Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tsiku la Yehova Lili Pafupi”

“Tsiku la Yehova Lili Pafupi”

“Tsiku la Yehova Lili Pafupi”

“Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza.”​—ZEFANIYA 1:14.

1, 2. (a) Kodi Akhristu akudikira tsiku lofunika liti? (b) Kodi tingafunikire kufunsa mafunso ati, ndipo n’chifukwa chiyani?

MTSIKANA wina wansangala, akudikira mwachidwi tsiku la ukwati wake. Mzimayi woyembekezera akudikira mwachikondi tsiku limene mwana wake adzabadwe. Munthu wogwira ntchito yemwe sanapume kwa nthawi yaitali, akudikirira kuyamba holide yomwe wakhala akuidikirira kwa nthawi yaitali. Kodi anthu onsewa akufanana bwanji? Onsewa akudikirira tsiku lofunika kwambiri, tsiku lomwe lidzakhudze moyo wawo. Iwo ali ndi chimwemwe mumtima mwawo koma pa zifukwa zosiyana kwambiri. Tsiku limene akudikira lidzafika ndithu, ndipo likadzafika akufuna kudzakhala okonzeka.

2 Mofanana ndi zimenezo Akhristu oona masiku ano, akudikirira mwachidwi kufika kwa tsiku lofunika kwambiri. Limeneli ndi “tsiku la Yehova” lalikulu. (Yesaya 13:9; Yoweli 2:1; 2 Petulo 3:12) Kodi “tsiku la Yehova” limene likudzali ndi liti, ndipo kodi kudza kwake kudzakhudza motani anthu? Ndiponso kodi ndi motani mmene tingatsimikizire kuti takonzekera kudza kwa tsikulo? N’kofunika kuti tifunefune mayankho a mafunso amenewa tsopano, chifukwa umboni ukusonyeza kuti mawu a m’Baibulo otsatirawa ndi oona, akuti: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza.”​—Zefaniya 1:14.

“Tsiku Lalikulu la Yehova”

3. Kodi “tsiku lalikulu la Yehova” n’chiyani?

3 Kodi “tsiku lalikulu la Yehova” n’chiyani? M’Malemba, mawu akuti “tsiku la Yehova” amaimira nthawi zapadera zimene Yehova anapereka chiweruzo kwa adani ake ndi kulemekezetsa dzina lake lalikulu. Anthu osakhulupirika a ku Yuda ndi ku Yerusalemu komanso anthu otsendereza anzawo omwe ankakhala ku Babulo ndi ku Iguputo onse anakumana ndi ‘masiku a Yehova,’ pamene Yehova anawaweruza. (Yesaya 2:1, 10-12; 13:1-6; Yeremiya 46:7-10) Komabe, “tsiku la Yehova” lalikulu kwambiri pa onse lidakali m’tsogolo. Limeneli ndi “tsiku” limene Yehova adzaweruze anthu amene amanyoza dzina lake. Tsikuli lidzayamba ndi kuwonongedwa kwa “Babulo Wamkulu,” ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga, ndipo mapeto ake adzakhala kuthetseratu zinthu zina zonse za dongosolo la zinthu loipali pa nkhondo ya Armagedo.​—Chivumbulutso 16:14, 16; 17:5, 15-17; 19:11-21.

4. Kodi n’chifukwa chiyani anthu ochuluka kwambiri padziko lonse ayenera kuchita mantha ndi tsiku la Yehova limene likuyandikira mofulumira?

4 Padziko lonse, anthu ochuluka kwambiri, kaya akudziwa kapena ayi, ayenera kuchita mantha ndi tsikuli limene likuyandikira mofulumira. Chifukwa chiyani? Kudzera mwa mneneri Zefaniya, Yehova anayankha kuti: “Tsikulo ndi tsiku la mkwiyo, tsiku la masauko ndi lopsinja tsiku la bwinja, ndi chipasuko, tsiku la mdima ndi la chisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii.” Zimenezitu n’zoopsa kwambiri. Kuphatikiza apo, mneneriyu anati: “Ndidzatengera anthu zowapsinja . . . popeza anachimwira Yehova.”​—Zefaniya 1:15, 17.

