Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuvumbula Wokana Khristu

Kuvumbula Wokana Khristu

Kuvumbula Wokana Khristu

KODI mukanadziteteza bwanji ngati mukanadziwa zoti m’dera lanu mwagwa mliri wakupha? Mukanadziteteza mwa kulimbitsa mphamvu yoteteza thupi lanu n’kupewa kuyandikana ndi anthu omwe angakupatsireni matendawo. Tingachitenso chimodzimodzi mwauzimu. Malemba amatiuza kuti wokana Khristu “ali kale m’dziko.” (1 Yohane 4:3) Ngati tikufuna kuti tisatengere “matendawa,” tiyenera kudziwa kaye “chimene chimawabweretsa” ndiyeno n’kuchipewa. N’zosangalatsa kuti Baibulo limatifotokozera bwinobwino nkhani imeneyi.

“Wokana Khristu” amatanthauza “wotsutsana ndi Khristu kapena wodziika m’malo mwa Khristu.” Motero, mawuwa amanena za onse amene amatsutsa Khristu kapena amanama kuti iwowo ndiwo Khristu kapena oimira Khristu. Yesu mwiniyo ananena kuti: “Amene sali kumbali yanga akutsutsana ndi ine [kapena kuti ndiye wokana Khristu], ndipo amene sasonkhanitsa pamodzi ndi ine amamwaza.”​—Luka 11:23.

Yohane analemba za wokana Khristu patadutsa zaka zoposa 60 Yesu atafa ndi kuukitsidwa, n’kupita kumwamba. Choncho, kuti tidziwe kuti zochitika zinazake ndi za wokana Khristu tiyenera kuona mmene zochitikazo zikukhudzira otsatira okhulupirika a Yesu padziko lapansi pano.​—Mateyo 25:40, 45.

Wokana Khristu Amatsutsa Akhristu

Yesu anachenjeza otsatira ake kuti dziko lonse lidzadana nawo. Iye anati: “Anthu adzakuperekani ku chisautso ndipo adzakuphani. Mitundu yonse idzadana nanu chifukwa cha dzina langa. Ndipo kudzauka aneneri ambiri onyenga ndi kusocheretsa anthu ambiri.”​—Mateyo 24:9, 11.

Popeza kuti ophunzira a Yesu amazunzidwa “chifukwa cha dzina [la Yesu],” owazunzawo mwachionekere ndi okana Khristu, kapena kuti olimbana ndi Khristu. “Aneneri onyenga,” omwe poyamba anali Akhristu, nawonso ali m’gulu lomweli. (2 Yohane 7) Yohane analemba kuti “okana Khristu ambiri” amenewo “anachoka pakati pathu, koma sanali a ife; chifukwa akanakhala a ife, akanakhalabe ndi ife.”​—1 Yohane 2:18, 19.

Mawu a Yesu ndi Yohane akuonetseratu poyera kuti wokana Khristu si munthu mmodzi ayi koma kuti ndi anthu ambiri osiyanasiyana. Komanso, chifukwa chakuti ndi aneneri onyenga, cholinga chawo chachikulu ndicho kusocheretsa anthu. Kodi zina mwa njira zawo n’ziti?

Kufalitsa Mabodza Achipembedzo

Mtumwi Paulo anachenjeza mtumiki mnzake Timoteyo kuti anayenera kusamala ndi ziphunzitso za ampatuko, monga Hemenayo ndi Fileto, amene “mawu awo adzafalikira ngati chilonda chonyeka.” Paulo ananenanso kuti: “Anthu amenewa apatuka pa choonadi, akumati kuuka kwa akufa kunachitika kale; ndipo akuwononga chikhulupiriro cha ena.” (2 Timoteyo 2:16-18) Zikuoneka kuti, Hemenayo ndi Fileto ankaphunzitsa zoti kuuka kwa akufa kunali kongophiphiritsira chabe ndipo kuti Akhristu anali atauka kale mwauzimu. Inde, ngakhale Paulo amene, anafotokoza momveka bwino kuti Mulungu amaona kuti munthu ali ndi moyo akakhala wophunzira weniweni wa Yesu. (Aefeso 2:1-5) Komabe, zimene Hemenayo ndi Fileto ankaphunzitsa zinkatsutsana ndi lonjezo la Yesu lakuti kudzakhala kuuka kwenikweni kwa akufa mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu.​—Yohane 5:28, 29.

