Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Iwe Uzikhala Wosangalala Basi”

“Iwe Uzikhala Wosangalala Basi”

“Iwe Uzikhala Wosangalala Basi”

“Uzichitira Yehova chikondwerero . . . , ndipo iwe uzikhala wosangalala basi.”​—DEUTERONOMO 16:15, NW.

1. (a) Kodi Satana anadzutsa nkhani zotani? (b) Kodi Yehova ananeneratu chiyani Adamu ndi Hava atapanduka?

SATANA atachititsa Adamu ndi Hava kupandukira Mlengi wawo, anadzutsa nkhani ziwiri zofunika kwambiri. Yoyamba, ananeneza Yehova kuti sanena zoona ndi kutinso amalamulira m’njira yolakwika. Yachiwiri, Satana ananena zinthu zosonyeza kuti anthu amatumikira Mulungu chifukwa cha zinthu zimene angapezepo basi. Nkhani yachiwiriyi anainena mosapita m’mbali mu nthawi ya Yobu. (Genesis 3:1-6; Yobu 1:9, 10; 2:4, 5) Ngakhale zinali choncho, Yehova anachitapo kanthu mwamsanga. Adamu ndi Hava akadali m’munda wa Edene, Yehova ananeneratu mmene adzathetsere nkhanizo. Ananeneratu kuti kudzabwera “mbewu” imene, pambuyo poti chitende chake chalaliridwa, idzalalira mutu wa Satana mpaka kumupha.​—Genesis 3:15.

2. Kodi Yehova ananena zinthu zina ziti zosonyeza momwe adzakwaniritsire ulosi wolembedwa pa Genesis 3:15?

2 Pamene nthawi inali kupita, Yehova ananena zinthu zina zokhudza ulosi umenewo, ndipo mwa kutero anasonyeza kuti udzakwaniritsidwadi pamapeto pake. Mwachitsanzo, Mulungu anauza Abulahamu kuti “mbewu” imeneyo idzaonekera pakati pa mbadwa zake. (Genesis 22:15-18) Chidzukulu cha Abulahamu, Yakobo, anakhala tate wa mafuko 12 a Isiraeli. Mu 1513 B.C.E., pamene mafuko amenewo anakhala mtundu, Yehova anawapatsa malamulo amene anaphatikizapo madyerero osiyanasiyana a pachaka. Mtumwi Paulo anati madyerero amenewo anali “mthunzi wa zimene zinali kubwera.” (Akolose 2:16, 17; Aheberi 10:1) Madyererowo ankachitira chithunzi mmene cholinga cha Yehova kwa Mbewuyo chidzakwaniritsidwire. Kuchita madyerero amenewo kunabweretsa chimwemwe chachikulu mu Isiraeli. Kukambirana mwachidule za madyererowa kulimbitsa chikhulupiriro chathu choti malonjezo a Yehova ndi odalirika.

Mbewuyo Ionekera

3. Kodi Mbewu yolonjezedwa inali ndani, ndipo chitende chake chinalaliridwa motani?

3 Patatha zaka zoposa 4,000 kuchokera pamene Yehova ananena ulosi wake woyambirira, Mbewu yolonjezedwayo inaonekera. Mbewuyo inali Yesu. (Agalatiya 3:16) Monga munthu wangwiro, Yesu anakhala wokhulupirika mpaka imfa, choncho anasonyeza kuti zimene Satana ananena zinali zabodza. Kuwonjezera apo, popeza Yesu anali wopanda uchimo, imfa yake inali nsembe ya mtengo wapatali. Ndi nsembe imeneyo, Yesu anamasula mbadwa zokhulupirika za Adamu ndi Hava ku uchimo ndi imfa. Imfa ya Yesu pa mtengo wozunzikirapo ndiko kunali ‘kulaliridwa chitende’ kwa Mbewu yolonjezedwayo.​—Aheberi 9:11-14.

