Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tinayesetsa Kuti Tikhale Olimba Mwauzimu

Tinayesetsa Kuti Tikhale Olimba Mwauzimu

Mbiri ya Moyo Wanga

Tinayesetsa Kuti Tikhale Olimba Mwauzimu

Yosimbidwa ndi Rolf Brüggemeier

Kalata yoyamba yomwe ndinalandira nditamangidwa inachokera kwa mnzanga. Iye anandiuza kuti mayi anga ndi achimwene anga aang’ono, Peter, Jochen, ndi Manfred, nawonso anali atamangidwa. Zimenezi zinapangitsa kuti achemwali anga aang’ono awiri atsale opanda makolo kapena achimwene awofe. Kodi n’chifukwa chiyani boma la East Germany linazunza banja lathu? Nanga n’chiyani chinathandiza banja lathu kuti likhale lolimba mwauzimu?

NKHONDO yachiwiri ya padziko lonse inasokoneza mtendere womwe tinali nawo tili ana n’kutionetsa nkhanza zoopsa. Abambo analowa usilikali m’gulu la nkhondo la dziko la German ndipo anafa ali kapolo wogwidwa ku nkhondo. Motero, amayi anga, omwe dzina lawo linali Berta, tsopano anayenera kusamalira ana 6. Woyamba anali ndi zaka 16 ndipo wotsiriza anali ndi chaka chimodzi.

Amayi anakhumudwa kwambiri ndi nkhani ya kupembedza chifukwa cha tchalitchi chomwe ankapitako, moti sankafuna n’komwe kumva chilichonse chonena za Mulungu. Koma tsiku lina mu 1949, Ilse Fuchs, mayi wochepa thupi, waulemu, anabwera pa khomo lathu kudzalalikira za Ufumu wa Mulungu. Mafunso omwe anafunsa komanso zimene anafotokoza zinawachitsa chidwi amayi. Phunziro la Baibulo linapatsa mayiwo chiyembekezo.

Koma poyamba, anyamatafe tinkakayikira. A boma la chipani cha Nazi ndipo kenako a boma la Chikomyunizimu anatilonjeza zinthu zambirimbiri, koma anatinamiza pa zinthu zonsezo. Ngakhale kuti anyamatafe tinkakayikira malonjezo ena onse a anthu, tinachita chidwi titadziwa Mboni zina zomwe zinali m’ndende zozunzirako anthu chifukwa chokana kuthandizira nkhondo. Chaka chotsatira, ineyo, Peter ndi amayi, tinabatizidwa.

Mng’ono wathu Manfred nayenso anabatizidwa, koma choonadi chinali chisanakhazikike mumtima mwake. Pamene a boma la Chikomyunizimu analetsa ntchito yathu mu 1950 ndipo apolisi ovuta a Stasi atam’panikiza, anaulula kumene tinkachitira misonkhano. Zimenezi n’zimene zinachititsa kuti amayi ndi ang’ono anga aja amangidwe.

Kutumikira M’nthawi ya Chiletso

Chifukwa cha chiletso, tinkafunika kunyamula mabuku mozemba n’kuwapititsa m’dziko la East Germany. Monga wonyamula mabuku, ndinkatenga mabukuwa m’chigawo chakumadzulo kwa Berlin, kumene mabuku athu sanali oletsedwa, n’kumawadutsitsa malire. Ndinawazembapo apolisi maulendo angapo, koma mu November 1950, anandigwira.

Apolisi a Stasi anandiika mu ndende yopanda mawindo, ya pansi panthaka. Masana sankandilola kugona, ndipo usiku ankandifunsa mafunso ndipo nthawi zina ankandimenya. Sindinkaonana ngakhale kulankhulana ndi am’banja langa mpaka mu March 1951 pamene amayi, Peter ndi Jochen anabwera ku khoti pa nthawi ya mlandu wanga. Anandilamula kukakhala ku ndende zaka 6.