Kenako maganizo oti kuuka kwa akufa kunali kongophiphiritsira anayambitsidwanso ndi gulu lina lotchedwa Anositiki. Chifukwa chokhulupirira kuti munthu angapeze nzeru kudzera mwa mizimu, Anositiki anaphatikiza Chikhristu champatuko ndi nzeru za Agiriki ndiponso ziphunzitso za m’mayiko akum’mawa. Mwachitsanzo, ankakhulupirira kuti chinthu china chilichonse chooneka kapena kukhudzidwa chinali choipa, ndipo pa chifukwa chimenecho, Yesu sanabwere mu thupi koma kuti anangooneka ngati ali ndi thupi la munthu. Chiphunzitsochi chimatchedwa Chidosetizimu. Monga mmene taonera, zimenezi n’zimene mtumwi Yohane anachenjeza.​—1 Yohane 4:2, 3; 2 Yohane 7.

Chiphunzitso china chabodza chomwe anachiyambitsa zaka mazana angapo pambuyo pake, chinali chiphunzitso chotchedwa Utatu woyera, chimene chimanena kuti Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse ndiponso Mwana wa Mulungu. M’buku lake lakuti The Church of the First Three Centuries, Dr. Alvan Lamson analemba kuti chiphunzitso cha Utatu “chinachokera kwina osati m’Malemba achiyuda kapena Malemba achikhristu. Chiphunzitso chimenechi chinakula, ndipo “Abambo Ophunzitsa Ziphunzitso za Plato” anachilowetsa mu Chikhristu. Kodi “Abambo Ophunzitsa Ziphunzitso za Plato” amenewa anali ndani? Anali atsogoleri achipembedzo ampatuko omwe anakopeka ndi ziphunzitso za katswiri wachikunja wofufuza za nzeru zapamwamba wachigiriki wotchedwa Plato.

Polowetsa chiphunzitso cha Utatu mu Chikhristu, wokana Khristu anachita ukathyali waukulu, chifukwa chiphunzitsochi chinachititsa kuti Mulungu aoneke ngati wosatheka kum’dziwa. Chinachititsanso kuti ubale wa pakati pa Mulunguyo ndi Mwana wake ukhale wovuta kuumvetsa. (Yohane 14:28; 15:10; Akolose 1:15) Tangoganizirani, kodi munthu ‘angayandikire bwanji Mulungu,’ monga mmene Malemba amanenera, ngati Mulunguyo ali wosatheka kum’dziwa?​—Yakobe 4:8.

Powonjezera kusokoneza anthu kumeneku, omasulira Baibulo ambiri anachotsa dzina la Mulungu, Yehova, mu Mabaibulo awo ngakhale kuti dzinalo limapezeka maulendo oposa 7,000 m’Malemba oyambirira. Ndithudi, kwa Mlengi wathu ndiponso Mawu ake ouziridwa, ndi mwano waukulu kwambiri kuyesa kum’bisa Wamphamvuyonseyu kuti akhale wosatheka kum’dziwa ndi kuti akhale wopanda dzina. (Chivumbulutso 22:18, 19) Ndiponso, kuchotsa dzina la Mulungu m’Baibulo ndi kuikamo maina aulemu monga Ambuye ndiponso Mulungu n’kusemphana ndi zimene pemphero lachitsanzo lomwe Yesu anapereka limanena. Mwa zina, pempheroli limati: “Dzina lanu liyeretsedwe.”​—Mateyu 6:9.

