Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tanthauzo la Kukonda Mnansi Wathu

Tanthauzo la Kukonda Mnansi Wathu

Tanthauzo la Kukonda Mnansi Wathu

“Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.”​—MATEYO 22:39.

1. Kodi timaonetsa bwanji kuti timakonda Mulungu?

KODI Yehova amafuna kuti anthu om’lambira azitani? Yesu anayankha funso limeneli mwachidule, m’mawu ochepa, osavuta kumvetsa, koma a tanthauzo lozama. Iye anati lamulo lalikulu koposa n’lakuti tizikonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, maganizo athu onse, ndiponso mphamvu zathu zonse. (Mateyo 22:37; Maliko 12:30) Monga tinaonera m’nkhani yam’mbuyo ija, kukonda Mulungu kumaphatikizanso kumumvera ndi kutsatira malamulo ake pobwezera chikondi chimene iye watisonyeza. Amene amakonda Mulungu saona kuti kuchita chifuniro chake n’kolemetsa, m’malo mwake kumawasangalatsa.​—Salmo 40:8; 1 Yohane 5:2, 3.

2, 3. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira lamulo lakuti tizikonda mnansi wathu, nangano zimenezi zikubweretsa mafunso otani?

2 Yesu anati lamulo lachiwiri lalikulu kwambiri n’logwirizana ndi loyamba lija, ndipo n’lakuti: “Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.” (Mateyo 22:39) Tsopano tikambirana za lamulo limeneli, ndipo m’pake kuti tikutero. Tikukhala m’nthawi yodziwika ndi chikondi cholakwika, chongofuna kudzipindulitsa wekha basi. Mouziridwa, mtumwi Paulo analongosola kuti “m’masiku otsiriza” anthu sadzakonda anzawo koma adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, ndi okonda zosangalatsa. Anati ambiri adzakhala “opanda chikondi chachibadwa,” kapena monga mmene Baibulo lina limanenera, adzakhala “opanda chikondi chachibadwa kwa mabanja awo.” (2 Timoteyo 3:1-4) Yesu Khristu analosera kuti: “Ambiri . . . adzaperekana okhaokha ndi kudana . . . . Ochuluka chikondi chawo chidzazirala.”​—Mateyo 24:10, 12.

3 Komabe, onani kuti Yesu sananene kuti chikondi cha aliyense chidzazirala. Nthawi zonse pamapezekabe anthu ena osonyeza chikondi chimene Yehova amafuna komanso chimene chili chomuyenerera. Anthu amene amakondadi Yehova amayesetsa kuona ena monga mmene iye amawaonera. Komano, kodi mnansi amene tiyenera kum’kondayo ndani? Kodi tizisonyeza bwanji chikondi kwa mnansi wathu? Malemba angatithandize kuyankha mafunso ofunikirawa.

Kodi Mnansi Wanga Ndani?

4. Malingana ndi Levitiko chaputala 19, kodi Ayuda ankayenera kusonyeza ndani chikondi?

4 Pouza Mfarisi uja kuti lamulo lachiwiri lalikulu kwambiri n’lakuti uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha, Yesu anali kunena za lamulo linalake limene Aisiraeli anapatsidwa. Lamuloli linalembedwa pa Levitiko 19:18. M’chaputala chomwechi, Ayuda anauzidwa kuti ayenera kuona anthu ena amene si Aisiraeli anzawo, monga anansi awo. Vesi 34 limati: “Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m’dziko momwemo; um’konde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m’dziko la Aigupto.” Motero, ngakhale anthu osakhala Ayuda, makamaka otembenukira ku Chiyuda, ankayenera kuwachitira zinthu mwachikondi.

5. Kodi Ayuda ankaona kuti kukonda mnansi wako n’kutani?

5 Komabe, atsogoleri a Chiyuda a m’nthawi ya Yesu, anali kuona nkhaniyi m’njira ina. Ena ankaphunzitsa anthu kuti mawu akuti “bwenzi” ndi “mnansi” ankatanthauza Ayuda okha basi. Anthu osakhala Ayuda anayenera kudana nawo. Aphunzitsi oterewa ankaona kuti anthu olambira Mulungu ayenera kunyoza osalambira Mulungu. Buku lina limati: “Maganizo amenewa anali okolezera moto wa udani. Anachititsa kuti pakhale zifukwa zambiri zoyambitsira udani.”