5. N’chifukwa chiyani mamiliyoni a anthu ena amadikira tsiku la Yehova mwachidwi?

5 Komabe, mamiliyoni a anthu ena, akudikira mwachidwi kufika kwa tsiku la Yehova. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti iwo akudziwa kuti idzakhala nthawi yopulumutsa ndi yowombola anthu olungama. Lidzakhala tsiku limene Yehova mwini adzapambana ndipo dzina lake lolemekezeka lidzayeretsedwa. (Yoweli 3:16, 17; Zefaniya 3:12-17) Kaya anthu akuchita mantha ndi tsikuli kapena akulidikirira mwachidwi, zikudalira kwambiri pa zimene anthuwo akuchita ndi moyo wawo tsopano. Kodi inu mumaona motani kufika kwa tsiku limenelo? Kodi mwalikonzekera? Kodi mfundo yakuti tsiku la Yehova lili pafupi imakhudza moyo wanu wa tsiku ndi tsiku tsopano lino?

“Kudzakhala Onyodola ndi Kunyodola Kwawo”

6. Kodi anthu ambiri amaliona bwanji “tsiku la Yehova,” ndipo n’chifukwa chiyani Akhristu oona sadabwa ndi zimenezi?

6 Ngakhale kuti m’nthawi imene tikukhalamoyi anthu akufunika kuchitapo kanthu mwachangu, anthu ambiri padziko lapansi sasamala n’komwe za kuyandikira kwa “tsiku la Yehova.” Amanyoza ndi kunyodola anthu amene akuwachenjeza za kuyandikira kwa tsikuli. Akhristu oona sadabwa ndi zimenezi. Iwo amakumbukira chenjezo limene mtumwi Petulo analemba, lakuti: “Mukudziwa kuti m’masiku otsiriza kudzakhala onyodola ndi kunyodola kwawo, otsatira zilakolako zawo, amene azidzati: ‘Kuli kuti kukhalapo kwake kolonjezedwa kuja? Taonani, kuchokera tsiku limene makolo athu anamwalira, zinthu zonse zikupitirirabe chimodzimodzi monga kuyambira pachiyambi cha chilengedwe.’”​—2 Petulo 3:3, 4.

7. N’chiyani chimene chingatithandize kukhalabe achangu?

7 Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kukana maganizo oipa amenewa n’kukhalabe achangu? Petulo anati: “Ndikulimbikitsa luso lanu la kulingalira bwino mwa kukukumbutsani, kuti mukumbukire mawu amene aneneri oyera ananena kale, ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi wathu kudzera mwa atumwi anu.” (2 Petulo 3:1, 2) Kumvetsera machenjezo aulosi kudzatithandiza ‘kulimbikitsa luso lathu la kulingalira bwino.’ Mwina takhala tikumva zikumbutso zimenezi mobwerezabwereza, koma n’kofunika kwambiri kuti tipitirize kumvetsera machenjezo amenewa tsopano, kuposa kale lonse.​—Yesaya 34:1-4; Luka 21:34-36.

8. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amanyalanyaza zikumbutso za m’Baibulo?

8 N’chifukwa chiyani anthu ena amanyalanyaza zikumbutso zimenezi? Petulo akupitiriza kuti: “Mwakufuna kwawo, amalephera kuzindikira mfundo iyi yakuti, kunali miyamba kuchokera kalekale, ndipo mwa mawu a Mulungu, dziko lapansi linali loumbika motsendereka pamwamba pa madzi ndi pakati pa madzi; ndipo mwa zimenezi, dziko la panthawiyo linawonongeka pamene linamizidwa ndi madzi.” (2 Petulo 3:5, 6) Inde, pali anthu amene safuna kuti tsiku la Yehova lifike. Safuna kuti china chilichonse chisokoneze moyo wawo. Safuna kuti Yehova akawaimbe mlandu chifukwa cha khalidwe lawo lodzikonda. Monga mmene Petulo ananenera, iwo amakhala motsatira “zilakolako zawo.”

9. Kodi anthu a m’masiku a Nowa ndi Loti anali ndi maganizo otani?

9 “Mwakufuna kwawo,” anthu onyodola amenewa amasankha kunyalanyaza kuti Yehova ankalowerera m’zochita za anthu kalelo. Onse awiri, Yesu Khristu ndi mtumwi Petulo anatchula zochitika ziwiri zoterozo, za “m’masiku a Nowa” ndi za “m’masiku a Loti.” (Luka 17:26-30; 2 Petulo 2:5-9) Chigumula chisanabwere, anthu sanasamale za chenjezo limene Nowa anapereka. Chimodzimodzinso Sodomu ndi Gomora asanawonongedwe, akamwini ake a Loti “anam’yesa wongoseka.”​—Genesis 19:14.

10. Kodi Yehova akunena chiyani za anthu amene akunyalanyaza za tsikulo?

10 Sizikusiyananso ndi masiku ano. Komabe, imvani zimene Yehova akunena kwa anthu amene akunyalanyaza, akuti: “Ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m’mtima mwawo, ‘Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.’ Ndipo zolemera zawo zidzakhala zakufunkhidwa; ndi nyumba zawo zabwinja; adzamangadi nyumba, koma sadzagonamo; adzawoka minda yampesa koma sadzamwa vinyo wake.” (Zefaniya 1:12, 13) Anthu angapitirize kuchita ntchito zawo zomwe amachita tsiku lililonse, koma sadzapeza phindu lililonse lokhalitsa ku ntchito yawo imene akugwira mwakhamayo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti tsiku la Yehova lidzafika mwadzidzidzi, ndipo chuma chilichonse chakuthupi chimene angapeze, sichidzawapulumutsa.​—Zefaniya 1:18.

“Uwalindilire”

11. Kodi ndi malangizo ati amene tiyenera kukumbukira?

11 Mosiyana ndi dziko loipa lomwe tikukhalamoli, tiyenera kukumbukira malangizo amene mneneri Habakuku anapereka akuti: “Masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.” (Habakuku 2:3) Ngakhale ngati tsikulo lingaoneke kuti likuchedwa chifukwa cha kaonedwe kathu kopanda ungwiro, tiyenera kukumbukira kuti Yehova sazengereza. Tsiku lake lidzafika panthawi yake yeniyeni, pa ola limene anthu sakuyembekezera.​—Maliko 13:33; 2 Petulo 3:9, 10.

12. Kodi Yesu anachenjeza chiyani, ndipo zimene anachenjezazo zikusiyana motani ndi zochita za otsatira ake okhulupirika?

12 Potsindika kufunika kodikira tsiku la Yehova, Yesu anachenjeza kuti ngakhale ena a otsatira ake adzasiya kukhala achangu. Ananeneratu za iwo kuti: “Koma ngati kapolo woipayo anganene mu mtima mwake kuti, ‘Mbuye wanga akuchedwa,’ ndi kuyamba kumenya akapolo anzake ndi kudya komanso kumwa limodzi ndi zidakwa zenizeni, mbuye wa kapolo ameneyo adzabwera pa tsiku limene iye sakuyembekezera ndi pa ola limene sakulidziwa, ndipo adzam’patsa chilango choopsa.” (Mateyo 24:48-51) Mosiyana ndi zimenezo, gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, mokhulupirika likukhalabe lachangu. Gulu la kapolo limeneli lakhalabe maso ndipo lasonyeza kuti ndi lokonzeka. Yesu waika gulu limeneli kuti ‘liyang’anire zinthu zake zonse’ pano pa dziko lapansi.​—Mateyo 24:42-47.

Tikufunika Kuchita Changu

13. Ndi motani mmene Yesu anasonyezera kufunika kochita changu?

13 Kunali kofunika kwa Akhristu oyambirira kukhalabe achangu. Anafunikira kuthawa mwamsanga kuchoka ku Yerusalemu pamene anaona mzindawo ‘utazingidwa ndi magulu ankhondo.’ (Luka 21:20, 21) Zimenezo zinachitika mu 66 C.E. Taonani mmene Yesu anasonyezera kufunika koti Akhristu m’nthawi imeneyo adzachite changu. Iye anati: “Munthu amene ali padenga la nyumba asadzatsike kukatenga katundu m’nyumba mwake; ndipo munthu amene ali m’munda asadzabwerere kunyumba kukatenga malaya ake akunja.” (Mateyo 24:17, 18) Popeza mbiri imasonyeza kuti Yerusalemu sanawonongedwe mpaka panadutsa zaka zina zinayi, ndiye n’chifukwa chiyani Akhristu anafunika kumvera msanga mawu a Yesu mu 66 C.E.?

