Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kondani Mulungu Amene Amakukondani

Kondani Mulungu Amene Amakukondani

Kondani Mulungu Amene Amakukondani

“Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.”​—MATEYO 22:37.

1, 2. Kodi zikuoneka kuti n’chiyani chinachititsa kuti Afarisi afunse funso lonena za lamulo lalikulu koposa m’Chilamulo?

FUNSO limene anafunsa likuoneka kuti linali lovuta kwambiri pakati pa Afarisi a m’nthawi ya Yesu. Kodi pa malamulo oposa 600 amene anali m’Chilamulo cha Mose, ndi liti limene linali lofunika koposa? Kodi linali lamulo lokhudzana ndi zopereka nsembe? Chifukwatu anthu ankapereka nsembe kuti akhululukidwe machimo komanso kuti athokoze Mulungu. Kapena kodi lamulo lofunika koposa linali lokhudza mdulidwe? Mdulidwe nawo unali nkhani yofunika chifukwa choti unali chizindikiro cha pangano la pakati pa Yehova ndi Abrahamu.​—Genesis 17:9-13.

2 Koma panalinso anthu ena osafuna kusintha chilichonse pankhaniyi. Zikuoneka kuti iwo ankaganiza kuti n’kulakwa kukweza lamulo linalake kuti likhale lofunika kuposa malamulo onse, chifukwa choti lamulo lililonse limene Mulungu anapereka linali lofunika, ngakhale kuti ena ankaoneka ngati osafunika kwenikweni. Afarisi anaganiza zofunsa Yesu funso lovutali. Ankaganiza kuti mwina yankho lake likanachititsa kuti anthu asiye kum’khulupirira. Ndiye mmodzi wa Afarisiwo anafika pamene panali Yesu n’kumufunsa kuti: “Kodi lamulo lalikulu koposa m’Chilamulo ndi liti?”​—Mateyo 22:34-36.

3. Kodi Yesu anati lamulo lofunikira koposa onse ndi liti?

3 Yankho limene Yesu anapereka n’lofunika kwambiri kwa ifeyo masiku ano. Muyankholo iye anatchulamo mwachidule mfundo yaikulu kwambiri ya kulambira koona, kuyambira kale mpaka panopo. Pogwira mawu lemba la Deuteronomo 6:5, Yesu anati: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu koposa komanso loyamba.” Ngakhale kuti Mfarisiyo anangofuna kudziwa lamulo limodzi lokha, Yesu anamuuza linanso. Pogwira mawu Levitiko 19:18, iye anati: “Lachiwiri, lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.’” Kenaka Yesu anasonyeza kuti kulambira koona kwagona pa malamulo awiriwa. Pofuna kuti asam’funse zoti andandalike malamulo onse otsalawo malingana n’kufunika kwawo, Yesu anatsiriza ndi mawu akuti: “Chilamulo chonse chagona pa malamulo awiri amenewa, kuphatikizaponso Zolemba za aneneri.” (Mateyo 22:37-40) M’nkhani ino, tifotokoza lamulo lofunika kwambiri pa malamulo awiri aja. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda Mulungu? Kodi timasonyeza bwanji zoti timam’konda? Ndipo kodi tingatani kuti tikhale ndi chikondi chimenechi? Kudziwa mayankho a mafunso amenewa n’kofunika kwambiri chifukwa choti, kuti tisangalatse Yehova tiyenera kum’konda ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, komanso maganizo athu onse.

Kufunika kwa Chikondi

4, 5. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Mfarisi sanadabwe ndi zimene Yesu ananena? (b) Kodi n’chiyani chimene Mulungu amaona kuti n’chofunika kuposa nsembe zosiyanasiyana?

4 Zikuoneka kuti Mfarisi amene anafunsa Yesu funso limeneli sanakhumudwe kapena kudabwa ndi yankholo. Iye ankadziwa kuti kukonda Mulungu ndi mbali yofunika ya kulambira koona, ngakhale kuti ambiri sankatero. M’masunagoge, anthu ambiri anali ndi chizolowezi chonena mokweza pemphero lotchedwa Shema, kapena kuti pemphero la chikhulupiriro, ndipo mawu ena m’pempheroli anali mawu opezeka pa Deuteronomo 6:4-9, pomwe Yesu anagwirapo mawu ake ena. Nkhani ya m’buku la Maliko imati kenaka Mfarisiyo anamuuza Yesu kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino mogwirizana ndi choonadi, ‘Iye ndi Mmodzi, ndipo palibenso wina koma Iye yekha’; kunena za kum’konda ndi mtima wonse, ndi kumvetsa konse, ndi mphamvu zonse, komanso kukonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha, n’zofunika kwambiri kuposa nsembe zonse zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.”​—Maliko 12:32, 33.

5 Inde, ngakhale kuti m’Chilamulo anthu ankayenera kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zina, kwa Mulungu chinthu chofunika kwambiri ndicho mtima wachikondi womwe atumiki ake ali nawo. Mpheta imene munthu wapereka kwa Mulungu chifukwa cha chikondi chake ndi kudzipereka kwake inali yofunika kwambiri kwa iye kuposa nkhosa zazimuna zambirimbiri. (Mika 6:6-8) Kumbukirani nkhani ya mayi wosauka wamasiye amene Yesu anamuona m’kachisi ku Yerusalemu. Makobili awiri aang’ono amene iye anapereka moponya zopereka sakanatha kugula ngakhale mpheta imodzi. Komatu Yesu anaona kuti ndalama zimenezi, zomwe mayiyu anazipereka chifukwa chokonda Yehova ndi mtima wake wonse, zinali zofunika kwambiri kuposa ndalama zambirimbiri zimene anthu olemera anapereka kuchokera pa chuma chawo chambirimbiri. (Maliko 12:41-44) N’zolimbikitsatu kwambiri kudziwa kuti chinthu chimene Yehova amaona kuti n’chofunika kwambiri ndicho kum’konda iyeyo, ndipotu tonsefe tingathe kukwanitsa kusonyeza kuti timam’konda ngakhale zinthu zitakhala bwanji m’moyo wathu.

6. Kodi Paulo analemba chiyani pa nkhani ya kufunika kwa chikondi?

6 Pogogomezera kufunika kwa chikondi pa kulambira koona, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati ndilankhula malilime a anthu ndi a angelo koma ndilibe chikondi, ndikhala ngati belu longolira, kapena chinganga chosokosera. Ndipo ngati ndili ndi mphatso yonenera, yodziwa zinsinsi zonse zopatulika, yodziwa zinthu zonse, komanso ngati ndili ndi chikhulupiriro chonse chokhoza kusuntha nacho mapiri, koma ndilibe chikondi, sindili kanthu. Ndipo ngati ndipereka zanga zonse kudyetsa ena, ndipo ngati ndipereka thupi langa kuti ndidzitame, koma ndilibe chikondi, sindinapindule m’pang’ono pomwe.” (1 Akorinto 13:1-3) Apatu n’zoonekeratu kuti chikondi n’chofunika kuti tizilambira Mulungu mom’sangalatsa. Komano kodi timasonyeza bwanji kuti Yehova timam’konda?

Mmene Timasonyezera Kukonda Yehova

7, 8. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova?

7 Anthu ambiri amakhulupirira kuti chikondi ndi chinthu chimene sitingathe kuchilamulira. Amati winawake wawadolola kapena wawazunguza mutu chifukwa chomukonda. Komatu, chikondi chenicheni sichimangotanthauza mmene tikumvera ayi. Chimadziwika ndi zochita osati kungokopeka mtima. Baibulo limati chikondi ndi “njira yopambana” ndipo limati ndi khalidwe limene tiyenera ‘kuyesetsa’ kukhala nalo. (1 Akorinto 12:31; 14:1) Limalimbikitsa Akhristu kuti azikonda ena, osati chabe “ndi mawu okha kapena ndi lilime lokha, koma mwa zochita ndi choonadi.”​—1 Yohane 3:18.

8 Kukonda Mulungu kumatilimbikitsa kuti tizichita zinthu zom’sangalatsa ndiponso kuteteza ndi kuikira kumbuyo ulamuliro wake pa zolankhula ndi zochita zathu. Kumatithandiza kupewa kukonda dziko ndi njira zake zoipa. (1 Yohane 2:15, 16) Anthu amene amakonda Mulungu amadana ndi zoipa. (Salmo 97:10) Kukonda Mulungu kumatanthauzanso kukonda mnansi wathu, ndipo tilongosola zimenezi m’nkhani yotsatira. Komanso kukonda Mulungu kumatanthauza kuti tizimumvera. Baibulo limati: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake.”​—1 Yohane 5:3.

9. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amakonda Mulungu?

9 Yesu anasonyeza ndendende zimene kukonda Mulungu kumatanthauza. Chifukwa cha chikondi, iye anachoka kwawo kumwamba n’kudzakhala padziko pano ngati munthu. Chikondi chinam’chititsa kupereka ulemerero kwa Atate wake mwa zochita zake ndi zophunzitsa zake. Chifukwa cha chikondi iye ‘anakhala womvera mpaka imfa.’ (Afilipi 2:8) Kumvera kumeneku, komwe kumasonyeza chikondi chake, kunatsegula njira kwa anthu okhulupirika kuti akhale olungama pamaso pa Mulungu. Paulo analemba kuti: “Mwa kusamvera kwa munthu mmodziyo [Adamu] ambiri anakhala ochimwa, momwemonso kudzera mwa kumvera kwa munthu mmodziyu [Khristu Yesu] ambiri adzakhala olungama.”​—Aroma 5:19.

10. N’chifukwa chiyani kukonda Mulungu kumatanthauzanso kukhala womvera?

10 Monga Yesu, ifenso timasonyeza kuti timakonda Mulungu pomumvera. Yohane, mtumwi wokondedwa wa Yesu analemba kuti: “Chikondi chimenechi chimatanthauza kuti tiziyendabe motsatira malamulo ake.” (2 Yohane 6) Anthu amene amakondadi Yehova amafunitsitsa kumvera malangizo ake. Iwo amadziwa kuti sangathe kulongosola mapazi awo pawokha, motero amadalira nzeru za Mulungu ndi kumugonjera akamawalangiza mwachikondi. (Yeremiya 10:23) Iwowo amachita zimene anachita anthu a maganizo apamwamba a ku Bereya amene analandira uthenga wa Mulungu “ndi chidwi chachikulu,” chifukwa anali ofunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu.” (Machitidwe 17:11) Iwo anafufuza Malemba mosamala kuti amvetse bwinobwino chifuniro cha Mulungu, chomwe chinawathandiza kuti asonyeze chikondi pokhala omvera m’njira zinanso.

11. Kodi kukonda Mulungu ndi mtima wathu wonse, maganizo athu onse, moyo wathu wonse, komanso mphamvu zathu zonse kumatanthauza chiyani?

11 Monga ananenera Yesu, kukonda Mulungu kumatanthauza kum’konda ndi mtima wathu wonse, maganizo athu onse, moyo wathu wonse, ndi mphamvu zathu zonse. (Maliko 12:30) Chikondi choterechi chimachokera mumtima, ndipo chimakhudza mmene tikumvera, zolakalaka zathu, komanso zakukhosi kwathu, ndipo timakhala ofunitsitsa kusangalatsa Yehova. Timakondanso Mulungu ndi maganizo athu. Sitidzipereka kwa iye m’chimbulimbuli, chifukwa timakhala titam’dziwa Yehovayo, makhalidwe ake, miyezo yake, ndi zolinga zake. Timagwiritsira ntchito moyo wathu wonsewu pom’tumikira ndi kum’tamanda. Ndipo timagwiritsanso ntchito mphamvu zathu m’njira yomweyi.

Chifukwa Chimene Tiyenera Kukondera Yehova

12. N’chifukwa chiyani Mulungu amafuna kuti tizim’konda?

12 Chifukwa chimodzi chimene tiyenera kukondera Yehova n’chakuti iye amafuna kuti tizisonyeza makhalidwe ake. Mulungu ndiye gwero komanso chitsanzo chachikulu kwambiri cha chikondi. Mouziridwa, mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Anthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu; tinalengedwa kuti tizitha kusonyeza chikondi. Ndipotu ulamuliro wa Yehova n’ngozikidwa pa chikondi. Iye amasangalala ndi anthu okhawo amene amam’tumikira chifukwa chokonda ndiponso kusangalala ndi kalamuliridwe kake ka chilungamo. Inde, chikondi n’chofunika kuti chilengedwe chonse chikhale mwamtendere ndiponso mogwirizana.

13. (a) N’chifukwa chiyani Aisiraeli anauzidwa kuti: ‘Muzikonda Yehova Mulungu wanu’? (b) N’chifukwa chiyani m’pomveka kuti Yehova amafuna kuti tizim’konda?

13 Chifukwa china chokondera Yehova n’chakuti timayamikira zimene watichitira. Kumbukirani kuti Yesu anauza Ayuda kuti: ‘Muzikonda Yehova Mulungu wanu.’ Sanali kufuna kuti iwo azikonda mulungu winawake wosadziwika, wokhala kutali ndi iwowo. Ayi, ankafunikira kukonda Mulungu amene anawasonyeza chikondi chake. Yehova ndiye anali Mulungu wawo. Iye ndiye anawatulutsa ku Iguputo n’kuwapititsa ku Dziko Lolonjezedwa, ndiye ankawateteza, kuwasamalira, ndi kuwakonda, ndipo ndiye ankawalanga mwachikondi. Masiku anonso, Yehova ndiye Mulungu wathu, ndiye anapereka nsembe mwana wake kuti tikhale ndi moyo wosatha. Mpaketu kuti Yehova amafuna kuti nafenso tizim’konda. Chikondi chathu n’chobwezera, chifukwa tikupemphedwa kukonda Mulungu amene amatikonda. Timakonda Mulungu amene “anayamba ndi iye kutikonda.”​—1 Yohane 4:19.

14. Kodi chikondi cha Yehova chili ngati chikondi cha kholo m’njira yotani?

14 Tingayerekezere mmene Yehova amakondera anthu ndi mmene kholo lachikondi limakondera ana ake. Ngakhale kuti n’ngopanda ungwiro, makolo okonda ana awo amavutika kwa zaka zambirimbiri posamalira ana awo, ndipo potero amawononga chuma chambiri ndi zinthu zinanso zambiri. Makolo amaphunzitsa, kulimbikitsa, kuthandiza, ndi kulangiza ana, chifukwa choti amafuna kuti anawo azisangalala ndi kukula bwino. Koma kodi makolo amafuna kuti anawo awachitire chiyani pobwezera zimenezi? Amafuna kuti anawo aziwamvera ndi kutsatira malangizo awo opindulitsa. Motero kodi si pomveka kuti Atate wathu wakumwamba amafuna kuti tiziyamikira zinthu zonse zimene watichitira?

Zimene Tingachite Kuti Tizikonda Mulungu

15. Kodi n’chiyani chimene timayambira kuchita ngati tikufuna kukonda Mulungu?

15 Sitinaonepo Mulungu kapena kumva mawu ake. (Yohane 1:18) Komatu iye akutiitana kuti tikhale mabwenzi ake. (Yakobe 4:8) Kodi tingatero m’njira yotani? Kuti tikonde munthu wina aliyense timayamba ndi kum’dziwa, chifukwatu n’zovuta kukonda kwambiri munthu amene sitikum’dziwa. Yehova watipatsa Mawu ake, Baibulo, kuti tiphunzire za iye. N’chifukwa chake Yehova, kudzera m’gulu lake, amatilimbikitsa kuwerenga Baibulo nthawi zonse. Baibulo ndilo limatiphunzitsa za Mulungu, makhalidwe ake, umunthu wake, komanso zimene wakhala akuchita ndi anthu kwa zaka masauzande ambiri zapitazo. Tikamasinkhasinkha nkhani zimenezi, timayamba kumumvetsa ndi kumukonda kwambiri.​—Aroma 15:4.