6. Kodi ndi mfundo ziwiri ziti zimene Yesu ananena pofotokoza za kukonda mnansi?

6 Pa ulaliki wake wa pa phiri, Yesu ananenapo nkhani imeneyi, ndipo anafotokoza za anthu amene ayenera kusonyezedwa chikondi. Iye anati: “Inu munamva kuti anati, ‘Uzikonda mnansi wako ndi kudana naye mdani wako.’ Koma ine ndikukuuzani: Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani; kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wa kumwamba, popeza kuti amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mateyo 5:43-45) Apa Yesu ananena mfundo ziwiri. Yoyamba inali yakuti, Yehova ndi wowolowa manja ndiponso wokoma mtima kwa anthu abwino ndi oipa omwe. Ndipo yachiwiri inali yakuti tizimutsanzira.

7. Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo la Msamariya wachifundo?

7 Panthawi ina, Myuda wina wodziwa bwino Chilamulo anafunsa Yesu kuti: “Nanga mnansi wanga ndani kwenikweni?” Yesu anayankha pomulongosolera fanizo lonena za Msamariya amene anapeza Myuda amene anachitidwa chifwamba n’kulandidwa katundu wake. Ngakhale kuti nthawi zambiri Ayuda ankanyoza Asamariya, Msamariyayu anakonza mabala a munthuyo n’kumupititsa kunyumba ya alendo kuti akasamalidwe bwinobwino n’kuchira. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Chikondi chathu cha mnansi chiyenera kufika kwa anthu enanso osakhala a fuko lathu lokha, mtundu wathu, kapena chipembedzo chathu chokha.​—Luka 10:25, 29, 30, 33-37.

Tanthauzo la Kukonda Mnansi Wathu

8. Kodi chaputala 19 cha Levitiko chimanena chiyani pa nkhani ya mmene tiyenera kusonyezera chikondi?

8 Kukonda mnansi, n’kofanana ndi kukonda Mulungu chifukwa si kuti kumangotanthauza mmene tikumvera mumtima, koma kumatanthauzanso zochita. Ndi bwino kuti tionenso bwino nkhani imene mukupezeka lamulo la pa Levitiko 19, lomwe limalimbikitsa anthu a Mulungu kukonda anansi awo monga amadzikondera okha. Pamenepa timawerenga kuti Aisiraeli analamulidwa kuti azilola anthu ovutika ndiponso alendo kukunkha m’minda yawo. Sankalekerera kuba, kuchita zachinyengo, kapena kunama. Pankhani ya kuweruza, Aisiraeli ankayenera kukhala opanda tsankho. Inde, ankayenera kupereka chidzudzulo pakafunika kutero, koma anauzidwa mwachindunji kuti: “Usamamuda m’bale wako mumtima mwako.” Malamulo amenewa ndi malamulo enanso ambiri ananenedwa mwachidule m’mawu akuti: “Uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha.”​—Levitiko 19:9-11, 15, 17, 18.

9. N’chifukwa chiyani Yehova analamulira Aisiraeli kuti apatuke ku mitundu ina?

9 Ngakhale kuti Aisiraeli anayenera kuonetsa chikondi kwa ena, anayeneranso kudzipatula kwa anthu amene amalambira milungu yonyenga. Yehova anawachenjeza za kuopsa ndiponso zotsatirapo za kukhala ndi mabwenzi oipa. Mwachitsanzo, ponena za mitundu imene Aisiraeli ankayembekezera kudzaigonjetsa, Yehova analamulira kuti: “Musakwatitsane nawo; musam’patse mwana wake wamwamuna mwana wanu wamkazi, kapena kutenga mwana wake wamkazi akhale wa mwana wanu wamwamuna. Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata Ine, kuti atumikire milungu ina; potero Yehova adzapsa mtima pa inu, ndipo adzakuwonongani msanga.”​—Deuteronomo 7:3, 4.

