Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za Nyimbo ya Solomo

Mfundo Zazikulu za Nyimbo ya Solomo

Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za Nyimbo ya Solomo

“NGATI kakombo pakati pa minga momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana aakazi.” “Ngati maula pakati pa mitengo ya m’nkhalango, momwemo, wokondedwa wanga pakati pa ana aamuna.” “Ndaniyo atuluka ngati mbanda kucha, wokongola ngati mwezi, woyera ngati dzuwa?” (Nyimbo ya Solomo 2:2, 3; 6:10) Mavesi amenewa ochokera m’buku la m’Baibulo la Nyimbo ya Solomo ndi apamwamba kwambiri. Buku lonseli ndi ndakatulo yodzaza ndi matanthauzo ndiponso yabwino kwambiri moti imatchedwa kuti, “nyimbo yoposa.”​—Nyimbo ya Solomo 1:1.

Nyimboyi inalembedwa ndi Mfumu Solomo ya ku Isiraeli wakale, makamaka cha m’ma 1020 B.C.E., chakumayambiriro kwa chaka cha 40 cha ulamuliro wake, ndipo imanena za nkhani ya chikondi cha mnyamata yemwe ndi m’busa ndi mtsikana wakumudzi, yemwe ndi Msulami. Pakati pa anthu amene anawatchula mu ndakatuloyi pali mayi ake a mtsikanayo ndi achimwene ake, ‘ana aakazi a ku Yerusalemu [akazi a kumpanda wa mfumu],’ ndi “ana aakazi . . . a Ziyoni [akazi a ku Yerusalemu].” (Nyimbo ya Solomo 1:5; 3:11) N’kovuta kwa munthu amene akuwerenga Baibulo kudziwa anthu onse amene akulankhula m’Nyimbo ya Solomo, koma zimenezi n’zotheka mwa kumvetsera zimene akulankhula kapena zimene akuuzidwa.

Monga mbali ya Mawu a Mulungu, uthenga wa m’Nyimbo ya Solomo ndi wofunika kwambiri pa zifukwa ziwiri. (Aheberi 4:12) Choyamba, umatiphunzitsa za mmene chikondi cha pakati pa mwamuna ndi mkazi chimakhalira. Chachiwiri, nyimboyi imasonyeza mtundu wa chikondi umene ulipo pakati pa Yesu Khristu ndi mpingo wa Akhristu odzozedwa.​—2 Akorinto 11:2; Aefeso 5:25-31.

MUSAYESE “KUGALAMUTSA CHIKONDI” MWA INE

(Nyimbo ya Solomo 1:1–3:5)

“Mnyamatayo andipsompsonetse ndi m’kamwa mwake; pakuti chikondi chako chiposa vinyo.” (Nyimbo ya Solomo 1:2) Makambirano a m’Nyimbo ya Solomo anayamba ndi mawu a mtsikana wodzichepetsa wochokera kumudzi amene anam’bweretsa m’hema wachifumu wa Solomo. Kodi anafika bwanji kumeneko?

Mtsikanayu anati: “Ana aamuna a amayi andikwiyira, anandisungitsa minda yamipesa.” Achimwene ake anamukwiyira chifukwa m’busa yemwe iye anali kum’konda anamuuza kuti apite limodzi kukayenda pa tsiku loti kwacha bwino m’ngululu. Pofuna kuti asapite, achimwene akewo anam’patsa ntchito yolondera ‘ankhandwe . . . aang’ono, amene ankawononga minda yamipesa.’ Ntchito imeneyi ndi imene inam’fikitsa kumene kunali Solomo. Kukongola kwake kunaoneka pamene anapita “ku munda wa mtedza,” ndipo anthu a Solomo anam’tenga.​—Nyimbo ya Solomo 1:6; 2:10-15; 6:11.

Pamene namwaliyu analankhula zoti akulakalaka m’busa wake wokondekayo, akazi akumpanda kwa mfumu anamuuza kuti ‘atuluke kukalondola bande la gululo’ ndipo akafunefune bwenzi lakelo. Koma Solomo sanamulole kupita. Posonyeza mmene ankasiririra kukongola kwake, anam’lonjeza “nkhata zagolidi ndi njumu zasiliva.” Koma mtsikanayu sanakopeke ndi zimenezo. M’busayo akukumana ndi gulu la Solomo, akumupeza namwaliyo, ndipo akulankhula mofuula kuti: “Taona, wakongolatu, bwenzi langa; namwaliwe taona, wakongola.” Namwaliyu akulumbirira akazi akumpanda wa mfumu kuti: “Musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi [mwa ine], mpaka chikafuna mwini.”​—Nyimbo ya Solomo 1:8-11, 15; 2:7; 3:5.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

1:2, 3—N’chifukwa chiyani kukumbukira chikondi cha m’busayo kukufanana ndi vinyo ndiponso dzina lake likunga mafuta? Monga mmene vinyo amakondweretsera mtima wa munthu, ndi mmene mafuta amaziziritsira tikawadzola pa mutu, kukumbukira chikondi cha mnyamatayo ndiponso dzina lake kunalimbikitsa ndi kutonthoza namwaliyo. (Salmo 23:5; 104:15) Akhristu oona, makamaka odzozedwa, amapeza mphamvu ndiponso amalimbikitsidwa akamaganizira za chikondi chimene Yesu Khristu wawasonyeza.

1:5—N’chifukwa chiyani mtsikana wakumudziyo anayerekezera thupi lake lakudalo ndi “mahema a Kedara”? Ubweya wa mbuzi, umene ankapangira nsalu, unkagwira ntchito zosiyanasiyana. (Numeri 31:20) Mwachitsanzo, “nsalu . . . za ubweya wa mbuzi” ankazigwiritsa ntchito kupangira “hema pamwamba pa kachisi.” (Eksodo 26:7) Monga mmene matenti a Abedouin amakhalira ngakhale masiku ano, mahema a Kedara angakhale kuti kawirikawiri ankapangidwa ndi ubweya wakuda wa mbuzi.

1:15—Kodi m’busayu akutanthauza chiyani pamene akunena kuti: “Maso ako akunga a nkhunda”? M’busayu akutanthauza kuti maso a bwenzi lakelo ndi ofewa ndiponso odekha ngati a nkhunda.

2:7; 3:5—N’chifukwa chiyani mtsikanayo akulumbirira akazi akumpanda wa mfumu pogwiritsa ntchito “mphoyo, ndi nswala ya kuthengo”? Mphoyo ndi nswala zili ndi maonekedwe ake ochititsa kaso ndiponso okongola kwambiri. Kwenikweni, Msulamiyu, akulumbirira akazi akumpanda wa mfumu kuti chilichonse chimene chili chochititsa kaso ndiponso chokongola chisautse chikondi mwa iye.

Zimene Tikuphunzirapo:

1:2; 2:6. Mawu ndi zochita zabwino zosonyeza chikondi zingakhale zoyenera pamene tili pachibwenzi. Komabe, mwamuna ndi mkazi ayenera kusamala kuti chimenechi chizikhala chikondi chenicheni osati chilakolako chonyansa, chimene chingawachititse chisembwere.​—Agalatiya 5:19.

1:6; 2:10-15. Achimwene ake a Msulamiyu sanamulole mlongo wawoyo kupita ndi wokondedwa wakeyo kwaokha kumapiri. Sikuti chifukwa chake chinali chakuti Msulamiyu anali wachiwerewere kapena kuti anali ndi zolinga zoipa ayi. M’malo mwake, ankafuna kumuteteza kuti asachite zinthu zimene zikanamuchimwitsa. Phunziro kwa anthu amene ali pachibwenzi ndi lakuti, ayenera kupewa kukhala kwaokha.

2:1-3, 8, 9Ngakhale anali wokongola, Msulamiyo, modzichepetsa ankadziona ngati “duwa lofiira [duwa wamba] la ku Saroni.” Chifukwa cha kukongola kwake ndi kukhulupirika kwake kwa Yehova, m’busayo ankamutenga Msulamiyo ngati “kakombo pakati pa minga.” Kodi mnyamatayo anali wotani? Chifukwa chakuti anali wokongola, kwa mtsikanayo ankafanana ndi “mphoyo.” Ayeneranso kuti anali mwamuna wokonda zauzimu ndiponso wokhulupirika kwa Yehova. Mtsikanayo anati: “Ngati maula [amene amapereka mthunzi ndi zipatso] pakati pa mitengo ya m’nkhalango, momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana aamuna.” Kodi chikhulupiriro ndiponso kudzipereka kwa Mulungu si makhalidwe ofunikira kuyang’ana mwa munthu amene tikufuna kudzakwatirana naye?

2:7; 3:5. Mtsikana wakumudzi ameneyu sanakopeke ndi Solomo. Komanso analumbirira akazi akumpanda wa mfumu kuti asayese kuutsa chikondi mwa iye kaamba ka aliyense kupatulapo m’busayo. N’kosatheka ndiponso kosayenera kwa munthu kukonda mwamuna kapena mkazi aliyense. Mkhristu amene akufuna mnzake woti akwatirane naye, ayenera kusankha mtumiki wokhulupirika wa Yehova basi.​—1 Akorinto 7:39.

“MUYANG’ANIRANJI PA MSULAMI?”

(Nyimbo ya Solomo 3:6–8:4)

Chinachake ‘chikukwera kutuluka m’chipululu ngati utsi wa tolo.’ (Nyimbo ya Solomo 3:6) Kodi atatuluka kuti akaone, akazi a ku Yerusalemu akuona chiyani? Akuona Solomo ndi anyamata ake akubwerera mu mzinda. Ndipo mfumuyo ikubwera limodzi ndi Msulami.

M’busa walondola namwaliyo ndipo posapita nthawi akupeza njira yomuonera. Pomutsimikizira za mmene amamukondera, mtsikanayo akufotokoza kuti akulakalaka kuchoka mu mzindawo. Akuti: “Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha, ndikamuka ku phiri la nipa, ndi ku chitunda cha mtanthanyerere.” Akuuza m’busayo kuti “alowe m’munda mwake, nadye zipatso zake zofunika.” M’busayo akuyankha kuti: “Ndalowa m’munda mwanga, mlongo wanga, mkwatibwi.” Akazi a ku Yerusalemu akuwauza kuti: “Idyani, atsamwalinu, imwani, mwetsani chikondi.”​—Nyimbo ya Solomo 4:6, 16; 5:1.

Atasimba maloto ake kwa akazi akumpanda wa mfumu, Msulamiyu akuwauza kuti: “Ndadwala ndi chikondi.” Akaziwo akumufunsa kuti: “Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji?” Ndipo iye akuyankha kuti: “Wokondedwa wanga ali woyera ndi wofiira, womveka mwa zikwi khumi.” (Nyimbo ya Solomo 5:2-10) Solomo atamutamanda monyanyira, Msulamiyu modzichepetsa akuyankha kuti: “Muyang’aniranji pa Msulami?” (Nyimbo ya Solomo 6:4-13) Poona umenewu ngati mwayi womukopa kuti am’konde, mfumuyi ikupitirizabe kumutamanda. Koma mtsikanayo, akukhalabe wolimba pa chikondi chake chomwe ali nacho pa m’busayo. Pomaliza Solomo akumulola kupita kwawo.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

4:1; 6:5—N’chifukwa chiyani tsitsi la namwaliyu likuyerekezeredwa ndi “gulu la mbuzi”? Akuliyerekezera motero mwina chifukwa chakuti tsitsi lake linali lonyezimira ndiponso lambiri ngati ubweya wakuda wa mbuzi.

4:11—Kodi mawu akuti ‘milomo yokha uchi’ ya Msulami ndiponso ‘uchi ndi mkaka zili pansi pa lilime lake,’ akutanthauza chiyani? Chisa cha uchi chimakhala chokoma ndiponso chotsekemera kuposa uchi umene wapita mphepo. Kufanizira kumeneku, komanso mfundo yoti uchi ndi mkaka zinali pansi pa lilime la namwaliyu, zimatsindika kuti Msulamiyo analankhula mawu abwino kwambiri.

5:12—Kodi Mawu akuti “ana a maso ake akunga nkhunda pambali pa mitsinje ya madzi; otsukidwa ndi mkaka,” amatanthauza chiyani? Namwaliyu akulankhula za maso okongola a bwenzi lake lokondeka. Mwina mwandakatulo akuyerekezera mbali yodera ya maso imene imazunguliridwa ndi mbali yoyera ya maso a bwenzi lakelo ndi nkhunda zodera zimene zikusamba mu mkaka.

5:14, 15—N’chifukwa chiyani manja ndi miyendo ya m’busayu ikulongosoledwa motere? Namwaliyu mwachionekere akuyerekezera zala za m’busayu ngati zing’anda zagolidi ndipo zikhadabo zake ngati krustalo. Akuyerekezera miyendo yake ndi “zoimiritsa za mwala wonyezimira” chifukwa ndi yamphamvu ndi yokongola.

6:4—N’chifukwa chiyani namwaliyu akuyerekezeredwa ndi “Tiriza”? Mzinda wa Akanani umenewu unagonjetsedwa ndi Yoswa ndipo pambuyo pa nthawi ya Solomo unakhala likulu loyambirira la ufumu wa kumpoto wa Isiraeli wa mafuko khumi. (Yoswa 12:7, 24; 1 Mafumu 16:5, 6, 8, 15) Buku lina limati: “Zikuoneka kuti mzinda umenewu uyenera kuti unali wokongola kwambiri, n’chifukwa chake pano anautchula.”

6:13—Kodi “Masewero akuguba” n’chiyani? Mawu amenewa angatanthauzenso “gule wa Mahanaimu.” Mzinda umene unkatchedwa ndi dzina limenelo unali mbali yakum’mawa kwa mtsinje wa Yorodano pafupi ndi chigwa cha Yaboki. (Genesis 32:2, 22; 2 Samueli 2:29) “Masewero akuguba” angatanthauze gule wina wake amene ankachitika mu mzinda umenewo makamaka pa madyerero.

7:4—N’chifukwa chiyani Solomo akuyerekezera khosi la Msulami ndi “nsanja ya minyanga”? Poyamba, mtsikanayo anatamandidwa motere: “Khosi lako likunga nsanja ya Davide.” (Nyimbo ya Solomo 4:4) Nsanja imakhala yaitali ndiponso yowonda, ndipo minyanga imakhala yosalala. Choncho Solomo anachita chidwi ndi kuwonda ndiponso kusalala kwa khosi la mtsikanayo.

Zimene Tikuphunzirapo:

4:1-7. Mwa kukana mawu okopa a Solomo, Msulamiyo, ngakhale anali wopanda ungwiro, anasonyeza kuti analibe khalidwe loipa. Choncho khalidwe lake labwino linawonjezera kukongola kwake. Ndi mmenenso akazi achikhristu ayenera kukhalira.

4:12. Monga munda wokongola womwe watchingidwa ndi mpanda, ndipo kuti munthu alowemo ayenera kulowera pa chipata chomwe chimakhala chokhoma, Msulamiyo anasonyeza chikondi chake pa mnyamata yekhayo amene adzakhale mwamuna wake. Chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwa akazi ndi amuna achikhristu osakwatiwa kapena kukwatira.

“MPHEZI YA YEHOVA”

(Nyimbo ya Solomo 8:5-14)

“Ndaniyu achokera kuchipululu, alikutsamira bwenzi lake?” anafunsa motero achimwene ake a Msulamiyo atamuona akubwerera kunyumba. Poyamba mmodzi mwa achimwene akewo anati: “Ngati ndiye khoma, tidzamanga pa iye nsanja yasiliva: ngati ndiye chitseko tidzam’tsekereza ndi matabwa amikungudza.” Tsopano popeza kuti chikondi cha Msulamiyu chayesedwa ndi kutsimikiziridwa kuti n’chosatha, iye anati: “Ndine khoma, mawere anga akunga nsanja zake: pamaso pa mnyamatayo ndinafanana ngati wopeza mtendere.”​—Nyimbo ya Solomo 8:5, 9, 10.

Chikondi chenicheni ndi “mphezi ya Yehova.” Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti chikondi choterocho chimachokera kwa Yehova. Iye ndi amene anatipatsa mtima wachikondi. Chikondi ndicho mphezi imene kung’anima kwake n’kosatha. Nyimbo ya Solomo imasonyeza bwino kuti chikondi cha pakati pa mkazi ndi mwamuna chingakhale ‘cholimba [chosalephera] ngati imfa.’​—Nyimbo ya Solomo 8:6.

Nyimbo yoposa ya Solomo imatiunikiranso za m’gwirizano umene ulipo pakati pa Yesu Khristu ndi anthu amene ali m’gulu la “mkwatibwi” wake wa kumwamba. (Chivumbulutso 21:2, 9) Chikondi cha Yesu pa Akhristu odzozedwa, chimaposa chikondi chilichonse cha pakati pa mwamuna ndi mkazi. Anthu amene ali m’gulu la mkwatibwi sagonja pa chikondi chawo. Yesu mwachikondi anafera ngakhale a gulu la “nkhosa zina.” (Yohane 10:16) Choncho, olambira onse oona, angatsanzire chitsanzo cha Msulami mwa kukhala ndi chikondi cholimba ndiponso kukhala odzipereka.

[Chithunzi pamasamba 18, 19]

Kodi Nyimbo ya Solomo ikutiphunzitsa kuyang’ana chiyani mwa munthu amene tikufuna kukwatirana naye?