Mfundo Zazikulu za M’buku la Yesaya—Gawo 1
Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’buku la Yesaya—Gawo 1
“NDIDZATUMIZA yani, ndipo ndani adzatitumikira ife?” Yehova atafunsa funso limeneli, Yesaya mwana wa Amozi anayankha kuti: “Ndine pano; munditumize ine.” (Yesaya 1:1; 6:8) Atatero, anapatsidwa ntchito yoti akhale mneneri. Zimene Yesaya anachita ali mneneri zinalembedwa m’buku la m’Baibulo lomwe lili ndi dzina lake.
Buku limene mneneri Yesaya analembali, limasimba za zinthu zimene zinachitika pa zaka 46, kuyambira mu 778 B.C.E. mpaka mu 732 B.C.E. Ngakhale kuti bukuli lili ndi mauthenga oweruza Yuda, Isiraeli, ndiponso mitundu yoyandikana nayo, nkhani yake yaikulu si chiweruzo. M’malo mwake, ndi ‘chipulumutso chochokera kwa Yehova Mulungu.’ (Yesaya 25:9) Ndipotu dzina lakuti Yesaya, limatanthauza “Chipulumutso cha Yehova.” Nkhani ino ilongosola mfundo zazikulu za mu Yesaya chaputala 1:1 mpaka chaputala 35:10.
“OTSALA ADZABWERA”
Baibulo silinena kuti uthenga wa ulosi umene unalembedwa m’machaputala asanu oyambirira a buku la Yesaya unaperekedwa liti, kaya Yesaya asanakhale mneneri kapena atakhala kale. (Yesaya 6:6-9) Komabe chimene chikudziwika n’chakuti, panthawiyi Yuda ndi Yerusalemu ndi odwala mwauzimu “kuchokera pansi pa phazi kufikira kumutu.” (Yesaya 1:6) Kupembedza mafano n’kofala. Atsogoleri awo ndi achinyengo. Azimayi ayamba kudzikuza. Anthu sakulambira Mulungu woona movomerezeka. Yesaya akuuzidwa kuti apite akapereke uthenga mobwerezabwereza kwa anthu osazindikira ndiponso osafuna kudziwa.
Yuda watsala pang’ono kuukiridwa ndi magulu ankhondo ophatikizana a Isiraeli ndi Aramu. Pogwiritsa ntchito Yesaya ndi ana ake monga “zizindikiro ndi zodabwitsa,” Yehova akutsimikizira Yuda kuti mgwirizano wa Isiraeli ndi Aramu supambana. (Yesaya 8:18) Koma ndi ulamuliro wa “Kalonga wa mtendere” wokha umene udzabweretse mtendere wosatha. (Yesaya 9:6, 7) Yehova adzaweruzanso Asuri, mtundu womwe akuugwiritsa ntchito ngati “chibonga cha mkwiyo” wake. Yuda adzapita ku ukapolo, koma ‘otsala awo adzabwera.’ (Yesaya 10:5, 21, 22) Chilungamo chenicheni chidzakhalako mu ulamuliro wa “mphukira” yophiphiritsira ya “pa tsinde la Jese.”—Yesaya 11:1.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1:8, 9—Kodi mwana wamkazi wa Ziyoni adzasiyidwa motani ngati “chitando cha m’munda wamphesa, ngati chilindo cha m’munda wamankhaka”? Zimenezi zikutanthauza kuti Yerusalemu akadzaukiridwa ndi Asuri, adzaoneka ngati wopandiratu chitetezo, ngati chitando cha m’munda wa mphesa kapena chilindo chosalimba m’munda wa mankhaka. Komabe, Yehova adzamuthandiza kuti asakhale ngati Sodomu ndi Gomora.
1:18—Kodi mawu akuti: “Tiyeni, tsono, tiweruzane,” akutanthauzanji? Uku sikunali kuwaitana kuti akambirane n’kumvana mfundo imodzi. M’malo mwake, vesi limeneli likusonyeza kuti panakhazikitsidwa dongosolo lochitira zinthu mwachilungamo, limene Woweruza wachilungamo, Yehova, akupereka kwa Aisiraeli mwayi woti asinthe ndi kudziyeretsa.
6:8a—N’chifukwa chiyani akunena kuti “ife” m’lemba limeneli? Mawu akuti “ife” akusonyeza kuti pali munthu wina yemwe ali ndi Yehova. N’zachidziwikire kuti ameneyu ndi “Mwana wake wobadwa yekha.”—Yohane 1:14; 3:16.