Okana Khristu Amakana Ufumu wa Mulungu

Okana Khristu ali pa kalikiliki m’nthawi imene tikukhalamo ino, yomwe ndi “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1) Cholinga chachikulu cha onyenga a m’nthawi ino amenewa ndicho kusocheretsa anthu ponena za ntchito yomwe Yesu ali nayo monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, boma la kumwamba limene posachedwapa lidzalamulira padziko lonse lapansi.​—Danieli 7:13, 14; Chivumbulutso 11:15.

Mwachitsanzo, atsogoleri ena achipembedzo amaphunzitsa kuti Ufumu wa Mulungu ndi khalidwe chabe la mumtima. Izi zilibe maziko ena aliwonse m’Malemba. (Danieli 2:44) Ena amanena kuti Khristu akugwira ntchito yake kudzera m’maboma ndi mabungwe amene anthu amakhazikitsa. Koma Yesu ananena kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yohane 18:36) Ndithu, Satana, osati Khristu, ndiye “wolamulira wa dziko” ndiponso “mulungu wa dongosolo lino la zinthu.” (Yohane 14:30; 2 Akorinto 4:4) Izi zikusonyezeratu chifukwa chake posachedwapa Yesu adzachotsa maboma onse a anthu n’kukhala Wolamulira yekhayo wa dziko lonse lapansi. (Salmo 2:2, 6-9; Chivumbulutso 19:11-21) Anthu amapempherera zimenezi akamanena Pemphero la Ambuye, kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” Mateyu 6:10, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Chifukwa choti amathandizira dongosolo la ndale za dzikoli, atsogoleri ambiri achipembedzo amatsutsa, ngakhale kuzunza, amene amalengeza zoona zake za Ufumu wa Mulungu. Chochititsa chidwi n’chakuti, buku la Chivumbulutso m’Baibulo limatchula za “Babulo Wamkulu,” yemwe ndi mkazi wachiwerewere wophiphiritsa, amene anali “ataledzera ndi magazi a oyera, ndiponso magazi a mboni za Yesu.” (Chivumbulutso 17:4-6) Amachitanso uhule mwauzimu pothandiza “mafumu” a dzikoli, kapena kuti olamulira andale, motero iwowo amam’konda. Mkazi wophiphiritsira ameneyu si winanso ayi, koma zipembedzo zonyenga za dzikoli. Zipembedzozi ndizo mbali yaikulu ya wokana Khristu.​—Chivumbulutso 18:2, 3; Yakobe 4:4.

Wokana Khristu Amaphunzitsa Anthu “Zowakomera M’khutu”

Kuwonjezera pa kukana choonadi cha m’Baibulo, anthu amene amadzitcha kuti ndi Akhristu amasiya kutsatira makhalidwe abwino a m’Baibulo pofuna kutsatira makhalidwe ena otchuka. Mawu a Mulungu anali ataneneratu za zimenezi, pamene anati: “Idzafika nthawi imene anthu [amene amanena kuti amatumikira Mulungu] sadzafunanso chiphunzitso chopindulitsa, koma mogwirizana ndi zilakolako za iwo eni, adzadzipezera okha aphunzitsi kuti amve zowakomera m’khutu.” (2 Timoteyo 4:3) Aphunzitsi achipembedzo amenewa amatchedwanso kuti “atumwi onama, antchito achinyengo, odzisandutsa atumwi a Khristu.” Baibulo limanenanso kuti: “Mapeto awo adzakhala monga mwa ntchito zawo.”​—2 Akorinto 11:13-15.

Ntchito zawo zimaphatikizapo “khalidwe lotayirira” lomwe ndi kusalabadira mfundo zabwino za makhalidwe. (2 Petulo 2:1-3, 12-14) Kodi si zoona kuti timaona atsogoleri ambiri achipembedzo pamodzi ndi nkhosa zawo akutsanzira kapena kulolera makhalidwe achikunja, monga kugonana amuna kapena akazi okhaokha ndiponso kugonana ndi munthu yemwe sanakwatirane naye? Komano, tayerekezani kaye makhalidwe otchukawa ndi zimene Baibulo limanena pa Levitiko 18:22, Aroma 1:26, 27; 1 Akorinto 6:9, 10; Aheberi 13:4, ndi Yuda 7.

