Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova ‘Adzaonetsetsa Kuti Chilungamo Chachitika’

Yehova ‘Adzaonetsetsa Kuti Chilungamo Chachitika’

Yehova ‘Adzaonetsetsa Kuti Chilungamo Chachitika’

“Nanga Mulungu sadzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa osankhika ake, amene amafuulira kwa iye usiku ndi usana?”​—LUKA 18:7.

1. Kodi ndani amene amakulimbikitsani, ndipo n’chifukwa chiyani?

PAKATI pa Mboni za Yehova padziko lonse lapansi, pali amuna ndi akazi achikhristu amene atumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri. Kodi mumawadziwa ena mwa anthu okondedwa amenewa? Mwina mungaganize za mlongo wachikulire amene anabatizidwa zaka zambiri zapitazo ndipo salephera kawirikawiri kufika pa misonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Kapena mungaganize za m’bale wokalamba amene mokhulupirika amachirikiza mpingo mu utumiki wa kumunda sabata iliyonse, ndipo wakhala akuchita zimenezi kwa zaka zambiri. Inde, ambiri mwa anthu okhulupirika amenewa ankaganiza kuti pofika tsopano Armagedo idzakhala itafika. Komabe, ngakhale kuti dziko lopanda chilungamoli lilipobe, chidaliro chawo m’malonjezo a Yehova sichinafooke ndiponso sanasiye kukhala otsimikiza mtima kuti ‘apirire mpaka mapeto.’ (Mateyo 24:13) Kulimba kwa chikhulupiriro chimene atumiki a Yehova okhulupirikawa amasonyeza, kumalimbikitsa mpingo wonse.​—Salmo 147:11.

2. N’chiyani chimatimvetsa chisoni?

2 Komabe, nthawi zina timaona khalidwe losiyana ndi limene tatchulali. Mboni zina zinachita nawo utumiki kwa zaka zambiri, koma m’kupita kwa nthawi chikhulupiriro chawo mwa Yehova chinazilala, ndipo anasiya kusonkhana ndi mpingo wachikhristu. Timamva chisoni kuona kuti anthu omwe anali anzathu asiya Yehova, ndipo timafunitsitsa ndi mtima wonse kupitirizabe kuthandiza “nkhosa yotayika” iliyonse kuti ibwerere m’gulu la nkhosa. (Salmo 119:176; Aroma 15:1) Komabe, timakhala ndi mafunso tikaona kuti ena akukhalabe okhulupirika pamene ena akutaya chikhulupiriro. N’chiyani chimene chimachititsa kuti Mboni zambiri zikhalebe zikukhulupirira malonjezo a Yehova pamene zina zikutaya chikhulupiriro? Kodi ifeyo patokha tingachite chiyani potsimikizira kuti tikukhulupirirabe zolimba kuti “tsiku lalikulu la Yehova” likuyandikira? (Zefaniya 1:14) Tiyeni tikambirane fanizo limene limapezeka mu Uthenga Wabwino wa Luka.

Chenjezo kwa Amene Ali ndi Moyo Pamene ‘Mwana wa Munthu Afika’

3. Kodi ndani kwenikweni angapindule ndi fanizo la mkazi wamasiye ndi woweruza, ndipo n’chifukwa chiyani?

3 Pa Luka chaputala cha 18, timapezapo fanizo la Yesu lonena za mkazi wamasiye ndi woweruza. Fanizoli ndi lofanana ndi lija la wolandira mlendo wolimbikira, limene tinalikambirana mu nkhani yapita. (Luka 11:5-13) Komabe, nkhani ya m’Baibulo imene muli fanizo la mkazi wamasiye ndi woweruzayi imasonyeza kuti zimenezi makamaka zikugwira ntchito kwa anthu amene ali ndi moyo pamene ‘Mwana wa munthu afika’ mu mphamvu ya Ufumu. Nthawi imeneyi inayamba mu 1914.​—Luka 18:8. *