6:11—Kodi Yesaya anatanthauzanji pamene anafunsa kuti “Ambuye mpaka liti?” Yesaya sanali kufunsa za kutalika kwa nthawi imene anayenera kulengeza uthenga wa Yehova kwa anthu osamva. M’malo mwake, ankafuna kudziwa kuti kudwala kwauzimu kwa anthuwo kudzapitirirabe kunyozetsa dzina la Mulungu mpaka liti?
7:3, 4—N’chifukwa chiyani Yehova anapulumutsa Ahazi mfumu yoipa? Mafumu a Aramu ndi Isiraeli anakonza zochotsa Mfumu Ahazi ya Yuda pampando wachifumu n’kuikapo wolamulira woti azingowamvera iwowo. Wolamulira wake anali mwana wamwamuna wa Tabeeli, yemwe sanali mbadwa ya Davide. Nzeru zochokera kwa Satana zimenezi zikanasokoneza pangano la Ufumu la pakati pa Yehova ndi Davide. Yehova anapulumutsa Ahazi n’cholinga choteteza mzere umene “Kalonga wa mtendere” adzabadwiremo.—Yesaya 9:6.
7:8—Kodi Efraimu ‘anathyokathyoka’ motani pasanathe zaka 65? “M’masiku a Peka mfumu ya Isiraeli,” m’pamene anthu a mu ufumu wa mafuko khumi anayamba kutumizidwa ku ukapolo ndiponso m’pamene dzikolo linayamba kudzadzidwa ndi anthu achilendo. Zimenezi zinachitika Yesaya atangonena kumene ulosi umenewu. (2 Mafumu 15:29) Ndipo zinapitirira mpaka m’masiku a mfumu ya Asuri yotchedwa Esaradoni, yemwe anali mwana wa Sanakeribu ndiponso wolowa m’malo mwake. (2 Mafumu 17:6; Ezara 4:1, 2; Yesaya 37:37, 38) Kusamutsasamutsa anthu kumeneku, kuwachotsa ndi kuwapititsa ku Samariya kunatenga nyengo ya zaka 65 zimene Yesaya anatchula pa Yesaya 7:8.
11:1, 10—Kodi Yesu Khristu, angakhale bwanji “mphukira pa tsinde la Jese” ndiponso “muzu wa Jese”? (Aroma 15:12) Yesu anali “mphukira pa tsinde la Jese” malinga ndi banja limene anabadwirako. Anali mbadwa ya Jese chifukwa chakuti anabadwa mu mzera wa Davide, mwana wa Jese. (Mateyo 1:1-6; Luka 3:23-32) Komano, mphamvu za ufumu zimene Yesu anapatsidwa, zimakhudza ubwenzi wake ndi makolo ake akale. Chifukwa chopatsidwa ulamuliro ndi mphamvu zopereka moyo wosatha pa dziko lapansi kwa anthu omvera, Yesu anakhala “Atate Wosatha” wa makolo ake akalewo. (Yesaya 9:6) Mwanjira imeneyi, iye anakhalanso “muzu” wa makolo ake, kuphatikizapo Jese.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:3. Tikamakana kuchita zinthu zimene Mlengi wathu amafuna kuti tizichita, ndiye kuti ng’ombe kapena abulu amadziwa zambiri kuposa ifeyo. Komano, tikayamikira zonse zimene Yehova watichitira, timapewa kuchita zinthu mosaganizira n’kumusiya Yehovayo.
1:11-13. Yehova amanyansidwa ndi miyambo yachipembedzo yachiphamaso komanso mapemphero amwambo. Tizikhala ndi zolinga zabwino pochita zinthu zinazake ndiponso popemphera.
1:25-27; 2:2; 4:2, 3. Pamene otsalira olapawo anabwerera ku Yerusalemu n’kukabwezeretsa kulambira koona m’pamene ukapolo unatha ndipo Yuda sanalinso bwinja ayi. Yehova n‘ngwachifundo kwa ochimwa amene alapa.
2:2-4. Kuchita nawo mwachangu ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira kukuthandiza anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana kuphunzira mtendere ndi kuyesetsa kukhala mwamtendere ndi anthu anzawo.
