuka kulupanga namuka nawo ku Babulo, nakhala iwo anyamata ake, ndi a ana ake, mpaka mfumu ya Perisiya idachita ufumu.’ Ndipo ponena za dzikolo imati: “Masiku onse a kupasuka kwake linasunga sabata.” (2 Mbiri 36:20, 21) Kodi pali umboni wina uliwonse wotsimikizira zimenezi umene ofukula zinthu zakale za m’mabwinja apeza?

M’magazini ya Biblical Archaeology Review, Ephraim Stern, katswiri wophunzira za m’mabwinja wa ku Palestina pa yunivesite ya Hebrew anasonyeza kuti: “Asuri ndi Ababulo onse anawononga mbali zazikulu za Isiraeli wakale, komabe umboni wochokera kwa anthu ofukula za m’mabwinja pa zotsatira za zipambano zawozo umanena za nkhani ziwiri zosiyana kwambiri.” Iye anati: “Pamene Asuri anasiya umboni wooneka wosonyeza kuti anafikapo ku Palestina, panalibenso umboni wina pambuyo pa kuwononga kwa Ababulo. . . . Sitipeza umboni wakuti munakhalapo anthu mpaka nthawi ya Aperisi. . . . Palibiretu umboni wosonyeza kuti kunakhalanso anthu. Panthawi yonseyo, panalibe tawuni ina iliyonse yowonongedwa ndi Ababulo imene inakhazikitsidwanso.”

Pulofesa Lawrence E. Stager wa pa yunivesite ya Harvard, anavomereza kuti: “M’dziko lonse la Filistia ndipo kenako m’dziko lonse la Yuda, mfumu ya Ababulo “potsata mfundo yowonongeratu zinthu zonse, inasiya dziko la kumadzulo kwa mtsinje wa Yordano lili ngati chipululu.” Stager anawonjezera kuti: “Mpaka pa nthawi imene Koresi Wamkulu, Mperesi amene anagonjetsa Ababulo, m’pamene panayambiranso umboni wa zinthu zakale zofukulidwa pansi . . . ku Yerusalemu ndi ku Yuda, kumene Ayuda ambiri andende anabwerera kwawo.”

N’zoonadi, mawu a Yehova onena za kukhaladi bwinja kwa Yuda anakwaniritsidwa. Zimene Yehova Mulungu amaneneratu nthawi zonse zimachitikadi. (Yesaya 55:10, 11) Tingakhulupirire Yehova ndi mtima wonse ndiponso malonjezo ake amene analembedwa m’Mawu ake, Baibulo.​—2 Timoteyo 3:16.