4. Kodi nsembe ya Yesu inachitiridwa chithunzi motani?

4 Yesu anafa pa Nisani 14, mu 33 C.E. * Mu Isiraeli, Nisani 14 linali tsiku lachisangalalo la madyerero a Pasika. Chaka chilichonse, pa tsiku limeneli mabanja ankadyera limodzi chakudya chomwe chinkaphatikizapo mwana wa nkhosa wopanda chilema. Mwa njira imeneyi, ankakumbukira ntchito imene magazi a mwana wa nkhosa anagwira pa kulanditsidwa kwa ana oyamba a Aisiraeli pamene mngelo wakupha anapha ana oyamba a Aiguputo pa Nisani 14, mu 1513 B.C.E. (Eksodo 12:1-14) Mwana wa nkhosa wa pa Pasika anachitira chithunzi Yesu, amene ponena za iye mtumwi Paulo anati: “Khristu waperekedwa kale monga nsembe yathu ya pasika.” (1 Akorinto 5:7) Mofanana ndi magazi a mwana wa nkhosa wa pa Pasika, magazi a Yesu omwe anakhetsedwa amapulumutsa anthu ambiri.​—Yohane 3:16, 36.

‘Chipatso Choyamba cha Akufa’

5, 6. Kodi Yesu anaukitsidwa liti, ndipo kodi zimenezi zinachitiridwa chithunzi motani m’Chilamulo? (b) Kodi kuukitsidwa kwa Yesu kunachititsa bwanji kuti zikhale zotheka kuti lemba la Genesis 3:15 likwaniritsidwe?

5 Pa tsiku lachitatu, Yesu anaukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo kuti apereke mtengo wa nsembe yake kwa Atate wake. (Aheberi 9:24) Kuukitsidwa kwake kunachitiridwa chithunzi ndi chikondwerero china. Tsiku lotsatizana ndi Nisani 14 linali poyambira pa Madyerero a Mkate Wopanda Chotupitsa. Tsiku lotsatira, pa Nisani 16, Aisiraeli ankabweretsa mtolo wa zipatso zoyamba za zokolola za balele, zomwe zinali zokolola zoyambirira kwambiri mu Isiraeli, kuti wansembe aweyule pamaso pa Yehova. (Levitiko 23:6-14) Choncho n’zoyenerera kwambiri kuti m’chaka cha 33 C.E., pa tsiku lomwelo la Nisani 16, Yehova analepheretsa nkhanza zonse zimene Satana anali kuchita zofuna kupheratu “mboni yokhulupirika ndi yoona” ya Yehova. Pa Nisani 16, mu 33 C.E., Yehova anaukitsa Yesu kwa akufa n’kumupatsa moyo wosafa monga mzimu.​—Chivumbulutso 3:14; 1 Petulo 3:18.

6 Yesu anakhala “chipatso choyamba cha amene akugona mu imfa.” (1 Akorinto 15:20) Mosiyana ndi anthu ena amene anaukitsidwapo kale, Yesu sanafenso. M’malo mwake, anakwera kumwamba n’kukakhala ku dzanja lamanja la Yehova, kumene anadikira mpaka kuikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Yehova. (Salmo 110:1; Machitidwe 2:32, 33; Aheberi 10:12, 13) Kuyambira pamene anakhala Mfumu, Yesu tsopano akhoza kulalira mutu wa mdani wamkuluyo, Satana, n’kumupheratu ndiponso akhoza kuwononga mbewu yake.​—Chivumbulutso 11:15, 18; 20:1-3, 10.

Anthu Enanso a Mbewu ya Abulahamu

7. Kodi Madyerero a Masabata anali chiyani?

7 Yesu ndiye Mbewu imene inalonjezedwa mu Edene ndipo pogwiritsira ntchito mbewu imeneyi Yehova ‘adzawononga ntchito za Mdyerekezi.’ (1 Yohane 3:8) Komabe, pamene Yehova analankhula ndi Abulahamu, anasonyeza kuti “mbewu” ya Abulahamu idzakhala anthu ambiri, osati munthu mmodzi yekha. Anati idzakhala “monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.” (Genesis 22:17) Kuonekera kwa anthu enanso a “mbewu” imeneyo kunachitiridwa chithunzi ndi madyerero enanso osangalatsa. Pakatha masiku 50 kuchoka pa Nisani 16, Aisiraeli ankakondwerera Madyerero a Masabata. Lamulo lokhudza madyerero amenewa limati: “Muwerenge masiku makumi asanu kufikira tsiku lotsata sabata lachisanu ndi chiwiri; pamenepo mubwere nayo kwa Yehova nsembe ya ufa watsopano. Mutuluke nayo m’zinyumba zanu mikate iwiri ya nsembe yoweyula, ikhale ya awiri a magawo khumi a efa; ikhale ya ufa wosalala, yopanga ndi chotupitsa, zipatso zoyamba za Yehova.” *​—Levitiko 23:16, 17, 20.