4. Kodi Yesu anafotokoza chiyani asanasimbe fanizo limene limapezeka pa Luka chaputala 18?

4 Asananene fanizoli, choyamba Yesu ananena kuti, umboni wa kukhalapo kwake mu mphamvu ya Ufumu udzaoneka kulikonse “monga mphezi” imene “imawala kuchokera mbali ina pansi pa thambo, kukafika mbali ina pansi pa thambo.” (Luka 17:24; 21:10, 29-33) Komabe, anthu ambiri amene akukhala mu “nthawi ya chimariziro” sadzasamala za umboni wooneka bwino umenewo. (Danieli 12:4) Chifukwa chiyani? Pa chifukwa chofanana ndi chimene anthu a m’nthawi ya Nowa ndiponso a m’nthawi ya Loti ananyalanyazira machenjezo a Yehova. M’nthawi imeneyo, anthu ‘anali kudya, anali kumwa, anali kugula, anali kugulitsa, anali kubzala, anali kumanga,’ mpaka tsiku limene anawonongedwa. (Luka 17:26-29) Anafa chifukwa chakuti anatanganitsidwa ndi ntchito zanthawi zonse zimenezo moti sanasamale za chifuniro cha Mulungu. (Mateyo 24:39) N’chimodzimodzinso ndi anthu ambiri masiku ano. Iwo ndi otanganitsidwa ndi ntchito za tsiku ndi tsiku moti amalephera kuona umboni woti mapeto a dziko ili losaopa Mulungu ali pafupi.​—Luka 17:30.

5. (a) Kodi Yesu anali kuchenjeza ndani, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) N’chiyani chimene chinachititsa kuti anthu ena ataye chikhulupiriro?

5 Mwachionekere, Yesu anali kuda nkhawa kuti otsatira akenso angathe kudodometsedwa ndi dziko la Satanali, ngakhale kufika ‘pobwerera ku zinthu zimene azisiya m’mbuyo.’ (Luka 17:22, 31) Ndithudi, zimenezi zachitika kwa Akhristu ena. Kwa zaka zambiri Akhristu amenewa analakalaka tsiku limene Yehova adzawononge dziko loipali. Komabe, ataona kuti Armagedo sinafike pa nthawi imene iwo anayembekezera, anakhumudwa. Chidaliro chawo pa kuyandikira kwa tsiku la Yehova lopereka chiweruzo chinazilala. Sanalinso achangu mu utumiki ndipo kenako anatanganitsidwa kwambiri ndi zochita wamba za m’moyo moti anali ndi nthawi yochepa yokha yochitira zinthu zauzimu. (Luka 8:11, 13, 14) M’kupita kwa nthawi, ‘anabwerera ku zinthu zimene anazisiya m’mbuyo.’ Zimenezi ndi zokhumudwitsa kwambiri.

Kufunika ‘Kopemphera Nthawi Zonse’

6-8. (a) Fotokozani fanizo la mkazi wamasiye ndi woweruza. (b) Kodi Yesu anafotokoza kuti fanizoli likugwira ntchito motani?

6 Kodi tingachite chiyani kuti tikhalebe ndi chidaliro cholimba pa kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Yehova? (Aheberi 3:14) Yesu anafunsa funso limenelo atangomaliza kuchenjeza ophunzira ake kuti asabwerere ku dziko loipa la Satana.

7 Luka ananena kuti Yesu “anawauza fanizo pofuna kuwasonyeza kufunika koti iwo azipemphera nthawi zonse, osaleka.” Yesu anati: “Mu mzinda winawake munali woweruza wina amene anali wosaopa Mulungu ndiponso wosasamala za munthu. Koma mu mzindawo munali mkazi wamasiye ndipo anali kupitapita kwa woweruza uja, kukam’pempha kuti, ‘Ndiweruzireni mlandu wanga ndi munthu amene akutsutsana nane kuti pachitike chilungamo.’ Kwa kanthawi ndithu woweruzayo samafuna, koma pambuyo pake anati mu mtima mwake, ‘Ngakhale sindiopa Mulungu kapena kusamala za munthu, komabe popeza mkazi wamasiyeyu akundivutitsa mosalekeza, ndionetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iye, kuti asapitirize kumangobwera ndi kundisautsa mapeto.’”

8 Atasimba fanizoli, Yesu anafotokoza mmene likugwirira ntchito kuti: “Mwamvatu zimene woweruzayo ananena ngakhale kuti anali wosalungama! Nanga Mulungu sadzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa osankhika ake, amene amafuulira kwa iye usiku ndi usana, ngakhale kuti amachita kuleza nawo mtima? Ndithu ndikukuuzani, Iye adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iwo mwamsanga. Koma, Mwana wa munthu akadzafika, kodi adzapezadi chikhulupiriro padziko lapansi?”​—Luka 18:1-8.