10. Kodi tizipewa chiyani?

10 Chimodzimodzinso, Akhristu amapewa kukhala paubwenzi ndi anthu amene angathe kufooketsa chikhulupiriro chawo. (1 Akorinto 15:33) Timalimbikitsidwa kuti: “Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira,” amene sali mbali ya mpingo wachikhristu. (2 Akorinto 6:14) Komanso, Akhristu amalimbikitsidwa kukwatira kapena kukwatiwa “kokha mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39) Komabe, anthu amene sakhulupirira Yehova ngati ifeyo tisamawanyoze ayi. Khristu anafera anthu ochimwa, ndipo ambiri amene poyamba ankachita zinthu zoipa anasintha njira zawo n’kubwerera kwa Mulungu.​—Aroma 5:8; 1 Akorinto 6:9-11.

11. Kodi njira yabwino kwambiri yosonyezera chikondi kwa anthu amene satumikira Yehova ndi iti, ndipo n’chifukwa chiyani zili choncho?

11 Njira yabwino kwambiri yosonyezera chikondi anthu amene satumikira Mulungu, ndiyo kutsanzira Yehova weniweniyo. Ngakhale kuti iye sakonda zoipa, amasonyeza kukoma mtima kwachikondi kwa anthu onse powapatsa mwayi woti asiye njira zawo zoipa n’kulandira moyo wosatha. (Ezekieli 18:23) Yehova “amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Petulo 3:9) Chifuniro chake n’chakuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Timoteyo 2:4) N’chifukwa chake Yesu anatuma ophunzira ake kuti akalalikire ndi kuphunzitsa ndi ‘kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyo 28:19, 20) Pochita nawo ntchito imeneyi, timasonyeza kuti timakonda Mulungu ndiponso anzathu, inde, ngakhale adani athu amene.

Kusonyeza Chikondi kwa Abale Athu Achikhristu

12. Kodi mtumwi Yohane analemba zotani pankhani ya kukonda abale athu?

12 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Tiyeni tichitire onse zabwino, koma makamaka achibale athu m’chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10) Poti ndife Akhristu, tili ndi udindo wosonyeza chikondi kwa anthu amene ali achibale athu m’chikhulupiriro, omwe ndi abale ndi alongo athu auzimu. Kodi chikondi chimenechi n’chofunika motani? Ponena mfundo yogwira mtima kwambiri imeneyi, mtumwi Yohane anati: “Aliyense amene amada m’bale wake ndi wopha munthu . . . Ngati wina anena kuti: “Ndimakonda Mulungu,” koma amada m’bale wake, ndi wonama. Pakuti amene sakonda m’bale wake amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.” (1 Yohane 3:15; 4:20) Awatu ndi mawu amphamvu kwambiri. Yesu Khristu anagwiritsira ntchito mawu akuti “wopha anthu” ndi “wabodza” ponena za Satana Mdyerekezi. (Yohane 8:44) Ndithu, sitingafune kuti mawu amenewa akhale akunena za ifeyo.

13. Kodi tingasonyeze motani chikondi kwa Akhristu anzathu?

13 Akhristu oona, ‘Mulungu amawaphunzitsa kukondana.’ (1 Atesalonika 4:9) “Tisakondane ndi mawu okha kapena ndi lilime lokha, koma mwa zochita ndi choonadi.” (1 Yohane 3:18) Chikondi chathu “chisakhale cha chiphamaso.” (Aroma 12:9) Chikondi chimachititsa kuti tizikhala okoma mtima, achifundo, okhululuka, oleza mtima ndi kuti tisakhale ochita nsanje, odzitama, odzimva, kapena ongoganizira zatokha. (1 Akorinto 13:4, 5; Aefeso 4:32) Chimatilimbikitsa ‘kutumikirana.’ (Agalatiya 5:13) Yesu anauza ophunzira ake kuti azikondana monga mmene iye anawakondera. (Yohane 13:34) Motero Mkhristu azilolera ngakhale kufera Akhristu anzake ngati pakufunika kutero.