8. Kodi pa Pentekosite wa mu 33 C.E. panachitika chinthu chapadera chotani?

8 Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, Madyerero a Masabata ankatchedwa Pentekosite (kuchokera ku mawu a Chigiriki otanthauza “cha chi 50”). Pa Pentekosite wa mu 33 C.E., Mkulu wa Ansembe wamkulu, Yesu Khristu woukitsidwayo, anatsanulira mzimu woyera pa gulu laling’ono la ophunzira 120 omwe anasonkhana mu Yerusalemu. Choncho ophunzira amenewo anakhala ana odzozedwa a Mulungu ndiponso abale ake a Yesu Khristu. (Aroma 8:15-17) Anakhala mtundu watsopano, “Isiraeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16) Kuyamba ndi anthu owerengeka, mtundu umenewo unali kudzakula mpaka kukwana anthu 144,000.​—Chivumbulutso 7:1-4.

9, 10. Kodi mpingo wa Akhristu odzozedwa unachitiridwa chithunzi motani pa Pentekosite?

9 Mpingo wa Akhristu odzozedwa unachitiridwa chithunzi ndi mikate iwiri ija yopanga ndi chotupitsa yomwe inkaweyulidwa pamaso pa Yehova pa Pentekosite aliyense. Popeza mikateyo inali yopanga ndi chotupitsa, inasonyeza kuti Akhristu odzozedwa adzakhalabe ndi chotupitsa cha uchimo wobadwa nawo. Komabe, akanatha kuyandikira kwa Yehova pa maziko a nsembe ya dipo ya Yesu. (Aroma 5:1, 2) N’chifukwa chiyani panali mikate iwiri? Zimenezo mwina zinkasonyeza mfundo yoti ana odzozedwa a Mulungu anadzachokera ku magulu awiri. Oyambirira anachokera mwa Ayuda enieni ndipo enawo anachokera mwa anthu Akunja.​—Agalatiya 3:26-29; Aefeso 2:13-18.

10 Mikate iwiri yomwe inkaperekedwa pa Pentekosite inkachokera ku zipatso zoyamba za zokolola za tirigu. Mofanana ndi zimenezo, Akhristu obadwa ndi mzimu amenewo amatchedwa “zipatso zina zoyamba za zolengedwa zake.” (Yakobe 1:18) Iwo ndi oyamba kukhululukidwa machimo awo pa maziko a magazi okhetsedwa a Yesu, ndipo zimenezo zimachititsa kuti zikhale zotheka kuti apatsidwe moyo wosafa kumwamba, kumene amalamulira ndi Yesu mu Ufumu wake. (1 Akorinto 15:53; Afilipi 3:20, 21; Chivumbulutso 20:6) Pa udindo wawo umenewo, tsiku lina posachedwapa “adzakusa [mitundu] ndi ndodo yachitsulo” ndipo adzaona ‘Satana atatswanyidwa pansi pa mapazi awo.’ (Chivumbulutso 2:26, 27; Aroma 16:20) Mtumwi Yohane anati: “Amenewa ndiwo amatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene apitako. Iwowa anagulidwa kuchokera mwa anthu, monga zipatso zoyamba zoperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.”​—Chivumbulutso 14:4.

Tsiku Logogomezera Chipulumutso

11, 12. (a) Kodi pa Tsiku la Chitetezo pankachitika zotani? (b) Kodi Aisiraeli ankapindula bwanji ndi nsembe za ng’ombe yamphongo ndi mbuzi ziwiri?

11 Pa tsiku lakhumi la mwezi wa Etanimu (umene kenaka unadzatchedwa Tishiri), * Aisiraeli ankakondwerera madyerero amene ankachitira chithunzi momwe nsembe ya dipo ya Yesu idzathandizire anthu. Pa tsiku limenelo, mtundu wonsewo unkasonkhana pamodzi kuti ukhale ndi Tsiku la Chitetezo pomwe anali kuwaperekera nsembe zophimba machimo awo.​—Levitiko 16:29, 30.