Peter, Jochen, ndi amayi anamangidwa patangotha masiku 6 pambuyo pa mlandu wanga. Kenako, mlongo wina anatenga mchemwali wanga Hannelore, amene anali ndi zaka 11, ndipo mayi aakulu anatenga Sabine, yemwe anali ndi zaka 7. Apolisi a Stasi omwe ankawalondera, ankaona amayi ndi ang’ono anga ngati zigawenga zoopsa, moti anawalanda ngakhale zingwe za nsapato zawo. Ankawauza kuti angoimirira nthawi yonse imene anali kuwafunsa. Nawonso anapatsidwa chilango chokakhala ku ndende zaka 6 aliyense.

Mu 1953, ine ndi Mboni zina zomwe zinali m’ndende, tinapatsidwa ntchito yomanga bwalo laling’ono loterapo ndege za nkhondo, koma tinakana. Otiyang’anira anatipatsa chibalo cha masiku 21 potikhazika kwatokha ndipo izi zinapangitsa kuti tisamagwire ntchito, tisamalembe kalata ndiponso kuti tizipatsidwa chakudya chochepa. Alongo ena anali kusunga buledi wochepa yemwe ankalandira n’kumadzatipatsako mobisa. Umu ndi mmene ndinadziwira Anni, mmodzi mwa alongowo, kenako ndinam’kwatira titatuluka m’ndende. Iyeyo anatuluka mu 1956 ndipo ine mu 1957. Patangotha chaka, titakwatirana, Ruth, mwana wathu wamkazi anabadwa. Peter, Jochen, ndi Hannelore anakwatira motsatizana.

Patapita zaka pafupifupi zitatu n’tatulutsidwa m’ndende, ndinamangidwanso. Wapolisi wina wa Stasi anandinyengerera kuti ndikhale kazitape wawo. Anandiuza kuti: “Ganizani mwanzeru bambo Brüggemeier. Mukudziwa mmene ndende imawawira, ife sitikufuna kuti mukavutikenso chonchija. Mukhoza kukhalabe Mboni, kumaphunzirabe, n’kumakambabe za Baibulo mmene mukufunira. Ifetu tikungofuna kuti muzitiuza zimene zikuchitika. Taganizani za mkazi wanu ndi mwana wanu wamng’ono uja.” Mawu omalizawo anandikhumudwitsa kwambiri. Komabe, ndinkadziwa kuti ndikapita ku ndende, Yehova angathe kusamalira banja langa kuposa mmene ndikanachitira ineyo, ndipo anaterodi.

Olamulira anali kum’kakamiza Anni kuti azigwira ntchito nthawi zonse ndipo anaika anthu oti azisamalira Ruth m’kati mwa mlungu. Anni anakana zimenezo ndipo ankagwira ntchito usiku kuti masana azitha kusamalira Ruth. Abale athu auzimu anatithandiza kwambiri ndipo ankapatsa mkazi wanga zinthu zambiri moti nayenso ankagawirako ena. Apa n’kuti ine nditakhala pafupifupi zaka 6 m’ndende.

Mmene Tinakhalirabe ndi Chikhulupiriro Tili M’ndende

Nditabwereranso kundende, Mboni zinzanga zomwe ndinkagona nazo chipinda chimodzi kundende imodzi zinafuna kudziwa zofalitsa zomwe zinatulutsidwa posachedwapa? Ndinasangalala kwambiri chifukwa choti ndinali n’tawerenga mwakhama magazini a Nsanja ya Olonda ndiponso ndinkapita ku misonkhano nthawi zonse, moti ndinawalimbikitsa kwambiri mwauzimu abale angawo.