“Pachitike Chilungamo”

9. Kodi mfundo yaikulu imene ili mu fanizo la mkazi wamasiye ndi woweruza ndi iti?

9 Mfundo yaikulu ya fanizo limeneli ikumveka bwino kwambiri. Mfundo yake yatchulidwa ndi anthu onse awiri amene ali m’fanizoli komanso ndi Yesu. Mkazi wamasiye anachonderera kuti: “Pachitike chilungamo.” Woweruzayo anati: “Ndionetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iye.” Yesu anafunsa kuti: “Nanga Mulungu sadzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika?” Ndipo ponena za Yehova, Yesu anati: “Iye adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iwo mwamsanga.” (Luka 18:3, 5, 7, 8) Kodi ndi liti kwenikweni pamene Mulungu “adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika”?

10. (a) Kodi kubwezera chilango m’zaka 100 zoyambirira kunachitika liti? (b) Nanga kodi ndi liti ndiponso ndi motani mmene chilungamo chidzachitikire kwa atumiki a Mulungu masiku ano?

10 M’zaka 100 zoyambirira, “masiku obwezera chilango” anafika mu 70 C.E. pamene Yerusalemu ndi kachisi wake zinawonongedwa. (Luka 21:22) Kwa anthu a Mulungu masiku ano, chilungamo chidzachitika pa “tsiku lalikulu la Yehova.” (Zefaniya 1:14; Mateyo 24:21) Pa nthawi imeneyo, Yehova ‘adzabwezera masautso kwa osautsa’ anthu ake, kudzera m’chilango chimene Yesu Khristu adzabwezera “kwa osadziwa Mulungu ndi kwa osamvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu.”​—2 Atesalonika 1:6-8; Aroma 12:19.

11. Kodi chilungamo chidzachitika “mwamsanga” m’njira yotani?

11 Komabe, kodi ndi motani mmene tingamvetsere lonjezo la Yesu lakuti Yehova adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika “mwamsanga”? Mawu a Mulungu amasonyeza kuti ‘ngakhale kuti [Yehova] amaleza mtima,’ adzaonetsetsa kuti pa nthawi yake chilungamo chichitike mwamsanga. (Luka 18:7, 8; 2 Petulo 3:9, 10) M’nthawi ya Nowa, pamene Chigumula chinafika, oipa anawonongedwa mwamsangamsanga. Chimodzimodzinso m’tsiku la Loti, pamene moto unagwa kuchokera kumwamba, anthu oipa anawonongedwa. Yesu anati: “Zidzakhalanso momwemo pa tsikulo pamene Mwana wa munthu adzaonekera.” (Luka 17:27-30) Anthu oipa ‘adzawonongedwanso modzidzimutsa.’ (1 Atesalonika 5:2, 3) Ndithudi, tingakhulupirire ndi mtima wonse kuti nthawi yowononga dziko la Satana ikadzakwana, Yehova sadzalola kuti lipitirize kukhalapo ngakhale kwa tsiku lina limodzi, chifukwa kutero sikungakhale chilungamo.

“Iye Adzaonetsetsa kuti Chilungamo Chachitika”

12, 13. (a) Kodi fanizo la Yesu la mkazi wamasiye ndi woweruza limatiphunzitsa zotani? (b) N’chifukwa chiyani tingakhulupirire kuti Yehova adzamva mapemphero athu ndi kuonetsetsa kuti chilungamo chachitika?

12 Fanizo la Yesu la mkazi wamasiye ndi woweruza likusonyezanso mfundo zina zofunika za choonadi. Posonyeza mmene fanizoli likugwirira ntchito, Yesu anati: “Mwamvatu zimene woweruzayo ananena ngakhale kuti anali wosalungama! Nanga Mulungu sadzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa osankhika ake?” N’zoona kuti Yesu sanali kuyerekezera Yehova ndi woweruza uja ngati kuti Mulungu adzachita ndi anthu okhulupirira mofanana ndi mmene woweruzayo anachitira ayi. M’malo mwake, Yesu anaphunzitsa otsatira ake phunziro lonena za Yehova posonyeza kusiyana pakati pa woweruzayo ndi Mulungu. Kodi Mulungu ndi woweruzayo tingawasiyanitse m’njira zina ziti?

13 Woweruza wa m’fanizo la Yesu anali “wosalungama,” pamene “Mulungu ndiye Woweruza wolungama.” (Salmo 7:11; 33:5) Woweruzayo analibe chidwi chilichonse mwa mkazi wamasiye, koma Yehova ali ndi chidwi mwa munthu wina aliyense. (2 Mbiri 6:29, 30) Woweruzayo sankafuna kuthandiza mkazi wamasiye, koma Yehova ndi wofunitsitsa ndiponso amakhala tcheru kuthandiza anthu amene akum’tumikira. (Yesaya 30:18, 19) Kodi pamenepa tikupezapo phunziro lanji? Ngati woweruza wosalungama anamvera zopempha za mkazi wamasiye uja ndi kuonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iye, ndiye kuti Yehova angamvere kwambiri mapemphero a anthu ake ndi kuonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iwo.​—Miyambo 15:29.