4:4. Yehova adzachotsa makhalidwe onse onyansa kuphatikizapo khalidwe lopha anthu.
5:11-13. Ngati sitiika malire ndiponso kudziletsa pa zinthu zosangalatsa zimene timachita ndiye kuti sitikuchita zinthu mwanzeru.—Aroma 13:13.
5:21-23. Akulu, kapena oyang’anira achikhristu, asamadziyese “anzeru ndi ochenjera.” Komanso azisonyeza kudziletsa ‘pakumwa vinyo’ ndipo azipewa kukondera.
11:3a. Ziphunzitso ndi chitsanzo cha Yesu zimasonyeza kuti kuopa Yehova kumadzetsa chimwemwe.
“AMBUYE ADZAM’CHITIRA CHIFUNDO YAKOBO”
Machaputala 13 mpaka 23 ali ndi mauthenga otsutsa amitundu. Komabe, “Ambuye adzam’chitira chifundo Yakobo” mwa kulola mafuko onse a Isiraeli kuti abwerere kwawo. (Yesaya 14:1) Uthenga wa chiwonongeko cha Yuda womwe uli m’chaputala 24 mpaka 27 ukutsagana ndi lonjezo lakuti zinthu zidzabwerera mwakale. Yehova akupsera mtima “oledzera a Efraimu [Isiraeli]” chifukwa chopanga mgwirizano ndi Aramu. Akupseranso mtima “wansembe ndi mneneri” chifukwa chopanga mgwirizano ndi Asuri. (Yesaya 28:1, 7) Arieli [Yerusalemu] nayenso anauzidwa kuti adzaona tsoka chifukwa ‘chotsikira ku Aiguputo’ kukafuna chitetezo. (Yesaya 29:1; 30:1, 2) Komabe, anthu amene amakhulupirira Yehova akulonjezedwa chipulumutso.
Monga “mwana wa mkango wobangula pa nyama yake,” Yehova adzateteza “phiri la Ziyoni.” (Yesaya 31:4) Komanso pali lonjezo ili: “Taonani mfumu idzalamulira m’chilungamo.” (Yesaya 32:1) Ngakhale ‘amithenga a mtendere’ analira kwambiri chifukwa choopa Asuri, komabe Yehova analonjeza kuti anthu ake adzachiritsidwa, “adzakhululukidwa mphulupulu zawo.” (Yesaya 33:7, 22-24) “Yehova akwiyira amitundu onse, nachitira ukali khamu lawo lonse.” (Yesaya 34:2) Yuda sapitirira kukhala bwinja. “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duwa.”—Yesaya 35:1.
Kuyankha Mafunso a M’malemba:
13:17—Kodi Amedi sanasamalire motani siliva ndipo sanakondwere ndi golidi m’njira yotani? Amedi ndi Aperisi ankaona kuti ulemerero wogonjetsa mdani wawo unali wofunika koposa zinthu zofunkha pankhondo. Koresi anasonyeza zimenezi popatsa Ayuda obwerera kwawo zipangizo za golidi ndi siliva zimene Nebukadinezara anafunkha m’kachisi.
14:1, 2—Kodi zinachitika motani kuti anthu a Yehova atengere m’ndende amitundu omwe poyamba anawatengera m’ndende iwowo ndiponso kuti ‘alamulire owavuta’? Zimenezi zinachitika kwa anthu ngati Danieli, amene anali ndi udindo waukulu ku Babulo pansi pa ulamuliro wa Amedi ndi Aperisi; Estere, amene anakhala mfumukazi ya Aperisi; Moredekai amene anakhala nduna yaikulu mu ufumu wa Aperisi.
20:2-5—Kodi Yesaya anayendadi mbulanda kwa zaka zitatu? N’kutheka kuti Yesaya anangochotsa chovala chake chapamwamba n’kumayenda ali ndi zovala zochepa chabe.—1 Samueli 19:24.
21:1—Ndi dera liti lomwe likutchedwa kuti “chipululu cha kunyanja”? Ngakhale kuti Babulo sanali kufupi ndi nyanja ina iliyonse, ndiye amene akutchulidwa m’njira imeneyi. Akutchedwa choncho chifukwa choti madzi a m’mitsinje ya Firate ndi Tigirisi ankasefukira m’deralo chaka ndi chaka n’kumapanga malo alowe ooneka ngati “kunyanja.”