Titawapempha Baibulo olondera ndende, anatiyankha kuti: “Kupereka Baibulo kwa Mboni za Yehova kuli ngati kupereka zida kwa munthu womangidwa kuti athyole ndende n’kuthawa.” Tsiku lililonse, abale amene anali kutsogolera ankasankha lemba loti tikambirane. Pa mphindi 30 zomwe tinkayenda tsiku lililonse powongola miyendo, palibe chomwe chinkatisangalatsa kwambiri kuposa kukambitsirana lemba la m’Baibulo la tsikulo. Ngakhale kuti tinkakhala motalikirana pa mtunda woposa mamita asanu ndipo sitimaloledwa kulankhulana, tinali kupezabe njira zotumizira lembalo kwa munthu wina. Tikabwerera m’maselo athu, timasonkhanitsa zomwe aliyense anamva, n’kukambitsirana mbali ya m’Baibulo ya patsikulo.

Kenako, kazitape wina anatiulula, motero ineyo ananditsekera m’selo yandekha. Ndinali wosangalala kwambiri panthawiyo podziwa kuti ndinali n’taloweza malemba ambirimbiri. Masiku omwe ndinali ndekhandekhawo ndinali kusinkhasinkha pa nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo. Kenaka anandisamutsira ku ndende ina, komwe wolondera anandiika ndi Mboni zina ziwiri, ndipo chosangalatsa kwambiri chinali chakuti anatipatsa Baibulo. Patapita miyezi 6 ndili m’ndende yandekha, ndinasangalala kuti pambuyo pake ndinathanso kukambirana nkhani za m’Baibulo ndi okhulupirira anzanga.

Mchimwene wanga Peter anali m’ndende ina ndipo analongosola motere zomwe zinam’thandiza kupirira: “Ndinkaganiza za moyo pa dziko lapansi latsopano ndipo ndinkadzaza maganizo anga ndi mfundo za m’Baibulo. Mbonife tinkalimbikitsana mwa kufunsana mafunso okhudza Baibulo kapena kufunsana zokhudza Malemba enaake. Moyo unali wovuta. Nthawi zina, anthu okwanira 11 ankatitsekera m’kachipinda kakang’ono ka mamita 12 mbali zonse. Chilichonse tinkachitira mmenemo, kudya, kugona, kusamba, ngakhale kudzithandiza kumene. Zimenezi zinatisokoneza maganizo ndipo mitima inkangokhala m’mwamba.”

Mchimwene wanga Jochen, nayenso anafotokoza zimene anakumana nazo m’ndende. Iye anati: Ndinkaimba nyimbo zomwe ndinkatha kukumbukira m’buku lathu la nyimbo. Tsiku lililonse ndinkasinkhasinkha za lemba lomwe ndalikumbukira. Nditatuluka, ndinapitiriza chizolowezi changa chophunzira zinthu zauzimu. Tsiku lililonse ndinkawerenga lemba la m’Baibulo ndi banja langa. Tinkakonzekeranso misonkhano yonse.”

Mayi Anatulutsidwa M’ndende

Amayi atamangidwa kwa zaka zoposa ziwiri, anawatulutsa. Ufulu wawo anaugwiritsa ntchito yophunzitsa Baibulo Hannelore ndi Sabine, ndipo zimenezi zinathandiza anawa kuti chikhulupiriro chawo chikhale ndi maziko olimba. Anawaphunzitsanso mmene angachitire ndi nkhani zimene zimabuka kusukulu chifukwa cha chikhulupiriro chawo mwa Mulungu. Hannelore anati: “Sitinkada nkhawa n’china chilichonse chomwe chikanachitika chifukwa cha zimenezi, popeza kuti tinkalimbikitsana kunyumba. Ubale wolimba wa m’banja lathu unatithandiza kuthana ndi mavuto omwe tinkakumana nawo.”

Hannelore anapitiriza kunena kuti: “Tinkaperekanso chakudya chauzimu kwa abale athu omwe anali m’ndende. Tinali kuwakopera pamanja magazini athunthu a Nsanja ya Olonda, polemba tizilembo ting’onoting’ono pa mapepala oterera. Tikatero, tinkawakulunga m’mapepala osalowa madzi n’kuwaika m’zipatso zooneka ngati mapichesi zomwe tinkawatumizira mwezi ndi mwezi. Tinkasangalala akatiyankha kuti zipatsozo zinali zokoma kwambiri kutanthauza kuti anali osangalala ndi chakudya chauzimu chomwe chinkabisidwa m’zipatso muja. Ntchitoyi inatilowerera kwambiri moti kunena zoona tinkasangalala nayo zedi.”

Moyo Wathu Panthawi ya Chiletso

Peter analongosola mmene moyo unalili panthawi ya chiletso m’dziko la East Germany. Iye anati: “Tinkakumana mwachinsinsi m’nyumba, m’timagulu tating’ono tomwe tinkalowa ndi kutuluka mosinthanasinthana. Pa msonkhano uliwonse tinkagwirizana za msonkhano wotsatira woti tidzakumanenso. Tinkauzana zimenezi m’njira zomva tokha kapena polemberana timanotsi poopa kuti angatimvere apolisi a Stasi.

Hannelore anafotokoza kuti: “Nthawi zina tinkalandira matepi a msonkhano. Zimenezi zinkachititsa kuti msonkhano uzikhala wosangalatsa. Kagulu kathu kakang’ono kankasonkhana kudzamvetsera malangizo a m’Baibulo kwa maola ambiri. Ngakhale kuti sitinkawaona okamba nkhaniwo, tinkatsatira bwinobwino pulogalamuyo n’kumalemba manotsi.”

Peter anafotokoza kuti: “Abale ambiri m’mayiko ena analolera kuvutika kuti atipatse mabuku ofotokoza za Baibulo. Pafupifupi zaka 10 khoma la Berlin lisanagwe mu 1989, abale anatipangira timabuku ting’onoting’ono. Pofuna kukapereka chakudya chauzimu ku East Germany, ena analolera kuwonongetsa galimoto zawo, kutaya ndalama zawo ndiponso ngakhale kutaya ufulu wawo umene. Usiku wa tsiku lina, banja lina lomwe tinkaliyembekezera silinafike. Apolisi anapeza mabuku n’kuwalanda galimoto yawo. Ngakhale kuti panali zoopsa zambiri chonchi, sitinaganize zosiya ntchitoyo kuti tikhale ndi moyo wamtendere.”

Mchimwene wanga wamng’ono Manfred, uja anatipereka mu 1950, anafotokoza chimene chinam’chititsa kuti akhalenso ndi chikhulupiriro cholimba. Iye anati: “Nditamangidwa kwa miyezi yochepa, ndinasamukira ku West Germany n’kusiya choonadi. Ndinabwerera ku East Germany mu 1954 n’kukwatira chaka chotsatira. Posakhalitsa, mkazi wanga anaphunzira choonadi, n’kubatizidwa mu 1957. Patapita nthawi, chikumbumtima chinayamba kundivuta, ndipo mothandizidwa ndi mkazi wanga, ndinabwereranso mu mpingo.

“Abale achikhristu amene ankandidziwa ndisanasiye choonadi anandilandira mwachikondi, ngati kuti panalibe chilichonse chomwe chinachitika. Ndi chinthu chosangalatsa munthu akakulonjera akumwetulira, n’kukukupatira. Ndine wosangalala kuyanjananso ndi Yehova ndiponso ndi abale anga.”

Tikupitirizabe Kumenya Nkhondo Yauzimu

Aliyense m’banja lathu wamenya zolimba nkhondo yachikhulupiriro. Peter anafotokoza kuti: “Masiku ano, mosiyana ndi kale lonse, tazunguliridwa ndi zinthu zambiri zosokeretsa ndiponso zochititsa munthu kukonda chuma. M’nthawi ya chiletso, tinali okhutira ndi zomwe tinali nazo. Mwachitsanzo, palibe aliyense amene ankafuna kukhala m’gulu lina la phunziro la buku pa zifukwa zodziwa yekha, ndipo panalibe amene ankadandaula kuti misonkhano ikuchitikira kutali komanso mochedwa. Tonsefe tinali okondwa kusonkhana pamodzi, ngakhale kuti enafe tinkafunika kuyembekezera mpaka 11 koloko usiku kuti nthawi yathu yochoka pa malo osonkhanapo ikwane.”