14, 15. N’chifukwa chiyani kunali kofunika kuti Akhristu a m’zaka 100 zoyambirira achitepo kanthu mwamsanga ataona kuti Yerusalemu wazingidwa ndi magulu ankhondo?

14 Ngakhale n’zoona kuti asilikali Achiroma sanawononge Yerusalemu mpaka m’chaka cha 70 C.E., m’zaka zinayizo kunalibe mtendere. Inde, zaka zimenezo zinadzaza chiwawa ndiponso kuphana. Wolemba mbiri wina anafotokoza kuti panthawi imeneyo m’Yerusalemu munali “nkhondo ya pachiweniweni yochititsa mantha imene inapha anthu kwambiri, ndiponso munali nkhanza zosaneneka.” Anyamata analembedwa usilikali kuti alimbitse chitetezo ndi kukatumikira ku nkhondo. Tsiku lililonse ankaphunzira za nkhondo. Anthu amene sanali kugwirizana ndi mfundo zokhwima za chitetezo zimenezo, ankaonedwa ngati oukira. Ngati Akhristu akanachedwa kuchoka mu mzindawo, zinthu zikanakhala zoopsa kwa iwo.​—Mateyo 26:52; Maliko 12:17.

15 Onani kuti Yesu anati, “amene ali ku Yudeya,” osati ku Yerusalemu chabe, anayenera kuyamba kuthawa. Zimenezi zinali zofunika chifukwa chakuti asilikali Achiromawo atangochoka ku Yerusalemu kwa miyezi yowerengeka, anayambiranso nkhondo yawoyo. Choyamba anagonjetsa Galileya mu 67 C.E., ndipo kenako m’chaka chotsatira anayamba kugonjetsa madera a Yudeya. Chifukwa cha zimenezi madera a kunja kwa mzinda wa Yerusalemu anali pa mavuto aakulu. Komanso zinali zovuta kwambiri kuti Myuda aliyense athawe kuchoka mu Yerusalemu mwenimwenimo. Zipata za mzindawo zinkalonderedwa, ndipo aliyense amene anayesera kuthawa ankaganiziridwa kuti anali kukagwirizana ndi Aroma.

16. Kodi Akhristu a m’zaka l00 zoyambirira anafunikira kukhala ndi mtima wotani kuti apulumuke pa nthawi ya mavuto imeneyo?

16 Tikaganizira mfundo zonsezi, tingamvetse chifukwa chimene Yesu anatsindikira kuti inali nthawi yofunika kuchita zinthu mwachangu. Akhristu anafunika kukhala odzimana, osalola chuma chakuthupi kuti chiwatanganitse. Anayenera kulolera “kulekana ndi chuma [chawo] chonse,” kuti amvere chenjezo la Yesu. (Luka 14:33) Anthu amene anamvera mwachangu ndi kuthawira ku mbali ina ya Yorodano anapulumutsidwa.

Kukhalabe Achangu

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala achangu kwambiri?

17 Maulosi a m’Baibulo amanena momveka bwino kuti tikukhala m’nthawi ya mapeto. Tiyenera kukhala achangu kwambiri kuposa n’kale lonse. Panthawi ya mtendere, msilikali sadera nkhawa ndiponso saganiza za kuopsa kwa nkhondo. Komabe, ngati saona kufunika kokhala tcheru nthawi zonse ndipo mwadzidzidzi n’kuitanidwa ku nkhondo, angakhale wosakonzekera, ndipo zotsatirapo zake zingakhale zoopsa. N’chimodzimodzinso mwauzimu. Tikalola kuti changu chathu chizilale, tingakhale osakonzekera kudziteteza ku zovuta zimene tingakumane nazo ndipo sitingadziwe pamene tsiku la Yehova likufika. (Luka 21:36; 1 Atesalonika 5:4) Ngati aliyense ‘wabwerera osam’tsata Yehova,’ ino ndi nthawi yakuti ayambenso kum’funafuna.​—Zefaniya 1:3-6; 2 Atesalonika 1:8, 9.

