Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ebla Mzinda Woiwalika Wapezekanso

Ebla Mzinda Woiwalika Wapezekanso

Ebla Mzinda Woiwalika Wapezekanso

M’chilimwe cha 1962, Paolo Matthiae, katswiri wachinyamata wa mbiri ya zinthu zakale zokumbidwa pansi wa ku Italy, anafufuza zigwa za kumpoto cha kumadzulo kwa Suriya, koma asakudziwa chimene angapezeko. Anthu ankaganiza kuti akatswiri okumba zinthu zakale sangapeze chilichonse m’katikati mwa dziko la Suriya. Komabe, patapita zaka ziwiri, anayamba kukumba m’dera la Tell Mardikh, lili pa mtunda wa makilomita 60 kumwera kwa Aleppo. Zimene anapeza kumeneko ndi zinthu zoti anthu ambiri amati ndizo ‘zinthu zofunika kwambiri pa zinthu zonse zakale zomwe zinakumbidwa m’zaka za m’ma 1900.’

ZOLEMBA zakale zinali kusonyeza kuti panali mzinda wotchedwa Ebla. Komabe, panalibe munthu amene ankadziwa kuti ndi pa chitunda chiti mwa zitunda zambirimbiri zomwe zili ku Middle East pamene angapeze mzindawo. Cholemba china chinasimba za kupambana kwa Sarigoni wa ku Akadd pamene anagonjetsa “mzinda wa Mari, wa Yarmuti, ndi wa Ebla.” M’cholemba china, Mfumu Gudea ya ku Sumeri inatchula za matabwa a mtengo wapatali omwe analandira kuchokera ku “mapiri a ku Ibla [Ebla].” Mu mzinda wa Karnak ku Igupto, dzina la Ebla linatchulidwanso mu mndandanda wa mizinda yakale yomwe Farao Thutmose Wachitatu anagonjetsa. Choncho, mungamvetse chifukwa chimene akatswiri a zinthu zakale zokumbidwa pansi anayesetsera kupeza mzinda wa Ebla.

Ndipo anapeza zinthu zambiri atapitiriza kukumba. Mu 1968, chidutswa cha chiboliboli cha mfumu ya ku Ebla yochedwa Ibbit-Lim chinapezedwa. Chinali ndi lumbiro lolembedwa mu chinenero cha Chiakadi, lomwe linasonyeza kuti chinaperekedwa kwa mulungu wamkazi Ishtar, yemwe “anali wotchuka kwambiri mu Ebla.” Inde, zokumbidwa pansi zinayamba kuvumbula “chinenero chatsopano, mbiri yatsopano, ndi chikhalidwe chatsopano.”

Mapale olembapo omwe anapezedwa mu 1974 ndi 1975 anatchula mobwerezabwereza dzina lakalelo la Ebla ndipo zimenezi zinatsimikizira kuti Tell Mardikh ndi malo amene kunali mzinda wakale wa Ebla. Zinthu zokumbidwa pansi zinasonyezanso kuti mzindawu unakhalapo kawiri. Ebla atawonongedwa nthawi yoyamba anamangidwanso koma anadzawonongedwanso kachiwiri ndipo kwa zaka zambirimbiri anaiwalika.

Mzinda wa Mbiri Zosiyanasiyana

Mizinda yakale kwambiri inkamangidwa m’zigwa zachonde, monga m’chigwa cha pakati pa mitsinje ya Tigirisi ndi Firate, komwe anthu ankalima malo ochepa chabe ndi kukolola zinthu zambiri. Mizinda yoyamba kutchulidwa m’Baibulo inali ku Mesopotamiya. (Genesis 10:10) Mzinda wa Ebla unamangidwa pamwamba pa miyala ya laimu ndipo n’chifukwa chake uli ndi dzinalo Ebla, lomwe kukhala ngati limatanthauza “Mwala Woyera.” Zikuoneka ngati malo amenewa anasankhidwa chifukwa cha miyala ya laimuyo, yomwe imasonyeza kuti madzi ndi osavuta kupeza. Zimenezi zinali zofunika kumalo amene n’kutali ndi mitsinje yaikulu.

Popeza kuti kudera limene kunali mzinda wa Ebla, sikunkagwa mvula yambiri, anthu m’derali ankangolima mphesa, mitengo ya maolivi, ndi mbewu monga tirigu basi. Komanso, dera limenelo linali labwino kuweteramo ziweto, makamaka nkhosa. Ndiponso, Ebla, yemwe anali pakati pa chigwa cha Mesopotamiya ndi gombe la nyanja ya Mediterranean, anali pamalo abwino a malonda a matabwa, miyala yodula, ndi zitsulo. Mzinda wa Ebla unali likulu la dera lomwe munali kukhala anthu pafupifupi 200,000. Pafupifupi anthu 10 pa anthu 100 alionse mwa anthuwo ankakhala mu mzindawo.