14. N’chifukwa chiyani sitiyenera kutaya chikhulupiriro kuti tsiku la Mulungu lopereka chiweruzo lidzafika?

14 Choncho, anthu amene ataya chikhulupiriro chawo kuti tsiku la Mulungu lopereka chiweruzo lidzafika, alakwitsa kwambiri. Chifukwa chiyani? Mwa kutaya chikhulupiriro chawo cholimba chakuti “tsiku lalikulu la Yehova” lili pafupi, amasonyeza kuti akukayikira ngati Yehova ndi wodalirika kuti angasunge malonjezo ake mokhulupirika. Koma palibe munthu aliyense amene ali ndi ufulu wotsutsa kukhulupirika kwa Mulungu. (Yobu 9:12) Funso lofunika ndi lakuti, Kodi ife patokha tidzakhalabe okhulupirika? Ndipo imeneyo ndi nkhani yeniyeni imene Yesu anadzutsa pa mapeto a fanizo la mkazi wamasiye ndi woweruza.

‘Kodi Adzapezadi Chikhulupiriro Choterechi pa Dziko Lapansi?’

15. (a) Kodi ndi funso liti limene Yesu anafunsa, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa chiyani?

15 Yesu anafunsa funso lochititsa chidwi lakuti: “Mwana wa munthu akadzafika, kodi adzapezadi chikhulupiriro [choterechi] padziko lapansi?” (Luka 18:8) Mawu akuti “chikhulupiriro choterechi” akusonyeza kuti Yesu sanali kungonena za chikhulupiriro china chilichonse, koma chikhulupiriro chinachake ndithu, chonga chimene mkazi wamasiye uja anali nacho. Yesu sanayankhe funso lakelo ayi. Anafunsa n’cholinga choti ophunzira ake aganizire kuti chikhulupiriro chawo chinali chotani. Kodi chinali kuzilala pang’onopang’ono, moti anali pangozi yobwerera ku zinthu zimene anazisiya m’mbuyo? Kapena kodi anali ndi chikhulupiriro chonga chimene mkazi wamasiye uja anasonyeza? Leronso, tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndi chikhulupiriro chotani chimene “Mwana wa munthu” akuchipeza mu mtima mwanga?’

16. Kodi mkazi wamasiye uja anali ndi chikhulupiriro chotani?

16 Kuti tikhale pakati pa anthu amene Yehova adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iwo, tiyenera kutsatira zimene anachita mkazi wamasiye uja. Kodi mkaziyo anali ndi chikhulupiriro chotani? Anasonyeza chikhulupiriro chake mwa kulimbikira “kupitapita kwa woweruza uja, kukam’pempha kuti ‘Ndiweruzireni mlandu . . . kuti pachitike chilungamo.’” Mkazi wamasiye ameneyo analimbikira kuti munthu wosalungama am’chitire chilungamo. Mofanana ndi zimenezi, atumiki a Mulungu masiku ano angakhale ndi chidaliro kuti Yehova adzawachitira chilungamo, ngakhale ngati patadutsa nthawi yaitali kuposa imene ayembekezera. Kuwonjezera apo, amasonyeza chidaliro chawo m’malonjezo a Mulungu mwa kulimbikira kupemphera, inde, mwa ‘kufuulira kwa Yehova usiku ndi usana.’ (Luka 18:7) Zoonadi, ngati Mkhristu atasiya kupempherera chilungamo kuti chichitike, angasonyeze kuti wasiya kudalira kuti Yehova adzathandiza atumiki ake.

17. Kodi tili ndi zifukwa zotani zolimbikirira kupemphera ndi kukhalabe n’chikhulupiriro kuti tsiku la Yehova lopereka chiweruzo lidzafikadi?