Mu 1959, amayi anaganiza zosamukira ku West Germany pamodzi ndi Sabine, yemwe panthawiyo anali ndi zaka 16. Chifukwa choti ankafuna kukatumikira kumene kunali ofalitsa Ufumu ochepa, ofesi ya nthambi inawatumiza ku Ellwangen, m’mzinda wa Baden-Württemberg. Ngakhale kuti amayi sanali ndi thanzi labwino, changu chawo chinachititsa Sabine kuyamba upainiya pamene anali ndi zaka 18. Sabine atakwatiwa, amayi, omwe panthawiyo anali ndi zaka 58, anaphunzira kuyendetsa galimoto kuti athe kuwonjezera zochita pa ntchito yolalikira. Ankakonda kwambiri utumiki umenewu mpaka imfa yawo mu 1974.

Ineyo nditamangidwa kachiwiri, ndinakhala kundende kwa zaka pafupifupi 6 ndipo kenaka ananditumiza ku West Germany mu 1965, popanda banja langa kudziwa. Koma patapita nthawi, mkazi wanga, Anni, ndi mwana wathu wamkazi, Ruth anabwera kudzakhala nane. Tinapempha ku ofesi ya nthambi kuti atitumize ku dera limene kuli ofalitsa ochepa, motero anatipempha kupita ku Nördlingen, Bavaria. Kumeneko n’kumene ana athu Ruth ndi mchimwene wake Johannes, anakulira. Anni anayamba utumiki wa upainiya. Chitsanzo chake chabwino chinalimbikitsa Ruth kuchita upainiya atangomaliza sukulu. Ana athu onsewo anakwatirana ndi apainiya. Panopa ali ndi mabanja ndipo tili ndi zidzukulu 6.

Mu 1987, ndinasiya ntchito mofulumira ndipo ndinayamba kuchita upainiya pamodzi ndi Anni. Patatha zaka zitatu, anandiitana ku ofesi ya nthambi ku Selters kuti ndikathandize nawo ntchito yokuza nthambiyo. Titatha pamenepo, tinathandiza nawo kumanga Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova yoyamba ku Glauchau, komwe poyamba kunali m’dziko la East Germany, ndipo pambuyo pake tinatumikira monga osamalira malowo. Chifukwa chofooka m’thupi, tinabwereranso kukhala ndi mwana wathu wamkazi ku mpingo wa Nördlingen, kumene tikuchita upainiya.

Chondisangalatsa n’chakuti, ang’ono anga ndi alongo anga onse ndiponso achibale anga ambiri akutumikirabe Mulungu wathu wabwino kwambiri, Yehova. M’zaka zonsezi, taphunzira kuti tikapitiriza kukhala olimba mwauzimu, tingathe kuona lemba la Salmo 126:3 likukwaniritsidwa m’moyo wathu. Lembali limati: “Yehova anatichitira ife zazikulu; potero tikhala okondwera.”

[Chithunzi patsamba 13]

Pa tsiku la ukwati wathu, mu 1957

[Chithunzi patsamba 13]

Ndili ndi banja langa mu 1948: (kutsogolo, kuchokera kumanzere kupita kumanja) Manfred, Berta, Sabine, Hannelore, Peter; (kumbuyo, kuchoka kumanzere kupita kumanja) ine ndi Jochen

[Zithunzi patsamba 15]

Kabuku ka panthawi ya chiletso ndi zida za apolisi a Stasi zomverera mawu mobisa

[Mawu a Chithunzi]

Forschungs- und Gedenkstätte NORMANNENSTRASSE

[Chithunzi patsamba 16]

Ndili ndi abale anga: (kutsogolo, kuchoka kumanzere kupita kumanja) Hannelore ndi Sabine; (kumbuyo, kuchoka ku manzere kupita ku manja) ineyo, Jochen, Peter, ndi Manfred