Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sukulu Imene Ophunzira Ake Amathandiza Anthu Padziko Lonse

Sukulu Imene Ophunzira Ake Amathandiza Anthu Padziko Lonse

Sukulu Imene Ophunzira Ake Amathandiza Anthu Padziko Lonse

MU MIPINGO yoposa 98,000 ya Mboni za Yehova yomwe ili m’mayiko oposa 200, anthu a mitundu yonse akuphunzitsidwa ndi Mulungu. Amaphunzira Baibulo, ndipo cholinga cha maphunzirowo n’kuthandiza anthu kuti apite patsogolo mwauzimu mwa kuphunzira za chifuniro cha Mulungu ndiponso mmene angakhalire ndi moyo mogwirizana ndi chifunirocho. Anthu amene amapita ku maphunziro amenewa amapindula kwambiri. Zimene amaphunzirazo, amauzanso anzawo, mogwirizana ndi malangizo a Yesu Khristu kwa atumwi ake.​—Mateyo 28:19, 20.

Kuwonjezera pa maphunziro amene amakhalapo nthawi zonse ku mipingo yawo, Mboni za Yehova zakhazikitsa sukulu zapadera. Imodzi mwa sukulu zimenezi ndi Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Sukuluyi anaitsegulira mu October 1987, ku Pittsburgh, Pennsylvania, m’dziko la United States. Kalasi loyamba linali ndi ophunzira 24 olankhula Chingelezi. Kuyambira nthawi imeneyo, maphunzirowa akhala akuchitika m’zinenero 21, m’mayiko 43. Padakali pano, akulu ndi atumiki othandiza osakwatira, ochokera m’mayiko oposa 90, alowa nawo sukuluyi. Ophunzirawo akamaliza maphunziro a masabata asanu ndi atatu amenewa, amatumizidwa kukatumikira kumene kukufunika atumiki ambiri, kaya m’dziko lawo lomwelo kapena m’dziko lina. Pomafika kumapeto kwa 2005, atumiki achikhristu oposa 22,000 anali atamaliza maphunziro a kusukulu imeneyi. Iwo adalitsidwa kwambiri chifukwa cha kuyesetsa kwawo modzichepetsa kuti apititse patsogolo zinthu za Ufumu ndiponso kuthandiza anthu ena.​—Miyambo 10:22; 1 Petulo 5:5.

Kukonzekera Kupita ku Sukuluyi

Pofuna kuti akapezeke ku Sukulu Yophunzitsa Utumikiyi, ophunzira ambiri amafunika kupempha tchuti ku ntchito yawo yolembedwa. Koma zimenezi nthawi zina zimakhala zovuta. Akhristu awiri a ku Hawaii, amene anaitanidwa kuti apite kusukuluyi anafunika kupempha tchuti ku ntchito yawo yauphunzitsi. Ali ndi chikhulupiriro choti zitheka, iwo anapereka kalata zawo zopempha tchuti, ndipo analongosola chifukwa chake ankafuna kupita kusukuluyo ndiponso mmene idzawathandizire. Onse awiri analoledwa kupita.

Nthawi zina, Mboni zomwe zinapempha tchuti kuti zikapezeke ku sukuluyi, zinauzidwapo kuti zikangopita, azichotsa ntchito. Izo zinasankha kukaphunzitsidwa ndi gulu la Yehova, ngakhale kuti kuchita zimenezo kunatanthauza kuti ntchito yawathera. Ena mwa anthu amenewa analandiranso kalata zochokera kwa mabwana awo, zowaitana kuti akamaliza sukuluyo, akayambenso ntchito. Kulimba mtima kotero pofuna kukapezeka ku sukuluyi tingakulongosole mwachidule motere: Perekani kalata yanu yopempha tchuti kwa abwana anu, pempherani kuti Yehova akuthandizeni, ndipo dikirani kuti Yehovayo achite mbali yotsalayo.​—Salmo 37:5.

‘Kuphunzitsidwa ndi Yehova’

Kusukulu imeneyi, amaphunzira Baibulo mozama kwambiri kwa masabata onse asanu ndi atatu amene sukuluyi imachitika. Amaphunzira za mmene anthu a Yehova alili gulu lochita chifuniro cha Mulungu. Amaphunziranso mmene iwowo angagwiritsire ntchito bwino Baibulo mu utumiki wa kumunda, pamisonkhano ya mpingo, ndi pamisonkhano ikuluikulu.

M’bale wina amene anamaliza maphunziro a kusukuluyi anaiyamikira kwambiri. Polemba kalata kwa m’bale wina amene anali asanapitebe ku sukulu yomweyi anati: “Ndikukuuza, udzalandira maphunziro abwino kwambiri kuposa ena onse amene unaphunzirapo. Udzamvetsa tanthauzo la lemba limene limanena za ‘kuphunzitsidwa ndi Yehova.’ Maphunziro ake amaumba ndi kuyenga mtima ndipo amathandiza kuti munthu atsanzire kwambiri chitsanzo cha Khristu Yesu. Zimene mukaphunzire kusukulu imeneyi zidzaposa zonse zimene mukuzidziwa panopa.”​—Yesaya 54:13.

Alaliki, Abusa, ndi Aphunzitsi

Padakali pano, anthu omwe anamaliza maphunziro ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki akutumikira m’mayiko 117. Ena mwa mayiko amenewa ndi zilumba za panyanja ya Atlantic, Caribbean, ndi Pacific ndiponso m’mayiko ambiri omwe muli maofesi a nthambi a Mboni za Yehova. Maofesi a nthambi anenapo kuti ophunzirawo amakhala achangu pantchito yolalikira, yaubusa, ndi yophunzitsa, chifukwa cha maphunziro abwino amene amaphunzira kusukuluyi. Maphunzirowo amawathandiza kuti azigwiritsa ntchito Baibulo mwaluso kwambiri mu utumiki wa kumunda. (2 Timoteyo 2:15) Akamayankha mafunso amene mwininyumba wafunsa, iwo kawirikawiri amagwiritsa ntchito buku la Kukambitsirana za m’Malemba * ndipo amaphunzitsanso ofalitsa Ufumu ena kuchita chimodzimodzi. Ena amatsanzira changu chawo, ndipo utumiki wawo umathandiza mipingo kukhala yolimba.

Akulu a mpingo ali ndi mwayi ‘woweta gulu la nkhosa,’ kuthandiza kusamalira zosowa zawo zauzimu. (1 Petulo 5:2, 3) Mkulu wina anati: “Tikuyamikira makonzedwe a ofesi ya nthambi omatitumizira abale ophunzitsidwa bwino kuti azitithandiza kunyamula katundu woweta gulu la nkhosa za Mulungu.” Nthambi ya dziko lina la kum’mawa kwa Asia inati: “Ophunzirawa ndi anthu achifundo kwambiri. Amagwira ntchito molimbika ndipo mpingo umawalemekeza. Amadziwika bwino ndi kudzichepetsa kwawo, chikondi chawo, ndi changu chawo, ndipo amayamikiridwa chifukwa cha zimenezi. Iwo amakhala odzimana mwa kufuna kwawo ndipo amakhala okondwa kusamukira ku mipingo imene ikufuna abusa.” (Afilipi 2:4) Amuna amenewa amalimbikitsa okhulupirira anzawo, ndipo ayenera kuyamikiridwa.​—1 Akorinto 16:18.

Kuwonjezera apo, alangizi a ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki amathandiza ophunzirawo kuwonjezera luso lawo lolankhula pagulu. Akamagwiritsa ntchito malangizo ndi uphungu woperekedwa ku sukuluyi, ambiri mwa ophunzirawo posapita nthawi amayamba kupatsidwa nkhani za pamisonkhano yadera ndiponso yachigawo. Woyang’anira dera wina anaona kuti anthu omwe anapita ku sukuluyi “amakamba bwino nkhani ndiponso amapereka zifukwa zomveka pofotokoza mfundozo.”​—1 Timoteyo 4:13.

M’dziko lina la mu Africa muno, kaphunzitsidwe ka pamisonkhano ya mpingo kanasintha n’kukhala kabwino kwambiri, itangochitika Sukulu Yophunzitsa Utumiki m’dzikolo ndiponso ophunzira ake atangotumizidwa ku mipingo. Akulu otumizidwa kuchokera ku sukuluyi akuthandiza pantchito yolalikira, yaubusa, ndi yophunzitsa, ndipo mipingo ikulimba mwauzimu.​—Aefeso 4:8, 11, 12.

Ntchito Yoyang’anira Mipingo Yapita Patsogolo

M’mipingo yambiri mukufunika akulu ndi atumiki othandiza ochuluka. Mipingo inanso sikanakhala n’komwe ndi akulu kupanda kutumizako omaliza maphunziro a ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Choncho, ophunzira ambiri amatumizidwa kuti akatumikire kumene kukufunika thandizo.

Nthambi zambiri zimanena kuti amuna amenewa “amadziwa bwino makonzedwe a gulu,” “amachita utumiki wawo kuchokera pansi pa mtima,” “amathandiza ena kuti ayamikire ndi kulemekeza gulu la Yehova,” ndipo “amathandiza kuti mipingo ikhale yachikondi ndiponso ikule mwauzimu.” Zimenezi zimatheka chifukwa ophunzirawo amatsatira zimene zalembedwa m’Mawu a Mulungu ndipo sadalira luntha lawo kapena nzeru zawo. (Miyambo 3:5-7) Amuna amenewa amakhaladi dalitso lauzimu ku mipingo yomwe akutumikira.

Kutumikira ku Magawo Akutali

Ena mwa ophunzirawa amakhala apainiya apadera omwe amakathandiza magulu akutali kuti akhale mipingo. Poyamikira thandizo la apainiyawo, mkulu wina wa m’dera lakutali ku Guatemala anati: “Kwa zaka 20 ndinali ndi nkhawa yoti kodi gawo lathu lalikululi tingalisamalire bwanji. Kawirikawiri ndinali kupempherera nkhani imeneyi. Abale amene anamaliza Sukulu Yophunzitsa Utumikiyi ndi ophunzitsidwa bwino kulankhula ndiponso kulinganiza zinthu, ndipo ndikuyamikira kuona kuti tsopano dera limeneli likusamalidwa mwachikondi.”

Anthu omaliza sukuluyi aphunzira kukhala othandiza kwambiri m’gawo lawo, mmene amayenda maulendo ataliatali kudutsa m’dera la mapiri kuti akafike m’midzi ing’onoing’ono yotalikirana. Mwachangu, iwo amayambitsa ndi kukhazikitsa magulu akutali, ngakhale kuti ena sanachitepo zimenezo. Mwachitsanzo, mkulu wina ku Niger anapempha thandizo la abale omaliza sukuluyi chifukwa anadziwa kuti abalewo angagwire ntchito yotamandika kudera lomwe anali kukhala. Makamaka m’madera akutali, zingakhale zosavuta kwa abale osakwatira kutumikira monga apainiya apadera ndiponso oyang’anira madera. Mofanana ndi mtumwi Paulo, iwo ayenera kulimbana ndi ‘zoopsa za m’mitsinje ndi achifwamba pamsewu, zoopsa m’chipululu,’ ndi mavuto awo, ngakhalenso nkhawa imene amakhala nayo pa mipingo imene akutumikira.​—2 Akorinto 11:26-28.

Kuthandiza Achinyamata

Malemba amalimbikitsa achinyamata kukumbukira Mlengi wawo. (Mlaliki 12:1) Abale achangu omaliza maphunziro a ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki amakhala zitsanzo zabwino kwa anyamata achikhristu. Abale awiri amene anamaliza sukuluyi atangofika mu mpingo wina ku United States, chiwerengero cha nthawi yonse imene abale amathera mu utumiki chinawirikiza kawiri. Kuwonjezera apo, chiwerengero cha apainiya okhazikika, kapena kuti olengeza Ufumu anthawi zonse, chinawonjezeka kuchoka pa awiri kufika pa 11. Izi ndi zomwe zachitika m’mipingo yambiri.

Ophunzirawo amalimbikitsanso abale achinyamata kuti aganizire zodzapita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Zimenezi zathandiza anthu ena amene sanakhalebe atumiki othandiza kuyamba kuyesetsa kuti ayenerere kukhala atumiki othandiza. Nthambi ya ku Netherlands imati, abale amene anamaliza Sukulu Yophunzitsa Utumiki ndi “zitsanzo zooneka kwa abale achinyamata amene akusinkhasinkha za zochita pamoyo wawo.”