17 Mmene zinthu zinalili ndi mkazi wamasiyeyo zimatisonyeza kuti tili ndi zifukwa zowonjezereka zolimbikirira kupemphera. Taonani kusiyana kwina pakati pa mmene zinthu zinalili kwa iyeyo ndi mmene zilili kwa ife. Mkazi wamasiyeyo anali kupitapita kwa woweruza uja ngakhale panalibe munthu wina aliyense wom’limbikitsa kutero, koma Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kwambiri kuti ‘tizilimbikira kupemphera.’ (Aroma 12:12) Panalibe chilichonse chotsimikizira mkazi wamasiyeyo kuti adzalandira zopempha zakezo, koma Yehova akutitsimikizira kuti adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika. Kudzera mwa mneneri wake, Yehova anati: “Akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.” (Habakuku 2:3; Salmo 97:10) Mkazi wamasiyeyo analibe munthu womuthandiza kuchonderera kuti pempho lake limveke msanga, koma ife tili ndi mthandizi wamphamvu, Yesu, “Iye ali kudzanja lamanja la Mulungu, ndipo amatilankhulira mochonderera kwa Mulunguyo.” (Aroma 8:34; Aheberi 7:25) Choncho, ngati mkazi wamasiyeyo, mosasamala kanthu kuti zinthu zinali zovuta kwa iye, anapitirizabe kuchonderera woweruza uja ndi chiyembekezo choti chilungamo chidzachitika, ndiye kuti ifeyo tiyenera kukhulupirira kwambiri kuti tsiku la Yehova lopereka chiweruzo lidzafikadi.

18. Ndi motani mmene pemphero lingalimbitsire chikhulupiriro chathu ndi kutithandiza kuti tichitiridwe chilungamo?

18 Fanizo la mkazi wamasiye, likutiphunzitsa kuti pali kugwirizana kwambiri pakati pa pemphero ndi chikhulupiriro ndiponso kuti kulimbikira kupemphera kungagonjetse zinthu zimene zingafooketse chikhulupiriro chathu. Zoonadi, zimenezi sizikutanthauza kuti kupemphera mongodzionetsera chabe kungatithandize kuti tisataye chikhulupiriro chathu ayi. (Mateyo 6:7, 8) Tikamapemphera chifukwa chakuti tikuzindikira kuti timadalira kwambiri Mulungu, m’pamene pemphero limatichititsa kuyandikira kwa Mulungu ndipo limalimbikitsa chikhulupiriro chathu. Ndipo popeza kuti chikhulupiriro ndi chofunika kuti tipulumuke, n’zomveka kuti Yesu anaona kufunika kolimbikitsa ophunzira ake kuti “azipemphera nthawi zonse, osaleka.” (Luka 18:1; 2 Atesalonika 3:13) N’zodziwikiratu kuti kufika kwa “tsiku lalikulu la Yehova” sikudalira pa mapemphero athu, tsikulo lidzafika kaya tilipempherere kapena ayi. Komabe, kuti ife patokha tichitiridwe chilungamo ndi kupulumuka nkhondo ya Mulungu, mosakayikira zikudalira chikhulupiriro chimene tili nacho komanso ngati tikukhala mogwirizana ndi mapemphero athu.

19. Ndi motani mmene tingasonyezere kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba choti Mulungu “adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika”?

19 Ngati titakumbukira, Yesu anafunsa kuti: “Mwana wa munthu akadzafika, kodi adzapezadi chikhulupiriro padziko lapansi?” Kodi yankho la funso lake lochititsa chidwi limenelo n’chiyani? Ndife osangalala kuti mamiliyoni a atumiki okhulupirika a Yehova padziko lonse lapansi masiku ano amasonyeza mwa mapemphero awo, kuleza mtima kwawo, ndi kulimbikira kwawo kuti alidi ndi chikhulupiriro chimenechi. Choncho, angayankhe funso la Yesu ndi mtima wonse kuti inde. Indedi, mosasamala kanthu za kupanda chilungamo kumene dziko la Satana limatichitira tsopano, tili ndi chikhulupiriro cholimba choti Mulungu adzaonetsetsa kuti “chilungamo chachitika kwa osankhika ake.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Kuti mumvetse bwino tanthauzo la fanizo limeneli, werengani Luka 17:22-33. Onani mmene zimene zalembedwa pa Luka 17:22, 24, 30, zonena za “Mwana wa munthu” zikutithandizira kuyankha funso lomwe lili pa Luka 18:8.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chiyani chachititsa kuti Akhristu ena ataye chikhulupiriro?

• N’chifukwa chiyani tingakhale ndi chikhulupiriro cholimba kuti tsiku la Yehova lopereka chiweruzo lidzafika?

• Tili ndi zifukwa ziti zolimbikirira kupemphera?

• Kulimbikira kupemphera kungatiteteze motani kuti tisataye chikhulupiriro chathu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

Ndi mfundo yaikulu iti imene yasonyezedwa mu fanizo la mkazi wamasiye ndi woweruza?

[Zithunzi patsamba 29]

Mamiliyoni a anthu masiku ano amakhulupirira kwambiri kuti Mulungu “adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika”