Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kudziwa Wokana Khristu?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kudziwa Wokana Khristu?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kudziwa Wokana Khristu?

Kalekale, Mulungu anauzira mtumwi Yohane kulemba kuti: “Munamva kuti wokana Khristu akubwera.” (1 Yohane 2:18) Awatu ndi mawu ochititsa chidwi kwambiri! Kwa zaka zambiri, anthu akhala akufuna kudziwa tanthauzo la mawuwa. Kodi wokana Khristu ndani? Kodi adzabwera liti? Nanga akadzabwera adzatani?

PALI anthu ambirimbiri amene akhala akutchedwa wokana Khristu. M’mbuyomu, ena amene anatchedwa kuti ndi “wokana Khristu” anali Ayuda, Apapa achikatolika, ndiponso mafumu achiroma. Mwachitsanzo, pa nthawi yomwe mfumu Frederick II (anabadwa mu 1194 n’kumwalira mu 1250) anasankha kukamenyana nawo nkhondo mothandiza tchalitchi chake, Papa Gregory IX anamutcha kuti ndi wokana Khristu ndipo anamuchotsa mumpingo. Papa Innocent IV, amene analowa m’malo mwa Papa Gregory, anachotsanso Frederick. Pobwezera, Frederick analengeza kuti Innocent ndiye anali wokana Khristu.

Mtumwi Yohane ndi wolemba Baibulo yekhayo amene anagwiritsa ntchito mawu akuti “wokana Khristu” ndiponso “okana Khristu.” M’makalata awiri otchedwa dzina lake, mawuwa amapezeka kasanu. Mavesi amene mawuwa akupezekamo andandalikidwa m’bokosi patsamba lotsatira. Kuchokera m’mavesi amenewa, tikhoza kuona kuti wokana Khristu ndi wabodza ndiponso wonyenga, amene cholinga chake ndicho kuwononga ubwenzi umene munthu ali nawo kwa Khristu ndi Mulungu. Choncho, mtumwiyu analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Okondedwa, musamakhulupirire mawu alionse ouziridwa, koma yesani mawu ouziridwawo kuti muone ngati ali ochokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onyenga ambiri alowa m’dziko.”​—1 Yohane 4:1.

Yesu nayenso anachenjeza za anthu achinyengo, kapena kuti aneneri onyenga ponena kuti: “Amabwera kwa inu atavala ngati nkhosa, koma mkati mwawo ali mimbulu yolusa. Mudzawazindikira ndi zipatso zawo [kapena kuti ntchito zawo].” (Mateyo 7:15, 16) Kodi pamenepa Yesu anali kuchenjeza otsatira ake za wokana Khristu wophiphiritsira? Tiyeni tione mmene tingam’dziwire wonyenga wankhanza ameneyu.