14. Kodi tingasonyeze bwanji chikondi m’banja?

14 Chikondi chiyenera kuoneka kwambiri m’banja lachikhristu ndipo makamaka pakati pa mwamuna ndi mkazi wake. Ukwati uyenera kukhala ubwenzi wapamtima kwambiri, n’chifukwa chake Paulo anati: “Amuna akonde akazi awo monga matupi awoawo.” Ndipo anawonjezera kuti: “Amene akonda mkazi wake adzikonda iye mwini.” (Aefeso 5:28) Paulo anabwereza malangizo amenewa pa mavesi asanu a patsogolo pa vesili. Mwamuna amene amakonda mkazi wake sangatsanzire Aisiraeli a m’nthawi ya Malaki amene ankachitira akazi awo zachinyengo. (Malaki 2:14) Mwamunayo amakonda mkaziyo. Amam’konda monga Khristu anakondera mpingo. Mkazi nayenso amalemekeza mwamuna wake chifukwa cha chikondi.​—Aefeso 5:25, 29-33.

15. Kodi anthu ena ananena ndi kuchita chiyani ataona ntchito yosonyeza chikondi chaubale.

15 N’zoonekeratu kuti chikondi choterechi n’chizindikiro cha Akhristu oona. Yesu anati: “Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana.” (Yohane 13:35) Chikondi cha pakati pathu chimakopa anthu kuti alambire Mulungu amene timakonda ndi kuimira. Mwachitsanzo, ku Mozambique kwachokera lipoti ili lonena za banja linalake la Mboni. “Sitinaonepo zoterezi ayi. Madzulo, kunawomba chimphepo chadzaoneni, ndipo kenaka kunagwa chimvula chamatalala. Chimphepocho chinawononga nyumba yathu ya mabango, n’kusasula malata pa denga lake. Abale athu ochokera m’mipingo yapafupi anabwera kudzatithandiza kumanganso nyumbayi, ndipo anzathu okhala nafe pafupi anadabwa n’kunena kuti: ‘Chipembedzo chanu n’chabwino kwambiri. Ife sitinathandizidwepo chonchi ku tchalitchi kwathu.’ Tinatsegula Baibulo n’kuwasonyeza lemba la Yohane 13:34, 35. Ambiri mwa amenewa tsopano akuphunzira Baibulo.”

Kukonda Anthu Pawokhapawokha

16. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kukonda gulu la anthu ndi kukonda anthu pawokhapawokha?

16 N’zosavuta kukonda anansi athu monga gulu. Komano kukonda anthu pawokhapawokha nthawi zina kumavuta. Mwachitsanzo, anthu ena amakonda anansi awo pongopereka zinthu kapena ndalama ku bungwe linalake lothandiza anthu ovutika. Inde, m’posavuta kwambiri kunena kuti timakonda mnansi wathu kusiyana ndi kukonda mnzathu wa kuntchito amene amaoneka kuti satiganizira, kapena kukonda munthu amene timakhala naye pafupi yemwe amachita zinthu zopsetsa mtima, kapenanso kukonda mnzathu amene amachita zinthu zotikhumudwitsa.

17, 18. Kodi Yesu anasonyeza bwanji chikondi kwa anthu pawokhapawokha, ndipo kodi anatero n’cholinga chotani?

17 Tingaphunzire za kukonda anthu pawokhapawokha, poona chitsanzo cha Yesu, amene anatsanzira ndendende makhalidwe a Mulungu. Ngakhale kuti anabwera padziko pano kudzachotsa uchimo wadziko, iye anasonyeza chikondi kwa anthu pawokhapawokha, monga kwa mayi wodwala, munthu wakhate, komanso mwana. (Mateyo 9:20-22; Maliko 1:40-42; 7:26, 29, 30; Yohane 1:29) Chimodzimodzinso, ifeyo timasonyeza chikondi kwa anzathu m’njira imene timachitira zinthu ndi anthu amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku.