Mabwinja a nyumba yaikulu yachifumu amasonyeza kuti pa nthawi imeneyo, mzinda wa Ebla unali wotukuka kwambiri. Anthu ankalowa ku nyumba yachifumuyo kudzera pa chipata chotalika pafupifupi mamita pakati pa 12 ndi 15. Nyumba yachifumuyo anachita kuiwonjezera m’kupita kwa nthawi, kuti ikhale yokwanira kugwiriramo ntchito za boma lamphamvu lomwe linali kukulirakulira. Ogwira ntchito m’bomalo ankayang’aniridwa ndi anthu ambiri popeza kuti mfumu ndi mkazi wake ankathandizidwa ndi “azimbuye” ndi “nduna.”

Mapale ndiponso zidutswa za mapale okwana 17,000 apezedwa. Poyambirira, n’kutheka kuti kunali mapale athunthu okwana 4,000 omwe ankasungidwa mosamala m’mashelufu amatabwa. Mapale olembedwawo amatsimikiza kuti Ebla anachita malonda kwambiri. Mwachitsanzo, zizindikiro za mafumu awiri a ku Igupto, zomwe zili pa mapalewo, zimasonyeza kuti Ebla ankachita malonda ndi Igupto. Mapalewo analembedwa makamaka m’chinenero chochita kuzokota cha ku Sumeri. Koma, ena analembedwa m’chinenero cha ku Ebla, chomwe ndi chinenero chakalekale cha Chisemitiki, ndipo chomwe anthu anatha kuwerenga ndi thandizo la mapalewo. Akatswiri a mbiri ya m’mayiko a ku Asia anadabwa kupeza chinenero cha Asemitiki chakale kwambiri choterechi. Mungachite chidwi kudziwa kuti ena a mapalewo ali ndi mndandanda wa mawu omwe analembedwa m’zinenero ziwiri, chinenero cha ku Sumeri ndiponso cha ku Ebla. Buku la Ebla​—Alle origini della civiltà urbana (Mzinda wa Ebla,womwe Unali pa Chiyambi cha Chitukuko) limatchula mapalewo kuti “mabuku otanthauzira mawu omwe ndi akale kuposa onse odziwika ndi anthu.”

Ziboliboli zimene zinakumbidwa pansi, zomwe zimaonetsa asilikali a ku Ebla akupha adani awo kapena akupereka mitu yodulidwa, zimasonyeza kuti Ebla anali ndi gulu la nkhondo lamphamvu. Komabe, ulemerero wa Ebla unatha pa nthawi imene maulamuliro a Asuri ndi Babulo anali kukula m’mphamvu zake. Ndi zovuta kudziwa bwinobwino mmene zinthu zinachitikira, koma zikuoneka ngati choyamba Sarigoni I (osati Sarigoni yemwe amatchulidwa m’lemba la Yesaya 20:1) ndipo kenako mdzukulu wake Naram-Sin anakamenya nkhondo ku Ebla. Zinthu zokumbidwa pansi zimasonyeza kuti nkhondo zimenezi zinali zachiwawa ndi zankhanza kwambiri.

Komabe, monga mmene tanenera, patapita nthawi mzindawu unayambiranso ndipo unadzakhalanso wofunika m’chigawo cha kumeneko. Mzinda watsopanowu unamangidwa motsatira ndondomeko yabwino kwambiri yomwe inapangitsa mzindawu kukhala wokongola kuposa kale. M’mbali ya m’munsi ya mzindawo munali malo opatulika operekedwa kwa mulungu wamkazi wotchedwa Ishtar, yemwe ankaonedwanso ndi anthu a ku Babulo monga mulungu wamkazi wa mphamvu za kubereka. Mwina munamvapo za chipata chotchuka kwambiri chotchedwa Ishtar, chomwe chinapezedwa m’mabwinja a mzinda wa Babulo. Nyumba ina yokongola kwambiri ku Ebla ikuoneka kuti inali yosungiramo mikango, yomwe inkaonedwa monga yopatulika kwa mulungu wamkazi Ishtar. Zimenezi zikutifikitsa pa nkhani ya kupembedza mu Ebla.

Kupembedza mu Ebla

Monga madera ena a kum’mawa kalelo, Ebla anali ndi gulu la milungu. Ina ya milunguyo inali Baala, Hadadi (dzina lomwe linali kuphatikizidwa ku mayina a mafumu ena a ku Suriya), ndi Dagani. (1 Mafumu 11:23; 15:18; 2 Mafumu 17:16) Anthu a ku Ebla ankaopa milungu yonseyi. Ankalemekezanso ngakhale milungu ya anthu ena. Zinthu zokumbidwa pansi zikusonyeza kuti, makamaka m’zaka za pakati pa 1000 ndi 2000 B.C.E., makolo achifumu akale ankalambiridwa monga milungu.

Koma, anthu a ku Ebla sanadalire kotheratu milungu yawo ayi. Mzinda watsopano wa Ebla unalinso ndi mipanda iwiri yaikulu yozungulira mzindawo, yomwe iyenera kuti inachititsa mantha mdani aliyense. Mpanda wa kunja unali wozungulira mtunda wa pafupifupi makilomita atatu. Ndipo mipandayo imaonekabe kumeneko.

Komabe, nawonso mzinda wa Ebla womangidwanso umenewu unatha. Mwina anali Ahiti mu 1600 B.C.E. amene anawonongeratu ulamulirowu womwe kale unali wamphamvu. Malinga ndi ndakatulo ina yakale, Ebla “anaphwanyidwa ngati mtsuko woumba.” Posakhalitsa, Ebla anayamba kuzimiririka. Chikalata cholembedwa ndi anthu odzitcha Akhristu, omwe anali kukamenya nkhondo ku Yerusalemu mu 1098, chimatchula malo omwe panali Ebla, kuti n’kumene kunali msasa wawo wakutali m’dziko lotchedwa Mardikh. Mzinda wa Ebla unali utaiwalikiratu, koma unapezekanso patapita zaka zambirimbiri.

[Bokosi patsamba 14]

EBLA AKUGWIRIZANA BWANJI NDI BAIBULO?

Mu 1976, nkhani ina yosindikizidwa mu magazini ya Biblical Archeologist (Katswiri wa Zinthu Zokumbidwa Pansi Zokhudza Baibulo) inachititsa chidwi akatswiri a maphunziro a Baibulo. Munthu amene anawerenga zolembedwa pa mapale amene anapezedwa ku Ebla anati, n’zotheka kuti mwa zinthu zina zimene zinalembedwa m’mapalewo munali mayina a anthu ndiponso a malo omwe anatchulidwa m’Baibulo, patapita zaka zambiri. Mwina ponena zimene nkhaniyo sinanene n’komwe, akatswiri ena anayamba kulemba kuti, zinthu zomwe zinakumbidwa pansi ku Ebla, zinatsimikizira kuti nkhani ya m’buku la Genesis ndi yoona. * Mjezuwiti wina dzina lake Mitchell Dahood, ananena kuti “mapale [opezedwa ku Ebla] akumveketsa zinthu zovuta kumvetsa m’Baibulo.” Mwachitsanzo, anakhulupirira kuti mapalewo akhoza kuthandiza kuthetsa “vuto losadziwa kuti dzina la Mulungu wa Isiraeli linayamba kudziwika liti.”

Tsopano mawu a pa mapalewo akuwerengedwa mosamala kwambiri. Popeza kuti chinenero cha Chiheberi ndiponso cha ku Ebla, ndi zinenero za Chisemitiki, n’zotheka kuti mayina ena a mizinda kapena a anthu angakhale ofananako mwinanso olingana ndendende ndi mayina otchulidwa m’Baibulo. Komabe, zimenezi sizikutsimikizira kuti mayinawo akutchula za malo kapena anthu ofanana ayi. Mmene zinthu zopezedwa ku Ebla zidzakhudzire maphunziro a Baibulo zidzaoneka m’tsogolo. Ponena za dzina la Mulungu, wolemba nkhaniyo m’magazini ya Biblical Archeologist anakana kuti sananenepo kuti dzina loti “Yahweh” limatchulidwa m’mapale opezedwa ku Ebla. Kwa akatswiri ena, chizindikiro chomasuliridwa kuti ja chikunena za mulungu mmodzi wa m’gulu la milungu yambiri ya ku Ebla. Koma, akatswiri ena ambiri amafotokoza chizindikirocho monga chizindikiro cha kalembedwe basi. Mulimonse mmene zilili, chizindikirocho sichikunena za Mulungu woona yekha, Yehova.​—Deuteronomo 4:35; Yesaya 45:5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Onani nkhani yofotokoza mmene zinthu zakale zokumbidwa pansi zimagwirizanira ndi Baibulo, m’chaputala 4 cha buku la Baibulo​—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lomwe limafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mapu/​Chithunzi patsamba 12]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

NYANJA YAIKULU

KANANI

SURIYA

Aleppo

Ebla (Tell Mardikh)

Mtsinje wa Firate

[Mawu a Chithunzi]

Archaeologist: Missione Archeologica Italiana a Ebla - Università degli Studi di Roma ‘La Sapienza’

[Chithunzi pamasamba 12, 13]

Chovala m’khosi cha golidi chomwe chinapangidwa cha m’ma 1750 B.C.E.

[Chithunzi patsamba 13]

Mabwinja a nyumba yaikulu yachifumu

[Chithunzi patsamba 13]

Chithunzi cha mapale amene akusungidwa m’chipinda chosungiramo zinthu zakale

[Chithunzi patsamba 13]

Phale lolembedwa

[Chithunzi patsamba 13]

Ndodo yachifumu ya ku Igupto yopangidwa pakati pa 1750 ndi 1700 B.C.E

[Chithunzi patsamba 13]

Msilikali wa ku Ebla ali ndi mitu ya adani

[Chithunzi patsamba 14]

Chipilala choperekedwa kwa mulungu wamkazi Ishtar

[Mawu a Chithunzi]

Missione Archeologica Italiana a Ebla - Università degli Studi di Roma ‘La Sapienza’

[Mawu a Chithunzi patsamba 13]

All images (except palace remains): Missione Archeologica Italiana a Ebla-Università degli Studi di Roma ‘La Sapienza’