16. Kodi kuganizira kwambiri utumiki wa Yesu kumatilimbikitsa bwanji kukonda Mulungu?

16 Njira yofunika kwambiri imene ingatithandize kuyamba kukonda kwambiri Yehova ndiyo kuganizira moyo ndi utumiki wa Yesu. Pajatu Yesu ankatsanzira Atate wake ndendende mpaka anafika ponena kuti, “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yohane 14:9) Kodi simukhudzidwa mtima mukaganizira za chifundo chimene Yesu anasonyeza poukitsa mwana wamwamuna wa mayi wamasiye uja? (Luka 7:11-15) Kodi si zosangalatsa kudziwa kuti Mwana wa Mulunguyu, yemwenso ali munthu woposa anthu onse amene anakhalako, anadzichepetsa n’kusambitsa mapazi a ophunzira ake? (Yohane 13:3-5) Kodi sizikukhudzani mtima kudziwa kuti ngakhale kuti Yesu anali munthu wamkulu ndiponso wanzeru koposa munthu wina aliyense, iye anali wosavuta kuti wina aliyense am’fikire, ngakhale ana? (Maliko 10:13, 14) Tikamasinkhasinkha zinthu zimenezi moyamikira, timakhala ngati Akhristu amene Petulo analemba za iwo kuti: “Ngakhale simunamuonepo [Yesu], mumam’konda.” (1 Petulo 1:8) Tikamakonda kwambiri Yesu, timayamba kukondanso kwambiri Yehova.

17, 18. Kodi ndi zinthu zotani zimene Yehova watipatsa mwachikondi zomwe pozisinkhasinkha zingatithandize kuti tizim’konda kwambiri?

17 Njira ina imene tingakondere kwambiri Yehova ndiyo kusinkhasinkha zinthu zambiri zimene iye watipatsa mwachikondi kuti tisangalale ndi moyo. Zinthu monga zachilengedwe zokongola, zakudya zambirimbiri zokoma, mabwenzi abwino otikonda, komanso zinthu zina zambirimbiri zosawerengeka zomwe zimatisangalatsa ndi kutikhutiritsa. (Machitidwe 14:17) Tikamadziwa zambiri zokhudza Mulungu, timakhalanso ndi zifukwa zambiri zoyamikira ubwino wake wopanda malire ndi kuwolowa manja kwake. Taganizirani zinthu zonse zimene Yehova wakuchitirani inuyo panokha. Kodi simukuvomereza kuti n’ngoyenera kuti muzim’konda?

18 Imodzi mwa mphatso zambiri za Mulungu ndi mwayi wom’fikira m’pemphero nthawi ina iliyonse, podziwa kuti iye ndi “Wakumva pemphero” motero amamva mapemphero athuwo. (Salmo 65:2) Yehova anapereka m’manja mwa Mwana wake wokondedwa, mphamvu zolamulira komanso zoweruza. Koma iye sapereka ntchito yomvera mapemphero, kwa wina aliyense, ngakhale mwana wake amene. Iye amamvetsera yekha mapemphero athu. Motero timakopeka ndi Yehova chifukwa cha mtima wake wotiganizira mwachikondiwu.

19. Kodi Yehova walonjeza zinthu zotani zomwe zimatichititsa kuti tizikopeka naye?

19 Timakopekanso ndi Yehova tikaganizira zimene wakonzera anthu. Iye walonjeza kuti athetsa matenda, chisoni, ndiponso imfa. (Chivumbulutso 21:3, 4) Anthu akadzakhala angwiro, palibe amene adzavutike maganizo, kulefuka, kapena kukumana ndi tsoka. Njala, umphawi, ndi nkhondo zidzatha. (Salmo 46:9; 72:16) Dziko adzalisintha kuti likhale paradaiso. (Luka 23:43) Yehova adzabweretsa madalitso amenewa, osati chifukwa choti sangachitire mwina ayi, koma chifukwa choti amatikonda.

20. Kodi Mose ananena chiyani pa nkhani ya ubwino wokonda Yehova?

20 Motero, pali zifukwa zambiri zokondera Mulungu wathu ndi kulola kuti chikondi chotere chikule. Kodi inuyo mupitiriza kukulitsa chikondi chimenechi, n’kulola kuti Mulungu azitsogolera zochita zanu? Zili ndi inu kutero kapena ayi. Mose anazindikira ubwino woyamba ndiponso kupitiriza kukonda Yehova. Kwa Aisiraeli akale, Mose anati: “Sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbewu zanu; kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kum’mamatira iye, pakuti iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka.”​—Deuteronomo 30:19, 20.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi n’chifukwa chiyani kukonda Yehova kuli kofunika kwa ife?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Mulungu?

• Kodi tili ndi zifukwa zotani zokondera Yehova?

• Kodi tingatani kuti tizikonda Mulungu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 20]

Yehova amaona kuti chikondi n’chinthu chofunika kwambiri, ndipotu tonsefe tingathe kusonyeza chikondi

[Zithunzi patsamba 23]

“Amene waona ine waonanso Atate.”​—Yohane 14:9