12 Pa Tsiku la Chitetezo, mkulu wa ansembe ankapha mwana wa ng’ombe wamphongo, ndipo ankalowa m’Malo Opatulikitsa n’kuwaza ena mwa magazi a ng’ombeyo kasanu ndi kawiri patsogolo pa chotetezera, kapena kuti chivundikiro cha Likasa. Kuchita zimenezi kunkaimira kupereka magaziwo pamaso pa Yehova. Nsembe imeneyo inali ya machimo a mkulu wa ansembeyo ndi “mbumba yake,” yomwe inali ansembe aang’ono ndi Alevi. Kenaka mkulu wa ansembeyo ankatenga mbuzi ziwiri. Imodzi ankaipha kuti ikhale nsembe yauchimo “yophera anthu.” Ena mwa magazi a mbuziwo nawonso ankawazidwa patsogolo pa chivundikiro cha Likasa m’Malo Opatulikitsa. Kenaka mkulu wa ansembe ankaika manja ake pa mutu wa mbuzi yachiwiriyo n’kuvomereza machimo a ana a Isiraeli. Akatero ankatumiza mbuziyo ku chipululu kuti itenge machimo a mtunduwo m’njira yophiphiritsira.​—Levitiko 16:3-16, 21, 22.

13. Kodi zochitika pa Tsiku la Chitetezo zinkachitira bwanji chithunzi ntchito ya Yesu?

13 Monga momwe zochitika zimenezo zinachitira chithunzi, Yesu, yemwe ndi Mkulu wa Ansembe wamkulu, amagwiritsa ntchito mtengo wa magazi ake opatsa moyo kuti anthu akhululukidwe machimo. Choyamba, mtengo wa magazi ake umagwiritsidwa ntchito pa “nyumba yauzimu” ya Akhristu odzozedwa okwana 144,000, ndipo zimenezi zimawachititsa kuti Yehova aziwayesa olungama komanso kuti aziwaona kuti ndi oyera. (1 Petulo 2:5; 1 Akorinto 6:11) Nsembe ya ng’ombe yamphongo inkachitira chithunzi zimenezi. Choncho njira inawatsegukira yoti akhoza kulandira cholowa chawo chakumwamba. Chachiwiri, mtengo wa magazi a Yesu umagwiritsidwa ntchito kuthandiza mamiliyoni ena a anthu amene amasonyeza chikhulupiriro mwa Khristu, monga momwe zinasonyezedwera ndi nsembe ya mbuzi. Amenewa adzapatsidwa moyo wosatha pa dziko lapansi lino, womwe ndi cholowa chomwe Adamu ndi Hava anataya. (Salmo 37:10, 11) Pa maziko a magazi ake okhetsedwa, Yesu amatenga machimo a anthu n’kuwachotsa, monga momwe mbuzi yamoyo ija inkatengera machimo a Aisiraeli m’njira yophiphiritsira n’kupita nawo kuchipululu.​—Yesaya 53:4, 5.

Kukondwera Pamaso pa Yehova

14, 15. Kodi n’chiyani chinkachitika pa Madyerero a Misasa, ndipo zimenezi zinkawakumbutsa chiyani Aisiraeli?

14 Pambuyo pa Tsiku la Chitetezo, Aisiraeli ankakhala ndi Madyerero a Misasa, omwe anali madyerero osangalatsa kwambiri kwa Ayuda pa chaka chonse. (Levitiko 23:34-43) Madyererowa ankachitika kuyambira pa tsiku la 15 mpaka pa tsiku la 21 m’mwezi wa Etanimu ndipo ankatha ndi msonkhano wopatulika pa tsiku la 22 la mweziwo. Madyererowa anali mapeto a nyengo yotuta zokolola ndipo inali nthawi yothokoza Mulungu chifukwa cha ubwino wake wochuluka. Pa chifukwa chimenecho, Yehova analamula anthu ochita madyererowo kuti: “Yehova Mulungu wako adzakudalitsa pa zokolola zako zonse ndi pa ntchito iliyonse ya dzanja lako, ndipo iwe uzikhala wosangalala basi.” (Deuteronomo 16:15, NW) Imeneyo iyenera kuti inalidi nthawi yachisangalalo!

15 Pa nthawi ya madyerero amenewa, Aisiraeli ankakhala m’misasa masiku 7. Choncho ankakumbutsidwa kuti pa nthawi inayake anakhalapo m’misasa m’chipululu. Madyererowa anawapatsa mwayi wabwino wosinkhasinkha za chisamaliro cha Yehova chofanana ndi cha tate. (Deuteronomo 8:15, 16) Ndipo popeza anthu onse, olemera kaya osauka, ankakhala m’misasa yofanana, Aisiraeliwo ankakumbutsidwa kuti onse anali ofanana pa nthawi ya madyerero amenewa.​—Nehemiya 8:14-16.

16. Kodi Madyerero a Misasa ankachitira chithunzi chiyani?

16 Madyerero a Misasa anali madyerero a pa nthawi yokolola, osangalalira kututa, ndipo anachitira chithunzi kututa kosangalatsa kwa anthu amene asonyeza chikhulupiriro mwa Yesu Khristu. Kututako kunayamba pa Pentekosite wa mu 33 C.E., pamene ophunzira 120 a Yesu anadzozedwa n’kukhala mbali ya “ansembe oyera.” Monga mmene Aisiraeli anakhalira m’misasa kwa masiku ochepa, odzozedwa amadziwa kuti ndi “alendo ndi osakhaliratu” m’dziko losaopa Mulunguli. Chiyembekezo chawo n’chokakhala kumwamba. (1 Petulo 2:5, 11) Kututa kwa Akhristu odzozedwa kumeneko kufika pamapeto pake “m’masiku otsiriza” ano, pamene omalizira a 144,000 akusonkhanitsidwa.​—2 Timoteyo 3:1.

17, 18. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti anthu enanso kuphatikiza pa Akhristu odzozedwa akupindula ndi nsembe ya Yesu? (b) Ndani panopa amene akupindula ndi Madyerero a Misasa ophiphiritsira ndipo kodi madyerero osangalatsa amenewa adzafika liti pachimake?

17 N’zochititsa chidwi kuti pa madyerero amenewa kalelo, ng’ombe zamphongo 70 zinkaperekedwa nsembe. (Numeri 29:12-34) Nambala ya 70 ikutanthauza 7 kuchulukitsa ndi 10, ndipo manambala amenewa m’Baibulo amaimira ungwiro wakumwamba ndi wa pa dziko lapansi. Choncho, nsembe ya Yesu idzathandiza anthu okhulupirika ochokera m’mabanja onse 70 amene anachokera kwa Nowa. (Genesis 10:1-29) Mogwirizana ndi zimenezo, mu nthawi yathu ino ntchito yotuta yakula n’kuphatikizapo anthu ochokera m’mitundu yonse amene amasonyeza chikhulupiriro mwa Yesu ndipo ali ndi chiyembekezo chodzakhala pa dziko lapansi la paradaiso.

18 Mtumwi Yohane anaona kututa kwa masiku anoku m’masomphenya. Choyamba anamva chilengezo cha kusindikizidwa chizindikiro kwa anthu omalizira m’gulu la 144,000. Kenaka anaona “khamu lalikulu limene munthu sanathe kuliwerenga,” litaima pamaso pa Yehova ndi Yesu, “nthambi za kanjedza zili m’manja mwawo.” Amenewa ‘anatuluka m’chisautso chachikulu’ n’kulowa m’dziko latsopano. Nawonso panopa ndi alendo osakhalitsa m’dongosolo lakale la zinthuli, ndipo akuyembekezera ndi chikhulupiriro nthawi imene “Mwanawankhosa . . . adzawaweta ndi kuwatsogolera ku akasupe a madzi a moyo.” Pa nthawi imeneyo, “Mulungu adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo.” (Chivumbulutso 7:1-10, 14-17) Madyerero a Misasa ophiphiritsirawo adzafika pachimake pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, pamene a khamu lalikulu limodzi ndi anthu okhulupirika oukitsidwa adzapatsidwe moyo wosatha.​—Chivumbulutso 20:5.