24:13-16—Kodi Ayuda anadzakhala motani ‘pakati pa dziko la anthu, ngati kugwedeza kwa mtengo wa azitona, ngati khunkha la mphesa, pakutha masika ake’? Monga mmene zipatso zina zimatsalira mu mtengo kapena mu mphesa atatha kukolola, ochepa okha ndi omwe anapulumuka chiwonongeko cha Yerusalemu ndi Yuda. Opulumukawo ankalemekezabe Yehova kulikonse kumene anawasamutsirako, kaya “kum’mawa” [Babulo yemwe anali chakum’mawa] kapenanso “m’zisumbu za m’nyanja,” [ya Mediterranean].
24:21—Kodi a “khamu la kumwamba, ndi mafumu a dziko lapansi” ndani? N’kutheka kuti “khamu la kumwamba” likutanthauza magulu a mizimu yoipa. Ngati zili choncho, ndiye kuti “mafumu a dziko lapansi” ndi olamulira a padziko lapansi, chifukwa amasonkhezeredwa kwambiri ndi ziwanda.—1 Yohane 5:19.
25:7—Kodi “chophimba nkhope chovundikira mitundu yonse ya anthu, ndi nsalu yokuta amitundu onse,” n’chiyani? Mawu ofanizira amenewa akunena za adani awiri a mtundu wa anthu. Adaniwa ndi uchimo ndi imfa.
Zimene Tikuphunzirapo:
13:20-22; 14:22, 23; 21:1-9. Nthawi zonse, mawu aulosi a Yehova amachitikadi, monga mmene zinachitikira ndi Babulo.
17:7, 8. Ngakhale kuti Aisiraeli ambiri sanamvere, ena anadalira Yehova. N’chimodzimodzinso masiku ano, ena m’matchalitchi achikhristu akumvetsera uthenga wa Ufumu.
28:1-6. Isiraeli adzagonja kwa Asuri, koma Mulungu adzaonetsetsa kuti anthu okhulupirika apulumuke. Yehova akapereka chiweruzo sasiya olungama popanda chiyembekezo.
28:23-29. Yehova amawongolera anthu oona mtima mogwirizana ndi zosowa zawo ndiponso mmene zinthu zilili.
30:15. Kuti tipulumutsidwe ndi Yehova m’pofunika kusonyeza chikhulupiriro mwa “kupuma” kapena kuti kupewa kufunafuna chipulumutso kudzera mwa zochita za anthu. Pokhala “chete” kapena kuti posachita mantha, timasonyezanso kuti sitikukayika kuti Yehova angathe kutiteteza.
30:20, 21. ‘Timaona’ Yehova ndi “kumva” mawu ake achipulumutso mwa kumvera zimene amanena kudzera m’Baibulo, lomwe ndi Mawu ake ouziridwa, komanso kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”—Mateyo 24:45.
Ulosi wa Yesaya Umalimbitsa Chidaliro Chathu M’Mawu a Mulungu
Ndife oyamikira zedi chifukwa cha uthenga wa Mulungu wopezeka m’buku la Yesaya. Maulosi amene anakwaniritsidwa kale amatilimbikitsa kuti ‘mawu amene amatuluka m’kamwa mwa Yehova, sadzabwerera kwa iye chabe.’—Yesaya 55:11.
Bwanji nanga za malonjezo onena za Mesiya, monga malonjezo a pa Yesaya 9:7 ndiponso 11:1-5, 10? Kodi salimbitsa chikhulupiriro chathu m’njira yotiwombolera imene Yehova anakonza? Bukuli lilinso ndi maulosi amene mbali zake zikuluzikulu zikukwaniritsidwa panopo kapena zidzakwaniritsidwa m’tsogolo. (Yesaya 2:2-4; 11:6-9; 25:6-8; 32:1, 2) Zoonadi, buku la Yesaya ndi umboni winanso wotsimikizira kuti “mawu a Mulungu ndi amoyo”!—Aheberi 4:12.
[Chithunzi patsamba 8]
Yesaya ndi ana ake anali “zizindikiro ndi zodabwitsa mu Isiraeli”
[Chithunzi pamasamba 8, 9]
Yerusalemu anadzakhala ngati “chitando cha m’munda wamphesa”
[Chithunzi patsamba 10]
Kodi anthu a mitundu yosiyanasiyana akuthandizidwa motani ‘kusula malupanga awo kuti akhale zolimira’?