18, 19. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kukumbukira nthawi zonse za “kukhalapo kwa tsiku la Yehova”?

18 N’chifukwa chake mtumwi Petulo akutilimbikitsa kuti nthawi zonse tizikumbukira za “kukhalapo kwa tsiku la Yehova.” Kodi tingachite motani zimenezi? Njira imodzi ndiyo kukhala otanganidwa ndi ntchito zoyera ndiponso za kudzipereka kwa Mulungu. (2 Petulo 3:11, 12) Kuchita nawo nthawi zonse zinthu zimenezi kudzatithandiza kudikira ndi chidwi kufika kwa “tsiku la Yehova.” Mawu a Chigiriki omasuliridwa kuti “kukumbukira nthawi zonse” makamaka amatanthauza “kufulumiza.” N’zoona kuti sitingathe kuchititsa nthawi imene yatsalayi kuti ifulumire mpaka kufika pa tsiku la Yehova. Komabe, pamene tikudikirira tsikulo, nthawi ingaoneke ngati ikudutsa mofulumira kwambiri ngati tili otanganitsidwa muutumiki wa Mulungu.​—1 Akorinto 15:58.

19 Kusinkhasinkha Mawu a Mulungu ndiponso kulingalira zikumbutso zimene zimapezeka m’Mawuwo, kungatithandize “kulakalaka kwambiri (kuyembekeza ndi kufulumiza) kufika” kwa tsikulo. Indedi, kungatithandize “kuyembekezera nthawi zonse” za tsikulo. (2 Petulo 3:12, The Amplified Bible; The New Testament, by William Barclay) Zikumbutso zimenezi zikuphatikizapo maulosi ambirimbiri amene amaneneratu osati kokha za kufika kwa tsiku la Yehova komanso za madalitso ochuluka amene adzaperekedwa kwa anthu amene ‘amalindilira Yehova.’​—Zefaniya 3:8.

20. Kodi ndi langizo liti limene tiyenera kutsatira?

20 Tsopano ino ndiyo nthawi yoti tonsefe titsatire langizo limene linaperekedwa kudzera mwa mneneri Zefaniya lakuti: “Usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova. Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.”​—Zefaniya 2:2, 3.

21. Kodi anthu a Mulungu atsimikiza mtima kudzachita chiyani m’chaka cha 2007?

21 Choncho, lemba limene lasankhidwa kukhala lemba la chaka cha 2007 n’loyenereradi, lakuti: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi.” Anthu a Mulungu akutsimikiza mtima kuti “lili pafupi [ndipo] lifulumira kudza.” (Zefaniya 1:14) ‘Silizengereza.’ (Habakuku 2:3) Choncho pamene tikudikirira tsiku limenelo, tiyeni tikhale tcheru ndi nthawi imene tikukhalayi, pozindikira kuti kukwaniritsidwa komaliza kwa maulosi amenewa kuli pafupi!

Kodi Mungayankhe?

• Kodi “tsiku lalikulu la Yehova” n’chiyani?

• N’chifukwa chiyani anthu ambiri amanyalanyaza kuti nthawi ino ndi yofunika kuchita changu?

• N’chifukwa chiyani Akhristu a m’zaka l00 zoyambirira anafunikira kuchita changu?

• Ndi motani mmene tingakhalire achangu kwambiri?

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 19]

Lemba la chaka cha 2007 lidzakhala lakuti: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi.”​—Zefaniya 1:14.

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Monga mmene zinalili m’masiku a Nowa, onyodola adzadzidzimutsidwa Yehova akadzachitapo kanthu

[Chithunzi patsamba 18]

Akhristu anayenera kuchitapo kanthu mwamsanga pamene anaona Yerusalemu “atazingidwa ndi asilikali ankhondo”