Kutumikira M’mipingo ya Chinenero China

M’mayiko ambiri, ntchito yolalikira uthenga wabwino kwa anthu m’chinenero chawo chobadwira ikupita patsogolo. Kawirikawiri abale amene anamaliza Sukulu Yophunzitsa Utumiki amaphunzira zinenero zina n’kukatumikira m’madera amene muli anthu ambiri ochokera ku mayiko ena. Mwachitsanzo, ku Belgium kukufunika alaliki a Ufumu ambiri kuti azilalikira m’madera amene muli anthu olankhula Chiabaniya, Chiperisiya, ndi Chirasha.

Mipingo ndi magulu azinenero zina a ku Britain, Germany, Italy, Mexico, ndi United States, ndi m’mayiko ena, akupindula kwambiri chifukwa cha oyang’anira oyendayenda, akulu, ndi atumiki othandiza amene anamaliza Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Nthambi ya ku Korea inanena kuti “abale omaliza sukuluyi oposa 200 akugwira ntchito yotamandika pothandiza mipingo ndi magulu achinenero china.”

Kugwira Ntchito Zina Modzichepetsa

Kuwonjezera pa kutumikira m’mipingo ndi magulu achinenero china, abale amene anamaliza Sukulu Yophunzitsa Utumikiyi amatumikiranso monga akulu, atumiki othandiza, ndi oyang’anira oyendayenda. Ena amatumizidwa kukatumikira ku mayiko ena, mwina mu Dipatimenti ya Utumiki ya panthambi ngati pakufunika atumiki mwamsanga. Abale ena amene ali ndi luso la zomangamanga angagwire nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu.

Chifukwa choti mipingo ndiponso madera akuchuluka kwambiri padziko lonse lapansi, oyang’anira oyendayenda ambiri akufunikanso. Pofuna kupeza amuna amenewa, abale ena amene anamaliza Sukulu Yophunzitsa Utumiki amasankhidwa n’kuphunzitsidwa kwa masabata khumi pokonzekera ntchito yoyendayenda, ndipo kenaka, amatumizidwa kukatumikira monga oyang’anira dera ogwirizira, kapena oyang’anira dera amene. Padakali pano, pafupifupi abale 1,300 amene anamaliza sukuluyi ndi oyang’anira oyendayenda m’mayiko oposa 97. M’dziko lina la mu Africa muno, oyang’anira dera 55 pa 100 alionse ndi oti anamaliza Sukulu Yophunzitsa Utumiki. M’dziko linanso la mu Africa mom’muno, chiwerengerochi chafika pa 70 mwa oyang’anira dera 100 alionse.

Anthu mazanamazana amene anamaliza sukuluyi ku Australia, Canada, Ulaya, mayiko ena a kum’mawa kwa Asia, ndi United States, atumizidwa ku mayiko ena kumene kukufunika thandizo. Mwanjira imeneyi, anthu a padziko lonse akupindula ndi sukulu imeneyi.

Kudzera mwa Mwana wake, Yesu Khristu, Yehova wadzutsa alaliki, abusa, aphunzitsi, ndi enanso amene akupititsa patsogolo zinthu za Ufumu m’masiku otsiriza ano. Kodi pali chiyembekezo chilichonse choti anthu a Mulungu adzapitirizabe kuwonjezereka? Inde, n’zodziwikiratu! Choncho, pakufunikabe amuna odzipereka kuti atumikire m’maudindo owonjezereka. (Yesaya 60:22; 1 Timoteyo 3:1, 13) Sukulu Yophunzitsa Utumiki imapatsa mwayi akulu ndi atumiki othandiza kuti akhale okonzeka kuchita zambiri mu utumiki wawo. Zimenezi zimawathandiza iwowo ndiponso anthu ena padziko lonse lapansi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Zithunzi patsamba 10]

Sukulu Yophunzitsa Utumiki ikupititsa patsogolo zinthu za Ufumu padziko lonse

[Zithunzi patsamba 13]

Kodi mukuganiza zodzapita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki kuti nanunso mudzathandize anthu ena?