18 Komabe tisaiwale kuti kukonda mnansi kumayenderana ndi kukonda Mulungu. Ngakhale kuti Yesu anathandiza osauka, kuchiza odwala, ndi kudyetsa anjala, cholinga chake pochita zimenezi ndiponso pophunzitsa anthu chinali chothandiza anthu kuti abwerere kwa Yehova. (2 Akorinto 5:19) Yesu ankachita zinthu zonse pofuna kuti Mulungu alandire ulemerero, ndipo sankaiwala kuti anali kuimira ndi kutsanzira Mulungu chifukwa ankam’konda. (1 Akorinto 10:31) Potsanzira Yesu, nafenso tingasonyeze kuti timakonda anansi athu komabe n’kusakhala mbali ya dziko la anthu oipali.

Kodi Tingakonde Bwanji Mnansi Wathu Mmene Timadzikondera Tokha?

19, 20. Kodi kukonda mnansi wathu mmene timadzikondera tokha kumatanthauza chiyani?

19 Yesu anati: “Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.” Mwachibadwa timadziganizira ndiponso timadzilemekeza. Tikanapanda kumatero, ndiye kuti lamuloli likanakhala lopanda tanthauzo kwenikweni. Kudzikonda tokha koyenereraku tisakusokoneze ndi khalidwe loipa lodzikonda lomwe mtumwi Paulo ananena pa 2 Timoteyo 3:2. M’malo mwake, ili ndi khalidwe loyenerera lodziona kuti ndiwe munthu wofunika. Katswiri wina wa maphunziro a Baibulo anafotokoza kuti ichi ndi “chikondi chabwinobwino chodzikonda wekha m’njira yosadziona kuti ‘ndine woposa ena’ kapena yodziona kuti ‘siine wonunkha kanthu.’”

20 Kukonda ena monga timadzikondera tokha kumatanthauza kuti tiziona ndiponso kuchitira ena zinthu zimene tingafune kuti ena azitichitira. Yesu anati: “Chotero zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.” (Mateyo 7:12) Onani kuti Yesu sananene kuti tizingoganizira zoipa zimene ena atichitirapo m’mbuyomo kenaka n’kubwezera zoipazo. Koma tiyeni tiziganizira zimene timafuna kuti ena azitichitira ndipo tikatero tizichita zimenezozo. Onaninso kuti Yesu sanasonyeze kuti ankangonena za anzathu ndi abale athu okha. Iye anati “anthu,” posonyeza kuti tiyenera kuchita zimenezi kwa anthu onse, kutanthauza munthu aliyense amene timakumana naye.

21. Kodi timaonetsa chiyani tikamasonyeza ena chikondi?

21 Kukonda mnansi wathu kumatiteteza kuti tisachite zoipa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Malamulo akuti, ‘Usachite chigololo, Usaphe munthu, Usabe, Usasirire mwa nsanje,’ ndiponso lamulo lina lililonse limene liliko, chidule chake chili m’mawu awa akuti, ‘Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.’ Chikondi sichikuchititsa zoipa kwa mnansi wako.” (Aroma 13:9, 10) Chikondi chimatichititsa kuti tifunefune njira zochitira zinthu zothandiza ena. Pokonda anthu anzathu, timasonyeza kuti timakondanso Yehova Mulungu, amene analenga anthu m’chifanizo chake.​—Genesis 1:26.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tizisonyeza ndani chikondi, nanga tizitero chifukwa chiyani?

• Kodi tingasonyeze bwanji chikondi kwa anthu amene satumikira Yehova?

• Kodi Baibulo limalongosola bwanji mmene tiyenera kukondera abale athu?

• Kodi kukonda mnansi wathu mmene timadzikondera tokha kumatanthauza chiyani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

“Mnansi wanga ndani kwenikweni?”

[Chithunzi patsamba 29]

Yesu amakondanso anthu pawokhapawokha