19. Kodi timapindula bwanji tikaganizira za madyerero omwe ankachitika mu Isiraeli?

19 Nafenso tikhoza ‘kukhala osangalala’ kwabasi tikamasinkhasinkha za tanthauzo la madyerero akale a Ayuda. N’zosangalatsa kwambiri kuona kuti Yehova anapereka zinthu zochitira chithunzi mmene ulosi wake womwe unanenedwa kalekale mu Edene udzakwaniritsidwire, ndipo n’zochititsa chidwi kwambiri kuona ulosiwu ukukwaniritsidwa pang’onopang’ono. Panopa, tikudziwa kuti Mbewu inaonekera ndipo inalaliridwa chitende. Tsopano Mbewuyo ndi Mfumu yakumwamba. Kuwonjezera apo, ambiri mwa a 144,000 asonyeza kale kukhulupirika kwawo mpaka imfa. Kodi n’chiyani chatsala kuti chichitike? Kodi kwatsala nthawi yaifupi motani kuti ulosiwo udzakwaniritsidwe wonse? Tikambirana zimenezi mu nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mwezi wa Nisani umafanana ndi miyezi ya March ndi April pa kalendala yathu masiku ano.

^ ndime 7 Pa nsembe yoweyula ya mikate iwiri yopanga ndi chotupitsa, nthawi zambiri wansembe ankanyamula mikateyo pa zikhato zake, kenaka ankakweza manja ake m’mwamba, ndipo ankayendetsa mikateyo uku ndi uko. Kuyendetsa kumeneku kunkaimira kupereka zinthu zoperekedwa nsembezo kwa Yehova.​—Onani buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, tsamba 528, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 11 Mwezi wa Etanimu, kapena kuti Tishiri, umafanana ndi miyezi ya September ndi October pa kalendala yathu masiku ano.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi mwana wa nkhosa wa pa Pasika ankachitira chithunzi chiyani?

• Kodi Madyerero a Pentekosite anachitira chithunzi kututa kotani?

• Kodi ndi zochitika ziti za pa Tsiku la Chitetezo zimene zinasonyeza momwe nsembe ya dipo ya Yesu idzagwiritsidwire ntchito?

• Kodi Madyerero a Misasa anachitira bwanji chithunzi kusonkhanitsidwa kwa Akhristu?

[Mafunso]

[Tchati pamasamba 22, 23]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Pasika

Nisani 14

Chochitika:

Mwana wa nkhosa wa pa Pasika anaphedwa

Chinachitira chithunzi

Yesu anaperekedwa nsembe

Madyerero a Mkate Wopanda Chotupitsa (Nisani 15-21)

Nisani 15

Chochitika:

Sabata

Nisani 16

Chochitika:

Kuperekedwa kwa balere

Chinachitira chithunzi

Kuukitsidwa kwa Yesu

Masiku 50

Madyerero a Masabata (Pentekosite)

Sivani 6

Chochitika:

Mikate iwiri inaperekedwa nsembe

Chinachitira chithunzi

Yesu anapereka abale odzozedwa ake kwa Yehova

Tsiku la Chitetezo

Tishiri 10

Chochitika:

Ng’ombe imodzi ndi mbuzi ziwiri zinaperekedwa nsembe

Chinachitira chithunzi

Yesu anapereka mtengo wa magazi ake m’malo mwa anthu onse

Madyerero a Misasa (Madyerero a Kututa, Chikondwerero cha Misasa)

Tishiri 15-21

Chochitika:

Aisiraeli ankakhala mosangalala m’misasa ndipo ankakondwerera kukolola, ng’ombe 70 zinkaphedwa

Chinachitira chithunzi

Kututa kwa odzozedwa ndi a “khamu lalikuru”

[Zithunzi patsamba 21]

Mofanana ndi magazi a mwana wa nkhosa wa pa Pasika, magazi a Yesu okhetsedwa amapulumutsa anthu ambiri

[Zithunzi patsamba 22]

Zipatso zoyamba za zokolola za balele zoperekedwa pa Nisani 16 zinkachitira chithunzi kuuka kwa Yesu

[Zithunzi patsamba 23]

Mikate iwiri yoperekedwa pa Pentekosite inkachitira chithunzi mpingo wa Akhristu odzozedwa

[Zithunzi patsamba 24]

Madyerero a Misasa ankachitira chithunzi kututa kosangalatsa kwa odzozedwa ndi a “khamu lalikulu” ochokera m’mitundu yonse