Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu Kupereka Ndemanga

Phunzitsani Ana Anu Kupereka Ndemanga

Phunzitsani Ana Anu Kupereka Ndemanga

PERLA yemwe amakhala ku Mexico akukumbukira kuti pamene anali mwana, amayi ake ankamuthandiza kukonzekera ndemanga zifupizifupi pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Tsopano Perla ali ndi mwana wamwamuna wa zaka zisanu. Kodi amamuthandiza bwanji mwana wakeyo? “Poyamba ndimakonzekera kaye. Ndikatero, ndimapeza ndime imene mwana wangayo angathe kumvetsa, ndiponso imene angathe kulongosola m’mawu akeake. Kenako timangokambirana za ndime imene iye amati ‘ndime yanga.’ Ndimamuuza kuti ailongosole pogwiritsa ntchito zitsanzo za zinthu zimene zimachitika nthawi zonse. Kenako timayeserera ndemangayo kambirimbiri. Timagwiritsa ntchito chinthu chilichonse chofanana ndi maikolofoni n’cholinga choti adziwe mmene angakagwirire maikolofoniyo popereka ndemanga. Ndine wosangalala kwambiri kuti msonkhano uliwonse sudutsa iye osapereka ndemanga kapena kukweza dzanja lake. Nthawi zambiri, amapita kwa amene akuchititsa msonkhanowo, misonkhano isanayambe n’kuwauza ndime imene akufuna kuyankha.”

Jens, yemwe ndi mkulu amene akutumikira gulu la anthu olankhula Chihindi, ali ndi ana aamuna awiri, wina ali ndi zaka ziwiri ndipo winayo zinayi. Iye ndi mkazi wake akamakonzekera misonkhano ndi ana awowo, amagwiritsa ntchito njira imene Jens anaphunzira kwa makolo ake. Iye anati: “Timaganiza za mbali imene anawo angamvetse bwino. Kenako timayesa kuwalongosolera mwachidule zimene nkhaniyo ikunena kapena mfundo zikuluzikulu za nkhaniyo, ndipo timawafunsa mafunso amene tikufuna kuti akayankhe pa msonkhano. Kawirikawiri timadabwa ndi ndemanga zochokera pansi pa mtima zimene amapereka. Kuyankha kwawo kumasonyezadi kuti akumvetsa. Zotsatira zake n’zakuti, ndemanga zawo zimatamandadi Yehova ndiponso zimasonyeza chikhulupiriro chawo.”