“Yesani Mawu Ouziridwa”

Monga taonera, m’pofunika kumvera zimene mtumwi Yohane ananena zoti tisapeputse zimene timakhulupirira. Yohane anachenjeza kuti: “Musamakhulupirire mawu alionse ouziridwa, koma yesani mawu ouziridwawo kuti muone ngati ali ochokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onyenga ambiri alowa m’dziko.”​—1 Yohane 4:1.

Taganizani za chitsanzo chabwino cha anthu “amaganizo apamwamba” omwe ankakhala m’mzinda wa Bereya m’nthawi ya atumwi. “Analandira mawuwo ndi chidwi chachikulu kwambiri. Anali kufufuza Malemba mosamala tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zinthuzo [zomwe Paulo ndi Sila analankhula] zinalidi choncho.” (Machitidwe 17:10, 11) Inde, ngakhale kuti anali ndi chidwi chophunzira, Abereya anaonetsetsa kuti zimene anamva ndi kuzivomereza zinali zochokeradi m’Malemba.

Masiku anonso, Akhristu oona satengeka ndi kusinthasintha maganizo kwa anthu m’dzikoli, koma amagwiritsa ntchito choonadi cha m’Baibulo. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ine ndikupitiriza kupemphera kuti chikondi chanu chipitirize kukula, limodzi ndi kudziwa zinthu molondola, komanso kuzindikira zinthu bwino lomwe.”​Afilipi 1:9.

Ngati simunachite zimenezo, konzani zoti ‘mudziwe zinthu molondola, komanso kuzindikira zinthu bwino lomwe,’ mwa kuphunzira zimene Baibulo limaphunzitsa. Amene amatsanzira Abereya sanamizidwa ndi “mawu achinyengo” a okana Khristu. (2 Petulo 2:3) M’malo mwake, amamasulidwa ndi choonadi chauzimu cha Khristu weniweni ndi otsatira ake oona.​—Yohane 8:32, 36.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 4]

ZIMENE BAIBULO LIMANENA ZA WOKANA KHRISTU

“Ana inu, inoyi ndi nthawi yotsiriza [yomwe ndi mapeto a nthawi ya atumwi], ndipo monga munamva kuti wokana Khristu akubwera, ngakhale tsopano alipo okana Khristu ambiri.”​—1 Yohane 2:18.

“Nanga wabodza n’kukhalanso ndani, ngati si uja amene amakana zakuti Yesu ndi Khristu? Ameneyu ndiye wokana Khristu, amene amakana Atate ndi Mwana.”​—1 Yohane 2:22.

“Mawu alionse ouziridwa amene savomereza zimenezi ponena za Yesu, amenewo sachokera kwa Mulungu, ndipo ndi ouziridwa ndi wokana Khristu amene munamva kuti akubwera, ndipo tsopano ali kale m’dziko.”​—1 Yohane 4:3.

“Onyenga ambiri alowa m’dziko, anthu amene amatsutsa zakuti kalero Yesu Khristu anabwera monga munthu. Ndipo otsutsa amenewa, ndiwo akupanga wonyenga uja ndi wokana Khristu.”​—2 Yohane 7.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 5]

WONYENGA WA NKHOPE ZAMBIRI

Mawu akuti “wokana Khristu” amanena za onse amene amakana zimene Baibulo limanena zokhudza Yesu Khristu, onse amene amatsutsa Ufumu wake, ndiponso onse amene amazunza otsatira ake. Mawuwa amatanthauzanso anthu enaake pawokhapawokha, mabungwe, ndiponso mayiko amene amanama kuti akuimira Khristu kapena amene amadzitukumula mwa kudziika pa udindo wa Mesiya polonjeza kubweretsa mtendere ndi bata lenileni, zinthu zomwe ndi Khristu yekha amene angazikwaniritse.

[Mawu a Chithunzi]

Augustine: ©SuperStock/​age fotostock

[Chithunzi patsamba 7]

Monga Abereya, tiyenera ‘kufufuza Malemba tsiku ndi tsiku’